Kodi Mungalikhulupirire Baibulo?
ANTHU ambiri adakakhulupirirabe Baibulo, ngakhale m’dziko lino lamakono. Mwachitsanzo, pakufufuza kwa Gallup kofunsa Amereka malingaliro awo, 80 peresenti anati amakhulupirira kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu ouziridwa. Kaya chiŵerengero kudera lanu nchachikulu mofanana ndi chomwechi kapena chikusiyana, inu mukudziŵa kuti okhulupirira ngati amenewo amafuna kuphunzitsidwa Baibulo kutchalitchi. Koma nthaŵi zambiri sizimatero. Mwachitsanzo, titenge chiphunzitso chakuti mzimu umakalangidwa munthu akafa.
Kodi pali malo alionse m’Baibulo pamene limaphunzitsa za puligatoliyo kapena za helo wamoto? Lero, akatswiri ambiri m’Dziko Lachikristu amakana. New Catholic Encyclopedia imati: “Kwenikweni, chiphunzitso cha Akatolika chonena za puligatoliyo ndi chamwambo, si cha m’Malemba Opatulika.” Ponena za helo, A Dictionary of Christian Theology imati: “Mu NT [Chipangano Chatsopano], sitipezamo kuti moto wa helo uli mbali ya maulaliki oyambirira.”
Ndipotu bungwe lofufuza ziphunzitso losankhidwa ndi Church of England posachedwapa linamveka mbiri pamene linanena kuti achisiyiretu chiphunzitso cha moto wa helo. Dr. Tom Wright, mkulu wa Litchfield Cathedral, anatero kuti mafotokozedwe akumbuyoku onena za helo “anapangitsa Mulungu kuoneka ngati wolusa ndipo anasiya ambiri akuvutika maganizo.” M’lipoti lawo, a bungwelo ananena kuti helo “kulibiretu.”a Mofananamo, New Catholic Encyclopedia inati ponena za chikhulupiriro cha Akatolika: “M’maphunziro a zaumulungu lerolino, amanena kuti helo yangokhala kulekana ndi Mulungu.”
Kwenikweni, zimene Baibulo limaphunzitsa pankhani ya moyo wa pambuyo pa imfa zimasiyana ndi ziphunzitso za puligatoliyo ndi moto wa helo. Nthaŵi zambiri Baibulo limanena kuti moyo umafa. “Moyo wochimwawo ndiwo udzafa.” (Ezekieli 18:4; yerekezerani ndi Baibulo la King James ndi la Douay lachikatolika.) Malinga ndi Baibulo, akufa sadziŵa kanthu, samva kupweteka. “Amoyo adziŵa kuti tidzafa; koma akufa sadziŵa kanthu bi.” (Mlaliki 9:5) Chiyembekezo chimene Baibulo limapereka ponena za akufa nchakuti adzauka mtsogolo. Pamene Lazaro bwenzi la Yesu anamwalira, Yesu ananena kuti imfa ili ngati tulo. Marita mlongo wa Lazaro anatchula za chiyembekezo chimene Baibulo limaphunzitsa pamene anati: “Ndidziŵa kuti adzauka m’kuuka tsiku lomaliza.” Mwa kuutsa Lazaro kwa akufa, Yesu anatsimikiza chiyembekezo chimenecho cha anthu.—Yohane 5:28, 29; 11:11-14, 24, 44.
Olemba mbiri amatero kuti chiphunzitso chakuti munthu ali ndi mzimu wosafa wolekana ndi thupi chinatengedwa ku filosofi yachigiriki osati m’Baibulo ayi. New Catholic Encyclopedia imanena kuti Ahebri akale sanaganize zakuti munthu ali ndi thupi ndi chinachake chimene sichifa. Ponena za chikhulupiriro cha Ahebri imati: “Pamene mpweya wa moyo unaloŵa mwa munthu woyamba amene Mulungu anamuumba kuchokera ku nthaka, anakhala ‘munthu wamoyo’ (G[enesis] 2.7). Imfa sanaione monga kulekana kwa zinthu ziŵiri zimene zinali mwa munthu, malinga ndi filosofi yachigiriki; mpweya wa moyo umachoka ndipo iyeyo amakhala ‘munthu wakufa’ (L[evitiko] 21.11; N[umeri] 6.6; 19.13). Pamalo onse aŵiriwo liwulo ‘munthu’ m’Chihebri ndi [neʹphesh], limene nthaŵi zambiri amati ‘mzimu’ pamene kwenikweni limatanthauza munthu.”
Insaikulopediyayo ikuteronso kuti akatswiri achikatolika posachedwapa “anenetsa kuti NT [Chipangano Chatsopano] sichiphunzitsa za mzimu wosafa malinga ndi chikhulupiriro cha Ahelene [Agiriki].” Pomaliza ikuti: “Yankho lokha pavutoli si nthanthi zafilosofi koma mphatso yaumulungu ya Chiukiriro.”
Baibulo Kapena Mwambo?
Nanga zinatheka bwanji kuti zikhulupiriro zosakhala za m’Baibulo zipezeke m’ziphunzitso za tchalitchi? Matchalitchi ambiri amati Baibulo ndilo limawalamulira pazonse. Mwachitsanzo, si kale kwambiri pamene Papa John Paul II ananena zakuti Malemba afunikira kuti “okhulupirira aziwalandira monga choonadi chonse ndipo monga maziko opambana a chikhulupiriro chathu.” Komanso, ambiri amavomereza kuti ziphunzitso za Dziko Lachikristu lerolino sizifanana ndi zija za Akristu a m’zaka za zana loyamba. Matchalitchi ochuluka amaganiza kuti kusinthaku kuli mbali ya kutukuka kwa pang’onopang’ono kwa chiphunzitso cha tchalitchi. Ndiponso, Tchalitchi cha Katolika chimakhulupirira kuti miyambo ya tchalitchi ili ndi mphamvu yofanana ndi Malemba. New Catholic Encyclopedia ikuti tchalitchi “sichikhulupirira kuti choonadi chimapezeka m’Malemba okha, komanso m’mwambo, kapenanso kuti chimapezeka m’mwambo wokha, komanso m’Malemba.”
Malinga ndi mbiri yakale, matchalitchi achotsa ziphunzitso za m’Malemba natenga zija zochokera m’miyambo. Ndipotu matchalitchi ambiri tsopano akukhulupirira kuti ziphunzitso za m’Baibulo nzolakwa. Mwachitsanzo, New Catholic Encyclopedia ikuti “nzodziŵikiratu kuti mawu ambiri a m’Baibulo sali oona konse powayerekezera ndi chidziŵitso chamakono cha sayansi ndi mbiri yakale.” Ponena za chiphunzitso cha m’Baibulo chakuti akufa sadziŵa kanthu, ikuwonjeza kuti: “Ngakhale pankhani zachipembedzo, OT [Chipangano Chakale] chimapereka chidziŵitso chosakwanira cha . . . moyo wa pambuyo pa imfa.” Insaikulopediya imeneyo ikutchula Salmo 6:5 (m’mabaibulo ena ndi vesi 6) monga chitsanzo: “Muimfa m’mosakumbukira Inu: m’mandamo adzakuyamikani ndani?” M’maseminale ena ndi makoleji a Apulotesitanti anasiya kuphunzitsa kuti Baibulo nlosalakwa. Komanso, m’Tchalitchi cha Katolika amakhulupirira kuti iwo ndiwo ali ndi mphamvu yophunzitsa, yomasulira nayo zimene Baibulo limaphunzitsa. Komano mungafunse kuti, ‘Bwanji nanga ngati kumasulira kwawoko kukutsutsa Malemba?’
Kufunika Kwake kwa Malemba
Yesu mobwerezabwereza anagwira Malemba monga umboni wake. Nthaŵi zambiri ankayamba mfundo zake mwa kunena kuti: “Kwalembedwa.” (Mateyu 4:4, 7, 10; Luka 19:46) Inde, pamene Yesu analankhula za ukwati wa munthu, sanatenge mfundo zake pamaganizo afilosofi yachigiriki ayi, koma pankhani ya chilengedwe ya Genesis. (Genesis 1:27; 2:24; Mateyu 19:3-9) Mwachionekere, Yesu anakhulupirira kuti Malemba ali ouziridwa ndi Mulungu ndi kuti ali oona. Popemphera kwa Mulungu, anati: “Mawu anu ndi choonadi.”—Yohane 17:17.b
Baibulo limanena zimene Yesu anachita kutsutsa atsogoleri achipembedzo a panthaŵi yake motere: “Mukaniza lamulo la Mulungu, kuti musunge mwambo wanu. . . . Muyesa achabe mawu a Mulungu mwa mwambo wanu.” (Marko 7:6-13) Mofananamo, mtumwi Paulo anakana kusanganiza chiphunzitso chake ndi filosofi yachigiriki kapena miyambo yolakwika. “Penyani,” anachenjeza motero. “Kuti pasakhale wina wakulanda inu ngati chuma, mwa kukonda nzeru kwake, ndi chinyengo chopanda pake, potsata mwambo wa anthu.” (Akolose 2:8; 1 Akorinto 1:22, 23; 2:1-13) Inalipo miyambo ina, kapena kuti ziphunzitso, zimene Paulo analimbikitsa Akristu kuti asunge, koma imeneyo inatengedwa m’Malemba ndipo inali yogwirizana nawo kwambiri. (2 Atesalonika 2:13-15) “Lemba lililonse adaliuzira Mulungu,” analemba Paulo, “kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera [kotheratu, NW], wokonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino.”—2 Timoteo 3:16, 17.
Paulo anaoneratu kuti padzakhala kupatuka pa Malemba. Anachenjeza Timoteo kuti: “Idzafika nthaŵi imene sadzalola chiphunzitso cholamitsa; . . . adzalubza dala pachoonadi.” Analimbikitsa Timoteo kuti: “Koma iwe, khala maso m’zonse.” (2 Timoteo 4:3-5) Komano motani? Njira imodzi ndiyo mwa kukhala “mfulu.” Dikishonale yachigiriki imamasulira liwuli la m’Baibulo kukhala “kufunitsitsa kuphunzira ndi kupenda chinthu mosakondera.” Luka anagwiritsa ntchito liwu limeneli pofotokoza omvetsera a Paulo ku Bereya wa m’zaka za zana loyamba. Ziphunzitso za Paulo zinali zatsopano kwa iwo, ndipo sanafune kusocheretsedwa. Powathokoza, Luka analemba kuti: “[Abereya] anali mfulu koposa a m’Tesalonika, popeza analandira mawu ndi kufunitsa kwa mtima wonse, nasanthula m’malembo masiku onse, ngati zinthu zinali zotero.” Kukhala kwawo mfulu sikunapangitse Abereyawo kukayikira, kusafuna kukhulupirira chilichonse ayi. M’malo mwake, zotsatira zake za kufufuza kwawo koona mtima zinali zakuti “ambiri a iwo anakhulupira.”—Machitidwe 17:11, 12.
Mapindu a Kutsata Baibulo
Akristu oyambirira anadziŵika chifukwa cha zinthu ziŵiri, kutsata kwawo kwambiri Baibulo ndi chikondi chawo chodzimana. Komabe, anthu ambiri lero ali ndi ‘maonekedwe a chipembedzo, koma mphamvu yake akuikana.’ (2 Timoteo 3:5) Mtundu uliwonse lerolino wa Chikristu chimene sichitsata Chikristu choyambirira mokhulupirika chilibe mphamvu yoti nkuthandiza anthu kukhala ndi moyo wabwino. Kodi zimenezi zingakhale chifukwa chimene timaonera chiwawa chowonjezereka, chiwerewere, kutha kwa mabanja ndi kukonda chuma m’mbali yaikulu ya Dziko Lachikristu? M’maiko ena “Achikristu” mukuchitika nkhondo zoopsa za mafuko ngakhale pakati pa anthu a chipembedzo chimodzi.
Kodi mzimu wa mfulu umene Abereya anali nawo watha? Kodi pali gulu lililonse la anthu amene amalikhulupirira ndi kulitsata Baibulo lerolino?
Encyclopedia Canadiana ikuti: “Ntchito ya Mboni za Yehova ndiyo kuyambitsanso ndi kukhazikitsanso Chikristu choyambirira chimene Yesu ndi ophunzira ake anatsata m’zaka za zana loyamba ndi lachiŵiri za nyengo yathu.” Ponena za Mboni, New Catholic Encyclopedia ikuti: “Zimaona Baibulo kukhala gwero lokha la chikhulupiriro chawo ndi malangizo a khalidwe.”
Mosakayikira ichi ndicho chifukwa chachikulu chimene Mboni za Yehova kuzungulira dziko lonse zimadziŵikira kukhala zotukuka mwauzimu, zamtendere ndi zachimwemwe. Chotero tikulimbikitsa oŵerenga athu kuphunzira zambiri ponena za ziphunzitso za Baibulo zopatsa thanzi lauzimu. Chidziŵitso chokulirapo chingatithandize kulidalira mokulirapo Baibulo ndi kukhala ndi chikhulupiriro cholimbirapo mwa Mulungu. Kuyesetsa nkofunika ndithu kuti tipeze mapindu osatha a chikhulupiriro chotero.
[Mawu a M’munsi]
a National Public Radio—“Morning Edition”
b Ngati mukufuna kudziŵa zambiri ponena za kudalirika kwa Baibulo, onani brosha lakuti Buku la Anthu Onse, lofalitsidwa ndi Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania.
[Chithunzi patsamba 6]
Mtumwi Paulo ndi enanso analalikira m’misika
[Chithunzi patsamba 7]
Mboni za Yehova “zimaona Baibulo kukhala gwero lokha la chikhulupiriro chawo ndi malangizo a khalidwe”