Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 4/1 tsamba 9-14
  • Moyo wa Pambuyo pa Imfa—Kodi Anthu Amakhulupirira Zotani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Moyo wa Pambuyo pa Imfa—Kodi Anthu Amakhulupirira Zotani?
  • Nsanja ya Olonda—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mayankho Ambiri, Mfundo Yake Imodzimodzi
  • Chiyambi cha Chiphunzitsocho
  • Ufumu wa Dziko Lonse wa Chipembedzo Chonyenga Ukula Kufika Kummaŵa
  • Nanga Bwanji za Chiyuda, Dziko Lachikristu, ndi Chisilamu?
  • Kodi Moyo Umapulumuka pa Imfa?
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Kawonedwe Kanu ka Moyo kamayambukira Moyo Wanu
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Kodi Chikhulupiriro Chanu cha Chiukiriro Ncholimba Motani?
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Kodi Chinthu Ichi Chochedwa “Moyo” n’Chiani?
    Kodi Moyo Uno Ndiwo Wokha Umene Ulipo?
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1999
w99 4/1 tsamba 9-14

Moyo wa Pambuyo pa Imfa​—Kodi Anthu Amakhulupirira Zotani?

“Atafa munthu, adzakhalanso ndi moyo kodi?”​—YOBU 14:14.

1, 2. Kodi ambiri amadzitonthoza motani wokondedwa wawo akamwalira?

M’NYUMBA ya maliro ku New York City, mabwenzi ndi achibale akudutsa mwakachetechete pa bokosi la maliro lotseguka mmene muli mnyamata wazaka 17 amene wamwalira ndi kansa adakali wamng’ono. Amayi ake osweka mtimawo akulira kwinaku akulankhula mobwerezabwereza kuti: “Panopo Tommy akusangalala. Mulungu wafuna kuti Tommy akakhale naye kumwamba.” Amayiwa amakhulupirira zimenezi chifukwa n’zimene anaphunzitsidwa.

2 Ku Jamnagar, India, pamtunda wa makilomita 11,000, wamkulu pa ana aamuna atatu akuyatsa nkhuni zotenthera mtembo wa atate wawo. Moto ukuthetheka, wansembe wotchedwa Brahman akulakatula mapemphero achisansikiriti kuti: “Mzimu wosafawo upitirize ndi khama lake pofuna kugwirizana ndi moyo weniweni.”

3. Kodi anthu kwanthaŵi yaitali akhala akuganiza za mafunso otani?

3 Imfa n’njosapeweka komanso ili kulikonse. (Aroma 5:12) Zimachitika kuti timafuna kudziŵa ngati imfa ili mapeto a zonse. Ataganizaganiza za chilengedwe cha zomera, Yobu mtumiki wakale wokhulupirika wa Yehova Mulungu anati: “Akaulikha mtengo pali chiyembekezo kuti udzaphukanso, ndi kuti nthambi yake yanthete siidzasoŵa.” Nanga bwanji za anthu? “Atafa munthu, adzakhalanso ndi moyo kodi?” Yobu anafunsa motero. (Yobu 14:7, 14) Kwanthaŵi yaitali, anthu kulikonse akhala akuganiza za mafunso akuti: Kodi kuli moyo pambuyo pa imfa? Ngati uliko, ndi wotani? Ndipo kodi anthu afika pokhulupirira zotani, ndipo n’chifukwa chiyani?

Mayankho Ambiri, Mfundo Yake Imodzimodzi

4. Kodi anthu a zipembedzo zosiyanasiyana amakhulupirira zotani ponena za moyo wa pambuyo pa imfa?

4 Akristu mwa dzina lokha ambiri amakhulupirira kuti munthu akamwalira amapita kumwamba kapena kuhelo. Koma Ahindu amakhulupirira kuti munthu amakabadwanso kwina. Malinga ndi zimene Asilamu amakhulupirira, kumakhala tsiku la chiweruzo pambuyo pa imfa, kumene Allah amapenda moyo wa munthu aliyense ndi kum’tumiza ku paradaiso kapena ku moto wa helo. M’mayiko ena, zikhulupiriro zawo ponena za akufa n’zosanganikirana, kwinaku miyambo yawo kwinaku Chikristu mwa dzina lokha, zimene zili zachilendo kwenikweni. Mwachitsanzo, Abuda ndi Akatolika ku Sri Lanka amasiya zitseko ndi mawindo zotsegula wina atamwalira panyumba pawo, ndipo amaika bokosi la maliro moti miyendo ya wakufayo iloze ku khomo la kutsogolo. Amakhulupirira kuti zimenezi zimathandizira mzimu wa wafukayo kutuluka. Akatolika ndi Apulotesitanti ambiri ku West Africa amatsata mwambo wophimba kalirole pamene wina wamwalira n’cholinga chakuti aliyense asayang’anemo ndi kuona mzimu wa munthu wakufayo. Kenako patapita masiku 40, achibale ndi mabwenziwo amachita phwando lokondwerera kukwera kwa mzimu wake kumwamba.

5. Kodi chikhulupiriro chachikulu chimene zipembedzo zambiri zimagwirizanapo n’chotani?

5 Ngakhale kuti pali kusiyanasiyana kotereku, zikuoneka kuti zipembedzo zambiri zimagwirizana ndithu pamfundo imodzi. Zimakhulupirira kuti chinachake m’kati mwa munthu​—chotchedwa mzimu kapena mzukwa​—sichifa ndipo chimapitiriza ndi moyo pambuyo pa imfa ya thupi. Pafupifupi zipembedzo zonse mazanamazana za Dziko Lachikristu ndi timagulu take zimakhulupirira kusafa kwa mzimu. Komanso chikhulupiriro chimenechi ndi chiphunzitso chovomerezeka m’Chiyuda. Ndicho maziko a chiphunzitso cha Chihindu chakuti munthu amakabadwanso kwina. Asilamu amakhulupirira kuti mzimu umakhalabe wamoyo thupi likafa. Aaborigini a ku Australia, okhulupirira za mizimu mu Afirika, Ashinto, ngakhale Abuda, onsewo amaphunzitsa mfundo yomweyi mosiyanasiyana.

6. Kodi akatswiri ena a maphunziro amaliona motani ganizo lakuti mzimu sufa?

6 Komanso alipo ena amene amakhulupirira kuti moyo umathera pa imfa. Kwa iwo, ganizo lakuti mzukwa wopanda thupi umapitiriza kukhala wamoyo utalekana ndi thupi n’lopandiratu nzeru. Miguel de Unamuno, katswiri wa maphunziro wachispanya wa m’zaka za zana la 20, analemba kuti: “Munthu wokhulupirira kusafa kwa mzimu kwenikweni amangolakalaka kuti bwenzi mzimu uli wosafa, komanso chilakolako chakecho n’chachikulu moti chimam’pangitsa kusaganiza mwanzeru.” Enanso amene amakhulupirira zofananazi amaphatikizapo anthu osiyanasiyana onga afilosofi akale Aristotle ndi Epicurus, Hippocrates dokotala, wafilosofi wa ku Scotland David Hume, katswiri wa maphunziro wa ku Arabia Averroës, ndi nduna yaikulu yoyambirira ya boma la India atapata ufulu, Jawaharlal Nehru.

7. Kodi ndi mafunso ati ofunika okhudza chikhulupiriro cha kusafa kwa mzimu amene panopo tiwapende?

7 Pokhala pali malingaliro otero ndi zikhulupiriro zoombana, tiyenera kufunsa kuti: Kodi tilidi ndi mzimu wosafa? Ngati mzimu umafadi, ndiye kuti chiphunzitso chonama chimenechi chinakhala motani mbali yaikulu m’zipembedzo zambiri lerolino? Kodi chikhulupirirocho chinachokera kuti? Tiyenera kupeza mayankho oona ndi okhutiritsa pamafunso ameneŵa chifukwa tsogolo lathu limadalira zimenezi. (1 Akorinto 15:19) Koma choyamba, tiyeni tipende mmene chiphunzitso cha kusafa kwa mzimu chinayambira.

Chiyambi cha Chiphunzitsocho

8. Kodi Socrates ndi Plato anathandizira motani kufutukula chikhulupiriro chakuti mzimu sufa?

8 Agiriki afilosofi a m’zaka za zana lachisanu B.C.E., Socrates ndi Plato, akuti ndiwo anali ena mwa oyamba kulimbikitsa chikhulupiriro chakuti mzimu sufa. Koma sindiwo anayambitsa chikhulupiriro chimenechi. M’malo mwake, anafutukula chiphunzitsocho nachisandutsa chiphunzitso cha filosofi, motero kuchipangitsa kukhala chokopa kwambiri ndi cholandirika kwa anthu ophunzira kwambiri m’nthaŵi yawo ndi m’tsogolo mwake. Choonadi n’chakuti Azolositiliya a ku Perisiya wakale ndi Aigupto amene anali oyambirira ankakhulupiriranso kusafa kwa mzimu. Chotero, funso nali, Kodi chiphunzitso chimenechi chinachokera kuti?

