Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 2/1 tsamba 6-7
  • Kodi Mungasonyeze Motani Kuti Ndinudi Wodzichepetsa?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mungasonyeze Motani Kuti Ndinudi Wodzichepetsa?
  • Nsanja ya Olonda—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chitsanzo cha Kristu cha Kudzichepetsa
  • Mmene Munthu Wodzichepetsa Amachitira Zinthu
  • Kudzichepetsa Kumasonyeza Chikondi ndi Kukhululukira
  • Khalani Odzichepetsadi
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Achimwemwe Ali Odzichepetsa
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Kodi Nkuvaliranji Kudzichepetsa?
    Nsanja ya Olonda—1991
  • ‘Valani Kudzichepetsa’
    Nsanja ya Olonda—2007
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1999
w99 2/1 tsamba 6-7

Kodi Mungasonyeze Motani Kuti Ndinudi Wodzichepetsa?

MULUNGU amakonda kwambiri kudzichepetsa koona. Yakobo analemba kuti: “Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo odzichepetsa.” (Yakobo 4:6) Panopo Yakobo mwina anali kunena za mfundo zingapo zofotokozedwa m’Malemba Achihebri. “Yehova n’ngwokwezeka, apenyanso wopepukayo; koma wodzikuza am’dziŵira kutali.” “Maso a munthu akuyang’anira kumwamba adzatsitsidwa, ndi kudzikweza kwa anthu kudzaŵeramitsidwa pansi; ndipo Yehova yekha adzakwezedwa.” “[Mulungu] anyozadi akunyoza, koma apatsa akufatsa chisomo.”​—Salmo 138:6; Yesaya 2:11; Miyambo 3:34.

Mtumwi Petro analimbikitsanso kudzichepetsa. Iye analemba kuti: “Nonsenu muvale kudzichepetsa kuti mutumikirane; pakuti Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo kwa odzichepetsa.”​—1 Petro 5:5.

Chitsanzo cha Kristu cha Kudzichepetsa

Mungafunse kuti, Kodi kukhala wodzichepetsa kuli ndi ubwino kapena phindu lotani? Kwa munthu amene akufunadi kukhala Mkristu woona yankho n’lofunika kwambiri​—kukhala wodzichepetsa ndiko kukhala monga Kristu. Yesu anasonyeza kudzichepetsa kwake mwa kulandira ntchito yapadera yobwera padziko lapansi kuchokera kumwamba ndi kukhala munthu wotsika, wa pansi pa angelo. (Ahebri 2:7) Ngakhale kuti anali Mwana wa Mulungu, iye anapirira chitonzo chochokera kwa adani ake achipembedzo. Iye sanasweke mtima poyesedwa, ngakhale kuti akanatha kuitanitsa makamu a angelo kuti adzam’thandize.​—Mateyu 26:53.

Pomalizira pake, Yesu anapachikidwa mwachitonzo pamtengo wozunzirapo, koma anakhalabe wokhulupirika kwa Atate wake. Choncho, Paulo analemba za iye kuti: “Mukhale nawo mtima m’kati mwanu umene unalinso mwa Kristu Yesu, ameneyo, pokhala nawo maonekedwe a Mulungu, sanachiyesa cholanda kukhala wofana ndi Mulungu, koma anadzikhuthula yekha, natenga maonekedwe a kapolo, nakhala m’mafanizidwe a anthu; ndipo popezedwa m’maonekedwe ngati munthu, anadzichepetsa yekha, nakhala womvera kufikira imfa, ndiyo imfa ya pamtanda [“pamtengo wozunzirapo,” NW].”​—Afilipi 2:5-8.

Choncho kodi tingasonyeze motani kuti ndifedi odzichepetsa? Pazochitika zenizeni, kodi ndi motani mmene tingachitire zinthu modzichepetsa m’malo mochita monyada?

Mmene Munthu Wodzichepetsa Amachitira Zinthu

Tiyeni tikambirane za kudzichepetsa pazochitika zenizeni, kaya ndi pantchito kapena mu utumiki wachikristu. Kuti ntchito iyende bwino, oyang’anira, mamanijala, ndi akapitawo angakhale ofunikira. Winawake ayenera kupanga zosankha. Kodi mumatani? Kodi mumaganiza kuti, “Kodi iyeyo amadziyesa ndani pondiuza zochita? Iyeyo anandipeza ndili kale pantchitoyi.” Inde, ngati ndinu wonyada, mudzakwiya pogonjera wina. Koma munthu wodzichepetsa amayesetsa ‘kusachita kanthu monga mwa chotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pake, komatu ndi kudzichepetsa mtima, kuyesa anzake omposa iye mwini.’​—Afilipi 2:3.

Kodi mumaliona bwanji lingaliro ngati lachokera kwa wina wamng’ono ndi inu kapena kwa mkazi? Ngati ndinu wodzichepetsa, mudzaliganizira. Ngati ndinu wonyada, mudzanyansidwa nalo kapena kulikaniratu. Kodi mungakondepo chiyani, chitamando ndi kusyasyalika zimene zingakuwonongetseni kapena uphungu wothandiza wokumangirirani?​—Miyambo 27:9; 29:5.

Kodi mungapirire tsoka? Kudzichepetsa kudzakuthandizani kulimbana ndi mavuto ndi kuwapirira, monga momwe anachitira Yobu. Ngati ndinu wonyada, mungakwiye ndipo mungachitepo kanthu moukira pamikhalidwe yovutayo ndi zina zimene mungaziyese chipongwe.​—Yobu 1:22; 2:10; 27:2-5.

Kudzichepetsa Kumasonyeza Chikondi ndi Kukhululukira

Anthu ena amavutika kuti anene kuti “Pepani. Ndinalakwitsa. Munali olondola.” Chifukwa chiyani? Ndi onyada kwambiri! Komabe, nthaŵi zambiri kupepesa koona kungaletse mosavuta mkangano wa pabanja.

Kodi mumakhala okonzeka kukhululukira ngati wina wakulakwirani? Kapena, chifukwa cha kunyada kwanu, kodi mumasunga chakukhosi, mwinamwake kwa masiku ndi miyezi yambiri, kukana kum’yankhula munthu amene mukuti anakulakwiraniyo? Kodi mumam’chitiranso nkhanza munthuyo pofuna kum’bwezera? Anthutu aphedwa powachitira nkhanza zoterozo. Ena, amuipitsira mbiri munthu wowalakwirayo. Mosiyana ndi zimenezo, munthu wodzichepetsa ndi wachikondi ndiponso wokhululuka. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti chikondi sichilingilira zoipa. Yehova anali wokonzeka kukhululukira Aisrayeli ngati akanasiya kunyada kwawo. Wotsatira wodzichepetsa wa Yesu amakhala wofunitsitsa kukhululukira, ngakhale mobwerezabwereza!​—Yoweli 2:12-14; Mateyu 18:21, 22; 1 Akorinto 13:5.

Munthu wodzichepetsa ‘amatsogolera pochitira wina ulemu.’ (Aroma 12:10) Baibulo la New International Version limati: “Lemekezani ena kwambiri koposa inu mwini.” Kodi mumatamanda ena ndi kuyamikira nzeru zawo ndi maluso awo? Kapena kodi nthaŵi zonse mumafuna kupeza kenakake kolakwika kuti muwaipitsire mbiri yawo? Inde, kodi mumatha kuthokoza anthu ena moona mtima? Ngati mumavutika kuchita zimenezi, mwinamwake simumadzimva kukhala wosungika ndiponso ndinu wonyada.

Munthu wonyada amakhala wotekeseka. Munthu wodzichepetsa ndi woleza mtima ndiponso wopirira. Bwanji za inuyo? Kodi mumavutika maganizo mukaona kuti wina wakuchitirani chipongwe? Maganizo oterowo n’ngosiyana kwambiri ndi kukhala woleza mtima. Ngati ndinu wodzichepetsa, simuzadziyesa munthu wofunika kwambiri. Kumbukirani zimene zinachitika pamene ophunzira a Yesu anadziyesa ofunika kwambiri​—anakangana kwadzaoneni ponena za amene adzakhala wamkulu. Anaiŵala kuti onsewo anali “akapolo opanda pake”!​—Luka 17:10; 22:24; Marko 10:35-37, 41.

Wolemba nkhani wina wachifalansa Voltaire anafotokoza kudzichepetsa kukhala “kudekha kwa moyo . . . mankhwala oletsera kunyada.” Inde, kudzichepetsa ndiko kusadzikuza. Munthu wodzichepetsa ali ndi mzimu wofatsa, osati wonyada. Ndi waulemu kwambiri ndiponso wakhalidwe labwino.

Choncho n’kuyesetseranji kukhala wodzichepetsa? Chifukwa chakuti Mulungu amakonda munthu wodzichepetsa ndipo kumatithandiza kukhala ndi chitsogozo cha Mulungu. Chifukwa chakuti Danieli analinso wodzichepetsa, Yehova anaona mneneriyo kukhala munthu ‘wokondedwa’ nam’tumizira masomphenya kudzera mwa mngelo! (Danieli 9:23; 10:11, 19) Kudzichepetsa kumadzetsa mfupo zambiri. Kumadzetsa mabwenzi oona amene amakukondani. Ndiponso, kumadzetsa madalitso a Yehova. “Mphotho ya chifatso ndi kuopa Yehova ndiye chuma, ndi ulemu, ndi moyo.”​—Miyambo 22:4.

[Chithunzi patsamba 7]

Mawu odzichepetsa opepesa angapangitse moyo kukhala wosangalatsa

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena