Kulimbitsa Chidaliro Chathu mwa Chilungamo cha Mulungu
“Ndakudziŵitsa amenewo lero . . . kuti ukhulupirire Yehova.” —MIYAMBO 22:19.
1, 2. (a) Kodi nchifukwa ninji Mboni za Yehova zimadalira Yehova? (Miyambo 22:19) (b) Kodi nchiyani chomwe chikusonyeza kuti ena afunikira kulimbitsa chidaliro chawo mwa Yehova?
AKRISTU oona ngodala chifukwa chakuti ali ndi chidziŵitso cholongosoka cha Yehova ndi zolinga zake. “Kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amawapatsa mwachikondi “zakudya [zauzimu] panthaŵi yake.” (Mateyu 24:45) Chidziŵitso chimene iwo amapeza chili maziko olimba omangapo chidaliro chawo mwa Mulungu. Choncho, monga gulu, Mboni za Yehova zimadalira kwambiri Yehova ndi chilungamo chake.
2 Komabe, zikuonetsa kuti, monga munthu aliyense payekha, Mboni zina zifunikira kulimbitsa chidaliro chimenecho. Nthaŵi zina Sosaite imalandira makalata okayikira mafotokozedwe opezeka m’zofalitsa zake. Kukayikira kumeneku kungachitike chifukwa cha masinthidwe a kamvedwe, mwinanso angafotokoze za nkhani zimene zamkhudza, makamaka ngati sizinamkondweretse.—Yerekezerani ndi Yohane 6:60, 61.
3. Kodi nchiyani chomwe chingachitikire ngakhale atumiki okhulupirika a Yehova, ndipo nchifukwa ninji?
3 Ngakhale atumiki oona a Yehova amayang’anizana ndi zimene Mlaliki 9:11 amanena kuti: “Ndinabweranso ndi kuzindikira pansi pano kuti omwe athamanga msanga sapambana m’liŵiro, ngakhale olimba sapambana m’nkhondo, ngakhale anzeru sapeza zakudya, ngakhale ozindikira bwino salemera, ngakhale odziŵitsa sawakomera mtima; koma yense angoona zomgwera m’nthaŵi mwake.” Kodi zimenezi zingakhale zoona motani m’lingaliro lina kapena lauzimu? Mwina tikudziŵa Akristu amene anali achangu pogwiritsira ntchito uphungu wa m’Baibulo, amphamvu pochirikiza choonadi, anzeru pogwiritsira ntchito mapulinsipulo a m’Baibulo, ndiponso okangalika pofunafuna chidziŵitso cholongosoka. Komabe, chifukwa cha ‘zowagwera m’nthaŵi mwake,’ ena mwina angadzione kuti akulephera kuchita zambiri chifukwa cha ngozi kapena ukalamba. Iwo angakhale ndi nkhaŵa yakuti mwina sadzaloŵa amoyo m’dziko latsopano la Mulungu.
4, 5. Kodi nchifukwa ninji Akristu alibe chifukwa cholekera kudalira chilungamo cha Yehova?
4 Pamene mnzake wamuukwati amwalira, Mkristu amasweka mtima ndipo amaona kuti watayikiridwa. Iwo monga okwatirana, mwina anatumikira Yehova kwa zaka zambirimbiri. Wotsalayo amadziŵa kuti imfa imadula chomangira chaukwati.a (1 Akorinto 7:39) Ndiye pokana kuziralitsa chidaliro chake, iye ayenera kumalingalira modziletsa.—Yerekezerani ndi Marko 16:8.
5 Ndithudi, nkwanzeru kuona imfa ya mnzathu wamuukwati, kholo lathu, mwana wathu, kapena bwenzi lathu lapamtima lachikristu monga nthaŵi yosonyezera kuti timadalira chilungamo cha Yehova! Ngakhale ngati tafedwa ndife, tingakhale ndi chidaliro chakuti Yehova sali wosalungama. Tingakhale ndi chidaliro chakuti aliyense amene adzapeza moyo wosatha—kaya mwa kupulumuka kapena kuukitsidwa—adzasangalala. Ponena za Mulungu, wamasalmo anati: “Muoloŵetsa dzanja lanu, nimukwaniritsira zamoyo zonse chokhumba chawo. Yehova ali wolungama m’njira zake zonse, ndi wachifundo m’ntchito zake zonse. Yehova ali pafupi ndi onse akuitanira kwa Iye, onse akuitanira kwa Iye m’choonadi. Adzachita chokhumba iwo akumuopa; nadzamva kufuula kwawo, nadzawapulumutsa.”—Salmo 145:16-19.
Kulingalira Kuti Tinavutika Pazinthu Zachabe
6, 7. (a) Kodi nchifukwa ninji Mboni zina zomwe zinavutika kumbuyoko tsopano zingakhale ndi kamvedwe katsopano? (b) Kodi nchifukwa ninji sitiyenera kulingalira kuti Yehova sanachite chilungamo pamene analola anthu amenewo kuti avutike kalelo?
6 Kumbuyoko, Mboni zina zinavutika chifukwa chokana kuchita zinthu zimene mwina chikumbumtima chawo chikuwalola kuchita tsopano. Mwachitsanzo, mwina zaka zambiri zapitazo ena anapanga chosankha choti asamachite nawo mautumiki ena amene anthu a m’dzikomo amafunikira kuchita. Tsopano mwina mbale angalingalire kuti akanachita utumikiwo popanda kuswa uchete wake wachikristu m’dongosolo lino lazinthu.
7 Kodi tingati Yehova sanachite chilungamo pomulola kuti avutike chifukwa chokana zinthu zimene tsopano angachite popanda zovuta zilizonse? Ambiri amene anayang’anizanapo ndi zimenezo sangalingalire motero. M’malo mwake, iwo amasangalala kuti anali ndi mwayi wosonyezera poyera ndiponso moonekeratu kuti anali otsimikiza mtima kuchirimika pankhani yokhudza ufumu wachilengedwe chonse. (Yerekezerani ndi Yobu 27:5.) Kodi munthu angakhale ndi chifukwa chotani chodandaulira pamene chikumbumtima chake chinamsonkhezera kuchirimika kuti asangalatse Yehova? Mwa kutsatira mapulinsipulo achikristu mokhulupirika mogwirizana ndi kamvedwe kawo kapena mwa kutsatira zimene chikumbumtima chawo chinawauza, iwo anasonyeza kuti anali oyenerera kukhala mabwenzi a Yehova. Ndithudi, nkwanzeru kupeŵa kuchita zinthu zimene zingasokoneze chikumbumtima chathu kapena zimene zingakhumudwitse ena. Tingalingalirepo za chitsanzo chabwino chimene anasonyeza mtumwi Paulo.—1 Akorinto 8:12, 13; 10:31-33.
8. Kodi nchifukwa ninji Akristu achiyuda, amene kale anali kutsatira Chilamulo, analibe chifukwa chokayikirira za chilungamo cha Yehova?
8 Pofuna kusangalatsa Yehova, Ayuda anafunikira kumvera Malamulo Khumi ndi malamulo enanso owonjezera pafupifupi 600. Pambuyo pake, m’makonzedwe achikristu, kumvera malamulo ameneŵa sikunalinso kofunika potumikira Yehova, ngakhalenso kwa Ayuda akuthupi enieniwo. Malamulo amene sanalinso kugwira ntchito anaphatikizapo onena za mdulidwe, kusunga Sabata, kupereka nsembe za nyama, ndiponso kusala zakudya zina. (1 Akorinto 7:19; 10:25; Akolose 2:16, 17; Ahebri 10:1, 11-14) Ayuda—kuphatikizapo atumwi—amene anakhala Akristu sanafunikirenso kusunga malamulo amene anali kuwatsatira pamene anali m’pangano la Chilamulo. Kodi iwo anadandaula kuti makonzedwe a Mulungu anali osalungama chifukwa chakuti poyamba anafuna kuti iwo azichita zinthu zimene tsopano sizinalinso zofunika? Ayi, iwo anasangalala chifukwa chakuti chidziŵitso chawo cha zolinga za Yehova chinawonjezereka.—Machitidwe 16:4, 5.
9. Kodi nchiyani chomwe chachitikira Mboni zina, koma kodi nchifukwa ninji izo zilibe chifukwa chodandaulira?
9 M’nthaŵi zamakono, pali Mboni zina zimene zinali kuumirira kuchita zinthu zokhazo zogwirizana ndi chikumbumtima chawo. Choncho, izo zinazunzidwa kwambiri kuposa ena. Pambuyo pake, chidziŵitso chowonjezereka chinawathandiza kuzindikira kuti angachite zinthuzo. Koma iwo sakudandaula chifukwa cha zimene anachita kumbuyoko mogwirizana ndi chikumbumtima chawo, ngakhale kuti mwina zimenezi zinawapangitsa kuvutika kwambiri. Tikuyamikira kuti iwo anafunitsitsa kuvutika pofuna kusonyeza kuti ngokhulupirika pamaso pa Yehova, ‘kuchita zonse chifukwa cha Uthenga Wabwino.’ Yehova amadalitsa kudzipereka kwaumulungu kotero. (1 Akorinto 9:23; Ahebri 6:10) Mtumwi Petro analemba mwanzeru kuti: “Ngati pochita zabwino, ndi kumvako zoŵaŵa mumapirira, kumeneko ndiko chisomo pa Mulungu.”—1 Petro 2:20.
Kutengapo Phunziro Pazimene Zinachitikira Yona
10, 11. Kodi Yona anasonyeza motani kuti sanadalire Yehova (a) pamene anauzidwa kuti apite ku Nineve? (b) pamene Mulungu sanawononge Anineve?
10 Atamuuza kuti apite ku Nineve, Yona anasonyeza kuti sanadziŵe kuti Yehova anali kumdalira. Atakumana ndi mavuto amene anadza chifukwa cha kusafuna kutsatira zomwe anauzidwa, Yona anagalamuka nazindikira cholakwa chake, nalola kukatumikira kudziko lina, ndipo anachenjeza Anineve za chiwonongeko chomwe chinayandikira. Koma panachitika chinthu chomwe sanayembekezere: Chifukwa chakuti Anineve analapa, Yehova ananena kuti sadzawawononga.—Yona 1:1–3:10.
11 Kodi Yona anachitanji atamva zimenezi? Atakhumudwa, iye anadandaulira Mulungu m’pemphero. Kwenikweni iye anadandaula kuti: ‘Ndinadziŵa kuti zitere. Nchifukwa chake sindinafune kubwera kuno ku Nineve poyamba paja. Tsopano, pambuyo pa zonse zomwe ndayang’anizana nazo, kuphatikizapo kuvutika kwanga ndi kuchita manyazi chifukwa chomezedwa ndi nsomba yaikulu, ndiponso pambuyo pogwira ntchito yovuta yochenjeza Anineve za chiwonongeko chomwe chinayandikira, taonani zotsatirapo zake! Ndinagwira ntchito ndi kuvutika pachabe! Zingakhale bwino nditangofa!’—Yona 4:1-3.
12. Kodi tingaphunzireponji pazimene zinachitikira Yona?
12 Kodi Yona anali ndi chifukwa chomveka bwino chodandaulira? Kodi Yehova analakwa pamene anachitira chifundo ochita zoipa olapawo? Kunena zoona, Yona anafunikira kusangalala; anthu zikwi zambiri anapulumuka! (Yona 4:11) Koma kupanda ulemu ndi kudandaula kwake zinasonyeza kuti iye sanali kudalira kwenikweni chilungamo cha Yehova. Sanali kukonda ena monga momwe anali kudzikondera. Tiyeni tiphunzirepo pazimene zinachitikira Yona ndipo tizidera nkhaŵa ena osati kudzidera nkhaŵa ife eni. Tidziŵe kuti kumvera Yehova, kutsatira chitsogozo chake choperekedwa kudzera m’gulu lake ndi kumvera zosankha zake, ndizo zofunika kwambiri. Tikudziŵa kuti “omwe aopa Mulungu naopa pamaso pake adzapeza bwino.”—Mlaliki 8:12.
Ino Ndiyo Nthaŵi Yolimbitsa Chidaliro Chathu!
13. Kodi tonsefe tingalimbitse motani chidaliro chathu mwa Yehova?
13 Kulimbitsa chidaliro chathu mwa Yehova nkofunika. (Miyambo 3:5-8) Inde, tiyenera kuchita zambiri osati kungopemphera kwa Yehova kuti atithandize kukhala achidaliro. Chidaliro chimakula ngati chizikidwa pa chidziŵitso cholongosoka, choncho masiku onse tiyenera kumachita phunziro laumwini la Baibulo, kuŵerenga Baibulo lenilenilo pamodzi ndi zofalitsa zofotokoza Baibulo. Kupezeka pamisonkhano yachikristu nthaŵi zonse nkopindulitsa kwambiri, kuphatikizapo kukonzekera bwino ndi kutengamo mbali monga momwe tingathere. Chidaliro chathu mwa Yehova ndi Mawu ake chimakulanso ngati tizoloŵera kugaŵana choonadi cha Baibulo ndi ena, tikumafotokoza mwaluso nkhani zimene ena sakumvetsetsa. Tikatero tidzakhala tikuyenda naye tsiku ndi tsiku.
14. Kodi nchifukwa ninji anthu a Mulungu posachedwapa adzafunikira kusonyeza chidaliro chawo chachikulu mwa Yehova?
14 Posachedwapa, chisautso chachikulu chomwe sichinachitikepo nkale lonse mumtundu wa anthu chidzayamba modzidzimutsa. (Mateyu 24:21) Pamene chidzafika, atumiki a Mulungu adzafunikira kusonyeza chidaliro chachikulu mwa Yehova ndi chilungamo chake ndiponso kudalira chitsogozo choperekedwa ndi gulu lake. Mophiphiritsira, iwo adzamvera mwachidaliro malangizo a Mulungu akuti: “Idzani, anthu anga, loŵani m’zipinda mwanu, nimutseke pamakomo panu; nimubisale kanthaŵi kufikira mkwiyo utapita.” (Yesaya 26:20) Iwo aloŵa kale m’malo achisungiko m’mipingo yoposa 85,000 m’maiko 232. Zilizonse zimene mawu akuti “loŵani m’zipinda mwanu” angaloŵetsepo, tingakhale ndi chidaliro chakuti Yehova adzatithandiza kuzitsatira.
15. Kodi nkhani ya chidaliro yagogomezeredwa motani mu 1998, ndipo nchifukwa ninji zimenezo zili zoyenerera?
15 Nkofunika kuti tilimbitse chidaliro chathu tsopano lino. Ngati sitidalira abale athu achikristu, gulu la Yehova ndiponso, kwenikweni Yehova iyemwini, sitingathe kupulumuka. Choncho, kulidi koyenerera kuti mu 1998, Mboni za Yehova kuzungulira dziko lonse lapansi zakhala zikukumbutsidwa mwa mawu a lemba lawo lachaka kuti, “aliyense amene adzaitana padzina la Yehova adzapulumuka”! (Aroma 10:13, NW) Tiyenera kupitirizabe kukhala ndi chidaliro chimenechi. Ngati tizindikira kuti chidaliro chathu chikuzirala ngakhale pang’ono pokha, tiyenera kuyesetsa kuti tichikulitse tsopano lino, inde, lero lomwe.
Chiweruzo cha Yehova Chidzakhala Cholungama
16. Kodi nchiyani chomwe chingachitikire chidaliro ngati sichikulitsidwa, ndipo kodi ndi motani mmene tingapeŵere zimenezi?
16 Pa Ahebri 3:14, Akristu odzozedwa akuchenjezedwa kuti: “Takhala ife olandirana ndi Kristu, ngatitu tigwiritsa chiyambi cha kutama kwathu [“chidaliro chathu,” NW] kuchigwira kufikira chitsiriziro.” Pulinsipulo la mawu ameneŵa limagwiranso ntchito kwa Akristu amene ali ndi chiyembekezo cha padziko lapansi. Chidaliro chomwe tinali nacho poyamba chingazirale ngati sitichikulitsa. Nkofunika chotani nanga kuti tipitirizebe kufunafuna chidziŵitso cholongosoka, tikumalimbitsa maziko omangapo chidaliro chathu!
17. Kodi nchifukwa ninji tingakhale ndi chidaliro chakuti Yesu adzaweruza mwachilungamo populumutsa anthu?
17 Mitundu yonse ya anthu posachedwapa idzasanthulidwa ndi Kristu pamene iye “adzalekanitsa iwo wina ndi mnzake, monga mbusa alekanitsa nkhosa ndi mbuzi.” (Mateyu 25:31-33) Tingakhale ndi chidaliro chakuti Kristu adzaweruza mwachilungamo anthu amene adzayenerera chipulumutso. Yehova wampatsa nzeru, kuzindikira, ndi mikhalidwe ina yofunika kuti ‘aweruze dziko lokhalamo anthu m’chilungamo.’ (Machitidwe 17:30, 31) Tiyeni tikhale ndi chikhulupiriro chofanana ndi cha Abrahamu, yemwe anati: “Musamatero ayi [Yehova], kupha olungama pamodzi ndi oipa, kuti olungama akhale monga oipa; musamatero ayi; kodi sadzachita zoyenera Woweruza wa dziko lonse lapansi?”—Genesis 18:25.
18. Kodi nchifukwa ninji sitifunikira kudera nkhaŵa kwambiri za zimene sitingathe kuzidziŵa tsopano lino?
18 Ngati tidalira kwambiri chilungamo cha Yehova, sitifunikira kuvutika kuti tipeze mayankho a mafunso ena monga akuti: ‘Kodi makanda ndi ana aang’ono adzaweruzidwa motani? Kodi Armagedo siidzafika anthu ena ambiri asanamve uthenga wabwino? Nanga bwanji za anthu ozungulira mutu? Nanga bwanji za . . . ?’ Kunena zoona, pakali pano sitingadziŵe mmene Yehova adzayendetsera zinthu zimenezi. Komabe, iye adzaziyendetsa mwachilungamo ndiponso mwachifundo. Tisamakayikire zimenezo. Ndithudi, tingadzadabwe ndiponso kusangalala pamene mwina adzaziyendetsa m’njira imene sitinali kuyembekezera.—Yerekezerani ndi Yobu 42:3; Salmo 78:11-16; 136:4-9; Mateyu 15:31; Luka 2:47.
19, 20. (a) Kodi nchifukwa ninji sikulakwa kufunsa mafunso oyenera? (b) Kodi Yehova adzapereka liti mayankho ofunika?
19 Gulu la Yehova sililetsa mafunso oona mtima ndiponso a panthaŵi yake, monga momwe otsutsa ena amanenera. (1 Petro 1:10-12) Komabe, Baibulo limatilangiza kuti tiyenera kupeŵa mafunso opusa, ongoyerekezera. (Tito 3:9) Ngati tifunsa mafunso oyenera ndi kufufuza m’Mawu a Mulungu ndiponso m’zofalitsa zachikristu kuti tipeze mayankho a m’Malemba, tingakulitse chidziŵitso chathu cholongosoka chimene chingalimbitse chidaliro chathu mwa Yehova. Gululi limatsatira chitsanzo cha Yesu. Iye sankanenapo chilichonse pamafunso amene nthaŵi yake yoyankha inali isanakwane. Iye anati: “Ndili nazo zambirinso zakunena kwa inu, koma simungathe kuzisenza tsopano lino.” (Yohane 16:12) Anavomerezanso kuti zinthu zina sanazidziŵe panthaŵiyo.—Mateyu 24:36.
20 Yehova adakali ndi zambiri zoti avumbule. Choncho, nkwanzerudi kumuyembekezera, tikumakhala ndi chidaliro chakuti iye adzakwaniritsa zolinga zake panthaŵi yoyenera. Tingakhale ndi chidaliro chakuti pamene nthaŵi ya Yehovayo idzafika, tidzasangalala pamene tidzapeza chidziŵitso chowonjezereka cha njira zake. Inde, tidzafupidwa, malinga ngati tidalira kotheratu Yehova ndi gulu limene iye akugwiritsira ntchito. Miyambo 14:26 ikutitsimikizira kuti: “Wakuopa Yehova akhulupirira kolimba; ndipo ana ake adzakhala ndi pothaŵirapo.”
[Mawu a M’munsi]
a Onani Nsanja ya Olonda (yachingelezi) ya October 15, 1967, tsamba 638; ndi ya June 1, 1987, tsamba 30.
Kodi Mukutipo Bwanji?
◻ Kodi nchifukwa ninji kuli kosayenera kulola mmene tikumverera mumtima kuziralitsa chidaliro chathu mwa Yehova?
◻ Kodi tingaphunzireponji pazimene zinachitikira Yona?
◻ Kodi nchifukwa ninji phunziro la Baibulo ndi kupezeka pamisonkhano zili zofunika kwambiri?
[Chithunzi patsamba 16]
Ngakhale ngati tafedwa ndife, tingakhale ndi chidaliro chakuti Yehova ali wolungama
[Zithunzi patsamba 18]
Kodi mukutsimikiza kuti mumadalira Yehova?