Kodi Akusiyiranji Chipembedzo?
CHAPAKATI pa zaka za zana la 19, zinali zosatheka kwa munthu wokhala ku Prussia (tsopano kumpoto kwa Germany) kunena kuti alibe chipembedzo. Ndithudi, munthu atasiya chipembedzo chachikulu napita kutchalitchi champatuko anali kulondedwa ndi apolisi. Zinthu zasintha chotani nanga!
Lerolino, chiŵerengero chachikulu cha Ajeremani akusiya matchalitchi awo. Zamveka kuti munthu mmodzi mwa anayi alionse alibe chipembedzo. Zinthu zofananazo zikuchitikanso ku Austria ndi ku Switzerland. Ngati mamembala achipembedzo ndiwo magazi achipembedzocho, ndiye kuti, monga momwe ananenera wolemba wa ku Germany Reimer Gronemeyer, “Magazi a matchalitchi a ku Ulaya akuchucha mochititsa mantha.”
Chifukwa Chimene Akukanira Chipembedzo
Kodi nchifukwa ninji ambiri akukana chipembedzo cholinganizidwa? Kaŵirikaŵiri, nchifukwa chosoŵa ndalama, makamaka m’maiko amene mamembala amafunikira kupereka msonkho wa tchalitchi. Ambiri amafunsa kuti, ‘Ndikaperekerenji kutchalitchi ndalama zomwe ndinapeza movutikira?’ Ena akukana chifukwa chakuti tchalitchicho chili ndi chuma chambiri ndi mphamvu. Mwinamwake iwo amagwirizana ndi malingaliro a Kadinala Joachim Meisner wa ku Cologne, Germany, yemwe ananena kuti chuma cha tchalitchi chingasonkhezere tchalitchicho kuti chizidera nkhaŵa kwambiri zinthu zakuthupi ndipo “chingasiye kukhulupirira Kristu ndi mtima wonse.”
Anthu ena akusiya matchalitchi awo chifukwa chakuti ngotopetsa, osasangalatsa, osakhoza kuthetsa njala yawo yauzimu. Iwo akufa ndi njala yomwe inanenedweratu ndi mneneri Amosi kuti, “si njala ya mkate kapena ludzu la madzi, koma njala ya kumva mawu a Yehova.” (Amosi 8:11) Chifukwa chakuti amalandira chakudya chochepa kwambiri m’chipembedzo chawo, iwo amachisiya.
Pamene kuli kwakuti mavuto omwe amapezawo alidi enieni, kodi kungakhale kukhoza kusiyiratu zachipembedzo? Talingalirani za munthu wanjala amene waona chinthu chimene chikuoneka ngati mkate. Komabe, pamene ayamba kuchidya, akupeza kuti nchopangidwa ndi mfumbemfumbe za matabwa. Kodi iye angasiye malingaliro ake oti adye ndi kuthetsa njala yake? Ayi, adzafunafuna chakudya chenicheni. Mofananamo, ngati chipembedzo chikulephera kuthetsa njala yauzimu ya mamembala ake, kodi iwo ayenera kusiyiratu zachipembedzo? Kapena kodi iwo adzachita mwanzeru mwa kufunafuna njira ina yothetsera njala yawo yauzimu? Zimenezo nzimene ambiri achita, monga momwe nkhani yotsatira ikusonyezera.