Yehova Amaonetsa Ulemerero Wake kwa Odzichepetsa
“Mphoto ya chifatso [“kudzichepetsa,” NW] ndi kuopa Yehova ndiye chuma, ndi ulemu, ndi moyo.”—MIYAMBO 22:4.
1, 2. (a) Kodi buku la Machitidwe limasonyeza motani kuti Stefano anali “munthu wodzala ndi chikhulupiriro ndi Mzimu Woyera”? (b) Kodi pali umboni wotani wosonyeza kuti Stefano anali wodzichepetsa?
STEFANO anali “munthu wodzala ndi chikhulupiriro ndi Mzimu Woyera.” Analinso munthu “wodzala ndi chisomo ndi mphamvu.” Monga mmodzi wa ophunzira oyambirira a Yesu, Stefano ankachita zizindikiro ndi zozizwitsa zikuluzikulu pakati pa anthu. Nthaŵi ina, kunabwera anthu ena kuti adzatsutsane naye, koma “sanathe kuilaka nzeru ndi Mzimu amene analankhula naye.” (Machitidwe 6:5, 8-10) N’zoonekeratu kuti Stefano anali kuphunzira mwakhama Mawu a Mulungu, ndipo anawafotokoza bwino kwa atsogoleri a chipembedzo achiyuda a m’masiku ake. Umboni watsatanetsatane umene anapereka, wolembedwa m’Machitidwe chaputala 7, umasonyeza kuti ankachita chidwi kwambiri ndi zolinga za Mulungu pamene zikukwaniritsidwa pang’onopang’ono.
2 Mosiyana ndi atsogoleri a chipembedzowo, amene ankadziona kuti ndi anthu apamwamba kuposa anthu wamba chifukwa cha udindo wawo ndiponso zinthu zimene anali kudziŵa, Stefano anali wodzichepetsa. (Mateyu 23:2-7; Yohane 7:49) Ngakhale kuti ankadziŵa bwino Malemba, iye anakhutira ndi ntchito imene anapatsidwa ‘yotumikira podyera’ n’cholinga choti atumwi adzipereke pa “kupemphera, ndi kutumikira mawu.” Stefano anali ndi mbiri yabwino pakati pa abale motero anasankhidwa kukhala m’gulu la amuna asanu ndi aŵiri a mbiri yabwino amene akanatha kugwira ntchito imeneyi yogaŵa chakudya tsiku ndi tsiku. Iye anavomera ntchitoyi modzichepetsa.—Machitidwe 6:1-6.
3. Kodi Stefano anaona chizindikiro chotani chapadera cha chisomo cha Mulungu?
3 Yehova anaona mtima wodzichepetsa wa Stefano, kuphatikizaponso chidwi chomwe anali nacho pa zinthu zauzimu ndi kukhulupirika kwake. Pamene Stefano anali kupereka umboni kwa gulu lankhanza la atsogoleri achiyuda m’Sanihedirini, anthu omutsutsa ‘anaona kuti nkhope yake inali ngati nkhope ya mngelo.’ (Machitidwe 6:15) Nkhope yake inali kuoneka ngati nkhope ya mthenga wa Mulungu, yokhala ndi mtendere wochoka kwa Mulungu waulemerero, Yehova. Atapereka umboni molimba mtima kwa anthu a Sanihedirini, Stefano anaona chizindikiro chapadera cha chisomo cha Mulungu. “Iye, pokhala wodzala ndi Mzimu Woyera, anapenyetsetsa Kumwamba, naona ulemerero wa Mulungu, ndi Yesu ali kuimirira pa dzanja lamanja la Mulungu.” (Machitidwe 7:55) Kwa Stefano, masomphenya ochititsa chidwi ameneŵa anam’tsimikiziranso kuti Yesu ndiyedi Mwana wa Mulungu ndiponso Mesiya. Analimbikitsa Stefano wodzichepetsayo ndipo anam’tsimikizira kuti Yehova anali kumuyanja.
4. Kodi Yehova amaonetsa ulemerero wake kwa ndani?
4 Monga momwe masomphenya a Stefano akusonyezera, Yehova amaonetsa ulemerero ndi cholinga chake kwa anthu oopa Mulungu amene ali odzichepetsa ndiponso amene amayamikira ubwenzi wawo ndi iye. Baibulo limati: “Mphoto ya kudzichepetsa ndi kuopa Yehova ndiye chuma, ndi ulemu, ndi moyo.” (Miyambo 22:4) Motero m’pofunika kwambiri kuti timvetse kuti kudzichepetsa kwenikweni n’kutani, zimene tingachite kuti tikhale ndi khalidwe lofunikali, ndiponso phindu limene timapeza pokhala anthu odzichepetsa pazinthu zonse m’moyo wathu.
Kudzichepetsa Ndi Khalidwe Limene Mulungu Amasonyeza
5, 6. (a) Kodi kudzichepetsa n’kutani? (b) Kodi Yehova wasonyeza motani kudzichepetsa? (c) Kodi kudzichepetsa kwa Yehova kuyenera kutikhudza motani?
5 Ena angadabwe kumva kuti Yehova Mulungu, amene ndi wam’mwambamwamba ndiponso waulemerero koposa m’chilengedwe chonse, ndiye chitsanzo chapamwamba kwambiri cha kudzichepetsa. Mfumu Davide inauza Yehova kuti: ‘Mwandipatsa chikopa cha chipulumutso chanu: Ndipo dzanja lamanja lanu landigwiriziza, ndipo kufatsa [“kudzichepetsa,” NW] kwanu kwandikuza ine.’ (Salmo 18:35) Pofotokoza kuti Yehova ndi wodzichepetsa, Davide anagwiritsira ntchito mawu a Chihebri amene kwenikweni amatanthauza “kuwerama.” Kuwonjezera pa mawu akuti “kudzichepetsa,” mawu enanso ochokera ku mawu a Chihebriwo ndi mawu monga “kufatsa,” ndi “kudzitsitsa.” Motero Yehova anasonyeza kudzichepetsa pamene anadzitsitsa kuti ayanjane ndi Davide, yemwe anali wopanda ungwiro, ndi kum’gwiritsira ntchito monga mfumu yomuimira. Monga momwe tikusonyezera timawu tapamwamba pa Salmo 18, Yehova anateteza ndi kuthandiza Davide, ndi kum’landitsa “m’dzanja la adani ake onse, ndi m’dzanja la Sauli.” Ndiyeno, Davide anadziŵa kuti ukulu kapena ulemerero uliwonse womwe anali nawo monga mfumu, anaupeza chifukwa chakuti Yehova anadzichepetsa ndi kumuchitira zinthu zina. Kuzindikira izi kunathandiza Davide kukhala wodzichepetsa.
6 Nanga bwanji ifeyo? Yehova anasankha kutiphunzitsa choonadi, ndipo n’kutheka kuti kudzera m’gulu lake watipatsa mwayi wochita utumiki winawake wapadera, kapena watigwiritsira ntchito mwanjira inayake pokwaniritsa chifuniro chake. Kodi tiyenera kuziona motani zimenezi? Kodi siziyenera kutichititsa kukhala odzichepetsa? Kodi sitiyenera kuyamikira kudzichepetsa kwa Yehova ndi kupeŵa kudzitama, komwe mosakayikira kungatigwetse m’mavuto aakulu?—Miyambo 16:18; 29:23.
7, 8. (a) Kodi kudzichepetsa kwa Yehova kunaonekera motani pa zimene anachita ndi Manase? (b) Pankhani ya kudzichepetsa, kodi Yehova ndiponso Manase amatipatsa chitsanzo mwa njira yotani?
7 Kuwonjezera pa kudzichepetsa kwambiri mwa kuyanjana ndi anthu opanda ungwiro, Yehova wasonyezanso kuti iye ndi wofunitsitsa kuchitira chifundo anthu ‘osauka’ kapena kuti odzichepetsa ngakhalenso kuwautsa, kapena kuwakweza kumene. (Salmo 113:4-7) Mwachitsanzo, taganizirani za nkhani ya Mfumu Manase ya Yuda. Iye anagwiritsira ntchito molakwika udindo wake wapamwamba monga mfumu ndi kulimbikitsa kulambira konyenga ndipo “anachita zoipa zambiri pamaso pa Yehova kuutsa mkwiyo wake.” (2 Mbiri 33:6) M’kupita kwa nthaŵi, Yehova analanga Manase polola kuti atsitsidwe pampando ndi mfumu ya Aasuri. Ali m’ndende, Manase “anapembedza Yehova Mulungu wake, nadzichepetsa kwambiri,” moti Yehova anam’bwezeretsa pampando ku Yerusalemu, “pamenepo anadziŵa Manase kuti Yehova ndiye Mulungu.” (2 Mbiri 33:11-13) Inde, pomaliza pake, Yehova anasangalala ndi mtima wodzichepetsa wa Manase, motero naye anasonyeza kudzichepetsa mwa kum’khululukira ndi kum’bwezeretsa pa ufumu.
8 Tikuphunzirapo zinthu zofunika kwambiri pankhani ya kudzichepetsa pa kufunitsitsa kwa Yehova kukhululukira ena komanso pa mtima wolapa wa Manase. Tizikumbukira nthaŵi zonse kuti zimene timachitira anthu ena amene mwinamwake atilakwira ndiponso mtima womwe timaonetsa tikachimwa zingakhudze mmene Yehova amachitira nafe zinthu. Yehova angathe kutichitira chifundo ngati ifeyo timakhululukira ena machimo awo ndi mtima wonse ndi kuvomereza modzichepetsa zolakwa zathu.—Mateyu 5:23, 24; 6:12.
Ulemerero wa Mulungu Umaonetsedwa kwa Odzichepetsa
9. Kodi kudzichepetsa kumasonyeza kufooka? Fotokozani.
9 Komabe tisaganize kuti kudzichepetsa limodzi ndi makhalidwe ena ofanana ndi khalidweli amasonyeza kufooka kapena chizoloŵezi cholekerera zinthu zoipa. Monga mmene Malemba Opatulika amasonyezera, Yehova ndi wodzichepetsa, koma amakwiya molungama ndiponso amasonyeza mphamvu zochuluka pakafunika kutero. Chifukwa cha kudzichepetsa kwake, Yehova amasamalira, kapena kuti kuganizira mwapadera, anthu odzichepetsa, koma amatalikirana ndi anthu onyada. (Salmo 138:6) Kodi Yehova wasonyeza motani kuwaganizira mwapadera atumiki ake odzichepetsa?
10. Kodi Yehova amaonetsa chiyani kwa anthu odzichepetsa, malinga ndi zimene zili pa 1 Akorinto 2:6-10?
10 Yehova wakhala akuonetsa anthu odzichepetsa mfundo zokhudza kukwaniritsidwa kwa cholinga chake ndipo wakhala akuchita izi panthaŵi yomwe iye wakonza kutero ndiponso mwa njira imene iye wasankha. Zinthu zaulemerero zimenezi n’zobisika kwa anthu amene monyada amadalira, kapena kuumirira nzeru kapena maganizo a anthu. (1 Akorinto 2:6-10) Koma anthu odzichepetsa, popeza kuti adziŵa zenizeni zokhudza cholinga cha Yehova, amalimbikitsidwa kulemekeza Yehova chifukwa chakuti amayamikira kwambiri ulemerero wake.
11. M’zaka 100 zoyambirira, kodi anthu ena anasonyeza motani kuti sanali odzichepetsa, ndipo zimenezi zinawavulaza motani?
11 M’zaka 100 zoyambirira, anthu ambiri kuphatikizapo ena odzitcha Akristu, sanali odzichepetsa ndipo anakhumudwa ndi zimene mtumwi Paulo anawauza pankhani ya cholinga cha Mulungu. Paulo anakhala “mtumwi wa anthu amitundu,” koma sanakhale mtumwi chifukwa cha mtundu womwe anachokera, maphunziro, msinkhu wake, kapena chifukwa chochita ntchito zabwino nthaŵi yaitali. (Aroma 11:13) Nthaŵi zambiri, anthu osaganizira zinthu mwauzimu amaona izi kukhala zizindikiro za munthu amene Yehova ayenera kum’gwiritsira ntchito. (1 Akorinto 1:26-29; 3:1; Akolose 2:18) Koma Paulo anasankhidwa ndi Yehova, malinga ndi kukoma mtima Kwake kwachikondi ndiponso cholinga Chake cholungama. (1 Akorinto 15:8-10) Anthu omwe Paulo anawatcha “atumwi oposatu,” komanso ena omwe anali kum’tsutsa, anakana kuvomereza Paulo ndiponso mfundo zake za m’Malemba. Kusadzichepetsa kunawalepheretsa kudziŵa ndi kumvetsa njira yaulemerero imene Yehova amakwaniritsira cholinga chake. Tiyeni tisapeputse kapena kuweruziratu m’maganizo mwathu anthu amene Yehova wasankha kuwagwiritsira ntchito kuti akwaniritse zofuna zake.—2 Akorinto 11:4-6.
12. Kodi chitsanzo cha Mose chikusonyeza motani kuti Yehova amakonda anthu odzichepetsa?
12 Komabe, pali zitsanzo zambiri za m’Baibulo zosonyeza mmene anthu odzichepetsa amakhalira ndi mwayi woona ulemerero wa Mulungu. Mose, amene anali “wofatsa woposa” anthu onse, anaona ulemerero wa Mulungu ndipo anakhala naye paubwenzi wolimba kwambiri. (Numeri 12:3) Munthu wodzichepetsayu, amene anakhala mbusa wamba kwa zaka 40, ndipo mosakayikira zambiri mwa zakazi zinatha ali ku Arabiya, anakondedwa ndi Mlengi m’njira zambiri. (Eksodo 6:12, 30) Mothandizidwa ndi Yehova, Mose anakhala wolankhulira ndiponso wolinganiza zinthu wamkulu wa mtundu wa Israyeli. Anali kulankhulana ndi Mulungu. M’masomphenya, iye anaona “maonekedwe a Yehova.” (Numeri 12:7, 8; Eksodo 24:10, 11) Anthu amene anavomereza mtumiki wodzichepetsa ndi woimira Mulungu ameneyu, nawonso anadalitsidwa. Mofanana ndi zimenezi, nafenso tidzadalitsidwa ngati tivomereza ndi kumvera Yesu, mneneri woposa Mose, komanso “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amene iye anam’sankha.—Mateyu 24:45, 46; Machitidwe 3:22.
13. Kodi ulemerero wa Yehova unaonetsedwa motani kwa abusa odzichepetsa m’zaka 100 zoyambirira?
13 Kodi ‘kuŵala kwa Ambuye kunaunikira’ ndani pamene angelo analengeza uthenga wabwino wa kubadwa kwa “Mpulumutsi, amene ali Kristu Ambuye”? Sanali atsogoleri achipembedzo odzikuza kapena anthu ofunika a maudindo akuluakulu, koma anali abusa odzichepetsa “okhala kubusa ndi kuyang’anira zoŵeta zawo usiku.” (Luka 2:8-11) Anthu ameneŵa sankapatsidwa ulemu chifukwa cha luso kapena ntchito yawo. Komatu ndi iwo amene Yehova anawaganizira ndipo anawasankha kukhala anthu oyamba kudziŵitsidwa za kubadwa kwa Mesiya. Inde Yehova amaonetsa ulemerero wake kwa anthu odzichepetsa ndi oopa Mulungu.
14. Kodi anthu odzichepetsa amalandira madalitso otani kuchoka kwa Mulungu?
14 Kodi zitsanzo zimenezi zikutiphunzitsa chiyani? Zikutiphunzitsa kuti Yehova amakonda odzichepetsa ndipo amawadziŵitsa ndi kuwathandiza kumvetsa cholinga chake. Iye amasankha anthu amene mwina alibe zinthu zimene anthu angawayembekezere kukhala nazo ndipo amawagwiritsira ntchito yodziŵitsa anthu ena cholinga chake chaulemerero. Izi ziyenera kutilimbikitsa kupitiriza kudalira Yehova, Mawu ake aulosi, ndi gulu lake kuti tipeze malangizo. Tingakhale otsimikiza kuti Yehova adzapitiriza kudziŵitsa atumiki ake odzichepetsa zinthu zimene zikuchitika zokhudza kukwaniritsidwa kwa cholinga chake chaulemerero. Mneneri Amosi anati: “Ambuye Yehova sadzachita kanthu osaulula chinsinsi chake kwa atumiki ake aneneri.”—Amosi 3:7.
Kulitsani Kudzichepetsa Kuti Muyanjidwe ndi Mulungu
15. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kuti tipitirize kukhala odzichepetsa, ndipo kodi mfundo imeneyi ikusonyezedwa motani m’zimene zinachitikira Mfumu Sauli ya Israyeli?
15 Kuti tikhale oyanjidwa ndi Mulungu mpaka muyaya, tiyenera kupitiriza kukhala anthu odzichepetsa. Zili choncho chifukwa chakuti munthu akakhala wodzichepetsa panthaŵi ina sizitanthauza kuti adzakhala wodzichepetsa nthaŵi zonse. N’zotheka kuti munthu asiye kukhala wodzichepetsa n’kuyamba kunyada ndiponso kudzikweza, zomwe zimapangitsa munthu kukhala wodzikuza ndiponso zimam’gwetsa m’mavuto. Izi n’zimene Sauli, munthu woyamba kudzozedwa kukhala mfumu ya Israyeli, anachita. Atangosankhidwa kumene, iye ankadziona kuti ndi ‘wamng’ono.’ (1 Samueli 15:17) Koma atalamulira zaka ziŵiri zokha, anachita zinthu zodzikuza. Iye ananyalanyaza zimene Yehova anakonza, zopereka nsembe kudzera mwa mneneri Samueli, ndipo anapeza zifukwa zosonyezera kuti sakanachitira mwina koma kupereka nsembeyo basi. (1 Samueli 13:1, 8-14) Ichi chinali chiyambi cha zinthu zambirimbiri zomwe anachita zosonyeza poyera kuti anali wodzikuza. Izi zinachititsa kuti mzimu wa Mulungu umuchokere komanso kuti Mulungu asiye kumuyanja, zomwe pomalizira pake zinam’dzetsera imfa yochititsa manyazi. (1 Samueli 15:3-19, 26; 28:6; 31:4) Phunziro lake apa n’loonekeratu: Tiyenera kuyesetsa kupitiriza kukhala odzichepetsa ndiponso ogonjera ndi kuchotsa maganizo odziona kuti ndife ofunika kwambiri, ndipo potero tingapeŵe kuchita chilichonse chosonyeza kudzikuza kumene kungapangitse kuti Yehova asatiyanjenso.
16. Kodi kusinkhasinkha za unansi wathu ndi Yehova ndiponso ndi anthu anzathu kungatithandize bwanji kukulitsa kudzichepetsa?
16 Ngakhale kuti pa chipatso cha mzimu wa Mulungu palibe kudzichepetsa, limeneli ndi khalidwe la Mulungu limene tiyenera kuyesetsa kukhala nalo. (Agalatiya 5:22, 23; Akolose 3:10, 12) Popeza kuti khalidweli limakhudzanso maganizo athu, kapena kuti mmene ifeyo timadzionera ndiponso mmene timaonera anthu ena, pamafunika khama kwambiri kuti tikhale odzichepetsa. Kuganizira mozama za unansi wathu ndi Yehova ndi anthu anzathu ndiponso kusinkhasinkha zimenezo kungatithandize kukhala odzichepetsa. Kwa Mulungu, anthu onse opanda ungwiro ali ngati udzu womwe umakhalapo kwa nthaŵi yochepa, kenako n’kuuma. Anthu ali ngati ziwala m’munda. (Yesaya 40:6, 7, 22) Kodi m’pomveka kuti udzu unyade chabe chifukwa chakuti ndi wotalikirapo kuposa udzu unzake? Kodi m’pomveka kuti chiwala chidzitukumule chifukwa chakuti chingadumphe kwambiri kuposa ziwala zina? N’kupanda nzeru ngakhale kungoganizira zimenezi. Motero, mtumwi Paulo anakumbutsa Akristu anzake kuti: “Akusiyanitsa iwe ndani? Ndipo uli nacho chiyani chosati wachilandira? Koma ngati wachilandira udzitamanda bwanji, monga ngati sunachilandira?” (1 Akorinto 4:7) Kusinkhasinkha malemba a m’Baibulo ngati ameneŵa kungatithandize kukulitsa ndi kusonyeza kudzichepetsa.
17. Kodi n’chiyani chinathandiza mneneri Danieli kukulitsa kudzichepetsa, ndipo kodi n’chiyani chingatithandize kuti tichite chimodzimodzi?
17 Mneneri wachihebri Danieli anatchedwa ‘wokondedwa’ kwambiri ndi Mulungu chifukwa cha “kudzichepetsa” kwake. (Danieli 10:11, 12) Kodi n’chiyani chinathandiza Danieli kukulitsa kudzichepetsa? Choyamba, iye anasonyeza kudalira Yehova ndi mtima wonse, anali kupemphera kwa iye nthaŵi zonse. (Danieli 6:10, 11) Kuwonjezera apo, Danieli anali kuphunzira mwakhama Mawu a Mulungu ndipo ankachita zimenezi ndi cholinga chabwino, zimene zinamuthandiza kuti nthaŵi zonse aziganizira za cholinga chaulemerero cha Mulungu. Komanso anali wofunitsitsa kuvomereza zolakwa zake, osati za anthu amtundu wake zokha. Ndipo anali ndi mtima wolimbikitsa chilungamo cha Mulungu osati wolimbikitsa zofuna zake. (Danieli 9:2, 5, 7) Kodi tingatolepo phunziro pa chitsanzo chabwino kwambiri cha Danieli ndi kuyesetsa kukulitsa ndi kusonyeza kudzichepetsa pazinthu zonse m’moyo wathu?
18. Kodi anthu odzichepetsa adzaona ulemerero wotani?
18 Miyambo 22:4 imati: “Mphoto ya kudzichepetsa ndi kuopa Yehova ndiye chuma, ndi ulemu, ndi moyo.” Inde, Yehova amakonda anthu odzichepetsa ndipo chotsatirapo chake ndi ulemerero ndi moyo. Wamasalmo Asafu, amene anangotsala pang’onong’ono kuti asiye kutumikira Mulungu, koma kenako Yehova anam’thandiza kusintha maganizo ake, anavomera modzichepetsa kuti: “Mudzanditsogolera ndi uphungu wanu, ndipo mutatero, mudzandilandira m’ulemerero.” (Salmo 73:24) Nanga bwanji masiku ano? Kodi anthu odzichepetsa adzaona ulemerero wotani? Kuwonjezera pa kukhala paunansi wosangalatsa ndi Yehova, iwo angayembekezere kudzaona kukwaniritsidwa kwa mawu ouziridwa a Mfumu Davide akuti: “Ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.” Kunena zoona ili ndi tsogolo laulemererodi!—Salmo 37:11.
Kodi Mukukumbukira?
• Kodi Stefano ndi chitsanzo chabwino chotani cha munthu wodzichepetsa amene Yehova anamuonetsa ulemerero Wake?
• Kodi Yehova Mulungu wasonyeza kudzichepetsa m’njira zotani?
• Kodi ndi zitsanzo ziti zimene zikusonyeza kuti Yehova amaonetsa ulemerero wake kwa odzichepetsa?
• Kodi chitsanzo cha Danieli chingatithandize bwanji kukulitsa kudzichepetsa?
[Bokosi patsamba 12]
Munthu Wosasintha Maganizo Ake Mwachisawawa Koma Wodzichepetsa
Pamsonkhano wa Ophunzira Baibulo (omwe tsopano amatchedwa Mboni za Yehova) mu 1919 ku Cedar Point, Ohio, m’dziko la U.S.A., Mbale J. F. Rutherford, yemwe anali ndi zaka 50 ndipo panthaŵiyi anali kuyang’anira ntchito ya Ophunzira Baibulowo, anadzipereka mosangalala kuti athandize kunyamula zikwama za obwera kumsonkhanowo ndi kuwaperekeza kuzipinda zawo. Patsiku lomaliza la msonkhanowo, iye anasangalatsa anthu omwe anabwerapo okwana 7,000 ndi mawu akuti: “Ndinu akazembe a Mfumu ya mafumu ndi Mbuye wa ambuye, olengeza kwa anthu . . . ufumu waulemerero wa Ambuye wathu.” Ngakhale kuti Mbale Rutherford anali munthu wosasintha mwachisawawa mfundo zake, wolankhula mwamphamvu ndiponso wosabwerera m’mbuyo pa zinthu zimene akukhulupirira kuti ndi zoona, mbaleyu analinso wodzichepetsa kwambiri kwa Mulungu, ndipo nthaŵi zambiri zimenezi zinali kuoneka m’mapemphero ake pa kulambira kwa m’maŵa pa Beteli.
[Chithunzi patsamba 9]
Stefano, munthu wodziŵa bwino Malemba, anagaŵa chakudya modzichepetsa
[Chithunzi patsamba 10]
Yehova anasangalala ndi mtima wodzichepetsa wa Manase
[Chithunzi patsamba 12]
Kodi n’chiyani chinapangitsa kuti Danieli akhale ‘wokondedwa’ kwambiri?