Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 2/1 tsamba 9-13
  • Woumba Wamkulu ndi Ntchito Yake

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Woumba Wamkulu ndi Ntchito Yake
  • Nsanja ya Olonda—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Woumba Afutukula Ntchito Yake
  • Kodi Mudzakhala Chotengera Chotani?
  • Timaumbidwa Kuti Tipirire Ziyeso
  • Kuumba Ana Athu
  • Kuumbidwa kwa Aliyense
  • Lolani Kuti Yehova Azikuumbani Ndi Malangizo Ake
    Nsanja ya Olonda—2013
  • Tiziyamikira Kuti Yehova Amatiumba
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
  • Chuma Chathu m’Zotengera Zadothi
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Pulogalamu Yatsopano ya Tsiku la Msonkhano Wapadera
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1999
w99 2/1 tsamba 9-13

Woumba Wamkulu ndi Ntchito Yake

“[Khalani] chotengera cha kuulemu, . . . chokonzera ntchito yonse yabwino.”​—2 TIMOTEO 2:21.

1, 2. (a) Kodi ndi motani mmene kulenga kwa Mulungu mwamuna ndi mkazi kunalili ntchito yapamwamba kwambiri? (b) Kodi n’chifukwa chiyani Woumba Wamkuluyo anapanga Adamu ndi Hava?

YEHOVA ndi Woumba Wamkulu. Ntchito yaluso pa chilengedwe chake inali kholo lathu loyamba, Adamu. Baibulo limatiuza kuti: “Yehova Mulungu anaumba munthu ndi dothi lapansi, nauzira mpweya wa moyo m’mphuno mwake; munthuyo nakhala wamoyo,” ndiko kuti “cholengedwa chopuma.” (Genesis 2:7, NW, mawu amtsinde) Cholengedwa chaumunthu choyamba chimenecho chinali changwiro, choumbidwa m’chifanizo chenicheni cha Mulungu, umboni wa nzeru Zake zaumulungu ndi kukonda kwake chilungamo.

2 Pogwiritsa ntchito zinthu zochokera m’nthiti ya Adamu, Mulungu anaumbanso wokwaniritsa komanso wothangata mwamuna​—mkazi. Hava anali wooneka bwino kupambana mkazi wokongola kwambiri lerolino. (Genesis 2:21-23) Ndiponso, anthu aŵiri oyambirirawo anapatsidwa matupi ndi maluso amene analinganizidwa bwino kuti akwaniritse ntchito imene anapatsidwa ya kupanga dzikoli kukhala paradaiso. Anapatsidwanso mphamvu ya kuchita zimene Mulungu anawalamula pa Genesis 1:28: “Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pa nsomba za m’nyanja, ndi pa mbalame za m’mlengalenga, ndi pa zamoyo zonse zakukwawa pa dziko lapansi.” Potsirizira pake, munda wa padziko lonse umenewu unali kudzadzazidwa ndi mabiliyoni a anthu achimwemwe, omangidwa pamodzi ndi chikondi chimene chili “chomangira cha mtima wamphumphu.”​—Akolose 3:14.

3. Kodi ndi motani mmene makolo athu oyambawo anakhalira zotengera zamanyazi, ndipo zotsatirapo zake zinali zotani?

3 Mwachisoni, makolo athu oyambawo modzifunira anasankha kugalukira ulamuliro wa Mlengi Mfumu yawo, Woumba Wamkulu. Zimene anachita zinakhala ngati zimene zinalongosoledwa pa Yesaya 29:15, 16: “Tsoka kwa iwo amene afunitsa kubisira Yehova uphungu wawo, ndi ntchito zawo zili mumdima, ndipo amati Ndani ationa ife? Ndani atidziŵa ife? . . . Kodi woumba adzayesedwa ngati dothi; kodi chinthu chopangidwa chinganene za iye amene anachipanga, Iye sanandipanga ine konse; kapena kodi chinthu choumbidwa chinganene za iye amene anachiumba, Iye alibe nzeru?” Kupulupudza kwawo kunabweretsa tsoka​—chiweruzo cha imfa yosatha. Ndiponso, mtundu wonse wa anthu wotuluka mwa iwo unalandira choloŵa cha uchimo ndi imfa. (Aroma 5:12, 18) Kukongola kwa chilengedwe cha Woumba Wamkuluyo kunaipitsidwa kwambiri.

4. Kodi tingatumikire ntchito yopatsa ulemu iti?

4 Komabe, ngakhale mmene tili opanda ungwiro teremu, ife mbadwa za Adamu wochimwayo tingatamande Yehova mwa mawu a Salmo 139:14: “Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa n’choopsa ndi chodabwitsa; ntchito zanu n’zodabwitsa; moyo wanga uchidziŵa ichi bwino ndithu.” Komabe, n’zomvetsa chisoni zedi kuti ntchito yoyambirira ya Woumba Wamkuluyo yaipitsidwa kwambiri!

Woumba Afutukula Ntchito Yake

5. Kodi luso la Woumba Wamkuluyo linali kudzasonyezedwa motani?

5 Mwachimwemwe, luso la Mlengi wathu monga Woumba linali kudzasonyezedwa kupitirira kwambiri pa kuumbidwa kwa chilengedwe chake choyambirira cha anthu. Mtumwi Paulo anati: “Koma munthu iwe, ndiwe yani wakubwezera Mulungu mawu? Kodi chinthu chopangidwa chidzanena ndi amene anachipanga, Undipangiranji ine chotero? Kodi kapena woumba mbiya sakutha kuchita zake padothi, kuumba ndi nchinchi yomweyo chotengera chimodzi chaulemu ndi china chamanyazi?”​—Aroma 9:20, 21.

6, 7. (a) Kodi ndi motani mmene anthu ambiri lerolino amasankhira kuumbidwa kaamba ka manyazi? (b) Kodi ndi motani mmene olungama amaumbidwira ku ntchito yaulemu?

6 Inde, ntchito ina ya Woumba Wamkuluyo idzaumbidwa ku ntchito yaulemu, ndipo ina, ku ntchito yamanyazi. Awo amene amasankha kuyendera pamodzi ndi dziko pamene likumka nililoŵerera m’matope a kupanda umulungu akuumbidwa m’njira yowapatsa chizindikiro cha kuwonongedwa. Pamene Mfumu yolemekezeka, Yesu Kristu, idzabwera kudzaweruza, zotengera ‘zamanyazi’ zoterozo zidzaphatikizapo anthu onse amene akakamirabe kukhala monga mbuzi amene, monga momwe Mateyu 25:46 amanenera, “adzachoka kumka ku chilango cha nthaŵi zonse.” Koma “olungama” amene ali ngati nkhosa, amene akuumbidwa ku ntchito ‘yaulemu,’ adzalandira ‘moyo wanthaŵi zonse.’

7 Olungama ameneŵa adzakhala atagonjera modzichepetsa poumbidwa ndi Mulungu. Iwo aloŵa m’njira ya moyo ya Mulungu. Avomereza uphungu umene uli pa 1 Timoteo 6:17-19 wakuti: “Asayembekezere chuma chosadziŵika kukhala kwake, koma Mulungu, amene atipatsa ife zonse kochulukira, kuti tikondwere nazo.” Iwo adzipereka “kuti achite zabwino, nachuluke ndi ntchito zabwino, nakondwere kugaŵira ena, nayanjane; nadzikundikire okha maziko okoma ku nyengo ikudzayi, kuti akagwire moyo weniweniwo.” Akuumbidwa ndi choonadi cha Mulungu ndipo ali ndi chikhulupiriro chosagwedera mu zimene Yehova akupereka kupyolera mwa Yesu Kristu, amene “anadzipereka yekha chiwombolo” kuti abwezeretse zonse zimene zinatayika mwa kuchimwa kwa Adamu. (1 Timoteo 2:6) Choncho tikufunikadi kugonjera mofunitsitsa ku uphungu wa Paulo wakuti ‘tivale [umunthu] watsopano, amene alikukonzeka watsopano [kuumbidwa], kuti akhale nacho chizindikiritso, monga mwa chifaniziro cha Iye amene anam’lenga iye’!​—Akolose 3:10.

Kodi Mudzakhala Chotengera Chotani?

8. (a) Kodi n’chiyani chimene chimachititsa munthu kukhala chotengera chamtundu womwe amakhala? (b) Kodi ndi zinthu ziŵiri ziti zimene zimasonkhezera kuumbidwa kwa munthu?

8 Kodi n’chiyani chimene chimachititsa munthu kukhala chotengera chamtundu womwe amakhala? Maganizo ake ndi khalidwe lake. Izi choyamba zimasonkhezeredwa ndi zikhumbo ndi zolingalira za mtima. Mfumu yanzeru Solomo inati: “Mtima wa munthu ulingalira njira yake; koma Yehova ayendetsa mapazi ake.” (Miyambo 16:9) Kachiŵiri, zimasonkhezeredwa ndi zinthu zimene timamva ndi kuona, mayanjano athu ndi zochitika pamoyo wathu. Motero kulidi kofunika kuti tilabadire uphungu wakuti: “Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru: koma mnzawo wa opusa adzaphwetekedwa.” (Miyambo 13:20) Monga momwe 2 Petro 1:16 akutichenjezera, tiyenera kupewa kutsatira “miyambi yachabe,” kapena mogwirizana ndi Baibulo la Knox la Roma Katolika, “nthano za anthu zopeka.” Izi zikuphatikizapo ziphunzitso ndi mapwando ochuluka a Dziko Lachikristu lampatuko.

9. Kodi ndi motani mmene tingalabadirire bwino poumbidwa ndi Woumba Wamkulu?

9 Motero, Mulungu angatiumbe malinga ndi mmene ifeyo tikulabadirira. Tingabwereze modzichepetsa pamaso pa Yehova pemphero la Davide lakuti: “Mundisanthule, Mulungu, nimudziŵe mtima wanga; mundiyese nimudziŵe zolingalira zanga. Ndipo mupenye ngati ndili nawo mayendedwe oipa, nimunditsogolere pa njira yosatha.” (Salmo 139:23, 24) Yehova akuchititsa kuti uthenga wa Ufumu ulalikidwe. Mitima yathu yalabadira bwino uthenga wabwinowo ndiponso chitsogozo chake chowonjezereka. Kupyolera mwa gulu lake iye amatipatsa mwayi wosiyanasiyana wokhudzana ndi kulalikira uthenga wabwino; tiyeni tiugwiritse, ndi kuusamala kwambiri mwayiwu.​—Afilipi 1:9-11.

10. Kodi tiyenera kulimbikira motani pa kutsatira mapologalamu auzimu?

10 Kulinso kofunika kuti nthaŵi zonse tizilingalira za Mawu a Mulungu, kutsatira pologalamu ya tsiku ndi tsiku ya kuŵerenga Baibulo ndi kumakonda kukambirana Malemba ndi utumiki wa Yehova m’mabanja athu ndiponso ndi mabwenzi athu. Pologalamu ya kulambira kwa mmaŵa panthaŵi ya chakudya cha m’maŵa yochitidwa ndi banja la Beteli ndi gulu la amishonale lililonse la Mboni za Yehova kaŵirikaŵiri imaphatikizapo kuŵerenga, mosinthasintha mlungu uliwonse, mbali yochepa ya Baibulo kapena Yearbook yatsopano. Kodi banja lanu lingachite zofananazo? Ndipo tonsefe timapindulatu kwambiri mwa mayanjano athu mu mpingo wachikristu, pamene tisonkhana pamodzi, ndipo makamaka mwa kutengamo mbali m’phunziro la Nsanja ya Olonda mlungu uliwonse!

Timaumbidwa Kuti Tipirire Ziyeso

11, 12. (a) Kodi uphungu wa Yakobo wokhudza ziyeso tingaugwiritse ntchito bwanji m’moyo wathu watsiku ndi tsiku? (b) Kodi zokumana nazo za Yobu zimatilimbikitsa motani kuti tikhalebe okhulupirika?

11 M’moyo wathu watsiku ndi tsiku, Mulungu amalola kuti tikumane ndi mikhalidwe inayake, ina mwa iyo ingakhale yovuta. Kodi tiyenera kuiona motani? Monga momwe tikulangizidwira pa Yakobo 4:8, tisanyansidwe, koma tiyandikire kwa Mulungu, kumukhulupirira ndi mtima wathu wonse, tikumakhala ndi chidaliro chakuti pamene ‘tiyandikira kwa iye, iye adzayandikira kwa ife.’ Zoonadi, tidzafunika kupirira mavuto ndi ziyeso, koma izo zimaloledwa chifukwa zimawonjezera kutiumba, ndipo chotsatirapo chake chimakhala chosangalatsa. Yakobo 1:2, 3 amatilimbikitsa kuti: “Muchiyese chimwemwe chokha, abale anga, mmene mukugwa m’mayesero amitundumitundu; pozindikira kuti chiyesedwe cha chikhulupiriro chanu chichita chipiriro.”

12 Yakobo anatinso: “Munthu poyesedwa, asanena, Ndiyesedwa ndi Mulungu; pakuti Mulungu sakhoza kuyesedwa ndi zoipa, ndipo Iye mwini sayesa munthu: koma munthu aliyense ayesedwa pamene chilakolako chake cha iye mwini chim’kokera, nichim’nyenga.” (Yakobo 1:13, 14) Tingakumane ndi ziyeso zambiri komanso zosiyanasiyana, koma monga momwe zinalili ndi Yobu, zonsezo zimachita mbali ina yake yotiumba. Ndi chilimbikitso champhamvudi chimene Malemba amatipatsa pa Yakobo 5:11 kuti: “Taonani tiwayesera odala opirirawo; mudamva za chipiriro cha Yobu, ndipo mwaona chitsiriziro cha Ambuye, kuti Ambuye ali wodzala chikondi, ndi wachifundo.” Monga zotengera zomwe zili m’dzanja la Woumba Wamkulu, tiyeni tikhaletu okhulupirika nthaŵi zonse, tikumakhala ndi chidaliro chonga cha Yobu pa chimene chidzakhala chitsiriziro chake!​—Yobu 2:3, 9, 10; 27:5; 31:1-6; 42:12-15.

Kuumba Ana Athu

13, 14. (a) Kodi ndi liti pamene makolo ayenera kuyamba kuumba ana awo, ndipo ayenera kukhala ndi cholinga chotani? (b) Ndi zotsatirapo zosangalatsa ziti zimene munganene?

13 Makolo angathandize kuumba ana awo, kungochokera pamene anawo ali makanda, ndipotu ana athu angakhale anthu okhulupirika kwambiri! (2 Timoteo 3:14, 15) Zimenezi zakhala zoona ngakhale pamene ziyeso zinali zovuta kwambiri. Zaka zingapo zapitazo, pamene chizunzo chinali pachimake m’dziko lina la mu Afirika, banja lina lodalirika linali kusindikiza Nsanja ya Olonda mwachinsinsi kuseri kwa nyumba yawo. Tsiku lina asirikali anali kubwera mumsewu umene unadutsa panyumba pawo, akufufuza m’nyumba iliyonse anyamata oti awapititse kunkhondo. Anyamata aŵiri a m’banjali anali ndi nthaŵi yokwanira yoti abisale, koma kutero kukanachititsa asirikaliwo kufufuza panyumbapo, zimene zikanawululitsadi makina osindikizira aja. Izi zikanachititsa kuti banja lonse lizunzidwe kapenanso mwina kuphedwa. Kodi n’chiyani chimene akanachita? Anyamata aŵiriwo anayankhula, molimba mtima anagwira mawu Yohane 15:13: “Palibe munthu ali nacho chikondi choposa ichi, chakuti munthu ataya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake.” Iwo anaumirira kukhalabe pachipinda chochezera. Asirikaliwo akanawapeza pomwepo ndipo mosakayika akanawazunza kwambiri kapena mwinanso kuwapha ngati atakana kupita kunkhondoko. Komano sakanapitiriza kufufuza. Makina osindikizira pamodzi ndi ena onse a m’banjamo akanakhala ali bwinobwino. Komabe, panachitika zodabwitsa. Asirikaliwo anailambalala nyumba imeneyi, ndi kupita ku nyumba zina! Zotengera zaumunthu zimenezo zoumbidwa kaamba ka ntchito yopatsa ulemu zinapulumuka, pamodzi ndi makina osindikizirawo, kuti zipitirize kufalitsa chakudya chauzimu cha panthaŵi yake. Mmodzi wa anyamata aŵiriwo ndi mlongo wake wina tsopano akutumikira pa Beteli; iye akugwiritsabe ntchito makina akalekalewo.

14 Ana angaphunzitsidwe kupemphera, ndipo Mulungu amayankha mapemphero awo. Chitsanzo chabwino kwambiri pankhaniyi chinachitika ku Rwanda panthaŵi ya kupululutsa anthu. Pamene mwana wina wamkazi wazaka zisanu ndi chimodzi pamodzi ndi makolo ake anauzidwa ndi zigaŵenga kuti akonzeke kuti awaphe ndi bomba la m’manja, iye anapemphera mofuula ndi molimbika mtima kuti awasiye napitirize kutumikira Yehova. Zimenezi zinachititsa kuti anthu ofuna kuwaphawo awaleke, nati, “Sitikuphani chifukwa cha mwanayu.”​—1 Petro 3:12.

15. Kodi Paulo anachenjeza za zinthu zowononga ziti?

15 Ana athu ambiri sangachite kukumana ndi mikhalidwe yovuta ngati imene yalongosoledwa pamwambapo, koma lerolino pali ziyeso zambiri zimene amakumana nazo kusukulu ndi m’malo oipa amene amakhala: kalankhulidwe konyansa, mabuku osonyeza zaumaliseche, zosangulutsa zoluluzika, ndi chisonkhezero cha mabwenzi awo kuti azichita zinthu zolakwika, ndi zofala m’madera ambiri. Mobwerezabwereza, mtumwi Paulo anachenjeza za zinthu zimenezi.​—1 Akorinto 5:6; 15:33, 34; Aefeso 5:3-7.

16. Kodi munthu angakhale chotengera cha ntchito yaulemu motani?

16 Atanena za zotengera “zina zaulemu, koma zina zopanda ulemu,” Paulo anati: “Ngati tsono munthu adziyeretsa yekha pa izi, adzakhala chotengera cha kuulemu, chopatulidwa, choyenera kuchita nacho Mbuye, chokonzera ntchito yonse yabwino.” Choncho tiyeni tilimbikitse achinyamata athu kuti azisamala mayanjano awo. ‘Athaŵe zilakolako za unyamata, natsate chilungamo, chikhulupiriro, chikondi, mtendere, pamodzi ndi iwo akuitana pa Ambuye ndi mitima yoyera.’ (2 Timoteo 2:20-22) Pologalamu yabanja ya ‘kumangirirana wina ndi mnzake’ ingakhale yabwino kwambiri pakuumba ana athu. (1 Atesalonika 5:11; Miyambo 22:6) Kuŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku ndi kumaliphunzira, pogwiritsa ntchito mabuku a Sosaite oyenerera, kungakhale kothandiza kwambiri.

Kuumbidwa kwa Aliyense

17. Kodi tidzaumbidwa motani ndi chilango, ndipo kodi padzakhala zotsatirapo zosangalatsa zotani?

17 Kuti atiumbe, Yehova amatipatsa uphungu kuchokera m’Mawu ake ndi kupyolera mwa gulu lake. Musanyalanyaze uphungu waumulungu woterowo! Umvetsereni mwanzeru, ndipo lolani kuti ukuumbeni kaamba ka ntchito ya Yehova yopatsa ulemu. Miyambo 3:11, 12 imalangiza kuti: “Mwananga, usapeputse mwambo wa Yehova, ngakhale kutopa ndi kudzudzula kwake; pakuti Yehova adzudzula omwe awakonda; monga atate mwana amene akondwera naye.” Uphungu winanso wautate ukuperekedwa pa Ahebri 12:6-11: “Iye amene Ambuye am’konda am’langa . . . Chilango chilichonse, pakuchitika, sichimveka chokondwetsa, komatu chowawa; koma chitatha, chipereka chipatso cha mtendere, kwa iwo ozoloweretsedwa nacho, ndicho cha chilungamo.” Njira yeniyeni yoperekera chilango choterocho iyenera kukhala Mawu ouziridwa a Mulungu.​—2 Timoteo 3:16, 17.

18. Ponena za kulapa, kodi tikuphunziranji pa Luka chaputala 15?

18 Yehova alinso wachifundo. (Eksodo 34:6) Iye amakhululuka pamene munthu asonyeza kulapa tchimo lake kuchokera pansi pa mtima, ngakhale likhale lalikulu kwambiri. Ngakhale ana ‘osakaza’ amasiku ano angaumbidwe kukhala zotengera zopereka ulemu. (Luka 15:22-24, 32) Machimo athu sangakhale aakulu ngati aja a mwana wosakaza. Koma kulabadira kwathu modzichepetsa uphungu wa m’Malemba nthaŵi zonse kudzatipangitsa kuumbidwa kuti tikhale zotengera zopatsa ulemu.

19. Kodi ndi motani mmene tingapitirizire kutumikira monga zotengera zopatsa ulemu m’manja mwa Yehova?

19 Pamene tinayamba kuphunzira choonadi, tinaonetsa kufunitsitsa koti Yehova atiumbe. Tinasiya njira zadziko, tinayamba kuvala umunthu watsopano, ndipo tinakhala Akristu odzipatulira ndi obatizidwa. Tinamvera uphungu wa pa Aefeso 4:20-24, ‘kuvula, kunena za makhalidwe athu oyamba, munthu wakale, wovunda potsata zilakolako za chinyengo; nitivale munthu watsopano, amene analengedwa monga mwa Mulungu, m’chilungamo, ndi m’chiyero cha choonadi.’ Tiyeni aliyense payekha tipitirize kukhala othifuka m’manja mwa Yehova, Woumba Wamkuluyo, nthaŵi zonse tikumatumikira monga zotengera za ntchito yopatsa ulemu!

Kubwereramo

◻ Kodi chifuno cha Woumba Wamkuluyo ndi chotani ponena za dziko lapansi?

◻ Kodi mungaumbidwe motani kaamba ka ntchito yopatsa ulemu?

◻ Kodi ana athu angaumbidwe m’njira yotani?

◻ Kodi chilango tiyenera kuchiona motani?

[Chithunzi patsamba 10]

Kodi mudzaumbidwa kaamba ka ntchito yopatsa ulemu kapena mudzakanidwa?

[Chithunzi patsamba 12]

Ana angaumbidwe kuyambira adakali akhanda

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena