Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w93 12/1 tsamba 19-24
  • Achimwemwe Ali Odzichepetsa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Achimwemwe Ali Odzichepetsa
  • Nsanja ya Olonda—1993
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chikhulupiriro mwa Yehova Chimatithandiza Kukhala Odzichepetsa
  • Kudzichepetsa​—Njira ya Nzeru
  • Kudzichepetsa Kumakulitsa Unansi Wabwino ndi Ena
  • Chikondi Chidzatithandiza Kukhala Odzichepetsa
  • Khalani Odzichepetsadi
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Kodi Mungasonyeze Motani Kuti Ndinudi Wodzichepetsa?
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Yehova Amaonetsa Ulemerero Wake kwa Odzichepetsa
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Yehova Amaona Kuti Atumiki Ake Odzichepetsa Ndi Amtengo Wapatali
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1993
w93 12/1 tsamba 19-24

Achimwemwe Ali Odzichepetsa

“Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo kwa odzichepetsa.”​—1 PETRO 5:5.

1, 2. Kodi ndimotani mmene Yesu Muulaliki wake wa pa Phiri anagwirizanitsira nkhani ya kukhala wachimwemwe ndi ya kukhala wodzichepetsa?

KODI kukhala wachimwemwe ndi kukhala wodzichepetsa nkogwirizana? Muulaliki wake wotchuka koposa, Yesu Kristu, munthu wamkulu woposa amene anakhalako, akulongosola mitundu isanu ndi inayi ya chimwemwe, kapena chisangalalo. (Mateyu 5:1-12, NW) Kodi Yesu anagwirizanitsa kukhala wachimwemwe ndi kukhala wodzichepetsa? Inde, anatero, chifukwa chakuti kukhala wodzichepetsa kumaloŵetsedwamo m’mitundu ingapo ya chimwemwe imene anaitchula. Mwachitsanzo, munthu afunikira kukhala wodzichepetsa kuti azindikire zosoŵa zake zauzimu. Ali odzichepetsa okha amene akumva njala ndi ludzu la chilungamo. Ndipo onyada sali ofatsa mtima ndiponso sali achifundo, kapena ofuna mtendere.

2 Odzichepetsa ali achimwemwe chifukwa chakuti kuli koyenera ndi kuwona mtima kukhala wodzichepetsa. Ndiponso, odzichepetsa ali achimwemwe chifukwa chakuti kuli kwanzeru kukhala wodzichepetsa; kumakulitsa maunansi abwino ndi Yehova Mulungu ndi Akristu anzathu. Kuwonjezerapo, anthu odzichepetsa ali achimwemwe chifukwa chakuti kudzichepetsako kuli chisonyezero cha chikondi chawo.

3. Kodi nchifukwa ninji kuwona mtima kumatifunikiritsa kukhala odzichepetsa?

3 Kodi nchifukwa ninji kuwona mtima kumafuna kuti tikhale odzichepetsa? Choyamba, chifukwa chakuti tonsefe tinalandira choloŵa cha kupanda ungwiro ndipo timalakwa mobwerezabwereza. Mtumwi Paulo anati ponena za iyemwini: “Ndidziŵa kuti mkati mwanga, ndiko m’thupi langa, simukhala chinthu chabwino; pakuti kufuna ndili nako, koma kuchita chabwino sindikupeza.” (Aroma 7:18) Inde, tonsefe tinachimwa ndipo timapereŵera paulemerero wa Mulungu. (Aroma 3:23) Kuwona mtima kudzatiletsa kukhala onyada. Kuvomereza cholakwa kumafuna kudzichepetsa, ndipo kuwona mtima kudzatithandizanso kuvomereza mlandu pamene tilakwa. Popeza kuti kaŵirikaŵiri timalephera kuchita zimene timakalimira, tili ndi chifukwa chabwino chokhalira odzichepetsa.

4. Kodi nchifukwa chotani choperekedwa pa 1 Akorinto 4:7 chimene chimatikakamiza kukhala odzichepetsa?

4 Mtumwi Paulo akutipatsa chifukwa china chimene kuwona mtima kuyenera kutipangitsira kukhala odzichepetsa. Iye anati: “Akusiyanitsa iwe ndani? Ndipo uli nacho chiyani chosati wachilandira? Koma ngati wachilandira udzitamanda bwanji, monga ngati sunachilandira?” (1 Akorinto 4:7) Nzosakayikitsa konse, kudzitengera ulemerero pa ife tokha, kukhala onyada ndi zimene tili nazo, maluso, kapena zipambano, sikukakhala kuwona mtima. Kuwona mtima kumatithandizira kukhala ndi chikumbumtima chabwino pamaso pa Mulungu, kotero kuti ‘tikhale nawo makhalidwe abwino m’zinthu zonse.’​—Ahebri 13:18.

5. Kodi ndimotani mmene kuwona mtima kudzatithandiziranso pamene tichita cholakwa?

5 Kuwona mtima kumatithandiza kukhala odzichepetsa pamene tichita cholakwa. Kudzatichititsa kukhala ovomereza mlandu mosavuta, m’malo moyesa kudzilungamitsa molakwa kapena kukankhira mlanduwo kwa munthu wina. Chifukwa chake, pamene kuli kwakuti Adamu anapatsa mlandu Hava, Davide sanapatse mlandu Bateseba, akumati, ‘Sakanayenera kusamba poonekera. Sindikanapeŵa kuyesedwa.’ (Genesis 3:12; 2 Samueli 11:2-4) Ndithudi, tinganene kuti kumbali ina, kukhala owona mtima kumatithandiza kukhala odzichepetsa; koma kumbali inanso, kukhala odzichepetsa kumatithandiza kukhala owona mtima.

Chikhulupiriro mwa Yehova Chimatithandiza Kukhala Odzichepetsa

6, 7. Kodi ndimotani mmene chikhulupiriro mwa Mulungu chimatithandizira kukhala odzichepetsa?

6 Chikhulupiriro mwa Yehova chidzatithandizanso kukhala odzichepetsa. Kuzindikira mmene Mlengiyo, Mfumu ya Chilengedwe Chonse, aliridi wamkulu kudzatiletsa kudziona kukhala ofunika mopambanitsa. Mneneri Yesaya akutikumbutsa bwino lomwe chotani nanga za zimenezi! Pa Yesaya 40:15, 22, timaŵerenga kuti: “Taonani, amitundu akunga dontho la m’mtsuko, naŵerengedwa ngati fumbi losalala la m’muyeso . . . Ndi Iye amene akhala pamwamba pa malekezero a dziko lapansi, ndipo okhalamo akunga ziŵala.”

7 Chikhulupiriro mwa Yehova chidzatithandizanso pamene tiona kuti tachitiridwa chisalungamo. Mmalo mopitirizabe kuŵaŵidwa mtima ndi nkhaniyo, modzichepetsa tidzadikira Yehova, monga momwe wamasalmo akutikumbutsira pa Salmo 37:1-3, 8, 9. Mtumwi Paulo akutchula mfundo yofananayo kuti: “Musabwezere choipa, okondedwa, koma patukani pamkwiyo; pakuti kwalembedwa, Kubwezera kuli kwanga, Ine ndidzabwezera, ati [Yehova, NW].”​—Aroma 12:19.

Kudzichepetsa​—Njira ya Nzeru

8. Kodi nchifukwa ninji kudzichepetsa kumakulitsa unansi wabwino ndi Yehova?

8 Zilipo zifukwa zambiri zimene kukhala wodzichepetsa kuliri njira ya nzeru. Chimodzi nchakuti, monga momwe kwasonyezedwa kale, kumakulitsa unansi wabwino ndi Mpangi wathu. Mawu a Mulungu amanena mosabisa pa Miyambo 16:5 kuti: “Yense wonyada mtima anyansa Yehova.” Timaŵerenganso pa Miyambo 16:18 kuti: “Kunyada kutsogolera kuwonongeka; mtima wodzikuza ndi kutsogolera kupunthwa.” Mwamsanga kapena pambuyo pake munthu wonyadayo amakhala wachisoni. Zingoyenera kutero chifukwa cha zimene timaŵerenga pa 1 Petro 5:5 kuti: “Nonsenu muvale kudzichepetsa kuti mutumikirane; pakuti Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo kwa odzichepetsa.” Mudzapeza mfundo yofananayo m’fanizo limene Yesu anapereka la Mfarisi ndi wamsonkho amene aliyense wa iwo anali kupemphera. Anali wamsonkho wodzichepetsayo amene anakhaladi wolungama kwambiri.​—Luka 18:9-14.

9. Kodi kudzichepetsa kumathandiza motani m’nthaŵi za mavuto?

9 Kudzichepetsa kuli njira ya nzeru chifukwa chakuti kumachititsa kukhala kosavuta kwa ife kulabadira uphungu wopezeka pa Yakobo 4:7 wakuti: “Potero mverani Mulungu.” Ngati tikhala odzichepetsa, sitidzapanduka pamene Yehova alola kuti tiyang’anizane ndi vuto. Kudzichepetsa kudzatikhozetsa kukhutira ndi mikhalidwe yathu ndi kupirira. Munthu wonyada samakhutira, amafuna zowonjezereka nthaŵi zonse, ndipo amapanduka poyang’anizana ndi mikhalidwe yovuta. Kumbali ina, munthu wodzichepetsa amapirira mavuto ndi ziyeso, monga momwe anachitira Yobu. Yobu anatayikiridwa chuma chake chonse ndipo anakanthidwa ndi nthenda yopweteka kwambiri, ndiyeno mkazi wake anamlangiza kutsatira njira ya kunyada, akumati: “Chitira Mulungu mwano, ufe.” Kodi iye anayankha motani? Cholembedwa cha Baibulo chimatiuza kuti: “Ananena naye, Ulankhula monga amalankhula akazi opusa. Ha! tidzalandira zokoma kwa Mulungu kodi, osalandiranso zoipa? Pa ichi chonse Yobu sanachimwa ndi milomo yake.” (Yobu 2:9, 10) Chifukwa chakuti Yobu anali wodzichepetsa, sanapanduke koma mwanzeru anagonjera pachilichonse chimene Yehova analola kudza pa iye. Ndipo pomalizira pake analandira mfupo yaikulu.​—Yobu 42:10-16; Yakobo 5:11.

Kudzichepetsa Kumakulitsa Unansi Wabwino ndi Ena

10. Kodi kudzichepetsa kumakulitsa motani maunansi athu ndi Akristu anzathu?

10 Kudzichepetsa kuli njira ya nzeru chifukwa chakuti kumakulitsa maunansi abwino ndi Akristu anzathu. Mtumwi Paulo akutipatsa uphungu woyenera kuti: “Musachite kanthu monga mwa chotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pake, komatu ndi kudzichepetsa mtima, yense ayese anzake omposa iye mwini; munthu yense asapenyerere zake za iye yekha, koma yense apenyererenso za mnzake.” (Afilipi 2:3, 4) Kudzichepetsa kudzatiletsa mwanzeru kupikisana ndi ena kapena kuyesa kudzionetsera kuti tawaposa. Mkhalidwe wamaganizo woterowo umadzetsa mavuto pa ife ndi pa Akristu anzathu.

11. Kodi kudzichepetsa kungatithandize motani kupeŵa kuchita zolakwa?

11 Nthaŵi zambiri, kudzichepetsa kudzatithandiza kupeŵa kuchita zolakwa. Motani? Chifukwa chakuti kudzichepetsa kudzatiletsa kukhala odzidalira mopambanitsa. Mmalo mwake, tidzayamikira uphungu wa Paulo wa pa 1 Akorinto 10:12 wakuti: “Iye wakuyesa kuti ali chiriri, ayang’anire kuti angagwe.” Munthu wonyada amadzidalira mopambanitsa, motero akhoza kuchita zolakwa mosavuta chifukwa cha zisonkhezero za ena kapena zifooko za iyemwini.

12. Kodi kudzichepetsa kudzatisonkhezera kukwaniritsa chofunika cha Malemba chotani?

12 Kudzichepetsa kudzatithandiza kumamatira kuzofunika za kukhala ogonjera. Pa Aefeso 5:21, timapatsidwa uphungu wakuti: ‘Gonjerani kwa wina ndi mnzake m’kuwopa Kristu.’ Ndithudi, kodi tonsefe sitimafunikira kukhala ogonjera? Ana amafunikira kukhala ogonjera kwa makolo awo, akazi kwa amuna awo, ndipo amuna kwa Kristu. (1 Akorinto 11:3, Aefeso 5:22; 6:1) Ndiyeno, mumpingo Wachikristu uliwonse, onse, kuphatikizapo atumiki otumikira, ayenera kugonjera akulu. Kodi sizowona kuti akulunso ayenera kukhala ogonjera kwa kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, makamaka monga momwe akuimiridwa ndi woyang’anira dera? Ndiyenonso, woyang’anira dera afunikira kukhala wogonjera kwa woyang’anira chigawo, ndipo woyang’anira chigawo kwa Komiti ya Nthambi ya dzikolo limene akutumikiramo. Bwanji nanga ziŵalo za Komiti ya Nthambi? Ziyenera ‘kugonjera kwa wina ndi mnzake’ ndiponso ku Bungwe Lolamulira, loimira gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, limenenso limagonjera kwa Yesu, Mfumu yoikidwa pampando wachifumu. (Mateyu 24:45-47) Mofanana ndi m’bungwe la akulu lililonse, ziŵalo za Bungwe Lolamulira ziyenera kulemekeza malingaliro a ena. Mwachitsanzo, wina angaganize kuti ali ndi lingaliro labwino kwambiri. Koma ngati ochuluka a ziŵalozo savomereza lingaliro lake, iye adzangoyenera kulisiya. Ndithudi, tonsefe tifunikira kukhala odzichepetsa, chifukwa chakuti tonse tili pansi pa munthu wina.

13, 14. (a) Kodi kudzichepetsa kudzatithandiza makamaka mumkhalidwe wotani? (b) Kodi nchitsanzo chotani chimene Petro anapereka ponena za kulandira uphungu?

13 Kudzichepetsa kumaoneka kukhala njira ya nzeru makamaka chifukwa chakuti kudzichepetsa kumakuchititsa kukhala kosavuta kwa ife kulandira uphungu ndi chilango. Aliyense wa ife amafunikira chilango panthaŵi zina, ndipo tiyenera kulabadira uphungu wa pa Miyambo 19:20 wakuti: “Tamvera uphungu, nulandire mwambo, kuti ukhale wanzeru pa chimaliziro chako.” Monga momwe kwasonyezedwera bwino lomwe, kudzichepetsa kumapha ululu wa chidzudzulo kapena chilango. Ndiponso, mtumwi Paulo, pa Ahebri 12:4-11, akutilangiza ponena za nzeru ya kulandira chilango modzichepetsa. Ndimwanjira yokhayi mmene tingayembekezere kutsatira njira yathu yamtsogolo mwanzeru ndipo mwakutero tikumapata mphotho ya moyo wosatha. Ha, chimenecho chidzakhala chotulukapo chosangalatsa chotani nanga!

14 Pamfundo imeneyi tikhoza kutchula chitsanzo cha mtumwi Petro. Iye analandira uphungu wamphamvu kuchokera kwa mtumwi Paulo, monga momwe timadziŵira m’nkhani ya pa Agalatiya 2:14 kuti: “Pamene ndinaona kuti sanali kuyenda kowongoka, monga mwa chowonadi cha uthenga wabwino, ndinati kwa Kefa [Petro] pamaso pa onse, Ngati inu muli Myuda mutsata makhalidwe a amitundu, ndipo si a Ayuda, mukangamiza bwanji amitundu atsate makhalidwe a Ayuda?” Kodi mtumwi Petro anakhumudwa? Osati kwanthaŵi yonse, ngati anatero nkomwe, monga momwe tingaonere m’mawu ake pambuyo pake akuti “mbale wathu wokondedwa Paulo” pa 2 Petro 3:15, 16.

15. Kodi kukhala kwathu odzichepetsa kumagwirizana motani ndi kukhala kwathu achimwemwe?

15 Palinso nkhani ya kukhala wokwanira, wokhutira. Sitingakhale achimwemwe konse kusiyapo ngati tili okhutira ndi mkhalidwe wathu, mwaŵi wathu, madalitso athu. Mkristu wodzichepetsa amakhala ndi mkhalidwe wamaganizo wakuti: “Ngati Mulungu achilola, ndidzachilandira,” umene mtumwi Paulo akunenadi, monga momwe timaŵerengera pa 1 Akorinto 10:13 kuti: “Sichinakugwerani inu chiyeso koma cha umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.” Chotero tikuonanso mmene kudzichepetsa kuliri njira ya nzeru, popeza kuti kumatithandiza kukhala achimwemwe mosasamala kanthu za mkhalidwe umene tilimo.

Chikondi Chidzatithandiza Kukhala Odzichepetsa

16, 17. (a) Kodi nchitsanzo cha Malemba chotani chimene chimagogomezera mkhalidwe waukulu koposa wotithandiza kukhala odzichepetsa? (b) Kodi nchitsanzo chakudziko chotani chimene chimaperekanso chitsanzo cha mfundo imeneyi?

16 Koposa china chilichonse, chikondi chopanda dyera, a·gaʹpe, chidzatithandiza kukhala odzichepetsa. Kodi nchifukwa ninji Yesu anakhala wokhoza kupirira modzichepetsa kwambiri chokumana nacho chake cha pamtengo wozunzirapo chimene Paulo akufotokozera Afilipi? (Afilipi 2:5-8) Kodi nchifukwa ninji iye sanalingalire konse za kufuna kulingana ndi Mulungu? Chifukwa chakuti, monga momwe iye mwini ananenera kuti: “Ndikonda Atate.” (Yohane 14:31) Ndicho chifukwa chake iye nthaŵi zonse anapereka ulemerero ndi ulemu kwa Yehova, Atate wake wakumwamba. Chifukwa chake, panthaŵi ina iye anagogomezera kuti Atate wake wakumwamba yekhayo ndiye anali wabwino.​—Luka 18:18, 19.

17 Chitsanzo cha mfundo imeneyi tikuchionanso m’chochitika cha m’moyo wa wolemba ndakatulo wakale wa ku America, John Greenleaf Whittier. Mwamuna ameneyu anali ndi bwenzi lake lachitsikana lapamtima pamene anali wachichepere, ndipo tsiku lina pampikisano wa kutchula zilembo za mawu, mtsikanayo anatchula zilembo za liwu lina molondola, pamene iye anazitchula molakwika. Mtsikanayo anaipidwa kwambiri ndi zimenezo. Chifukwa ninji? Monga momwe wandakatuloyo analembera, mtsikanayo anati: “Ndili wachisoni kuti ndinatchula zilembo za liwulo molondola. Sindimafuna kukhala wokuposa . . . chifukwa chakuti, ndimakukonda zedi.” Inde, ngati tikonda munthu wina, tidzafuna munthu ameneyo kukhala wotiposa, osati ife kukhala womposa, chifukwa chakuti chikondi nchodzichepetsa.

18. Kodi kudzichepetsa kudzatithandiza kulabadira uphungu wotani wa Malemba?

18 Limeneli lili phunziro labwino kwa Akristu onse, makamaka abale. Ponena za mwaŵi wapadera wautumiki, kodi tidzasangalala ngati wapatsidwa kwa mbale wathu mmalo mwa ife, kapena kodi tidzachita nsanje ndi kaduka? Ngati tikondadi mbale wathu, tidzasangalala kuti iye anapeza gawo lapadera limenelo kapena kudziŵika kapena mwaŵi wautumiki. Inde, kudzichepetsa kudzakuchititsa kukhala kosavuta kulabadira uphungu wakuti: “Mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu.” (Aroma 12:10) Matembenuzidwe ena amati: “Lemekezanani wina ndi mnzake koposa inumwini.” (New International Version) Ndiyeno timalangizidwanso ndi mtumwi Paulo kuti: “Mwa chikondi chitiranani ukapolo.” (Agalatiya 5:13) Inde, ngati tili ndi chikondi, tidzasangalala kutumikira abale athu, kuwachitira ukapolo, tikumaika zabwino zawo ndi ubwino wawo patsogolo pa zathu, kumene kumafunikira kudzichepetsa. Kudzichepetsa kudzatiletsanso kudzitama ndipo motero tikumapeŵa kudzutsa mwa ena mzimu wa nsanje kapena kaduka. Paulo analemba kuti chikondi “sichidziŵa kudzitamanda, sichidzikuza.” Kulekeranji? Chifukwa chakuti cholinga cha kudzitamandira ndi kudzikuza nchadyera, chodzigangira, pamene kuli kwakuti chikondi ndicho kupanda dyera kwenikweniko.​—1 Akorinto 13:4.

19. Kodi nzitsanzo za Baibulo zotani zimene zimasonyeza kuti kudzichepetsa ndi chikondi zimagwirizana, monga momwe kumachitira kunyada ndi dyera?

19 Unansi wa Davide ndi Mfumu Sauli ndi mwana wake Jonatani uli chitsanzo chochititsa chidwi cha mmene chikondi ndi kudzichepetsa ziliri zogwirizana kwambiri ndi mmene kunyada ndi dyera zilirinso zogwirizana. Chifukwa cha chipambano cha Davide m’nkhondo, akazi a Israyeli anaimba kuti: “Sauli anapha zikwi zake, koma Davide zikwi zake zankhani.” (1 Samueli 18:7) Pokhala wosadzichepetsa konse, koma mmalo mwake, wonyada kwambiri, Sauli kuyambira pamenepo anasunga chidani cha kufuna kupha Davide. Zinali zosiyana chotani nanga zimenezi ndi mzimu wa mwana wake Jonatani! Timaŵerenga kuti Jonatani anakonda Davide monga moyo wake wa iyemwini. (1 Samueli 18:1) Motero kodi Jonatani anachita motani pamene, m’kuchitika kwa zinthu, kunakhala koonekeratu kuti Yehova anali kudalitsa Davide ndi kuti iye, osati Jonatani, akaloŵa m’malo Sauli kukhala mfumu ya Israyeli? Kodi Jonatani anachita nsanje kapena kudukidwa? Osati mpang’ono pomwe! Chifukwa cha chikondi chake chachikulu kwa Davide, iye anakhoza kunena, monga momwe timaŵerengera pa 1 Samueli 23:17 kuti: “Usawopa; chifukwa dzanja la Sauli atate wanga silidzakupeza; iwe udzakhala mfumu ya Israyeli, ndipo ine ndidzakhala wotsatana nawe, ichinso Sauli atate wanga achidziŵa.” Chikondi chachikulu cha Jonatani kwa Davide chinamchititsa kuvomereza modzichepetsa zimene anaziona kukhala chifuniro cha Mulungu ponena za amene anali kudzaloŵa mmalo a atate wake monga mfumu ya Israyeli.

20. Kodi ndimotani mmene Yesu anasonyezera kugwirizana kwathithithi kwa chikondi ndi kudzichepetsa?

20 Chimene chimagogomezeranso kugwirizana kwa chikondi ndi kudzichepetsa ndicho chimene chinachitika pausiku womalizira umene Yesu Kristu anali ndi atumwi ake asanafe. Pa Yohane 13:1, timaŵerenga kuti Yesu, “anakonda ake a iye yekha a m’dziko lapansi, anawakonda kufikira chimaliziro.” Pambuyo pake, timaŵerenga kuti, Yesu anasambitsa mapazi a atumwi ake, akumachita monga mtumiki wamba. Ha, ndiphunziro lamphamvu lotani nanga la kudzichepetsa!​—Yohane 13:1-11.

21. Mwachidule, kodi nchifukwa ninji tiyenera kukhala odzichepetsa?

21 Ndithudi, pali zifukwa zambiri zokhalira odzichepetsa. Kudzichepetsa kuli chinthu choyenera, ndipo kuli kuwona mtima. Kuli njira ya chikhulupiriro. Kumakulitsa unansi wabwino ndi Yehova Mulungu ndi okhulupirira anzathu. Kuli njira ya nzeru. Koposa zonse, kuli njira ya chikondi ndipo kumadzetsa chimwemwe chenicheni.

Kodi Mungayankhe Motani?

◻ Kodi kuwona mtima kumathandiza m’njira zotani kukhala wodzichepetsa?

◻ Kodi chikhulupiriro mwa Yehova chingatithandize motani kukhala odzichepetsa?

◻ Kodi nchiyani chimasonyeza kuti kukhala wodzichepetsa kuli njira ya nzeru?

◻ Kodi nchifukwa ninji chikondi makamaka chili chotithandiza kwambiri kukhala odzichepetsa?

[Chithunzi patsamba 21]

Yobu anagonjera modzichepetsa kwa Yehova. ‘Sanachitire Mulungu mwano kuti afe’

[Chithunzi patsamba 23]

Petro anagonjera modzichepetsa pamene Paulo anampatsa uphungu poyera

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena