Pulogalamu Yatsopano ya Tsiku la Msonkhano Wapadera
Mutu wa tsiku la msonkhano wapadera wa chaka chautumiki cha 2008 ndi wakuti, “Ndife Dongo, Ndipo Yehova Amatiumba Ngati Mbiya,” ndipo mutu umenewu wachokera pa lemba la Yesaya 64:8. Malangizo a m’Malemba omwe adzaperekedwa pa msonkhano umenewu adzatithandiza kumvetsa bwino nzeru, chilungamo ndi chikondi cha Yehova monga Woumba Mbiya Wamkulu.
Nkhani ya woyang’anira dera yakuti, “Khalani Ziwiya Zolemekezeka Muutumiki,” idzasonyeza mmene anthu ambiri akhalira ndi mwayi wodziwa choonadi ndiponso kuuzako ena. Nkhani yakuti, “Kusinkhasinkha Kumateteza” idzasonyeza mmene kusinkhasinkha mfundo zolungama za Yehova kumatitetezera. Mlendo adzakamba nkhani zomwe zili ndi mitu iyi: “Musamatengere Nzeru za Dongosolo Lino la Zinthu” ndi “Lolani Kuti Woumba Mbiya Wamkulu Akuumbeni.” Makolo ndi achinyamata adzalimbikitsidwa ndi nkhani yakuti, “Achinyamata Amene Yehova Akuwagwiritsira Ntchito” ndiponso yakuti, “Makolo Ali Ndi Udindo Waukulu Pantchito Youmba.” M’mbali yofunsa mafunso ndi zitsanzo, tidzasangalala kumva ndi kuona zimene abale ndi alongo athu akuchita mu utumiki wawo. Anthu amene akufuna kusonyeza kudzipereka kwawo kwa Mulungu mwa ubatizo wa m’madzi ayenera kuuza woyang’anira wotsogolera mwamsanga. Musadzaiwale magazini yanu ya Nsanja ya Olonda yomwe idzaphunziridwe mlungu wa tsiku la msonkhano wapadera.
Zinthu zilizonse zimene Woumba Mbiya Wamkulu akufuna amazichita. Koma aliyense wa ife ayenera kusankha zimene angachite poumbidwa. Anthu omwe amagonjera Yehova ndi kulola kukhala ngati ntchintchi ya dongo pagome la woumba mbiya, amawaumba kuwakulungiza ndi kuwawotcha kukhala ziwiya zamtengo wapatali. Tikamamvera Yehova, timalemekeza ulamuliro wake ndipo timalandira madalitso ambiri.