9. Kodi gwero limodzi limene linakhudza chikhalidwe cha Igupto, Perisiya, ndi Girisi n’liti?

9 “M’dziko lakale,” likutero buku lakuti The Religion of Babylonia and Assyria, “Igupto, Perisiya, ndi Girisi anatengera chipembedzo cha ku Babulo.” Ponena za zikhulupiriro zachipembedzo za Igupto, bukulo likupitiriza kuti: “Chifukwa cha kugwirizana pachiyambi kwa Igupto ndi Babulo, malinga ndi umboni wosonyezedwa pamiyala ya ku El-Amarna, panali mipata yochuluka zedi yoti malingaliro ndi miyambo ya Ababulo n’kuloŵa m’zipembedzo za Igupto.”a Zofananazo zinachitikanso ndi chikhalidwe chakale cha Aperisiya ndi Agiriki.

10. Kodi Ababulo ankakhulupirira zotani ponena za moyo wa pambuyo pa imfa?

10 Koma kodi Ababulo akale ankakhulupirira kusafa kwa mzimu? Pamfundo imeneyi, Polofesa Morris Jastrow, Jr., wa pa Yunivesite ya Pennsylvania, U.S.A., analemba kuti: “Anthu ngakhale atsogoleri achipembedzo [a ku Babulo] sanaganize konse kuti zingatheke kuti moyo umene unaliko n’kutheratu. [Iwo] ankaona imfa monga njira yopitira ku moyo wina, ndi kuti kufa [m’moyo uno] kumangosonyeza kuti n’zosatheka kupewa kusintha kumene imfa imadzetsa pamoyo wa munthu.” Inde, Ababulo ankakhulupirira kuti moyo wamtundu wina wake umapitiriza pambuyo pa imfa. Zimenezi ankazisonyeza mwa kukwirira ziŵiya limodzi ndi akufawo zoti akagwiritse ntchito m’moyo wa pambuyo pa imfa.

11, 12. Pambuyo pa Chigumula, kodi gwero la chiphunzitso cha kusafa kwa mzimu linali liti?

11 Inde, chiphunzitso cha kusafa kwa mzimu chinachokera ku Babulo wakale. Kodi zimenezi zili ndi tanthauzo lililonse? Indedi, chifukwa malinga ndi Baibulo, mzinda wa Babele, kapena kuti Babulo, unakhazikitsidwa ndi Nimrode, mdzukulutuvi wa Nowa. Pambuyo pa Chigumula cha padziko lonse m’nthaŵi ya Nowa, anthu onse ankalankhula chinenero chimodzi chokha ndiponso anali ndi chipembedzo chimodzi. Nimrode anali “mpalu wamphamvu pamaso pa [“wotsutsana ndi” NW] Yehova” komanso iye ndi omtsatira ake anafuna ‘kudzipangira iwo okha dzina.’ Mwa kukhazikitsa mzindawo ndi kumangamo nsanja, Nimrode anayambitsa chipembedzo china.​—Genesis 10:1, 6, 8-10; 11:1-4.

12 Malinga ndi nthano zakale, amati Nimrode anafa imfa yachiwawa. N’zomveka kuti atamwalira, Ababulo akanakonda kum’lemekeza kwambiri monga munthu amene anakhazikitsa mzindawo, kuumanga, ndiponso monga mfumu yake yoyamba. Popeza kuti anthu ankakhulupirira kuti mulungu Marduk (Merodake) ndiye anakhazikitsa Babulo ndipo mafumu ena a Babulo ankatchedwa ndi dzina lake, akatswiri ena a maphunziro anena kuti Marduk amaimira Nimrode woyesedwa mulungu. (2 Mafumu 25:27; Yesaya 39:1; Yeremiya 50:2) Ngati zilidi choncho, ndiye kuti ambiri podzafika m’nthaŵi ya Nimrode ankakhulupirira kuti munthu ali ndi mzimu umene umapulumuka imfa. Mulimonse, mbiri imasonyeza kuti pambuyo pa Chigumula, gwero la chiphunzitso cha kusafa kwa mzimu linali Babele, kapena kuti Babulo.

13. Kodi chiphunzitso cha kusafa kwa mzimu chinafalikira motani padziko lonse lapansi, ndipo zotsatira zake zinali zotani?

13 Baibulo limasonyezanso kuti Mulungu analepheretsa zolinga za omanga nsanjawo ku Babele mwa kusokoneza chinenero chawo. Chifukwa cholephera kumvana, iwo anasiya ntchito yawoyo nabalalika “padziko lonse lapansi.” (Genesis 11:5-9) Tisaiŵale kuti ngakhale chinenero cha ofuna kumanga nsanjawa chinasintha, kuganiza kwawo komanso zikhulupiriro zawo sizinasinthe. Chotero, kulikonse kumene anapita, ananyamulanso zikhulupiriro zawo zachipembedzo. Mwanjira imeneyi, ziphunzitso zachipembedzo zachibabulo​—kuphatikizapo cha kusafa kwa mzimu​—zinafalikira padziko lonse lapansi ndipo zinakhala maziko a zipembedzo zazikulu za dziko. Motero ufumu wa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga unakhazikika, umene Baibulo limaufotokoza bwino kukhala ‘Babulo Wamkulu, Amayi wa Achigololo ndi wa Zonyansitsa za Dziko.’​—Chivumbulutso 17:5.

Ufumu wa Dziko Lonse wa Chipembedzo Chonyenga Ukula Kufika Kummaŵa

14. Kodi zikhulupiriro zachipembedzo za ku Babulo zinafalikira motani m’dera lalikululo la India?

14 Olemba mbiri ena amati zaka 3,500 zapitazo, kusamukasamuka kunapangitsa anthu a fuko la Aryan oyererapo kuchoka kumpoto chakumadzulo kupita ku chigwa cha Indus, chimene panopo kwenikweni chili ku Pakistan ndi India. Kenako anamwazikana m’madambo a mtsinje wa Ganges ndi mu India yense. Akatswiri ena amati zikhulupiriro zachipembedzo zimene anthu osamukawo anali nazo zinatengedwa ku ziphunzitso zakale za ku Iran ndi ku Babulo. Ndiyeno zikhulupiriro zimenezi zachipembedzo zinakhala maziko a Chihindu.

15. Kodi chikhulupiriro cha kusafa kwa mzimu chinayamba motani kukhudza Chihindu chamakono?

15 Ku India chikhulupiriro cha kusafa kwa mzimu chinasanduka chiphunzitso chakuti munthu akafa amakabadwanso kwina. Ahindu anzeru, povutika maganizo ndi vuto la dziko lonse la kuipa ndi kuvutika kwa anthu, anafika pa limene amatcha lamulo la Karma, lamulo lakuti pali chochitika pali chochititsa. Ataphatikiza lamulo limeneli ndi chikhulupiriro cha kusafa kwa mzimu, anafika pa chiphunzitso chakuti munthu akafa amakabadwanso kwina, ndi kuti zabwino ndi zoipa zimene munthu amachita pamoyo wake amakafupidwa kapena kulangidwa m’moyo wotsatira. Cholinga cha anthu okhulupirika ndi moksha, kutanthauza kumasuka ku moyo wa kubadwa mobwerezabwereza ndi kugwirizana ndi chimene amati moyo weniweni, kapena Nivana. Zaka mazana ambiri zapita, pamene Chihindu chinkafalikira, chiphunzitso chakuti munthu amakabadwanso kwina chinkafalikiranso. Ndipo chiphunzitso chimenechi chakhala mzati waukulu wa Chihindu chamakono.

16. Kodi ndi chikhulupiriro chotani cha moyo wa pambuyo pa imfa chimene chinakhala champhamvu m’zikhulupiriro zachipembedzo ndi miyambo ya anthu ochuluka ku East Asia?

16 M’Chihindu munatuluka zipembedzo zina, monga Chibuda, Chijaini, ndi Chisiki. Izinso zimakhulupirira kuti munthu akafa amakabadwanso kwina. Ndiponso, pamene Chibuda chinaloŵa m’madera ambiri a ku East Asia​—China, Korea, Japan, ndi kwina kulikonse​—chinasintha kwambiri chikhalidwe ndi chipembedzo cha gawo lonselo. Zimenezi zinayambitsa zipembedzo zokhala ndi zikhulupiriro zambiri zachibuda, kukhulupirira mizimu, ndi kulambira mizimu ya makolo. Zamphamvu kwambiri mwa zimenezo ndi Chitao, Chikomfyushani, ndi Chishinto. Motero chikhulupiriro chakuti moyo umapitiriza pambuyo pa imfa ya thupi chakhala champhamvu kwambiri m’zikhulupiriro zachipembedzo ndi m’miyambo ya anthu ochuluka kudera limenelo la dziko.

Nanga Bwanji za Chiyuda, Dziko Lachikristu, ndi Chisilamu?

17. Kodi Ayuda akale ankakhulupirira zotani ponena za moyo wa pambuyo pa imfa?

17 Kodi anthu a zipembedzo za Chiyuda, Dziko Lachikristu, ndi Chisilamu amakhulupirira zotani ponena za moyo wa pambuyo pa imfa? Pa zipembedzo zimenezi, Chiyuda ndicho chakale koposa. Chiyuda chinayamba pafupifupi zaka 4,000 zapitazo m’nthaŵi ya Abrahamu​—kale kwambiri Socrates ndi Plato asanayambe kukonza chiphunzitso cha kusafa kwa mzimu. Ayuda akale ankakhulupirira kuti akufa adzauka osati kuti munthu amabadwa ali ndi mzimu wosafa. (Mateyu 22:31, 32; Ahebri 11:19) Nangano chiphunzitso cha kusafa kwa mzimu chinaloŵa motani m’Chiyuda? Mbiri yakale imapereka yankho.

18, 19. Kodi chiphunzitso cha kusafa kwa mzimu chinaloŵa motani m’Chiyuda?

18 Mu 332 B.C.E., Alexander Wamkulu analanda Middle East, kuphatikizapo Yerusalemu. Pamene om’loŵa m’malo Alexander anapitiriza zolinga zake zofalitsa Chihelene, panakhala kusanganikirana kwa zikhalidwe ziŵiri​—cha Agiriki ndi cha Ayuda. M’kupita kwa nthaŵi, Ayuda anayamba kudziŵa zikhulupiriro za Agiriki, ndipo ena anakhala afilosofi.

19 Philo wa ku Alexandria, wa m’zaka za zana loyamba C.E., anali mmodzi wa Ayuda otero afilosofi. Iye ankalemekeza Plato ndipo anayesetsa kulongosola Chiyuda malinga ndi filosofi yachigiriki, komwe kunali kulambulira njira Ayuda anzeru a m’tsogolo mwake. Talmud​—ndemanga zolembedwa za arabi zofotokoza chilamulo cha pakamwa​—ilinso ndi zikhulupiriro zachigiriki. “Arabi okonza Talmud,” ikutero Encyclopaedia Judaica, “ankakhulupirira kuti mzimu umapitiriza kukhalako pambuyo pa imfa.” Pambuyo pake mabuku a zinsinsi achiyuda, monga Cabala, amafika ngakhale pophunzitsa kuti munthu akafa amakabadwanso kwina. Chotero chikhulupiriro cha kusafa kwa mzimu chinaloŵa m’Chiyuda kudzera kukhomo lakumbuyo la filosofi yachigiriki, titero kunena kwake. Nanga tingati chiyani ponena za mmene chiphunzitsocho chinaloŵera m’Dziko Lachikristu?

20, 21. (a) Kodi Akristu oyambirira ankaiona motani filosofi ya Plato, kapena yachigiriki? (b) Kodi zinatani kuti pakhale kugwirizana pakati pa zikhulupiriro za Plato ndi ziphunzitso zachikristu?

20 Chikristu chenicheni chinayamba ndi Yesu Kristu. Ponena za Yesu, Miguel de Unamuno, amene wagwidwa mawu poyambirira, analemba kuti: “Iye m’malo mwake ankakhulupirira kuuka kwa anthu m’thupi, malinga ndi Chiyuda, osati kuti mzimu sufa, malinga ndi zimene Plato [Mgiriki] ankakhulupirira.” Iye anafika ponena kuti: “Chiphunzitso cha kusafa kwa mzimu . . . ndicho chikhulupiriro chachikunja cha filosofi.” Chifukwa cha zimenezi, titha kuona chifukwa chake mtumwi Paulo anachenjeza zolimba Akristu a m’zaka za zana loyamba za ‘kukonda nzeru, ndi chinyengo chopanda pake, potsata mwambo wa anthu, potsata zoyamba za dziko lapansi, osati potsata Kristu.’​—Akolose 2:8.

21 Kodi ndi liti ndipo ndi motani mmene “chikhulupiriro chachikunja cha filosofi” chimenechi chinaloŵera m’Dziko Lachikristu? New Encyclopædia Britannica ikunena kuti: “Kuyambira chapakati pa zaka za zana lachiŵiri AD, Akristu amene anaphunzira filosofi yachigiriki anayamba kuganiza kuti n’kofunika kuphunzitsa chikhulupiriro chawo malinga ndi [filosofiyo], kuti iwo eniwo akhutiritse nzeru zawo ndiponso kuti atembenuze anthu akunja ophunzira kwambiri. Filosofi imene inawakhalira bwino kwambiri inali chiphunzitso cha Plato.” Afilosofi aŵiri oyambirira amene anali ndi mphamvu yaikulu pa ziphunzitso za Dziko Lachikristu anali Origen wa ku Alexandria ndi Augustine wa ku Hippo. Onse aŵiri anatengera zikhulupiriro za Plato ndipo ndiwo anali patsogolo kugwirizanitsa zikhulupiriro zomwezo ndi ziphunzitso zachikristu.

22. Kodi chiphunzitso cha kusafa kwa mzimu chakhalabe chachikulu motani m’Chisilamu?

22 Pamene kuli kwakuti chikhulupiriro cha kusafa kwa mzimu chinaloŵa m’Chiyuda ndi m’Dziko Lachikristu kuchokera kwa Plato, chikhulupiriro chimenecho chinalipo kale m’Chisilamu kuchokera pachiyambi. Koran, buku lopatulika la Asilamu, limaphunzitsa kuti munthu ali ndi mzimu umene umapitiriza kukhalako iye atamwalira. Imanena kuti pomaliza mzimu umapita kumunda wa paradaiso kumwamba kapena umapita kukalangidwa kuhelo wamoto. Panopo sitikunena kuti akatswiri a maphunziro achiluya sanayese kugwirizanitsa ziphunzitso zachisilamu ndi filosofi yachigiriki. Kwenikweni, Aluya anatsata ziphunzitso za Aristotle pamlingo winawake. Komabe, Asilamu amakhulupirirabe kusafa kwa mzimu.

23. Kodi ndi mafunso otani ofunika okhudza moyo wa pambuyo pa imfa amene tidzapenda m’nkhani yotsatira?

23 Mwachionekere, zipembedzo kuzungulira dziko lonse zayambitsa zikhulupiriro zosiyanasiyana zodabwitsa ponena za moyo wa pambuyo pa imfa, zozikidwa pa chiphunzitso chakuti mzimu sufa. Ndipo zikhulupiriro zotero zakhudza, inde, ngakhale kulamulira anthu mamiliyoni zikwizikwi ndi kuwapanga akapolo. Chifukwa cha zonsezi, tikukakamizika kufunsa kuti: Kodi zitheka kudziŵa zenizeni zimene zimachitika tikamwalira? Kodi moyo umakhalakobe pambuyo pa imfa? Kodi Baibulo limati chiyani pankhaniyi? Tidzapenda zimenezi m’nkhani yotsatira.

[Mawu a M’munsi]

a El-Amarna ndi malo opezekako mabwinja a mzinda wakale wa Akhetaton wa ku Igupto, umene amati unamangidwa m’zaka za zana la 14 B.C.E.

Kodi Mungafotokoze?

◻ Kodi ndi mfundo imodzi yotani imene imapezeka m’zikhulupiriro zochuluka za zipembedzo yokhudza moyo wa pambuyo pa imfa?

◻ Kodi mbiri yakale ndi Baibulo zimasonyeza motani kuti Babulo wakale ndiye gwero la chiphunzitso cha mzimu wosafa?

◻ Kodi zipembedzo za Kummaŵa zikukhudzidwa motani ndi chikhulupiriro cha ku Babulo cha mzimu wosafa?

◻ Kodi chiphunzitso cha kusafa kwa mzimu chinaloŵa motani m’Chiyuda, Dziko Lachikristu, ndi m’Chisilamu?

[Zithunzi pamasamba 12, 13]

Chilakiko cha Alexander Wamkulu chinapangitsa chikhalidwe cha Agiriki kusanganikirana ndi cha Ayuda

Augustine anayesa kugwirizanitsa filosofi ya Plato ndi Chikristu

[Mawu a Chithunzi]

Alexander: Musei Capitolini, Roma; Augustine: Kuchokera m’buku la Great Men and Famous Women

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena