Kodi Mukukumbukira?
Kodi mwapindula powerenga magazini aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Tayesani kuyankha mafunso otsatirawa:
• Kodi n’chifukwa chiyani tifunika kusunga umphumphu wathu wachikhristu?
Kusunga umphumphu kumatithandiza kukhala ku mbali ya ulamuliro wa Yehova. Timachita zimenezi chifukwa timakonda Yehova ndiponso timafuna kutsimikizira kuti Satana ndi wabodza. Komanso Yehova amatiweruza mogwirizana ndi umphumphu wathu, choncho kusunga umphumphu n’kofunika kwambiri pa chiyembekezo chathu.—12/15, masamba 4-6.
• Kodi mayina ena osonyeza udindo wapadera wa Yesu pokwaniritsa cholinga cha Mulungu ndi ati?
Mwana wobadwa yekha. Mawu. Amen. Mkhalapakati wa chipangano chatsopano. Mkulu wa Ansembe. Mbewu yolonjezedwa.—12/15, tsamba 15.
• Kodi zimene Eliya anachita pouza mnyamata wake kuyang’ana kunyanja pamene iye ankapempherera mvula, zikusonyeza chiyani? (1 Maf. 18:43-45)
Zimenezi zikusonyeza kuti Eliya ankadziwa mmene madzi amayendera kuti afike pokhala mvula. Mitambo ikapangidwa pamwamba pa nyanja, imawombedwa ndi mphepo kupita kumtunda, kenako mitamboyo imabweretsa mvula.—1/1, masamba 15-16.
• Kodi tingachite chiyani kuti tizisangalala kwambiri ndi utumiki wathu?
Tiyenera kukonzekeretsa mitima yathu mwa kuganizira mmene tingathandizire bwino anthu. Tikamalalikira, tizikhala ndi cholinga choyambitsa maphunziro a Baibulo. Tikakumana ndi anthu opanda chidwi, tiyenera kusintha kalalikidwe kathu kuti tikope chidwi cha anthu a m’gawo lathu.—1/15, masamba 8-10.
• Kodi matenda a khate omwe amafotokozedwa m’Baibulo ndi ofanana ndi khate la masiku ano?
Matenda a khate analiko m’nthawi za m’Baibulo. (Lev. 13:4, 5) Baibulo limatchulanso khate limene linkapezeka m’zovala ndi m’nyumba. “Khate” limeneli liyenera kuti linali mtundu wina wa nkhungu. (Lev. 13:47-52)—2/1, tsamba 19.
• Kodi ziphunzitso za m’Baibulo ziyenera kukhudza bwanji maganizo komanso zochita za Mkhristu pa maliro?
Ngakhale kuti Mkhristu angalire okondedwa ake akamwalira, iye amadziwa kuti akufa sadziwa kanthu. Iye amapewa miyambo yokhudzana ndi chikhulupiriro chakuti akufa angathe kuthandiza kapena kuvulaza amoyo. Iye amapewa zimenezi ngakhale anthu osakhulupirira akumunena. Pofuna kupewa mavuto, Akhristu ena amalemba malangizo a mmene mwambo wa maliro awo udzayendetsedwere.—2/15, masamba 29-31.
• Malinga ndi Salmo 1:1, kodi ndi zinthu zitatu ziti zimene tiyenera kupewa kuti tikhale osangalala?
Vesili limatchula “uphungu wa oipa,” “njira ya ochimwa,” ndi “bwalo la onyoza.” Zoonadi, kuti tikhale osangalala, tiyenera kupewa anthu amene amanyoza kapena kunyalanyaza malamulo a Mulungu. M’malomwake, tiyenera kukondwera ndi chilamulo cha Yehova.—3/1, tsamba 17.
• Kodi “buku la Yasari” komanso “buku la Nkhondo za Yehova,” ndi mabuku a m’Baibulo amene anasowa? (Yos. 10:13; Num. 21:14)
Ayi. Zikuoneka kuti mabuku amenewa analipodi m’nthawi za m’Baibulo ndipo anatchulidwa ndi olemba Baibulo, koma sanali ouziridwa.—3/15, tsamba 32.
• Kodi ndi kusintha kwakukulu kotani komwe kunachitika pomasulira Baibulo la Chilatini lamakono?
Mu 1979, Papa Yohane Paulo Wachiwiri anavomereza Baibulo latsopano la Chilatini lotchedwa Nova Vulgata. Baibuloli litangotuluka, linali ndi dzina la Mulungu lakuti Iahveh m’malo ena. (Eks. 3:15; 6:3) Koma Baibuloli litakonzedwanso mu 1986, malo amene munali dzina lakuti Iahveh anaikamo dzina lakuti Dominus [Ambuye].—4/1, tsamba 22.