Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 10/1 tsamba 24-27
  • Ndinapeza Chinthu Choposa Golidi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndinapeza Chinthu Choposa Golidi
  • Nsanja ya Olonda—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zinthu Zinandisokoneza ku America
  • Kukumana ndi Achibale
  • Kukhala ndi Banja Ndiponso Maliro
  • Kuphunzira Choonadi
  • Kupeza Kumene Ndinabadwira
  • Kuika Choonadi Patsogolo
  • Kukumbukira Mlengi Wathu Kuyambira Paunyamata
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Kuyandikira kwa Mulungu Kunandithandiza Kulaka
    Galamukani!—1993
  • Kulera Ana Eyiti M’njira za Yehova Inali Ntchito Yovuta Komanso Yosangalatsa
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Kodi Ndingam’bwezere Chiyani Yehova?
    Nsanja ya Olonda—2009
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1998
w98 10/1 tsamba 24-27

Ndinapeza Chinthu Choposa Golidi

YOSIMBIDWA NDI CHARLES MYLTON

Tsiku lina Atate anati: “Titumize Charlie ku America kumene ndalama zimamera m’mitengo. Akhoza kupezako zina ndi kutitumizira kuno!”

KWENIKWENI, anthu ankaganiza kuti misewu ya ku America njagolidi. Moyo unali wosautsa kwadzaoneni m’masiku amenewo kummaŵa kwa Ulaya. Makolo anga anali ndi famu yaing’ono ndipo anali kuŵeta ng’ombe zingapo ndi nkhuku pang’ono. Tinalibe magetsi kapena mipope ya madzi m’nyumba. Komano, sindife tokha, anansi anthu onse analibenso.

Ndinabadwira ku Hoszowczyk pa January 1, 1893, zaka pafupifupi 106 zapitazo. Mudzi wathu unali ku Galicia, chigawo chimene panthaŵiyo chinali mu ufumu wa Austro-Hungary. Tsopano Hoszowczyk ili kummaŵa kwa Poland kufupi ndi maiko a Slovakia ndi Ukraine. Kumeneko, nyengo yachisanu inali kuzizira koopsa ndipo kunali kukhala chipale chofeŵa chochuluka kwambiri. Pamene ndinali ndi zaka ngati zisanu ndi ziŵiri, ndinali kuyenda mtunda wa theka la kilomita kukamtsinje ndi kukumba dzenje ndi nkhwangwa kuti nditungemo madzi. Madziwo ndinali kupita nawo kunyumba ndipo Amayi anali kuwagwiritsira ntchito pophika ndi kuyeretsa. Zovala anali kuzichapira kukamtsinjeko, akumagwiritsira ntchito miyala ikuluikulu ya madzi oundana monga pochapira.

Ku Hoszowczyk kunalibe sukulu, koma ndinaphunzira kulankhula Chipolishi, Chirasha, Chisilovaki ndi Chiyukireniya. Tinaleredwa m’tchalitchi cha Greek Orthodox, ndipo ndinali mnyamata wotumikira kuguwa. Ngakhale ndinali wamng’ono, ndinakhumudwabe ndi ansembe amene ankanena kuti tisamadye nyama Lachisanu pamene iwowo anali kudya.

Anzathu ena anali atabwerako ku United States komwe anapita kukagwira ntchito ndipo anabwera ndi ndalama zokonzera nyumba zawo ndi kugula makina olimira. Ndizo zinasonkhezera Atate kunena zonditumiza ku America ndi anansi athu ena amene anali kukonzekera ulendo wina wakomweko. Munali mu 1907 mmenemo pamene ndinali ndi zaka 14.

Zinthu Zinandisokoneza ku America

Posapita nthaŵi ndinali pasitima yapamadzi, ndipo patapita milungu iŵiri tinali titadutsa nyanja ya Atlantic. Panthaŵiyo, unayenera kukhala ndi ndalama zokwanira madola 20 kuti asakubweze kudziko lakwanu. Ndinali ndi ndalama ya siliva imene inali madola 20, choncho ndinakhala mmodzi mwa anthu mamiliyoni amene anadutsa pachisumbu chotchedwa Ellis Island, ku New York, khomo la America. Komano ndalama sizinamere m’mitengo, ndiponso misewu sinali yagolidi. Ndipotu yambiri inali yafumbi!

Tinakwera sitima yapamtunda yopita ku Johnstown, Pennsylvania. Amuna amene ndinali nawo anali kudziŵako kumeneko ndipo anali kudziŵa nyumba ina ya alendo yoti ndikakhalemo. Cholinga changa chinali chakuti ndikapeze mlongo wanga wamkulu amene anali kukhala ku Jerome, Pennsylvania, kumene pambuyo pake ndinadziŵa kuti ndi ulendo wa makilomita ngati 25 okha. Koma ndinali kunena kuti Yarome, m’malo mwa Jerome, chifukwa chakuti “J” m’chinenero chakwathu timamtchula ngati “Y.” Panalibe amene anamvapo za Yarome, ndinalidi m’dziko lachilendo, ndisakulankhula bwino Chingelezi ndiponso ndi ndalama zochepa.

Masiku onse mmaŵa ndinali kufunafuna ntchito. Pamizere yaitali panja pa ofesi yolemba antchito, anali kungotengapo anthu aŵiri kapena atatu. Choncho tsiku lililonse ndinali kubwerera kumene ndinali kukhala kukaphunzira Chingelezi mothandizidwa ndi mabuku ena ophunzitsa Chingelezi. Nthaŵi zina ndinali kupeza maganyu wamba, koma panapita miyezi yambiri, ndipo ndalama zanga zinali pafupi kutha.

Kukumana ndi Achibale

Tsiku lina ndinadutsa pafupi ndi hotela yokhala ndi bawa pafupi ndi siteshoni ya sitima ya pamtunda. Chakudya cha m’bawamo chinanunkhiradi bwino! Masangweji, buledi wasoseji pakati, ndi zokhwasula zina pabawapo zinali zaulere utagula moŵa, umene unali pamtengo wa masenti asanu tambula imodzi yaikulu. Ngakhale kuti ndinali ndisanakwanitsebe zaka zogula moŵa, wogulitsa m’bawamo anandimvera chisoni nandigulitsa moŵa.

Ndili kudya, amuna ena anabwera nati: “Fulumira, imwa msanga! Sitima yopita ku Jerome ikubwera.”

“Mukunena Yarome?” Ndinafunsa.

“Iyayi, Jerome,” anatero amunawo. Mpamene ndinadziŵa kumene mlongo wanga anali kukhala. Ndipotu pabawapo, ndinakumana ndi mwamuna wina amene anali kukhala pakhomo lachitatu kuchoka pakhomo la mlongo wanga! Choncho ndinagula tikiti ya sitimayo ndipo ndinampeza mlongo wanga pomalizira pake.

Mlongo wanga ndi mwamuna wake anali ndi nyumba ya alendo mmene munali kugona okumba malasha, ndipo ndinayamba kukhala nawo. Anandipezera ntchito yoyang’anira makina opopa madzi kuwatulutsa mumgodimo. Nthaŵi iliyonse makinawo atasiya kugwira ntchito, ndinali kupita kukaitana woikonza. Ndinali kulandirirapo ndalama zokwana masenti 15 patsiku. Kenako ndinagwira ntchito zapanjanji, ntchito youmba njerwa, ndiponso ngakhale ntchito yoimira kampani ya inshuwalansi. Pambuyo pake ndinasamukira ku Pittsburgh kumene Steve mbale wanga anali kukhala. Kumeneko, tinali kugwira ntchito m’nyumba yopangira zitsulo za steel. Sindinapangepo ndalama zokwanira zoti nkuzitumiza kwathu.

