Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 7/1 tsamba 4-6
  • Chifukwa Chimene Ena Akusinthira Chipembedzo Chawo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chifukwa Chimene Ena Akusinthira Chipembedzo Chawo
  • Nsanja ya Olonda—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mayankho a Mafunso Ovuta
  • Kodi Cholinga cha Moyo Nchiyani?
  • Kupirira Mavuto a m’Moyo
  • Unansi Wathithithi ndi Mulungu
  • Chipembedzo Choona Nchopindulitsa!
  • Tinatembenukira ku Magwero a Chilungamo Chowona
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Kodi Mikayeli Mkulu wa Angelo Ndi Ndani?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Kodi Mikayeli Mkulu wa Angelo ndi Ndani?
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Kodi Yesu Amatchedwanso Mikayeli, Mkulu wa Angelo?
    Nsanja ya Olonda—2010
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1998
w98 7/1 tsamba 4-6

Chifukwa Chimene Ena Akusinthira Chipembedzo Chawo

Kwa anthu ambiri, chipembedzo changokhala chizindikiro chabe. Chingasonyeze kumene munthu amapita mwa apo ndi apo Lamlungu, kumene adzakwatira, ndiponso kumene adzaikidwa atamwalira. Koma sichinena mtundu wa munthu amene iye ali kapenanso zimene iye amadziŵa ndi kukhulupirira. Mwachitsanzo, pa kufufuza kwina anapeza kuti 50 peresenti ya odzitcha Akristu sanadziŵe munthu amene anapereka Ulaliki wa Paphiri. Komatu ngakhale mtsogoleri wotchuka wa ku India Mohandas Gandhi, Mhindu, anamdziŵa munthuyo!

KODI nzodabwitsa kuona anthu akusiya chipembedzo pamene kuli kwakuti ambiri a iwo amadziŵa zochepa zokhudza chikhulupiriro chawo? Ayi, nzosadabwitsa. Komabe, nthaŵi zina sangatero. Anthu amene avomera kuthandizidwa kuphunzira Baibulo nthaŵi zambiri amadabwa chifukwa chakuti limawapindulitsa kwambiri. Baibulo lenilenilo limati: ‘Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m’njira yoyenera iwe kupitamo.’​—Yesaya 48:17.

Kodi anthu amene adakali ndi njala yauzimu ayenera kuchitanji? Sayenera kusiya cholinga chawo chotumikira Mulungu! M’malo mwake, ayenera kuyang’ana m’Baibulo ndi kuona zimene Mulungu iyemwini adzawaonetsa.

Mayankho a Mafunso Ovuta

Pamene Bernd anali ndi zaka zisanu ndi ziŵiri zakubadwa, iye anaona amayi wake akumwalira.a Nthaŵi yonse imene anali wamng’ono, anali kudzifunsa kuti, ‘Kodi amayi wanga ali kuti? Bwanji ndikukula popanda iwo?’ Monga wachinyamata, Bernd anali kupita kutchalitchi mokangalika. Podera nkhaŵa za mavuto omwe anthu amayang’anizana nawo, iye anali ndi chiyembekezo chakuti tsiku lina adzakhala wantchito wopereka thandizo kumaiko ena. Komabe, iye anavutika ndi mafunso amene tchalitchi chake chinalibe mayankho ake okhutiritsa.

Kenaka Bernd analankhula kwa mnzake wapasukulu amene anali mmodzi wa Mboni za Yehova. Wachinyamata ameneyu anauza Bernd za m’Baibulo kuti amayi wake sadziŵa kalikonse, akugona mu imfa. Bernd anadziŵa mavesi ambiri a m’Baibulo omwe amafotokoza zimenezi, monga Mlaliki 9:5, yemwe amati: “Akufa sadziŵa kanthu bi.” Choncho, Bernd analibenso chifukwa chodandaulira kuti kaya amayi wake akuvutika mumkhalidwe winawake monga purigatoriyo​—kapena akuzunzika kwambiri kwinakwake. Ngakhale kuti chiphunzitso chakuti moyo sukufa chimapezeka m’zipembedzo zambiri, Bernd anaona kuti Baibulo limati moyo wa munthu ndiye munthu weniweniyo. Munthu atafa, moyowo umafa. “Moyo wochimwawo ndiwo udzafa.”​—Ezekieli 18:4.

Bernd anazindikiranso za chiyembekezo chosangalatsa kwambiri cha akufa. Anadziŵerengera m’buku la m’Baibulo la Machitidwe kuti: “Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.” (Machitidwe 24:15) Iye anachita chidwi chotani nanga pomwe anazindikira kuti chiukiriro chimenechi chidzachitikira pompano padziko lapansi, limene Mulungu adzalisandutsanso paradaiso!​—Salmo 37:29; Chivumbulutso 21:3, 4.

Posakhalitsa, njala yauzimu ya Bernd inathetsedwa ndi chidziŵitso chenicheni cha m’Baibulo. Bernd sanasiyiretu zachipembedzo. M’malo mwake, anasiya tchalitchi chomwe chinalephera kuthetsa njala yake ndipo anayamba kutsatira mtundu wachipembedzo chozikidwa kotheratu pa Baibulo. Iye anati: “Zimenezi zinachitika zaka 14 zapitazo, ndipo chiyambire nthaŵiyo sindinadandaulepo chifukwa cha zimene ndinachita. Tsopano ndikudziŵa kuti Mlengi sindiye amene amadzetsa mavuto. Satana ndiye mulungu wa dongosolo lino, ndipo ndiye amene amachititsa mavuto omwe amatigwera. Koma Mulungu posachedwapa adzakonza zonse zomwe zawonongeka ndi dziko la Satanali. Amayi wanganso adzaukitsidwa. Zimenezo zidzakhala zosangalatsa chotani nanga!”

Mwamwayi, Bernd wakwaniritsa cholinga chake cha kugwira ntchito yothandiza anthu m’maiko ena. Iye amagwira ntchito m’dziko lina kuthandiza ena kuphunzira za Ufumu wa Mulungu, chinthu chokhacho chomwe chidzathetsadi mavuto awo. Mofanana ndi Bernd, anthu mamiliyoni ambiri adziŵa kuti Mulungu adzathetsa mavuto omwe anthu akuyang’anizana nawo. Iwo azizwa kwambiri kuona kuti pali chipembedzo chimene chimathandiza kuthetsa njala yawo yauzimu.​—Mateyu 5:3.

Kodi Cholinga cha Moyo Nchiyani?

Pamene maiko a Kumadzulo akusumikabe maganizo kwambiri pa zinthu zakuthupi, anthu ambiri amafunsa kuti, ‘Kodi cholinga cha moyo nchiyani?’ Yankho lake limapezeka m’Baibulo, monga momwe Michael anaonera. Chapakati pa zaka za m’ma 1970, Michael analingalira zoloŵa m’gulu lina lachiwawa. Anali ndi cholinga chimodzi chokha pamoyo wake​—kulondalonda ndi kuthana ndi anthu amene anawalingalira kuti ndiwo anali kupangitsa kuti ulamuliro wachikapitolizimu ukhale wankhanza. “Nthaŵi zonse pochoka panyumba ndinkatenga mfuti,” iye anatero. “Cholinga changa chinali kupha akuluakulu ambiri andale ndi ochirikiza chikapitolizimu monga momwe ndingathere. Ndinafuna kuika moyo wanga pangozi kuti ndikwaniritse cholinga chimenechi.”

Michael ankapita kutchalitchi, koma palibe ndi mmodzi yemwe m’tchalitchi chake amene anafotokoza za cholinga chenicheni cha moyo. Choncho, pamene Mboni za Yehova zinafika panyumba pake ndi kumsonyeza mayankho a m’Baibulo a mafunso ake, Michael anamvetsera mwatcheru. Anayamba kupezeka pamisonkhano kukalambira pa Nyumba ya Ufumu yakwawoko ya Mboni za Yehova.

Mabwenzi ake a Michael anachita chidwi kwambiri chifukwa chakuti iye anayamba kusangalatsidwa ndi Baibulo. “Mubwere kumsonkhano Lamlungu lino,” Michael anawapempha motero. “Mutakakhalakhala, ngati zimene mukamve sizikakusangalatsani, mukabwerere kunyumba.” Zimenezo zinachitikadi. Nkhani yozikidwa pa Baibulo yamphindi 45 itatha, mabwenzi ake ambiri anatuluka m’nyumbamo. Koma mmodzi​—Susan​—anakhalira. Msungwanayu anachita chidwi ndi zimene anamva. Pambuyo pake, Michael ndi Susan anakwatirana ndipo anabatizidwa monga Mboni za Yehova. “Tsopano ndikudziŵa chifukwa chake tili pano padziko lapansi,” anatero Michael. “Tinalengedwa ndi Yehova. Cholinga chathu chenicheni pamoyo wathu ndicho kumdziŵa iye ndi kuchita chifuniro chake. Zimenezo ndizo zimadzetsa chikhutiro chenicheni!”

Anthu mamiliyoni ambiri alinso ndi chikhulupiriro chonga cha Michael. Iwo amagwiritsira ntchito mawu a m’Baibulo akuti: “Mawu atha, zonse zamveka zatha; opa Mulungu, musunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi.”​—Mlaliki 12:13.

Kupirira Mavuto a m’Moyo

Tonsefe tikuona kukwaniritsidwa kwa ulosi wopezeka pa 2 Timoteo 3:1 wakuti: “Masiku otsiriza zidzafika nthaŵi zoŵaŵitsa.” Palibe amene angathaŵe mavuto a “nthaŵi zoŵaŵitsa” zimenezi. Koma Baibulo limatithandiza kuti tipirire.

Talingalirani za Steven ndi Olive, okwatirana. Pamene anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, iwo, mofanana ndi enanso ambiri, anali ndi mavuto a pabanja. “Chikondi chathu chinali kutha pang’onopang’ono,” akufotokoza motero Steven. “Tinali ndi zolinga ndi zokonda zosiyana.” Kodi nchiyani chomwe chinawathandiza kuti apitirize kukhalira pamodzi? “Mboni za Yehova zinatisonyeza mmene tingagwiritsirire ntchito mapulinsipulo a Baibulo pamoyo wathu,” akupitiriza motero Steven. “Kwa nthaŵi yoyamba, tinadziŵa tanthauzo la kukhala wopanda dyera ndi kusamalira ena. Kugwiritsira ntchito mapulinsipulo a Baibulo kunatimangirira pamodzi. Tsopano tikusangalala ndi ukwati wachimwemwe ndi wokhazikika.”

Unansi Wathithithi ndi Mulungu

Malinga nkufufuza kwa Gallup kwa posachedwapa, 96 peresenti ya Aamereka amakhulupirira Mulungu, ndipo ambiri a ameneŵa amapemphera kwa iye. Komabe, pa kufufuza kwina kwapadera, anapeza kuti chiŵerengero cha opezeka kutchalitchi ndi kusunagoge tsopano chatsika kwambiri patapita chabe theka la zaka zana. Anapezanso kuti 58 peresenti ya Aamereka amanena kuti amapita kutchalitchi mwina kamodzi kokha pamwezi. Mwachionekere, chipembedzo sichinawayandikizitse kwa Mulungu. Ndipotu vuto limeneli silikupezeka ku United States kokha ayi.

Linda anakulira ku Bavaria. Anali Mkatolika wokangalika ndipo ankapemphera nthaŵi ndi nthaŵi. Panthaŵi imodzimodziyo, iye anali kuchita mantha ndi zimene zidzachitika mtsogolo. Sanadziŵe chilichonse ponena za zomwe Mulungu akufuna kuchitira anthu. Pamene anali ndi zaka 14 zokha zakubadwa, Linda anakumana ndi Mboni za Yehova, ndipo akuti: “Zimene ananena zinali zochititsa chidwi, choncho, ndinalandira zofalitsa zothandizira kuphunzira Baibulo ndipo nthaŵi yomweyo ndinaziŵerenga.” Patapita zaka ziŵiri, Linda anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. “Chilichonse chomwe ndinaphunzira ponena za Mulungu kuchokera m’Baibulo chinali chogwira mtima,” iye akutero. Linda anasiya tchalitchi chake ndipo anabatizidwa monga mmodzi wa Mboni za Yehova pausinkhu wa zaka 18.

Kodi nchiyani chomwe chinapangitsa Linda kusintha chipembedzo chake? Iye akufotokoza kuti: “Tchalitchi changa chinandithandiza kuzindikira kuti kuli Mulungu, ndipo ndinaphunzira kumkhulupirira. Koma sanali kusonyeza umunthu wake weniweni ndipo anali kutali kwambiri. Phunziro langa la Baibulo linalimbitsa chikhulupiriro changa mwa Mulungu ndiponso linandithandiza kuti ndimdziŵe ndi kumkonda. Tsopano ndili ndi unansi wathithithi wamtengo wapatali ndi Mulungu, chinthu chimene chili chopindulitsa kwambiri kuposa china chilichonse.”

Chipembedzo Choona Nchopindulitsa!

Kodi chipembedzo chanu chimakutsogolerani mwauzimu ndi kukusonyezani mmene Baibulo lingakuthandizireni kupirira mavuto a m’moyo? Kodi chimaphunzitsa chiyembekezo cha m’Baibulo chonena za mtsogolo? Kodi chimakupangitsani kukhala paunansi wathithithi ndi Mlengi, unansi wozikidwa pa chidziŵitso cholongosoka cha Baibulo? Ngati sichitero, musaleme. M’malo mosiyiratu zachipembedzo, funafunani mtundu wa kulambira wozikidwa kotheratu pa Baibulo. Mukadzatero mudzafanana ndi amene anatchulidwa mu ulosi wa m’buku la m’Baibulo la Yesaya kuti: “Atero Ambuye Yehova, Taonani atumiki anga adzadya . . . atumiki anga adzamwa . . . atumiki anga adzasangalala . . . atumiki anga adzaimba ndi mtima wosangalala.”​—Yesaya 65:13, 14.

[Mawu a M’munsi]

a Maina ena asinthidwa m’nkhani ino.

[Zithunzi pamasamba 4, 5]

Baibulo limatithandiza kudziŵa ndi kukonda Mulungu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena