Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 9/1 tsamba 22-23
  • Beteli—Mzinda wa Zabwino ndi Zoipa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Beteli—Mzinda wa Zabwino ndi Zoipa
  • Nsanja ya Olonda—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Beteli Akhala Pachimake pa Chipanduko
  • Kodi Ntchito Iyi Ingakhale Yabwino Kwambiri kwa Inu?
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Kupenya ndi Chiyamikiro pa “Nyumba ya Mulungu”
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Mukuitanidwa!
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Ntchito Zabwino Zimene Yehova Sangaziiwale
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2019
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1998
w98 9/1 tsamba 22-23

Beteli​—Mzinda wa Zabwino ndi Zoipa

MIZINDA ina imatchuka ndi zabwino​—kapena zoipa​—mogwirizana ndi zimene zimachitika mmenemo. Koma Beteli unali mzinda wosiyanako chifukwa chakuti unatchuka ndi zabwino ndi zoipa zomwe. Khololo Yakobo anatcha mzindawu kuti Beteli, dzina lomwe limatanthauza “Nyumba ya Mulungu.” Koma patapita zaka chikwi, mneneri Hoseya anatcha mzindawu kuti “Nyumba ya Zopweteka.” Kodi nchifukwa ninji mzindawu nthaŵi ina unali wabwino koma nthaŵi ina woipa? Ndipo kodi mbiri yake ingatiphunzitsenji?

Mbiri ya mzinda wa Beteli ndi anthu a Mulungu inayamba mu 1943 B.C.E., Abrahamu asanafe. Panthaŵiyo, mzindawo unali kutchedwa Luzi, dzina lake loyambirira lachikanani. Unali m’dziko lamapiri, pamtunda wa makilomita 17 kumpoto kwa Yerusalemu. Tayerekezerani kuti mukuona Abrahamu ndi Loti mwana wa mbale wake pamwamba pa limodzi mwa mapiri a ku Beteli akupenya dziko lachonde m’Chigwa cha Yordano. Abrahamu akuuza Loti mwaluso za mmene angagaŵanire malo odyetsako ziŵeto zawo, ndipo akuti: “Tisachite ndewu, ine ndi iwe, abusa anga ndi abusa ako: chifukwa kuti ife ndife abale. Dziko lonse silili pamaso pako kodi? Ulekanetu ndi ine: ukamka iwe kudzanja lamanzere, ine ndimka kudzanja lamanja: ukamka iwe kudzanja lamanja, ine ndimka kudzanja lamanzere.”​—Genesis 13:3-11.

Abrahamu sanagwiritsire ntchito ufulu wake woyambira kusankha. M’malo mwake, iye analola kuti mwana wa mbale wakeyo ndiye ayambe kusankha mbali imene anaikonda. Ifenso tingatsanzire chitsanzo cha Abrahamu chabwinochi. Tingathetse mikangano ngati tiyamba ndife kulankhula modekha ndi kuchita zinthu modzichepetsa.​—Aroma 12:18.

Patapita zaka zambiri pamene mdzukulu wa Abrahamu Yakobo anagonera pa Luzi, iye analota maloto achilendo. Iye anaona “makwerero anaima pansi, pamwamba pake ndipo padafikira kumwamba: ndipo, taonani, amithenga a Mulungu analinkukwera, analinkutsika pamenepo. Taonani, Yehova anaima pamwamba pake.” (Genesis 28:11-19; yerekezerani ndi Yohane 1:51.) Malotowo anali ndi tanthauzo lofunika. Amithenga amene Yakobo anaona anali kudzamthandiza kukwaniritsa lonjezo la Mulungu lonena za mbewu. Malo okwezeka a Yehova pamwamba pa makwererowo anasonyeza kuti iye adzauza amithengawo kuti agwire ntchito imeneyi.

Chitsimiziko chimenechi cha chichirikizo cha Mulungu chinamsonkhezera kwambiri Yakobo. Atadzuka kutuloko, iye anatcha malowo kuti Beteli, kutanthauza “Nyumba ya Mulungu,” ndipo iye analumbira kwa Yehova kuti: “La zonse mudzandipatsa ine, ndidzakupatsani inu limodzi la magawo khumi.”a (Genesis 28:20-22) Pozindikira kuti chilichonse chimene anali nacho chinachokera kwa Mulungu, iye anali wofunitsitsa kumbwezera mooloŵa manja posonyeza kuyamikira.

Lerolino palinso angelo amene amathandiza Akristu. (Salmo 91:11; Ahebri 1:14) Akristuwo angayamikirenso madalitso awo mwa kukhala ‘ooloŵa manja mwa chiyamiko cha kwa Mulungu.’​—2 Akorinto 9:11, 12.

M’kupita kwa nthaŵi, mbadwa za Yakobo zinasanduka mtundu. Mtsogoleri wawo Yoswa anagonjetsa mfumu yachikunja ya Beteli atangoyamba kumene kulanda Kanani. (Yoswa 12:16) M’nthaŵi za Oweruza, mneneri wamkaziyo Debora anali kukhala pafupi ndi Beteli ndipo anauza anthu mawu a Yehova. Samueli anali kukayenderanso Beteli moŵirikiza pamene anali kuweruza mtundu wa Israyeli.​—Oweruza 4:4, 5; 1 Samueli 7:15, 16.

Beteli Akhala Pachimake pa Chipanduko

Koma Beteli anasiyana ndi kulambira koyera Ufumuwo utagaŵanika mu 997 B.C.E. Mfumu Yerobiamu anakhazikitsa likulu la kulambira ana a ng’ombe pa Beteli, akumati mwana wa ng’ombeyo akuimira Yehova. (1 Mafumu 12:25-29) Nchifukwa chake, pamene anali kulosera za chiwonongeko cha Beteli, Hoseya anatchula malowa kuti anali “Betaveni,” dzina lotanthauza “Nyumba ya Zopweteka.”​—Hoseya 10:5, 8.

Ngakhale kuti Beteli anali likulu la zopweteka zauzimu, zinthu zomwe zinali kuchitika kumeneko zinali zoti tingatengerepo maphunziro opindulitsa. (Aroma 15:4) Limodzi mwa maphunziro amenewo nlonena za mneneri wosatchulidwa dzina lake amene anatumizidwa kuchokera ku Yuda kupita ku Beteli kukaneneratu za chiwonongeko cha maguwa a nsembe ndi ansembe ake. Yehova anamuuzanso kuti abwerere ku Yuda​—mtunda wa makilomita ochepa chakummwera​—osadya kalikonse kapena kumwa madzi. Mneneri ameneyu analosera molimba mtima pamaso pa Yerobiamu, mfumu ya Israyeli, kutemberera guwa la nsembe la Beteli. Koma kenaka mneneriyo sanamvere Mulungu mwa kudya chakudya m’nyumba ya mneneri wina wokalamba wokhala m’Beteli. Chifukwa ninji? Mneneri wokalambayo ananama kuti mngelo wa Yehova anamuuza kuti achereze mneneri mnzakeyo. Chifukwa cha kusamvera kwake, mneneri wa ku Yudayo anaphedwa mwadzidzidzi.​—1 Mafumu 13:1-25.

Ngati wokhulupirira mnzathu akutiuza kuti tichite chinachake chokayikitsa, kodi tingachitenji? Kumbukirani kuti ngakhale uphungu wokhala ndi cholinga chabwino ungakhale wovulaza ngati uli wolakwika. (Yerekezerani ndi Mateyu 16:21-23.) Mwa kufunafuna chitsogozo cha Yehova mwapemphero ndi kuphunzira Mawu ake, tidzapeŵa tchimo longa limene anachita mneneri wosadziŵikayo.​—Miyambo 19:21; 1 Yohane 4:1.

Patapita zaka pafupifupi 150, mneneri Amosi anapitanso kumpoto kukalosera motsutsana ndi Beteli. Amosi anadzudzula molimba mtima omvetsera ake okwiyawo, kuphatikizapo Amaziya wansembe, amene anauza Amosi mwaukali kuti ‘athaŵire kudziko la Yuda.’ Koma Amosi anauza Amaziya mopanda mantha za masoka amene anali kudzagwera nyumba ya wansembeyo. (Amosi 5:4-6; 7:10-17) Chitsanzo chake chikutikumbutsa kuti Yehova angawalimbitse mtima atumiki ake odzichepetsa.​—1 Akorinto 1:26, 27.

M’kupita kwa nthaŵi, Mfumu Yosiya ya Yuda yokhulupirikayo inagumula ‘guwa la nsembe linali ku Beteli, natentha msanje, naupondereza ukhale fumbi, natentha chifanizocho.’ (2 Mafumu 23:15, 16) Akulu lerolino angatsanzire chitsanzo chake chabwino mwa kuchita zonse zimene Mulungu akuwauza ndiponso mwa kutsogolera pakusunga mpingo kuti ukhale woyera.

Zochitika zimenezi za m’mbiri ya Beteli zikusonyeza bwino lomwe zotsatirapo za chilungamo ndi makhalidwe oipa, ndiponso zotsatirapo za kumvera ndi kusamvera Yehova. Zaka zambiri kumbuyoko, Mose anauza anthu a mumtundu wa Israyeli kuti adzipangire chosankha, ndipo anati: “Ndaika pamaso panu lerolino moyo ndi zokoma, imfa ndi zoipa.” (Deuteronomo 30:15, 16) Kulingalira mozama za mbiri ya Beteli kudzatilimbikitsa kuti tizichita zinthu mogwirizana ndi “Nyumba ya Mulungu,” malo a kulambira koona, m’malo mochita zinthu mogwirizana ndi “Nyumba ya Zopweteka.”

[Mawu a M’munsi]

a Yakobo ndiponso Abrahamu anali kupereka chakhumi modzifunira.

[Chithunzi patsamba 23]

Mabwinja pamene panali Beteli, kumene Yerobiamu anakhazikitsako likulu la kulambira ana a ng’ombe

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena