Ambiri Amati Ali Nchikhulupiriro
“YESU ndi wodabwitsa! Ndi wodabwitsa!” mayi wina wopembedza ku Brazil anatero. Ndithudi, palibe amene angakane za mphamvu ya dzina la Yesu. M’mbiri yonse, anthu mwakufuna kwawo avutika ndi kufa chifukwa cha iye.
Mtumwi Petro ndi mtumwi Yohane ankalalikira ‘motchula dzina la Yesu’ mu Yerusalemu. Chifukwa cha kulalikira kwawoko, anamangidwa ndi kukwapulidwa. Koma iwo “anapita kuchokera ku bwalo la akulu, nakondwera kuti anayesedwa oyenera kunyozedwa chifukwa cha dzinalo.”—Machitidwe 5:28, 41.
Antipa anali Mkristu wina wa m’zaka za zana loyamba amene ankalemekeza dzina la Yesu. M’buku lomalizira la Baibulo, Chivumbulutso, Yesu anatchula iye monga “mboni yanga, wokhulupirika wanga, amene anaphedwa pali inu, kuja akhalako Satana.” (Chivumbulutso 2:13) Pamodzi ndi Akristu ena ku Pergamo, Antipa sanalole kukana kukhulupirira kwake mwa Kristu. Antipa sanaleke kulitchulatchula dzina la Yesu ngakhale kuti zimenezo zinali zoti zimtayitsa moyo wake!
Patapita pafupifupi zaka 50, mu 155 C.E., wina wodzitcha Mkristu wotchedwa Polycarp anakumana ndi chiyeso chofananacho pamene analamulidwa kuti anyoze Kristu. Yankho lake linali lakuti: “Ndamtumikira kwa zaka 86, ndipo sanandichitirepo choipa. Ndingachitire bwanji chipongwe Mfumu yanga imene inandipulumutsa?” Popeza sanalole kumkana Kristu, Polycarp anatenthedwa pamtengo.
Atumwi, Antipa, ndi ena anatsimikiza kuchitira umboni za Kristu mwa kulolera kufa! Koma bwanji nanga anthu lerolino?
Dzina la Yesu Lerolino
Dzina la Yesu lidakapangitsabe anthu kuganiza kwambiri. Ku maiko a ku Latin America, m’zaka makumi a posachedwa kwawonjezeka matchalitchi a anthu omwe amati amakhulupirira Yesu. Ngakhale timidzi ting’onoting’ono tili ndi tchalitchi cha Chipentecostal. Komanso panthaŵi yomweyo, matchalitchi amenewa akuwonjezera kuloŵerera kwawo pandale. Mwachitsanzo, mipando 31 ya Brazil Congress and Senate ili m’manja mwa mamembala a matchalitchi amenewa.
Mfundo yaikulu ya chipembedzo chatsopano mu United States ndi Yesu. Otsatira ake amadzitcha kuti Osunga Lonjezo. Magazini ya Time inapereka lipoti lakuti mu 1997, chiŵerengero cha opezeka pamisonkhano yawo chinakwera kuchokera pa 4,200 mu 1991 kufika pa 1.1 miliyoni mu 1996. Imodzi mwa nyimbo zawo imati: “O chipambano mwa Yesu, Mpulumutsi wanga kwa muyaya.”
Komabe simalingaliro onse obwera chifukwa cha dzina la Yesu amene amakhala abwino. Dzina lake lapangitsa kuti mbendera za nkhondo ziulutsidwe. Ayuda ananyongedwa, akunja anaphedwa, opanduka kuzunzidwa, kudulidwa ziwalo, ndi kutenthedwa pamtengo—zonsezi m’dzina la Yesu. Ndipo, posachedwapa, kupangira chipembedzo malonda kwafika poipa kwambiri. Konseku nkupotoza dzina la Yesu ndi kuligwiritsa ntchito moipa, mosiyana ndi zimene limaimira!
Kuwonjezera apo zimadzutsa mafunso ena ogwira mtima: Kodi chimapangitsa munthu kukhulupirira dzina la Yesu nchiyani? Ndipo kodi Mboni za Yehova zimaiona motani nkhaniyi? Nkhani yotsatira iyankha mafunso amenewa.