Yerusalemu Woyenereradi Dzina Lake
‘Sangalalani kunthaŵi zonse ndi ichi ndichilenga; pakuti taonani, ndilenga Yerusalemu wosangalala [“wosangalatsa,” NW].’—YESAYA 65:18.
1. Kodi Ezara ankauona motani mzinda wosankhidwa wa Mulungu?
POKHALA wophunzira Mawu a Mulungu wakhama, wansembe wachiyudayo Ezara anayamikira zedi kugwirizana kumene Yerusalemu anali nako panthaŵi ina ndi kulambira koyera kwa Yehova. (Deuteronomo 12:5; Ezara 7:27) Kukonda kwake mzinda wa Mulungu kukuonekera m’chigawo cha Baibulo chimene anauziridwa kulemba—Mbiri Yoyamba ndi Yachiŵiri ndi Ezara. M’nkhani zosimba mbiri yakale zimenezi, dzinalo Yerusalemu likupezeka pafupifupi chigawo chimodzi mwa zinayi za nthaŵi 800 zimene dzinalo limapezeka m’Baibulo lonse.
2. Kodi dzina la Yerusalemu, lili ndi tanthauzo lotani la ulosi?
2 M’Chihebri cha m’Baibulo, tinganene kuti dzinalo “Yerusalemu” linalembedwa mumtundu wa Chihebri wotchedwa kuti mtundu wotchula zinthu ziŵiriziŵiri. Mtundu wotchula zinthu ziŵiriziŵiri nthaŵi zambiri amaugwiritsira ntchito potchula zinthu zimene zili ziŵiriziŵiri, monga maso, makutu, manja, ndi mapazi. Mumtundu wotchula zinthu ziŵiriziŵiri umenewu, dzinalo Yerusalemu tikuliona kuti likulosera mtendere wamitundu iŵiri umene anthu a Mulungu adzakhala nawo—wauzimu ndi wakuthupi. Malemba sanena ngati Ezara anazimvetsa zimenezi. Koma pokhala wansembe, iye anayesetsa kuthandiza Ayuda kukhala pamtendere ndi Mulungu. Ndipotu anachita zambiri kuti Yerusalemu akhaledi mogwirizana ndi tanthauzo la dzina lake, ndiko kuti, “Mwini [kapena, Maziko a] Mtendere Wamitundu Iŵiri.”—Ezara 7:6.
3. Kodi pakupita zaka zingati tisanayambenso kuŵerenga za zochita za Ezara, ndipo kodi tikumpeza akutani?
3 Baibulo silinena kumene Ezara anali pazaka 12 zimene zinapitapo kuchokera pamene iye anachezera Yerusalemu ndi pamene Nehemiya anafika mumzindawo. Mkhalidwe woipa wauzimu wa mtunduwo panthaŵi imeneyo ukusonyeza kuti Ezara kunalibe. Koma tikupeza Ezara akutumikiranso monga wansembe wokhulupirika ku Yerusalemu linga la mzindawo litangomangidwanso kumene.
Tsiku la Msonkhano Wochititsa Chidwi
4. Kodi patsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chiŵiri wa Israyeli panali kuchitikanji?
4 Linga la Yerusalemu linamalizidwa panthaŵi yabwino ya mwezi waphwando wofunika kwambiri wa Tishiri, mwezi wachisanu ndi chiŵiri pakalendala yachipembedzo ya Israyeli. Patsiku loyamba la Tishiri panali phwando lapadera la mwezi watsopano lotchedwa kuti Phwando la Kuliza Malipenga. Patsiku limenelo, ansembe ankaliza malipenga kwinaku nsembe zikuperekedwa kwa Yehova. (Numeri 10:10; 29:1) Tsikuli linali kukonzekeretsa Aisrayeli kaamba ka Tsiku la Chitetezo lapachaka lomwe linali kuchitika patsiku la 10 la Tishiri ndi Madyerero a Kututa achisangalalowo oyamba patsiku la 15 mpaka pa 21 mwezi womwewo.
5. (a) Kodi Ezara ndi Nehemiya analigwiritsira ntchito bwino motani “tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chiŵiri”? (b) Kodi nchifukwa chiyani Aisrayeli analira?
5 “Tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chiŵiri,” “anthu onse” anasonkhana, mwina atalimbikitsidwa ndi Nehemiya ndi Ezara kuti asonkhane. Amuna, akazi, ndi “yense wakumva ndi kuzindikira” analipo. Choncho, ana aang’ono analipo ndipo anatchera khutu pamene Ezara anaimirira pachiunda ndi kuŵerenga Chilamulo “kuyambira mbandakucha kufikira msana.” (Nehemiya 8:1-4) Nthaŵi ndi nthaŵi, Alevi anathandizira anthuwo kuti amvetsetse zimene zinali kuŵerengedwa. Zimenezi zinachititsa Aisrayeli kugwetsa misozi pamene anazindikira mmene iwo ndi makolo awo analephereratu kumvera Chilamulo cha Mulungu.—Nehemiya 8:5-9.
6, 7. Kodi Akristu angaphunzireponji pa zimene Nehemiya anachita poletsa Ayuda kulira?
6 Koma imeneyi sinali nthaŵi yochita chisoni ndi kulira. Limenelo linali phwando, ndipo anthu anali atangomaliza kumene ntchito yomanganso linga la Yerusalemu. Choncho Nehemiya anawathandiza kukhala ndi malingaliro oyenerera mwa kunena kuti: “Mukani, mukadye zonona, mukamwe zozuna, nimumtumizire gawo lake iye amene sanamkonzeratu kanthu; chifukwa lero ndilo lopatulikira Ambuye wathu; ndipo musamachita chisoni; pakuti chimwemwe cha Yehova ndicho mphamvu yanu.” Momvera, “[anapita] anthu onse kudya ndi kumwa, ndi kutumiza magawo, ndi kusekerera kwakukulu; popeza anazindikira mawu amene adawafotokozera.”—Nehemiya 8:10-12.
7 Anthu a Mulungu lerolino angaphunzirepo zambiri pankhani imeneyi. Awo amene ali ndi mwayi wa kukhala ndi mbali pamisonkhano yampingo ndi misonkhano yaikulu ayenera kumakumbukira zimene zanenedwa pamwambazo. Kuwonjezera pa kupereka uphungu wofuna kuwongolera zinthu umene umakhala wofunika nthaŵi zina, misonkhano imeneyo imasonyeza mapindu ndi madalitso amene amadza mwa kukwaniritsa zimene Mulungu amafuna. Anthu ayenera kuyamikiridwa pantchito zawo zabwino ndi kulimbikitsidwa kuti apirire. Anthu a Mulungu ayenera kuchoka pamisonkhano imeneyi ali ndi mitima yosangalala chifukwa cha malangizo olimbikitsa a m’Mawu a Mulungu amene alandira.—Ahebri 10:24, 25.
Msonkhano Winanso Wosangalatsa
8, 9. Kodi ndi msonkhano wapadera wotani umene unachitika patsiku lachiŵiri la mwezi wachisanu ndi chiŵiri, zimene zinapangitsa anthu a Mulungu kuchitanji?
8 Patsiku lachiŵiri la mwezi wapadera umenewo, “akulu a nyumba za makolo a anthu onse, ansembe, ndi Alevi anasonkhana pamodzi kwa Ezara mlembi, kuti atole nzeru za mawu a chilamulo.” (Nehemiya 8:13) Ezara anali woyenerera bwino kuchititsa msonkhano umenewu, popeza kuti “adaikiratu mtima wake kuchifuna chilamulo cha Yehova, ndi kuchichita, ndi kuphunzitsa m’Israyeli malemba ndi maweruzo.” (Ezara 7:10) Mosakayikira, msonkhano umenewu unasonyeza mbali zimene anthu a Mulungu anayenera kuwongolera mwa kutsatira kwambiri pangano la Chilamulo. Nkhani yaikulu inali kufunika kwa kukonzekera bwino Phwando la Misasa limene anali kudzakondwerera.
9 Phwando lotenga mlungu wonse limeneli linachitika m’njira yoyenera, pamene anthu onse anakhala m’misasa yopangidwa ndi nthambi ndi masamba a mitengo yamitundumitundu. Anthu anamanga misasa imeneyi pamadenga awo athyathyathya, m’mabwalo awo, m’mabwalo a kachisi, ndi m’makwalala a Yerusalemu. (Nehemiya 8:15, 16) Imeneyotu inali nthaŵi yabwino kwambiri yosonkhanitsira anthu ndi kuwaŵerengera Chilamulo cha Mulungu! (Yerekezerani ndi Deuteronomo 31:10-13.) Anachita zimenezi tsiku ndi tsiku, “kuyambira tsiku loyamba kufikira tsiku lotsiriza” la phwandolo, zimene zinachititsa anthu a Mulungu kukhala ndi “chimwemwe chachikulu.”—Nehemiya 8:17, 18.
Tisamanyalanyaze Nyumba ya Mulungu
10. Kodi nchifukwa ninji analinganiza msonkhano wapadera patsiku la 24 la mwezi wachisanu ndi chiŵiri?
10 Pali nthaŵi ndi malo abwino owongolerera zolakwa zazikulu za anthu a Mulungu. Mwachionekere ataona kuti imeneyi ndiyo nthaŵi yake, Ezara ndi Nehemiya analinganiza tsiku losala kudya patsiku la 24 m’mwezi wa Tishiri. Chilamulo cha Mulungu chinaŵerengedwanso, ndipo anthu anaulula machimo awo. Kenako Alevi anafotokozanso mmene Mulungu anachitira mwachifundo ndi anthu ake opanduka, ndiponso anatamanda Yehova ndi mawu okoma, ndi kuchita “pangano lokhazikika” lolembedwa ndi akulu awo, Alevi, ndi ansembe.—Nehemiya 9:1-38.
11. Kodi Ayuda anadzimanga okha ndi “pangano lokhazikika” lotani?
11 Anthu onse analumbira kuti adzachita zolembedwa mu “pangano lokhazikika” limenelo. Anati “adzayenda m’chilamulo cha Mulungu.” Ndiponso anavomera kuti sadzakwatirana ndi “anthu a m’dziko.” (Nehemiya 10:28-30) Komanso, Ayuda analonjeza kuti adzachita Sabata, kupereka ndalama chaka chilichonse pochirikiza kulambira koona, kupereka nkhuni kuguŵa la nsembe, kupereka nkhosa ndi ng’ombe zawo zoyamba kubadwa kuti zikaperekedwe nsembe, ndi kupereka zipatso zoundukula za minda yawo kuzipinda zodyera za kachisi. Ndithudi, iwo anatsimikiza mtima ‘kusasiya [“kusanyalanyaza,” NW] nyumba ya Mulungu wawo.’—Nehemiya 10:32-39.
12. Kodi kusanyalanyaza nyumba ya Mulungu kumaphatikizaponji lerolino?
12 Lerolino, anthu a Yehova ayenera kusamala kwambiri kuti sakunyalanyaza mwayi ‘wotumikira usana ndi usiku’ m’mabwalo a kachisi wamkulu wauzimu wa Yehova. (Chivumbulutso 7:15) Zimenezi zimafuna mapemphero osatha ochokera pansi pa mtima kuti kulambira Yehova kupite patsogolo. Kuchita mogwirizana ndi mapemphero ameneŵa kumafuna kukonzekera misonkhano yachikristu ndi kutengamo mbali, kukhala ndi mbali m’makonzedwe olalikira uthenga wabwino, ndi kuthandiza ofuna mwa kubwererako ndiponso, ngati nkotheka, kuchita nawo maphunziro a Baibulo. Ambiri amene safuna kunyalanyaza nyumba ya Mulungu amapereka ndalama zothandizira ntchito yolalikira ndi kusamalira malo a kulambira koona. Tingachirikizenso kumanga nyumba zosonkhaniramo zofunika mwamsangazo ndi kumazisunga zoyera ndiponso zaudongo. Njira yaikulu yosonyezera chikondi cha panyumba yauzimu ya Mulungu ndiyo kuchirikiza mtendere wa okhulupirira anzathu ndi kuthandiza aliyense wofuna thandizo lakuthupi kapena lauzimu.—Mateyu 24:14; 28:19, 20; Ahebri 13:15, 16.
Kuperekedwa Kwachisangalalo
13. Kodi ndi nkhani iti imene inafunikira kuisamalira mwamsanga linga la Yerusalemu lisanaperekedwe, ndipo ambiri anapereka chitsanzo chabwino chotani?
13 “Pangano lokhazikika” lomwe linapangidwa m’tsiku la Nehemiya linakonzekeretsa anthu akale a Mulungu kaamba ka kuperekedwa kwa linga la Yerusalemu. Koma panali nkhani inanso yofunabe chisamaliro chamwamsanga. Tsopano atazingidwa ndi linga lalikulu lokhala ndi zipata 12, Yerusalemu anafunikira kukhala ndi anthu ochulukirapo. Ngakhale kuti munkakhala Aisrayeli ena, ‘mudziwo tsono unali wachitando, ndi waukulu; koma anthu anali m’mwemo anali oŵerengeka.’ (Nehemiya 7:4) Kuti athetse vutoli, anthu “anachita maere, kuti libwere limodzi la magawo khumi likhale m’Yerusalemu, mudzi wopatulika.” Kutsatira makonzedwe ameneŵa mofunitsitsa kunasonkhezera anthu kudalitsa “amuna onse akudzinenera mwaufulu kuti adzakhala m’Yerusalemu.” (Nehemiya 11:1, 2) Chimenechi nchitsanzo chabwino kwambiri kwa olambira oona lerolino amene mikhalidwe yawo imawalola kusamukira kumene kukufunika thandizo la Akristu ofikapo!
14. Kodi kunachitika zotani patsiku lopereka linga la Yerusalemu?
14 Posapita nthaŵi anayamba kukonzekera zinthu zofunika za patsiku lalikulu la kuperekedwa kwa linga la Yerusalemu. Oimba anasonkhanitsidwa kuchokera m’mizinda yapafupi ya m’Yuda. Oimbawa anaikidwa m’magulu aŵiri aakulu oimba ziyamiko, ndipo gulu lililonse linatsatiridwa ndi anthu oyenda mwadongosolo. (Nehemiya 12:27-31, 36, 38) Magulu oimba ndi anthu owatsatira anayambira pamalo ena ake akutali kwambiri ndi kachisi palinga, mwinamwake ku Chipata cha ku Chigwa, ndi kuloŵera kumalo osiyana mpaka atakumana panyumba ya Mulungu. “Anaphera nsembe zambiri tsiku lija, nasekerera; pakuti Mulungu anawakondweretsa ndi chimwemwe chachikulu; ndi akazi omwe ndi ana anakondwera; ndi chikondwerero cha Yerusalemu chinamveka kutali.”—Nehemiya 12:43.
15. Kodi nchifukwa ninji kuperekedwa kwa linga la Yerusalemu sikunadzetse chisangalalo chosatha?
15 Baibulo silitchula tsiku pamene chikondwerero chachikulu chimenechi chinachitika. Mosakayikira, linali tsiku lalikulu kwambiri, ngati silinali chimake, cha kubwezeretsedwa kwa Yerusalemu. Zoonadi, munali zambiri zofunika kumangidwa mumzindamo. M’kupita kwa nthaŵi, nzika za Yerusalemu zinasiya kaimidwe kawo kabwino kauzimu. Mwachitsanzo, pamene Nehemiya anachezera mzindawo kachiŵiri, anapeza kuti anthu ananyalanyazanso nyumba ya Mulungu ndi kuti Aisrayeli anali kukwatiranso akazi akunja. (Nehemiya 13:6-11, 15, 23) Zolemba za mneneri Malaki zikuchitiranso umboni za mkhalidwe woipa umodzimodziwu. (Malaki 1:6-8; 2:11; 3:8) Choncho kupatuliridwa kwa linga la Yerusalemu sikunadzetse chisangalalo chosatha.
Wodzetsa Chisangalalo Chosatha
16. Kodi ndi zochitika zazikulu zotani zimene anthu a Mulungu akuyembekezera?
16 Lerolino, anthu a Yehova akudikira mwachidwi nthaŵi pamene Mulungu adzalaka adani ake onse. Chilakikochi chidzayamba ndi kuwonongedwa kwa ‘Babulo Wamkulu’—mzinda wophiphiritsa wopangidwa ndi zipembedzo zonse zonyenga. (Chivumbulutso 18:2, 8) Kuwonongedwa kwa chipembedzo chonyenga kudzakhala mbali yoyamba ya chisautso chachikulu chikudzacho. (Mateyu 24:21, 22) Patsogolo pathupa palinso chochitika chachikulu kwambiri—ukwati wakumwamba wa Ambuye Yesu Kristu ndi mkwatibwi wake wa nzika 144,000 za “Yerusalemu Watsopano.” (Chivumbulutso 19:7; 21:2) Sitingathe kunena nthaŵi yeniyeni pamene kuyanjana kwakukulu kumeneku kudzachitika, koma chidzakhaladi chochitika chosangalatsa.—Onani Nsanja ya Olonda, August 15, 1990, masamba 30-1.
17. Kodi tikudziŵaponji ponena za kumalizidwa kwa Yerusalemu Watsopano?
17 Tikudziŵa kuti Yerusalemu Watsopano watsala pang’ono kumalizidwa. (Mateyu 24:3, 7-14; Chivumbulutso 12:12) Mzindawu sudzakhala chokhumudwitsa monga momwe Yerusalemu wapadziko lapansi analili. Zili choncho chifukwa chakuti nzika zake zonse ndi otsatira a Yesu Kristu odzozedwa ndi mzimu, oyesedwa, ndiponso oyengedwa. Chifukwa cha kukhulupirika kwawo mpaka imfa, aliyense wa iwo adzakhala atasonyeza kuti ndi wokhulupirika kosatha kwa Mfumu ya Chilengedwe Chonse, Yehova Mulungu. Zimenezo zili ndi tanthauzo lalikulu kwa mtundu wonse wa anthu—amoyo ndi akufa!
18. Kodi nchifukwa chiyani tiyenera ‘kukhala okondwa ndi kusangalala kunthaŵi zonse’?
18 Talingalirani zimene zidzachitika pamene Yerusalemu Watsopano ayamba kusamalira anthu amene akusonyeza chikhulupiriro m’nsembe ya Yesu ya dipo. “Taonani,” analemba motero mtumwi Yohane. “Chihema cha Mulungu chili mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nawo, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nawo, Mulungu wawo; ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; zoyambazo zapita.” (Chivumbulutso 21:2-4) Ndiponso, Mulungu adzagwiritsira ntchito makonzedwe onga mzinda ameneŵa kukonzanso mtundu wa anthu kukhala anthu angwiro. (Chivumbulutso 22:1, 2) Zimenezi ndi zifukwa zabwino chotani nanga ‘zokhalira okondwa ndi kusangalala kunthaŵi zonse ndi zimene Mulungu akuzilenga tsopano’!—Yesaya 65:18.
19. Kodi paradaiso wauzimu amene Akristu asonkhanitsidwamo ndiye chiyani?
19 Komabe, anthu olapa sayenera kuyembekezera mpaka nthaŵiyo kuti alandire thandizo la Mulungu. M’chaka cha 1919, Yehova anayamba kusonkhanitsa omalizira a 144,000 m’paradaiso wauzimu, mmene zipatso za mzimu wa Mulungu—monga chikondi, chimwemwe, ndi mtendere—zili zochuluka. (Agalatiya 5:22, 23) Chinthu chochititsa chidwi ndi paradaiso wauzimu ameneyu ndicho chikhulupiriro cha anthu ake odzozedwa, amene abala zipatso zambirimbiri potsogoza kulalikira kwa uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu padziko lonse lapansi. (Mateyu 21:43; 24:14) Chotsatirapo chake ndicho chakuti “nkhosa zina” pafupifupi mamiliyoni asanu ndi imodzi, oyembekezera kukhala padziko lapansi, aloledwanso kuloŵa m’paradaiso wauzimu ndi kuchita ntchito yobala zipatso mosangalala. (Yohane 10:16) Iwo ayeneretsedwa kuchita zimenezi mwa kudzipatulira kwa Yehova Mulungu pamaziko a kukhulupirira kwawo nsembe ya dipo ya Mwana wake, Yesu Kristu. Kuyanjana kwawo ndi anthu oyembekezera kukhala a m’Yerusalemu Watsopano kwakhaladi dalitso. Chotero, mwa zochita zake ndi Akristu odzozedwa, Yehova wamanga maziko olimba a “dziko lapansi latsopano”—dziko la anthu oopa Mulungu amene adzaloŵa m’mabwalo apadziko lapansi a Ufumu wakumwamba.—Yesaya 65:17; 2 Petro 3:13.
20. Kodi ndi motani mmene Yerusalemu Watsopano adzakhalira mogwirizana ndi dzina lake?
20 Mtendere umene anthu a Yehova ali nawo tsopano m’paradaiso wawo wauzimu adzakhalanso nawo m’paradaiso weniweni wapadziko lapansi posachedwapa. Zimenezo zidzachitika pamene Yerusalemu Watsopano adzatsika kumwamba kudzadalitsa anthu. M’njira ziŵiri, anthu a Mulungu adzakhala ndi mtendere wolonjezedwa pa Yesaya 65:21-25. Pokhala olambira Yehova ogwirizana m’paradaiso wauzimu, odzozedwa amene adzapita kwawo ku Yerusalemu Watsopano wakumwamba ndi awo a “nkhosa zina” tsopano ali mumtendere woperekedwa ndi Mulungu. Ndipo mtendere umenewu udzafika mpaka m’Paradaiso weniweni, pamene ‘kufuna kwa Mulungu kudzachitika padziko lonse, monga momwe kukuchitikira kumwamba.’ (Mateyu 6:10) Inde, mzinda wakumwamba waulemerero wa Mulunguwo udzakhala woyenereradi dzina lakuti Yerusalemu monga ‘Maziko [olimba] a Mtendere Wamitundu Iŵiri.’ Kunthaŵi zosatha, udzaima monga chinthu chodzetsa chitamando kwa Mlengi wake Wamkulu, Yehova Mulungu, ndi kwa Mfumu Mkwati wake, Yesu Kristu.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi nchiyani chinakwaniritsidwa pamene Nehemiya anasonkhanitsa anthu m’Yerusalemu?
◻ Kodi Ayuda akale anayenera kuchitanji kuti asanyalanyaze nyumba ya Mulungu, ndipo kodi ifeyo tiyenera kuchitanji?
◻ Kodi “Yerusalemu” akuloŵetsedwapo motani pankhani yodzetsa chisangalalo ndi mtendere wokhalitsa?
[Mapu patsamba 23]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
ZIPATA ZA YERUSALEMU
Manambala akusonyeza kukwera kwa malowo m’mamita lerolino
CHIPATA CHA NSOMBA
CHIPATA CHA MZINDA WAKALE
CHIPATA CHA EFRAIMU
CHIPATA CHA KUNGONDYA
Linga Lachitando
Khwalala
CHIPATA CHA KUCHIGWA
DERA LACHIŴIRI
Linga Lakale Lakumpoto
MUDZI WA DAVIDE
CHIPATA CHA KUDZALA
Chigwa cha Hinomu
Nsanja
CHIPATA CHA NKHOSA
CHIPATA CHAKAIDI
Malo a Kachisi
CHIPATA CHA HAMIFIKADI
CHIPATA CHA AKAVALO
OFELA
Khwalala
CHIPATA CHA KUMADZI
Kasupe wa Gihoni
CHIPATA CHA CHITSIME
Munda wa Mfumu
Rogeli
Chigwa (Chapakati) cha Tyropoeon
Mtsinje wa Kidroni
740
730
730
750
770
770
750
730
710
690
670
620
640
660
680
700
720
740
730
710
690
670
Umene uyenera kukhala ukulu wa linga la Yerusalemu panthaŵi imene mzindawo unawonongedwa ndiponso pamene Nehemiya anatsogolera kumangidwanso kwa lingalo