Kukhala ndi Banja Ndiponso Maliro

Popita kuntchito tsiku lina, ndinaona msungwana wina ataima kutsogolo kwa nyumba imene anali kugwirapo ntchito. Mumtima mwanga ndinati, ‘Komatu nchiphadzuŵa.’ Patapita milungu itatu, mu 1917, ineyo ndi Helen tinakwatirana. Pazaka khumi zotsatira, tinakhala ndi ana asanu ndi mmodzi, mwa amene mmodzi anamwalira adakali wakhanda.

Mu 1918 kampani ya sitima zapamtunda ya Pittsburgh Railways inandilemba ntchito yoyendetsa sitima ya mumzindamo. Pafupi ndi siteshoni ya sitimayo panali lesitilanti pamene tinali kumwa khofi. Mkatimo, amuna aŵiri achigiriki, eni malowo, sanali kusamala kuti kaya wagula chiyani, malinga atakulalikira za m’Baibulo. Ndinali kuwauza kuti: “Kodi mukutanthauza kuti dziko lonse lapansi nlolakwa ndipo inu nokha aŵiri ndinu amene muli olondola?”

“Iyayi, ziŵerengeni m’Baibulo!” anali kutero. Koma panthaŵiyo, analephera kundikhutiritsa.

Mwachisoni, mu 1928, Helen wanga wokondedwa anadwala. Kuti ana azisamaliridwa bwino, ndinawapereka ku Jerome kwa mlongo wanga ndi mwamuna wake kuti adzikakhala nawo. Panthaŵiyi anali atagula famu. Ndinali kuwachezera anawo kaŵirikaŵiri ndi kusiya ndalama zogulira chakudya chawo mwezi uliwonse. Ndinali kuwatumiziranso zovala. Mwachisoni, matenda a Helen anakula, ndipo pa August 27, 1930 anamwalira.

Ndinasungulumwa ndipo ndinasweka mtima. Nditapita kwa wansembe kukapanga makonzedwe a maliro, iye anati: “Sulinso m’tchalitchi chino. Sunapereke mtulo koposa chaka chimodzi.”

Ndinafotokoza kuti mkazi wanga anadwala kwa nthaŵi yaitali kwambiri ndi kuti ana anga ndinali kuwapatsa ndalama zotsala kuti azipereka kutchalitchi cha ku Jerome. Komabe, wansembeyo anavomera kutsogoza maliro nditakongola madola 50 kuti ndilipire ndalama zimene sindinalipire kutchalitchi. Wansembeyo anafunanso ndalama zina madola 15 kuti achititse Misa kunyumba kwa mlamu wanga wamkazi kumene mabwenzi ndi achibale anakonzekera kukumana kuti akapereke ulemu womaliza kwa Helen. Ndinalephera kupeza madola 15 amenewo, koma wansembeyo anavomera kuchititsa Misa kuti ndikampatse ndalamayo ndikakalandira.

Nditalandira ndinagwiritsira ntchito ndalamazo kugulira ana nsapato ndi zovala za kusukulu. Ndiyeno, patapita milungu pafupifupi iŵiri, wansembe uja anadzakwera m’sitima yanga. “Udakali ndi ndalama yanga ija madola 15,” anatero. Ndiyeno, potsika anandiopseza kuti, “Ndikupita kwa bwana wako kuti andipatse ndalamazo pamalipiro ako.”

Nditaŵeruka, ndinapita kwa bwana wanga ndi kumuuza zimene zachitika. Ngakhale kuti anali Mkatolika, iye anati, “Wansembe ameneyo akabwera kuno, ndidzamuuza mosabisa kuti khalidwe lake nloipa!” Mawuwo anandipatsa maganizo, ‘Ansembe amangofuna ndalama zathu, koma palibe zimene atiphunzitsa za m’Baibulo.’

Kuphunzira Choonadi

Pamene tsono ndinali m’lesitilanti ija ya amuna aŵiri achigiriki, tinakambitsirana zimene zinandichitikira ndi wansembe. Chotero, ndinayamba kuphunzira Baibulo ndi Ophunzira Baibulo, dzina la Mboni za Yehova panthaŵiyo. Ndinali kuŵerenga Baibulo ndi mabuku ofotokoza Baibulo usiku wonse. Ndinaphunzira kuti Helen sanali kuzunzika ku purigatoriyo, monga momwe wansembeyo anali atanenera, koma anali mtulo ta imfa. (Yobu 14:13, 14; Yohane 11:11-14) Ndithudi, ndinapeza chinthu choposa golidi​—chimenecho chinali choonadi!

Patapita milungu ingapo, posonkhana ndi Ophunzira Baibulo nthaŵi yoyamba pa Garden Theatre ku Pittsburgh, ndinatukula mkono ndi kunena kuti, “Ndaphunzira zochuluka ponena za Baibulo kuposa zimene ndaphunzira zaka zanga zonse ku tchalitchi.” Pambuyo pake, atafunsa za amene anafuna kuchita nawo ntchito yolalikira tsiku lotsatira, ndinatukulanso mkono.

Ndiyeno, pa October 4, 1931, ndinasonyeza kudzipatulira kwanga kwa Yehova mwa kubatizidwa m’madzi. Nthaŵi imeneyo ndinatha kuchita lendi nyumba ndi kutenganso ana anga kuti ndidzikhala nawo, nditalemba wantchito wowasamalira. Mosasamala kanthu za ntchito zanga za pabanja, kuyambira m’January 1932 mpaka m’June 1933, ndinachita nawo utumiki wapadera wotchedwa auxiliary (wothandiza), umene ndinkathera maola 50 mpaka 60 mwezi uliwonse kulankhula ndi ena za Baibulo.

Chapanthaŵiyi ndinayamba kuona mkazi wina wokongola amene anaoneka kuti nthaŵi zonse amakwera m’sitima yanga popita kuntchito kwake ndi pobwerako. Tinali kukumana maso m’galasi londisonyeza kumbuyo kwa sitima. Ndi mmene ineyo ndi Mary tinadziŵirana. Tinatomerana ndipo mu August 1936 tinakwatirana.

Pomadzafika mu 1949, chifukwa cha kukhalitsa kwanga pantchito, ndinatha kusankha nthaŵi ya ntchito imene inandipatsa mpata wochita upainiya, dzina la utumiki wanthaŵi zonse. Mwana wanga wamng’ono kwambiri wamkazi, Jean, anali atayamba upainiya mu 1945, ndipo tinachitira pamodzi upainiyawo. Pambuyo pake, Jean anadziŵana ndi Sam Friend, amene anali kutumikira pa Beteli, likulu la Mboni za Yehova ku Brooklyn, New York.a Anakwatirana mu 1952. Ndinapitirizabe upainiya ku Pittsburgh ndipo ndinali kuchititsa maphunziro a Baibulo ambiri, panthaŵi ina mabanja 14 mlungu uliwonse. Mu 1958, ndinapuma pantchito yanga yoyendetsa sitima. Pambuyo pake, kuchita upainiya kunali kosavuta, popeza kuti sindinali kugwiranso ntchito yamaola asanu ndi atatu patsiku.

Mu 1983, Mary anadwala. Ndinayesa kumsamalira monga momwe anandisamalirira bwino kwa zaka pafupifupi 50. M’kupita kwa nthaŵi, pa September 14, 1986, iye anamwalira.

Kupeza Kumene Ndinabadwira

Mu 1989, Jean ndi Sam ananditengera kumisonkhano yaikulu ku Poland. Tinapitanso kudera kumene ndinakulira. Arasha atalanda chigawo chimenecho cha dziko lapansi, iwo anasintha maina a matauni ake ndi kutumiza anthu a kumeneko kumaiko ena. Mmodzi mwa abale anga anali atatumizidwa ku Istanbul ndipo mlongo wanga wina ku Russia. Ndipo anthu amene tinali kufunsa sanalidziŵe dzina la mudzi wakwathu.

Kenako ndinazindikira mapiri ena amene anali chapatali. Pamene tinali kuyandikira, ndinazindikiranso zinthu zina​—phiri laling’ono, mphambanu ina ya njira, tchalitchi, mlatho wa pamtsinje wina. Mwadzidzidzi, tinaona chikwangwani chonena kuti “Hoszowczyk”! Posachedwapo, Akomyunisti anali atatha mphamvu, ndipo maina oyambirira a midzi anali atabwezeretsedwa.

Nyumba yathu kunalibenso, koma uvuni imene tinali kuigwiritsira ntchito pophikira panja inaliko, itakwiririka pansi mbali ina. Ndiyeno ndinaloza mtengo wina waukulu ndi kunena kuti: “Mwauona mtengowu. Ndinaudzala ndisanapite ku America. Taonani mmene wakulira!” Pambuyo pake tinapita kumanda, kufufuza maina a achibale, koma sitinapeze alionse.

Kuika Choonadi Patsogolo

Mwamuna wa Jean atamwalira mu 1993, Jean anandifunsa ngati ndikufuna kuti achoke pa Beteli kuti adzandisamalire. Ndinamuuza kuti kuchita zimenezo kungakhale kulakwa zedi, ndipo sindinasinthe malingaliro. Ndinakhala ndekha mpaka pamene ndinali ndi zaka 102 zakubadwa, komano ndinafunikira kusamutsidwira kunyumba yosungiramo okalamba ndi odwala. Ndidakali mkulu mu Mpingo wa Bellevue ku Pittsburgh, ndipo abale amadzanditenga kupita nane kumisonkhano ku Nyumba ya Ufumu pamasiku a Lamlungu. Ngakhale kuti sinditha kulalikira monga kale, ndidakali mmodzi mwa apainiya athanzi lofooka.

Pazaka zonsezi, ndasangalala ndi sukulu zapadera zophunzitsa oyang’anira zokonzedwa ndi Watch Tower Society. M’December chaka chatha, ndinapezekapo pazigawo zina za Sukulu ya Utumiki wa Ufumu ya akulu a m’mipingo. Ndiponso pa April 11 chaka chino, Jean ananditengera ku Chikumbutso cha imfa ya Kristu, chikumbutso chimene ndimasangalala kwambiri kutengamo mbali chaka chilichonse chiyambire 1931.

Ena mwa amene ndaphunzitsa Baibulo akutumikira monga akulu tsopano, ena ndi amishonale ku South America, ndiponso ena ali ndi adzukulu, ndipo akutumikira Mulungu ndi ana awo. Atatu mwa ana anga enieni​—Mary Jane, John, ndi Jean​—limodzi ndi ochuluka mwa ana awo ndi adzukulu awo akutumikira Yehova Mulungu mokhulupirika. Ndikungopemphera kuti tsiku lina mwana wanga wina wamkazi ndi adzukulu anga otsalawo ndi adzukulu tubzi adzachitenso chimodzimodzi.

Tsopano pamene ndili ndi zaka 105 zakubadwa, ndikulimbikitsabe aliyense kuphunzira Baibulo ndi kuuzako ena zimene aphunzira. Inde, ndatsimikizira kuti ngati umamatira kwa Yehova, sudzakhumudwa konse. Ndiye kuti inunso mungakhale ndi chinthu choposa golidi amene amawonongeka​—choonadi chimene chimatipangitsa kukhala paunansi wamtengo wapatali ndi Wotipatsa Moyo wathu, Yehova Mulungu.

[Mawu a M’munsi]

a Nkhani yosimba za moyo wa Sam Friend ili m’kope la Nsanja ya Olonda la August 1, 1986, masamba 22-6.

[Chithunzi patsamba 25]

Pamene ndinali kuyendetsa sitima

[Chithunzi patsamba 26]

Kunyumba yosungiramo okalamba kumene ndikukhala tsopano

[Chithunzi patsamba 27]

Chikwangwani chimene tinapeza mu 1989

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena