Kodi Dziko Lapansi Lidzawonongedwa?
ZAKA za zana la 20 zili pafupi kutha, ndipo zaka za zana la 21 zili pafupi kuyamba. Chifukwa cha zimenezi, anthu ochuluka amene sakanasamala kwenikweni za maulosi onena za chiwonongeko akusinkhasinkha ngati posachedwapa kudzachitika chinthu chowonongeratu dziko lapansi.
Mwina mwaonapo nkhani za m’ma nyuzipepala kapena m’magazini zonena za zimenezi—ngakhale mabuku athunthu onena za nkhani imeneyi. Sitikudziŵa kuti zaka za zana la 21 zidzayamba ndi zochitika zotani. Anthu ena amanena kuti kufika kumapeto a chaka cha 2000 kwangokhala kumaliza chaka chimodzi basi (kapena mphindi imodzi, kuchokera mu 2000 kufika mu 2001) ndipo mwina sikudzakhala zochitika zazikulu. Ambiri akudera nkhaŵa kwambiri za mmene pulaneti lathu lidzakhalira mtsogolo kwambiri.
Ulosi wina umene ukutchulidwa kwambiri masiku ano ndiwo wakuti panthaŵi ina yake—kaya posachedwa pompa kapena mtsogolo kwambiri—pulaneti la Dziko Lapansi lidzawonongedwa kotheratu. Taonani maulosi angapo odetsa nkhaŵa ameneŵa.
M’buku lake lakuti The End of the World—The Science and Ethics of Human Extinction (Kutha kwa Dziko Lapansi—Sayansi Ndiponso Njira ya Kutha kwa Anthu), lomwe linafalitsidwa choyamba mu 1996, wolemba wake amene alinso wafilosofi John Leslie anafotokoza njira zitatu zimene moyo wa anthu ungathere padziko lapansi. Choyamba anafunsa kuti: “Kodi nkhondo ya zida za nyukiliya zokhazokha ndiyo ingakhale mapeto a fuko la anthu?” Kenako anawonjezera kuti: “Kwenikweni chimene chingachitike . . . chingakhale kutha chifukwa cha rediyeshoni: matenda a kansa, kufooka kwa mphamvu ya m’thupi yotetezera matenda moti matenda opatsirana adzakhala paliponse, kapena zilema zobadwa nazo zambirimbiri. Ndiponso tizilombo tofunika kuti malo okhala akhale abwino tingadzafe.” Njira yachitatu imene a Leslie akutchula ndiyo yakuti dziko lapansi lingadzaombane ndi nyenyezi zotchedwa kuti makometi kapena kuombana ndi pulaneti lina laling’ono: “Pali makometi ndi mapulaneti aang’ono ngati zikwi ziŵiri a mtunda wa pakati pa kilomita imodzi ndi makilomita khumi ukulu wake ndipo mpita wawo ukuonetsa kuti tsiku lina angadzaombane ndi Dziko Lapansi. Palinso chiŵerengero chaching’ono kwambiri (kuyerekeza kungakhale kungolota) cha makometi ndi mapulaneti ameneŵa aakulu kwambiri, ndiponso chiŵerengero chachikulu kwambiri cha makometi ndi mapulaneti aang’ono.”
Mafotokozedwe Ochititsa Nthumanzi a “Tsiku Lachiwonongeko”
Kapena mvetserani wasayansi wina, Paul Davies, profesa wa pa Yunivesite ya Adelaide, ku Australia. Nyuzipepala ya Washington Times inamfotokoza kuti ndi “wolemba za sayansi waluso koposa kumbali zonse ziŵiri za nyanja ya Atlantic.” Mu 1994 analemba buku lakuti The Last Three Minutes (Mphindi Zitatu Zomalizira), limene latchedwa kuti “amayi wa mabuku onse onena za chiwonongeko.” Mutu woyamba wa buku limeneli ukutchedwa “Tsiku Lachiwonongeko,” ndipo limafotokoza chochitika choyerekezera cha zimene zingachitike ngati kometi itaombana ndi Dziko Lapansi. Taŵerengani mbali ina ya mafotokozedwe ake ochititsa nthumanzi:
“Pulaneti ligwedezeka ndi mphamvu ya zivomezi zikwi khumi. Mphepo yamphamvu yokankhidwa ndi kometi iomba dziko lapansi, kusalaza nyumba ndi zina zonse zomangidwa, kuphwanya kalikonse komwe kali m’njira yake. Mtunda wathyathyathya wozungulira malo pamene kometi yagwera uthuvuka makilomita angapo m’mwamba monga mapiri a miyala yosungunuka, kusiya dzenje lakuya kwambiri pa Dziko Lapansi ndiponso lamakilomita 150 tsidya ndi tsidya. . . . Mtambo waukulu wonga fumbi wa zidutswa uthuvuka mumlengalenga, kutsekereza kuunika kwa dzuŵa papulaneti lonse. Kuunika kwa dzuŵa tsopano kwaloŵedwa m’malo ndi kunyezimira kwa miyala mabiliyoni ambiri yowononga, imene itentha nthaka ndi moto wawo waukulu, pamene zinthu zomwe zinathuvukazo ziloŵanso mumlengalenga kuchokera kuthambo.”
