Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 4/15 tsamba 14-19
  • Yehova Amakwaniritsa Malonjezo Ake kwa Okhulupirika

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yehova Amakwaniritsa Malonjezo Ake kwa Okhulupirika
  • Nsanja ya Olonda—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chikhulupiriro Chenicheni m’Nthaŵi Zakale
  • Zotsatirapo za Kupanda Chikhulupiriro
  • Chikhulupiriro Chosonyezedwa m’Nthaŵi Yathu
  • Tsogolo Losangalatsa kwa Okhulupirika
  • Tsogolo Labwino Litsimikizirika
  • Dalirani Yehova Kuti Adzakwaniritsa Chifuno Chake
    Nsanja ya Olonda—1994
  • ‘Kuyenda mwa Chikhulupiriro Osati mwa Chionekedwe’
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Mtambo Waukulu Wotere wa Mboni!
    Nsanja ya Olonda—1987
  • “Limbitsani Mitima Yanu”
    Nsanja ya Olonda—1999
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1998
w98 4/15 tsamba 14-19

Yehova Amakwaniritsa Malonjezo Ake kwa Okhulupirika

“Wolonjezayo ali wokhulupirika.”​—AHEBRI 10:23.

1, 2. Kodi nchifukwa ninji tingakhulupirire kotheratu malonjezo a Yehova?

YEHOVA akupempha atumiki ake kuti akulitse ndi kusunga chikhulupiriro cholimba mwa iye ndi malonjezo ake. Ndi chikhulupiriro chimenecho, munthu angakhulupirire Yehova ndi mtima wake wonse kuti Iye adzachita zimene walonjeza kuchita. Mawu ake ouziridwa amati: “Yehova wa makamu walumbira, nati, Ndithu monga ndaganiza, chotero chidzachitidwa; ndipo monga ndapanga uphungu, chotero chidzakhala.”​—Yesaya 14:24.

2 Mawu akuti, “Yehova wa makamu walumbira,” akusonyeza kuti iye akulumbira kuchokera pansi pa mtima kuti adzakwaniritsa malonjezo ake. Nchifukwa chake Mawu ake amati: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; umlemekeze m’njira zako zonse, ndipo iye adzawongola mayendedwe ako.” (Miyambo 3:5, 6) Ngati tikhulupirira Yehova ndi kukhala ofunitsitsa kutsogozedwa ndi nzeru yake, mosalephera konse njira zathu zidzatitsogolera ku moyo wosatha, chifukwa chakuti nzeru ya Mulungu ndiyo “mtengo wa moyo wa akuigwira.”​—Miyambo 3:18; Yohane 17:3.

Chikhulupiriro Chenicheni m’Nthaŵi Zakale

3. Kodi Nowa anasonyeza motani kuti anakhulupirira Yehova?

3 Mbiri ya zimene Yehova anachita kwa anthu amene anali ndi chikhulupiriro chenicheni imachitira umboni za kudalirika kwake. Mwachitsanzo, zaka zoposa 4,400 zapitazo, Mulungu anauza Nowa kuti dziko la m’tsiku lake linali kudzawonongedwa ndi Chigumula cha dziko lonse. Iye anauza Nowa kuti amange chingalawa chachikulu kuti apulumutsiremo miyoyo ya anthu ndi nyama. Kodi Nowa anachitanji? Ahebri 11:7 akutiuza kuti: “Ndi chikhulupiriro Nowa, pochenjezedwa ndi Mulungu za zinthu zisanapenyeke, ndi pochita mantha, anamanga chingalawa cha kupulumutsiramo iwo a m’nyumba yake.” Kodi nchifukwa ninji Nowa anakhulupirira chinthu chimene chinali chisanachitikepo kumbuyoko, chinthu ‘chosapenyeka’? Chifukwa chakuti anadziŵa zimene Mulungu anachita kumbuyoko ndi fuko la anthu ndipo anazindikira kuti chilichonse chimene Mulungu anena chimachitikadi. Choncho Nowa anali ndi chidaliro chakuti Chigumula chinali kudzachitikadi.​—Genesis 6:9-22.

4, 5. Nchifukwa ninji Abrahamu anakhulupirira Yehova ndi mtima wake wonse?

4 Chitsanzo china cha chikhulupiriro chenicheni ndiye Abrahamu. Pafupifupi zaka 3,900 zapitazo, Mulungu anamuuza kuti apereke nsembe Isake, mwana yekhayo amene anabala mwa mkazi wake, Sara. (Genesis 22:1-10) Kodi Abrahamu anachitanji? Ahebri 11:17 amati: “Ndi chikhulupiriro Abrahamu, poyesedwa, anapereka nsembe Isake.” Komabe, panthaŵi yakuti tsopano achite zimenezo, mngelo wa Yehova anamletsa Abrahamu. (Genesis 22:11, 12) Nanga kodi nchifukwa ninji Abrahamu anavomera kuchita chinthu chotero? Chifukwa chakuti, malinga nkunena kwa Ahebri 11:19, anadziŵa “kuti Mulungu ngwokhoza kuukitsa [Isake], ngakhale kwa akufa.” Koma kodi Abrahamu anakhulupirira bwanji za chiukiriro pamene sanachionepo ndipo panalibe zolemba zakale zilizonse zonena za chiukiriro?

5 Kumbukirani kuti Sara anali ndi zaka 89 pamene Mulungu anawalonjeza mwana. Mimba ya Sara inali yoti singabale mwana​—inali yakufa, kunena kwake titero. (Genesis 18:9-14) Mulungu anautsa mimba ya Sarayo, ndipo anabala Isake. (Genesis 21:1-3) Abrahamu anadziŵa kuti pakuti Mulungu anakhoza kuutsa mimba ya Sara yakufayo, ndiye kuti Iye analinso wokhoza kuutsa Isake akanafuna kutero. Ponena za Abrahamu, Aroma 4:20, 21 amati: “Poyang’anira lonjezo la Mulungu sanagwedezeka chifukwa cha kusakhulupirira, koma analimbika m’chikhulupiriro, napatsa Mulungu ulemu, nakhazikikanso mumtima kuti, chimene Iye analonjeza, anali nayonso mphamvu ya kuchichita.”

6. Kodi Yoswa anasonyeza motani kuti anadalira Yehova?

6 Zaka zoposa 3,400 zapitazo pamene Yoswa anali ndi zaka zoposa zana limodzi zakubadwa, ndipo atadzionera m’moyo wake za kukhulupirika kwa Mulungu, anapereka chifukwa ichi cha chidaliro chake: “Mudziŵa m’mitima yanu yonse, ndi m’moyo mwa inu nonse, kuti pa mawu okoma onse Yehova Mulungu wanu anawanena za inu sanagwa padera mawu amodzi; onse anachitikira inu, sanasoŵapo mawu amodzi.”​—Yoswa 23:14.

7, 8. Kodi ndi ntchito yopulumutsa moyo iti imene anachita Akristu okhulupirika a m’zaka za zana loyamba, ndipo nchifukwa ninji?

7 Pafupifupi zaka 1,900 zapitazo, anthu ambiri odzichepetsa anasonyeza chikhulupiriro chenicheni. Iwo anazindikira mwa kukwaniritsidwa kwa ulosi wa m’Baibulo kuti Yesu analidi Mesiya ndipo anavomereza ziphunzitso zake. Pokhala ndi maziko olimba a zochitika zenizeni zimenezi ndiponso a Malemba Achihebri, anakhulupirira zimene Yesu anaphunzitsa. Choncho, pamene Yesu anauza otsatira ake kuti chiweruzo chaukali cha Mulungu chinali kudza pa Yudeya ndi Yerusalemu chifukwa cha kupanda chikhulupiriro kwawo, iwo anakhulupirira zimene ananena. Ndipo pamene anawauza zimene anayenera kuchita kuti apulumutse miyoyo yawo, anachita zimenezo.

8 Yesu anauza okhulupirira kuti pamene Yerusalemu anazingidwa ndi asilikali, anayenera kuthaŵa. Magulu ankhondo achiroma anafikadi kudzamenyana ndi Yerusalemu m’chaka cha 66 C.E. Komano pambuyo pake Aromawo anangochoka pachifukwa chosadziŵika. Chimenecho chinali chizindikiro kwa Akristu kuti achoke mumzindamo, chifukwa Yesu anali atawauza kuti: “Pamene paliponse mudzaona Yerusalemu atazingidwa ndi magulu a ankhondo, zindikirani pamenepo kuti chipululutso chake chayandikira. Pamenepo iwo ali m’Yudeya athaŵire kumapiri, ndi iwo ali mkati mwa uwo atuluke, ndi iwo ali kumiraga asaloŵemo.” (Luka 21:20, 21) Amene anali ndi chikhulupiriro chenicheni anatuluka m’Yerusalemu ndi m’madera ozungulira nathaŵira kumalo achisungiko.

Zotsatirapo za Kupanda Chikhulupiriro

9, 10. (a) Kodi atsogoleri achipembedzo anasonyeza motani kuti sanakhulupirire Yesu? (b) Kodi zotsatirapo za kupanda chikhulupiriro kumeneko zinali zotani?

9 Kodi aja opanda chikhulupiriro chenicheni anachitanji? Sanathaŵe pamene anali ndi mpata wochita zimenezo. Anaganiza kuti atsogoleri awo adzawapulumutsa. Komatu atsogoleri amenewo ndi atsatiri awo nawonso anauona umboni wakuti Yesu analidi Mesiya. Nanga nchifukwa ninji sanakhulupirire zimene ananena? Chifukwa cha kuipa mtima kwawo. Zimenezi zinasonyezedwa kumbuyoko pamene anaona anthu wamba ambiri akupita kwa Yesu ataukitsa Lazaro. Yohane 11:47, 48 amati: “Ansembe aakulu ndi Afarisi anasonkhanitsa akulu [khoti lalikulu la Ayuda], nanena, Titani ife? Chifukwa munthu uyu [Yesu] achita zizindikiro zambiri. Ngati timleka Iye kotero, onse adzakhulupirira Iye; ndipo adzadza Aroma nadzachotsa malo athu ndi mtundu wathu.” Vesi 53 limati: “Chifukwa chake, kuyambira tsiku lomwelo anapangana kuti amuphe Iye.”

10 Chinali chozizwitsa chabwino chotani nanga chimene Yesu anachita​—kuukitsa Lazaro kwa akufa! Koma atsogoleri achipembedzowo anafuna kupha Yesu chifukwa chakuti anachita zimenezo. Kuipa mtima kwawo kwakukuluko kunasonyezedwanso pamene “ansembe aakulu anapangana kuti akaphe Lazaronso; pakuti ambiri a Ayuda anachoka chifukwa cha iye, nakhulupirira Yesu.” (Yohane 12:10, 11) Lazaro anali atangoukitsidwa kumene kwa akufa, koma ansembewo anafuna kuti iye afenso! Iwo sanasamale za chifuniro cha Mulungu kapena za ubwino wa anthu. Anali odzikonda, ongosamala za maudindo awo, ndi mapindu awo basi. “Anakonda ulemerero wa anthu koposa ulemerero wa Mulungu.” (Yohane 12:43) Koma anakhaula chifukwa cha kupanda chikhulupiriro kwawo. M’chaka cha 70 C.E., magulu ankhondo achiroma anabweranso ndi kudzawononga malo awo ndi mtundu wawo, ndipo ambiri a iwo anaphedwa.

Chikhulupiriro Chosonyezedwa m’Nthaŵi Yathu

11. Kuchiyambi kwa zaka za zana lino, kodi chikhulupiriro chenicheni chinasonyezedwa motani?

11 M’zaka za zana lino, pakhalanso amuna ndi akazi ambiri a chikhulupiriro chenicheni. Mwachitsanzo, kalelo kuchiyambi kwa ma 1900, anthu ambiri analingalira kuti adzakhala ndi tsogolo lamtendere, ndiponso losangalatsa. Panthaŵi imodzimodziyo, awo amene anaika chikhulupiriro mwa Yehova anali kulengeza kuti mtundu wa anthu unali pafupi kuyang’anizana ndi mavuto oipitsitsa. Zimenezo nzimene Mawu a Mulungu analosera mu Mateyu chaputala 24, 2 Timoteo chaputala 3, ndi malo enanso. Zimene anthu a chikhulupiriro amenewo ananena zinachitikadi, kuyambira mu 1914 ndi Nkhondo Yadziko I. Dziko linaloŵadi mu “masiku otsiriza” ndi “nthaŵi zoŵaŵitsa” zonenedweratuzo. (2 Timoteo 3:1) Kodi atumiki a Yehova anadziŵa motani zimene zinali kudzachitika m’dziko pamene ena sanadziŵe? Chifukwa chakuti monga Yoswa, iwo anali ndi chikhulupiriro chakuti palibe mawu alionse a Yehova amene adzapita pachabe.

12. Lerolino, kodi ndi lonjezo la Yehova liti limene atumiki ake amalikhulupirira kotheratu?

12 Lerolino, atumiki a Yehova amene amamkhulupirira iye, chiŵerengero chawo chafika pafupifupi mamiliyoni asanu ndi imodzi kuzungulira dziko lonse. Chifukwa cha umboni wa kukwaniritsidwa kwa mawu aulosi a Mulungu, iwo amadziŵa kuti posachedwapa Mulungu adzachotsa dongosolo la zinthu lachiwawa ndi loipali. Choncho iwo ali ndi chidaliro chakuti nthaŵi yayandikira pamene adzaona kukwaniritsidwa kwa 1 Yohane 2:17, amene amati: “Dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthaŵi yonse.” Atumiki a Yehova amakhulupirira ndi mtima wawo wonse kuti iye adzakwaniritsa lonjezo lake.

13. Kodi mungakhulupirire Yehova kufikira pati?

13 Kodi mungakhulupirire Yehova kufikira pati? Mungapereke moyo wanu wonse kwa iye! Ngakhale ngati mutaya moyo wanu tsopano pomtumikira, adzakubwezerani moyo wabwinopo pachiukiriro. Yesu akutitsimikizira kuti: “Ikudza nthaŵi, imene onse ali m’manda adzamva mawu ake, nadzatulukira.” (Yohane 5:28, 29) Kodi mukudziŵa dokotala aliyense, mtsogoleri wandale, wasayansi, wabizinesi, kapena munthu wina aliyense amene angachite zimenezo? Mbiri yawo ikusonyeza kuti sangathe. Yehova angathe, ndipo adzaterodi!

Tsogolo Losangalatsa kwa Okhulupirika

14. Kodi ndi tsogolo losangalatsa motani limene Mawu a Mulungu amalonjeza okhulupirika?

14 Yesu anafotokoza kuti dziko lapansi latsopano lidzakhalapodi mu Ufumu wakumwamba wa Mulungu, ndipo anati: “Odala ali akufatsa; chifukwa adzalandira dziko lapansi.” (Mateyu 5:5) Zimenezo zinagogomezera lonjezo la Mulungu lopezeka pa Salmo 37:29 lakuti: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.” Yesu atangokhala pang’ono kufa ndipo pamene wochita zoipa wina anasonyeza chikhulupiriro mwa iye, Yesu anati kwa munthu ameneyo: “Udzakhala ndi ine m’Paradaiso.” (Luka 23:43) Inde, monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, Yesu adzaukitsira munthu ameneyu ku moyo padziko lapansi ndi kumpatsa mwayi wa kukhala ndi moyo kosatha m’Paradaiso ameneyo. Lerolino, onse amene amakhulupirira Ufumu wa Yehova akhoza kuyembekezeranso kudzakhala m’Paradaiso pamene “[Mulungu] adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa.”​—Chivumbulutso 21:4.

15, 16. Kodi nchifukwa ninji moyo udzakhala wamtendere kwambiri m’dziko latsopano?

15 Tiyeni tilingalire zamtsogolo m’dziko latsopano limenelo. Yerekezerani kuti taloŵa kale m’dzikolo. Taona kale anthu okondwa akukhala pamodzi mwamtendere wochuluka. Iwo akuona zinthu zofanana ndi zimene zinafotokozedwa pa Yesaya 14:7 kuti: “Dziko lonse lapuma, lili du; iwo ayamba kuimba nyimbo.” Nchifukwa ninji akuchita zimenezi? Chifukwa china nchakuti, onani kuti zitseko za nyumba zawo zilibe maloko. Ali osafunika, pakuti kulibenso upandu kapena chiwawa. Zangofanana ndendende ndi mmene Mawu a Mulungu ananenera kuti: “Adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwaopsa.”​—Mika 4:4.

16 Kulibenso nkhondo, pakuti lamulo la dzikoli sililola nkhondo. Zida zonse zasulidwa kukhala zipangizo zogwirira ntchito zamtendere. Yesaya 2:4 wakwaniritsidwa m’lingaliro lenileni, amene amati: “Adzasula malupanga awo akhale zolimira, ndi nthungo zawo zikhale anangwape; mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.” Ndithudi nzimene timayembekezera zimenezo! Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti nzika zambiri za m’dziko latsopano limeneli zinaphunzira kuchita zimenezo pamene zinali kutumikira Mulungu m’dziko lakale.

17. Kodi ndi mikhalidwe iti imene idzakhalapo mu Ufumu wa Mulungu?

17 Chinanso chimene mukuona nchakuti kulibenso umphaŵi. Palibe aliyense amene akukhala m’chithando kapena amene wavala nsanza kapena wopanda nyumba. Aliyense ali ndi nyumba yabwino ndi malo osamalika bwino okhala ndi mitengo ndi maluŵa okongola. (Yesaya 35:1, 2; 65:21, 22; Ezekieli 34:27) Ndipo palibenso njala chifukwa chakuti Mulungu wakwaniritsa lonjezo lake lakuti padzakhala chakudya cha mwana alirenji kwa onse: “M’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pa mapiri.” (Salmo 72:16) Ndithudi, mwa chitsogozo cha Ufumu wa Mulungu, paradaiso waulemerero akufutukuka padziko lonse lapansi, monga momwedi Mulungu analinganizira kalekale mu Edene.​—Genesis 2:8.

18. M’dziko latsopano, kodi ndi zinthu ziti zimene sizidzaopsanso anthu?

18 Mukuzizwanso ndi thanzi limene aliyense ali nalo. Zili choncho chifukwa chakuti tsopano ali ndi matupi ndi maganizo angwiro. Palibenso matenda, zopweteka, kapena imfa. Palibe aliyense amene ali pampando wamawilo kapena wogona m’chipatala. Zonsezo zinapitiratu. (Yesaya 33:24; 35:5, 6) Ndithudi, palibenso nyama imene ili yoopsa, pakuti mwa mphamvu yake, Mulungu wazikhalitsa zamtendere!​—Yesaya 11:6-8; 65:25; Ezekieli 34:25.

19. Kodi nchifukwa ninji tsiku lililonse la m’dziko latsopano lidzakhala ‘lokondweretsa’?

19 Anthu okhulupirika a m’dziko latsopanoli akulitukula mochititsa kaso chotani nanga! Nyonga ndi maluso awo, ndiponso chuma cha dziko lapansi, akuzigwiritsira ntchito m’njira yabwino, osati yovulaza ena; kuthandizana, osati kupikisana. Ndiponso, aliyense amene mukumana naye ndi munthu amene mungamkhulupirire, chifukwa chakuti, monga momwe Mulungu analonjezera, onse ali ‘ophunzitsidwa ndi Yehova.’ (Yesaya 54:13) Popeza kuti aliyense akulamuliridwa ndi malamulo a Mulungu, ‘dziko lapansi ladzala ndi odziŵa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.’ (Yesaya 11:9) Kunena zoona, tsiku lililonse m’dziko latsopanoli muli ‘kukondwera,’ mofanana ndi kunena kwa Salmo 37:11.

Tsogolo Labwino Litsimikizirika

20. Kodi tiyenera kuchitanji kuti tidzakhale ndi tsogolo lamtendere?

20 Kodi tiyenera kuchitanji kuti tidzakhale nawo mtsogolo mwabwino chotero? Yesaya 55:6 akutiuza kuti: “Funani Yehova popezeka Iye, itanani Iye pamene ali pafupi.” Ndipo pamene tikumfunafuna, tiyenera kukhala ndi maganizo onenedwa pa Salmo 143:10 akuti: “Mundiphunzitse chokonda Inu; popeza Inu ndinu Mulungu wanga.” Awo amene amachita zinthu zimenezi angayende mowongoka pamaso pa Yehova m’masiku ano otsiriza ndipo angayembekezere tsogolo labwino. “Tapenya wangwiro, ndipo taona woongoka mtima! Pakuti kumatsiriziro ake a munthuyo kuli mtendere. Koma olakwa adzawonongeka pamodzi: matsiriziro a oipa adzadulidwa.”​—Salmo 37:37, 38.

21, 22. Kodi Mulungu akukonzanji lerolino, ndipo kodi maphunziro akuchitika motani?

21 Tsopano lino Yehova akupempha anthu a mumtundu uliwonse amene akufuna kuchita chifuniro chake kuti achitepo kanthu. Iye akuwakonza kukhala maziko a mtundu wa anthu wa m’dziko lake latsopano, monga momwe ulosi wa m’Baibulo unaneneratu kuti: “Masiku otsiriza [m’nthaŵi imene tikukhalamo], . . . anthu ambiri adzanka, nati, Tiyeni tikwere kunka ku phiri la Yehova [kulambira kwake koona kokwezeka] . . . Iye adzatiphunzitsa za njira zake, ndipo tidzayenda m’mayendedwe ake.”​—Yesaya 2:2, 3.

22 Chivumbulutso 7:9 chimafotokoza za ameneŵa kukhala “khamu lalikulu, . . . ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe.” Vesi 14 limati: “Ndiwo akutuluka m’chisautso chachikulu,” opulumuka pamapeto a dongosolo lilipoli. Maziko ameneŵa a dziko latsopano lerolino apangidwa ndi anthu pafupifupi mamiliyoni asanu ndi imodzi, ndipo atsopano ambiri akugwirizana nawo chaka chilichonse. Atumiki okhulupirika onsewa a Yehova akuphunzitsidwa mmene angadzakhalire m’dziko lake latsopano. Akuphunzira maluso auzimu ndi maluso ena ofunikira kusandutsa dzikoli kukhala paradaiso. Ndipo amakhulupirira kwambiri kuti Paradaiso ameneyo adzafikadi chifukwa chakuti “wolonjezayo ali wokhulupirika.”​—Ahebri 10:23.

Mfundo Zobwereza

◻ Kodi kupanda chikhulupiriro kunali ndi zotsatirapo zotani m’zaka za zana loyamba?

◻ Kodi atumiki a Mulungu angamkhulupirire kufikira pati?

◻ Kodi anthu okhulupirika akuyembekezera tsogolo lotani?

◻ Kodi tiyenera kuchitanji kuti tidzakhale ndi tsogolo lachimwemwe m’dziko latsopano la Mulungu?

[Chithunzi patsamba 18]

Tsopano lino Yehova akukonza maziko a mtundu wa anthu wa m’dziko latsopano

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena