Ogwirizana Panjira Yabwino Koposa ya Moyo
Ngati chiŵerengero cha anthu padziko lonse lapansi chipitirizabe kukwera, posachedwapa padzakhala anthu 6,000,000,000 padziko lonse lapansi. Ngakhale kuti onse anachokera kwa kholo limodzi, ambiri akuoneka kuti sakudziŵa kuti ali m’banja lapadziko lonse loyenera kutsatira Mlengi wanzeru ndiponso wachikondi. Kusagwirizana ndiponso udani umene uli pakati pa mitundu, mafuko, ndi zikhalidwe zimachitira umboni za mkhalidwe womvetsa chisoni umenewu.
PONENA za mkhalidwe umene ulipowu padziko, kugwirizana kwa anthu padziko lonse kungaoneke ngati cholinga chosatheka. The Columbia History of the World imati: “Ponena za funso lofunika koposalo la mmene tingakhalire mu umodzi, dziko limene tikukhalamoli lilibe njira yatsopano iliyonse yochitira zimenezo, ndi imodzi yomwe.”
Komabe, kudzetsa mgwirizano pakati pa anthu onse padziko lonse sikufunikira lingaliro latsopano. Njira yopezera mgwirizano njolongosoledwa m’Malemba Opatulika. Kwenikweni, njokhudzana ndi kulambira Iye amene analenga dziko lapansi ndi zamoyo zonse zili momwemo. Kugwirizana koona kwa malingaliro, zolinga, ndi njira ya moyo kulipo kale pakati pa anthu a Mulungu. Iwo, amene chiŵerengero chawo tsopano chikuposa mamiliyoni asanu ndi theka m’mayiko 233, n’ngogwirizana pokhulupirira kuti njira ya moyo ya Mulungu ndiyo njira yabwino koposa. Monga wamasalmo, iwo amapemphera kuti: “Mundionetse njira yanu, Yehova; ndidzayenda m’choonadi chanu: muumbe mtima wanga ukhale umodzi kuti uliope dzina lanu.”—Salmo 86:11.
Kugwirizana kwa anthu kumeneku pa kulambira koyera kunaloseredwa kalekale ndi mneneri Yesaya. Iye analemba kuti: “Padzakhala masiku otsiriza, kuti phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pa nsonga ya mapiri, ndipo lidzakwezedwa pamwamba pa zitunda; mitundu yonse idzasonkhana kumeneko. Ndipo anthu ambiri adzanka, nati, Tiyeni tikwere kunka ku phiri la Yehova, ku nyumba ya Mulungu wa Yakobo; ndipo Iye adzatiphunzitsa za njira zake, ndipo tidzayenda m’mayendedwe ake.”—Yesaya 2:2, 3.
Kugwirizana kwa Mboni za Yehova nkwapadera. M’mipingo yoposa 87,000 padziko lonse lapansi, iwo amadya chakudya chauzimu chimodzimodzi pamisonkhano yawo ya mlungu ndi mlungu. (Mateyu 24:45-47) Komabe, kuyambira cha pakati pa 1998 mpaka kuchiyambi kwa 1999, Mboni zinasonyeza kugwirizana kwawo m’njira inanso—mwa kusonkhana pa Misonkhano yawo ya “Njira ya Moyo ya Mulungu” yamasiku atatu padziko lonse lapansi. M’mayiko 13, misonkhano imeneyi inali ndi nthumwi zambiri zochokera kumayiko osiyanasiyana ndipo inatchedwa kuti misonkhano ya mitundu yonse. Ina inatchedwa kuti misonkhano yachigawo. Koma misonkhano yonseyi inali ndi pologalamu imodzimodzi ya zinthu zabwino zauzimu.
Zinali zosangalatsatu kwambiri kuona nthumwi zambirimbiri zachimwemwe, zovala bwino zikuloŵa m’nyumba zosonkhaniramo ndi m’masitediyamu kuti ziphunzitsidwe ndi Yehova! Zinalidi monga momwe nthumwi ina kumsonkhano wa mitundu yonse wa ku Michigan, U.S.A. inanenera. Iyo inati: “Zinali zosangalatsa zedi kuona abale athu ochokera padziko lonse lapansi—ku Czech Republic, Barbados, Nigeria, Hungary, England, Holland, Ethiopia, Kenya, ndi mayiko enanso ambiri—akukupatirana! Zinali zokondweretsa kuona abale akukhala pamodzi mogwirizana, kugwetsa misozi yachisangalalo chifukwa cha chikondi chimene ali nacho kwa wina ndi mnzake ndi kwa Mulungu wawo wamkuluyo, Yehova.” Nkhani yotsatira idzapenda pologalamu ya misonkhano imeneyo imene anthu miyandamiyanda padziko lonse lapansi anasangalala nayo.
[Mawu a Chithunzi patsamba 3]
Mountain High Maps® Copyright © 1997 Digital Wisdom, Inc.