Ndiyeno Profesa Davies anagwirizanitsa chochitika choyerekezera chimenechi ndi zomwe ena ananeneratu kuti kometi yotchedwa Swift-Tuttle idzaombana ndi dziko lapansi. Iye anawonjezerapo chenjezo lakuti ngakhale kuti chochitika ngati chimenechi sichingachitike posachedwapa, malinga ndi kapenyedwe kake “panthaŵi inayake Swift-Tuttle, kapena chinthu chofanana nacho, chidzagunda Dziko Lapansi.” Malingaliro akewa ngozikidwa pa ziŵerengero zoyerekezera zomwe zikusonyeza kuti zinthu 10,000 zofika pa theka la kilomita kufutukuka kwake kapena kuposapo zimadutsa mpita wa Dziko Lapansi.
Kodi mumakhulupirira kuti zinthu zochititsa mantha zimenezi zidzachitikadi? Chiŵerengero chodabwitsa cha anthu amakhulupirira. Koma sadera nkhaŵa chifukwa chakuti amadzilimbitsa mtima mwa kulingalira kuti sizidzachitika iwo adakali moyo. Koma kodi nchifukwa ninji pulaneti la Dziko Lapansi liyenera kuwonongedwa—posachedwapa kapena zaka zikwi zambiri mtsogolo? Ndithudi, si dziko lapansi lenilenilo limene likuvutitsa kwambiri okhalamo ake, anthu kapena nyama. M’malo mwake, kodi si anthu enieniwo amene akuchititsa mavuto ambiri a m’zaka za zana lino la 20, kuphatikizapo kufuna ‘kuwonongeratu dziko’?—Chivumbulutso 11:18.
Zowonongedwa Chifukwa cha Kusasamala kwa Munthu Zikonzedwanso
Bwanji nanga za chinthu chimene chingachitike mosavuta chakuti munthu weniweniyo angawonongeretu kapena kusakaza dziko lapansi mwa kusasamala kwake ndi umbombo wake? Nzachidziŵikire kuti magawo ena aakulu a dziko lapansi awonongedwa kale mwa kugwetsa mitengo yochulukitsitsa, kuipitsa mpweya mosalamulirika, ndi kuipitsa madzi. Zaka ngati 25 zapitazo, olemba mabuku Barbara Ward ndi René Dubos anazifotokoza bwino zimenezi mwachidule m’buku lawo lakuti Only One Earth (Dziko Lapansi Limodzi Lokha) kuti: “Mbali zitatu zazikulu zoipitsidwa zimene tiyenera kufufuza—mpweya, madzi, ndi nthaka—kwenikweni ndizonso mbali zitatu zofunika koposa kuti pulaneti lathu likhale ndi zamoyo.” Ndipo zinthu sizinawongokere kwenikweni chiyambire nthaŵiyo, sichoncho kodi?
Poganizira kuti munthu angawonongedi dziko lapansi mwa kupanda nzeru kwake, tingapeze chilimbikitso mwa kulingalira za mphamvu yodabwitsa yodzichiritsa ndi kudzikonzanso ya pulaneti la Dziko Lapansi. Pofotokoza za mphamvu yodzikonzanso yodabwitsa imeneyi, René Dubos ananena mawu olimbikitsawa m’buku lina lakuti The Resilience of Ecosystems (Kudzikonzanso kwa Chilengedwe):
“Anthu ambiri amaopa kuti kuyesa kutetezera malo okhala kuti asawonongeke kwayamba mochedwa kwambiri chifukwa chakuti zambiri zachilengedwe zimene zawonongeka sizingakonzeke. Pandekha ndikuona kuti kupanda chiyembekezo kumeneku nkosayenera chifukwa chakuti chilengedwe chili ndi mphamvu yaikulu yokonzanso zinthu zake zimene zinawonongeka kotheratu.
“Chilengedwe chimadzichiritsa mwa njira zingapo. . . . Njira zimenezi zimachititsa chilengedwe kuthetsa zotsatirapo za kuwononga mwa kungoyambitsanso pang’onopang’ono mkhalidwe woyamba wachilengedwe.”
Zingachitike
Chitsanzo chodziŵika bwino cha zimenezi m’zaka zaposachedwapa ndicho kuyeranso pang’onopang’ono kwa mtsinje wotchuka wa Thames, ku London. Buku lakuti The Thames Transformed (Kusinthanso kwa Thames), lolembedwa ndi Jeffery Harrison ndi Peter Grant, likusimba za chipambano chachikulu chimenechi chosonyeza zimene zingachitike pamene anthu agwira ntchito mogwirizana ndi cholinga chimodzi chabwino. Bwanamkubwa wa Edinburgh ku Britain analemba m’mawu ake oyamba a bukulo kuti: “Imeneyi tsopano ndi nkhani yaikulu kwambiri ya chipambano moti njoyenera kuifalitsa mosasamala kanthu kuti ingachititse anthu ena kuganiza kuti mavuto a kusunga zinthu zachilengedwe si aakulu kwambiri monga momwe ankaonera. . . . Iwo onse angalimbikitsidwe ndi zimene zinachitika ku Thames. Chosangalatsa nchakuti zingachitike ndiponso zochita zawo zingapambane.”
M’mutu wakuti “Kuyeretsa Kwakukulu,” Harrison ndi Grant akulemba mogwira mtima za zimene zachitidwa pazaka 50 zapitazo: “Kwa nthaŵi yoyamba padziko lapansi, mtsinje woipitsidwa kotheratu ndiponso wokhala ndi maindasitale ambiri wakhalanso bwino moti mbalame za m’dambo ndi nsomba zochuluka zabwerera ku mtsinjewo. Kusintha kofulumira kumeneku, kwa mkhalidwe umene poyamba unaoneka ngati wosatheka kuukonzanso kumapereka chilimbikitso ngakhale kwa osunga zachilengedwe amene anatayiratu chiyembekezo.”
Kenako iwo akusimba za kusinthako kuti: “Mtsinjewo unaipiraipira m’kupita kwa zaka, ndipo mwina kuipitsa kwakukulu komaliza kunadzachitika m’Nkhondo Yadziko Yachiŵiri pamene mipope yaikulu yotenga zakuchimbudzi inawonongedwa. Cha m’ma 1940 ndi m’ma 1950 mtsinje wa Thames unali utaipiratu. Mtsinjewo sunasiyane kwenikweni ndi mtaya weniweni wapoyera wa zakuchimbudzi; madzi ake anali akuda bi, analibe mpweya wa okosijeni, ndipo m’miyezi ya m’chilimwe, fungo loipa lochokera ku mtsinje wa Thames linali kumveka kumalo akutali. . . . Nsomba zambiri zomwe zinalimo zinatha, kungosiyapo zingapo zotchedwa eel zimene zinapulumuka chifukwa chakuti zimatha kupuma zili pamwamba pa madzi. Mbalame zimene zinali m’zigawo zowongoka za mtsinjewo zodutsa m’tauni zokhala ndi nyumba mmbali mwake pakati pa London ndi Woolwich zinachepa kwambiri ndipo kunangotsala mbalame zotchedwa mallard ndi mtundu wina wa akakoŵa, ndipo zinakhalabe kumeneko chifukwa cha dzinthu dzimene dzinali kutayikira m’madoko, osati chifukwa cha chakudya chawo chachibadwa. . . . Ndani panthaŵiyo akanakhulupirira za kubwezeretsedwa kwakukulu kumene kunali pafupi kuchitika? Pazaka khumi zigawo zimodzimodzizo za mtsinjewo zinali kudzasintha kuchokera pa malo opandiratu mbalame kukhala kothaŵira mitundu yambiri ya mbalame za m’dambo, kuphatikizapo mbalame zakuthengo ngati 10,000 ndi mbalame zomwe zimayenda m’madzi 12,000 zomwe zimabwera m’nyengo yachisanu.”
Inde, zimenezo zikufotokoza kusintha kwa malo amodzi okha m’dera limodzi laling’ono la dziko lapansi. Ngakhale zili motero, tingatengepo maphunziro pachitsanzo chimenechi. Chikusonyeza kuti anthu sayenera kuganiza kuti pulaneti la Dziko Lapansi lidzawonongedwa chifukwa cha kusasamala, umbombo, ndi kupanda nzeru kwa munthu. Maphunziro oyenera ndi kuyesayesa mogwirizana pacholinga chimodzi chopindulitsa mtundu wa anthu zingathandizire dziko lapansi kukonzanso ngakhale chilengedwe chake chimene chinawonongedwa kotheratu, malo okhala, ndi nthaka yake. Nanga bwanji za kuwonongedwa ndi mphamvu yochokera kwina, monga kometi kapena pulaneti ina yaing’ono yodziyendera?
Nkhani yotsatira ikupereka njira yopezera yankho lokhutiritsa la funso lovuta limeneli.
[Mawu Otsindika patsamba 5]
Maphunziro ndi kuyesayesa mogwirizana kungathandizire dziko lapansi kukonzanso zowonongedwa zake zazikulu