Mulungu Sazengereza Nalo Lonjezo Lake
“YEHOVA, ndidzafuula mpaka liti osamva inu?” Amene ananena mawuwa anali mneneri wachihebri Habakuku, amene anakhalako m’zaka za zana lachisanu ndi chiŵiri B.C.E. Koma mawuwo sakumveka odabwitsa, si choncho? Mwachibadwa, ife anthu timafuna kuti nthaŵi yomweyo kapena mwamsanga tikhale ndi zinthu zimene tikulakalaka. Zimenezi zili choncho makamaka masiku athu ano ofuna kusangalala nthaŵi yomweyo.—Habakuku 1:2.
M’zaka za zana loyamba, analipo anthu ena amene mwachionekere ankaganiza kuti Mulungu akanakwaniritsa kale malonjezo ake. Iwo anataya mtima kwambiri moti anafika poganiza kuti Mulungu akuzengereza kapena kuti akuchedwa. Chifukwa cha zimenezo, mtumwi Petro anawakumbutsa kuti Mulungu amaona nthaŵi mosiyana ndi mmene ife timaionera. Petro analemba kuti: “Ichi chimodzi musaiŵale, okondedwa inu, kuti tsiku limodzi likhala kwa Ambuye ngati zaka chikwi, ndi zaka chikwi ngati tsiku limodzi.”—2 Petro 3:8.
Malinga ndi njira imeneyi yoŵerengera nthaŵi, munthu wazaka 80 wangokhala ndi moyo pafupifupi maola aŵiri, ndipo mbiri yonse ya anthu yangokhalako pafupifupi masiku asanu ndi limodzi. Tikamaona zinthu mwanjira imeneyi, zimakhala zofeŵerapo kwa ife kumvetsa mmene Mulungu amachitira nafe.
Komabe, sikuti Mulungu alibe nayo ntchito nthaŵi. M’malo mwake, amasunga nthaŵi kwambiri. (Machitidwe 1:7) Ndiye chifukwa chake Petro akupitiriza kuti: “Ambuye sazengereza nalo lonjezano, monga ena achiyesa chizengerezo; komatu aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena awonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.” (2 Petro 3:9) Kusiyana ndi anthu, Mulungu sapanikizika kuchita zinthu ngati kuti nthaŵi idzam’thera. Pokhala “Mfumu yosatha,” ali ndi mphamvu yodabwitsa yooneratu patali ndipo amadziŵa nthaŵi pamene zochita zake zidzathandiza kwambiri onse okhudzidwa.—1 Timoteo 1:17.
Atafotokoza chifukwa chimene Mulungu amaonekera ngati akuzengereza, Petro akupereka chenjezo ili: “Tsiku la Ambuye lidzadza ngati mbala.” Panopo akutanthauza kuti tsiku loŵerengera mlandu lidzafika pamene anthu sakuliyembekezera. Kenako, m’mavesi otsatira, Petro akutchula chiyembekezo chodabwitsa cha amene ali “m’mayendedwe opatulika ndi m’chipembedzo,” kuti angapulumuke ndi kuloŵa mu “miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano” zolonjezedwa ndi Mulungu.—2 Petro 3:10-13.
Zimenezi ziyenera kutithandiza kuyamikira kwambiri kuti chiweruzo cha Mulungu sichinafikebe. Kuleza mtima kwake kwatitheketsa kudziŵa chifuno chake ndi kusintha moyo wathu kuti tikalandire madalitso amene walonjeza. Kodi sitiyenera kuyesa “kulekerera kwa Ambuye wathu chipulumutso,” zimene Petro akulimbikitsa? (2 Petro 3:15) Komanso, kuleza mtima kwa Mulungu kuli ndi mbali ina.
Mlingo wa Mphulupulu Woyenera Kukwanira
Pophunzira zochita za Mulungu ndi anthu akale, timaona kuti iye ankayembekezera kaye asanawononge kufikira chiyembekezo chonse chakuti anthuwo adzawongokera chitatheratu. Mwachitsanzo, za chiweruzo chake pa Akanani, Mulungu anauziratu Abrahamu za machimo awo kukali zaka zambiri. Koma nthaŵi yopereka chiweruzo chake inali isanakwane. Sinakwane bwanji? Baibulo limati: “Pakuti mphulupulu za Aamori [Akanani] sizinakwaniridwe,” kapenanso malinga ndi mmene Baibulo la Knox limanenera: “Kuipa kwa Aamori [kunali] kusanafike pachimake.”—Genesis 15:16.a
Komabe, patapita zaka ngati 400 Mulungu anapereka chiweruzo, ndipo Aisrayeli, mbadwa za Abrahamu, analanda dzikolo. Akanani angapo, monga Rahabu ndi Agibiyoni, anapulumuka chifukwa cha mtima wawo ndi ntchito zawo, koma ochuluka anali atafika ponyansitsa malinga ndi zimene zapezedwa ndi okumba m’mabwinja nthaŵi zino. Iwo ankalambira mphamvu ya kubala, ankachita uhule wapakachisi, ndi kupereka ana nsembe. Halley’s Bible Handbook imati: “Ofukula m’mabwinja amene amakumba mabwinja a mizinda ya Kanani amadabwa chifukwa chake Mulungu sanawawononge mwamsanga koposa ndi mmene anachitira.” Pomaliza pake, ‘mlingo wa machimo a Akanani unadzaza’; kuipa kwawo ‘kunafika pachimake.’ Palibe amene akanaimba Mulungu mlandu wa kusalungama pamene analola dziko kuyeretsedwa kwinaku kupulumutsa aja amene anali ndi mtima wabwino.
Zofananazo tikuzipeza m’tsiku la Nowa. Ngakhale kuti anthu anali oipa Chigumula chisanadze, Mulungu mwachifundo analola nthaŵi yawo kupitirira ndi zaka zina 120. M’kati mwa nthaŵi imeneyo, Nowa anali “mlaliki wa chilungamo.” (2 Petro 2:5) M’kupita kwa nthaŵi, kuipa kwawo mwachionekere kunafika pachimake. “Mulungu anaona dziko lapansi, ndipo taonani, linavunda; pakuti anthu onse anavunditsa njira yawo pa dziko lapansi.” (Genesis 6:3, 12) ‘Mlingo wa machimo awo utakwanira’; kupita kwa nthaŵi kunafikitsa zolingalira zawo zoipa pachimake. Pamene Mulungu anachitapo kanthu, chinali chilungamo chosapeneka. Anthu asanu ndi atatu okha ndiwo anali olungama pamaso pa Mulungu, ndipo iye anawapulumutsa.
Njira imeneyi tikuionanso ndi mmene Mulungu anachitira ndi Israyeli. Ngakhale kuti iwo anakhala osakhulupirika nachita zonyansa, Mulungu analeza nawo mtima zaka mazanamazana. Nkhaniyo imati: “Yehova . . . anatumiza kwa iwo . . . mithenga yake, nalaŵirira mamaŵa kuituma, chifukwa anamvera chifundo anthu ake, . . . koma . . . [a]napeputsa mawu ake, naseka aneneri ake, mpaka ukali wa Mulungu unaukira anthu ake, mpaka panalibe cholanditsa.” (2 Mbiri 36:15, 16) Anthu anafika poti sakanathanso kuwongokera. Yeremiya yekha ndi enanso oŵerengeka ndiwo anapulumuka. Mulungu sakanatchedwa wosalungama pamene pomaliza pake anapereka chiweruzo pa ena onse.
Nthaŵi Yafika Yoti Mulungu Achitepo Kanthu
Malinga ndi zitsanzo zimenezi, titha kuona kuti Mulungu sakupereka chiweruzo pa dongosolo la zinthu lilipoli kufikira nthaŵi yake itakwana. Zimenezi zikusonyezedwa ndi lamulo lopatsidwa kwa wonyonga wophiphiritsa woikidwa ndi Mulungu lakuti: “Tumiza zenga lako lakuthwa, nudule matsango a munda wampesa wa m’dziko; pakuti mphesa zake zapsa ndithu. Ndipo mngelo anaponya zenga lake ku dziko nadula mphesa za m’munda wa m’dziko, naziponya moponderamo mphesa mwamukulu mwa mkwiyo wa Mulungu.” Onani kuti kuipa kwa anthu ‘kunapsa,’ kutanthauza kuti, kunafika poti sikungawongokerenso. Pamene Mulungu apereka chiweruzo, palibe amene adzakayikira chilungamo cha kuloŵererapo kwake.—Chivumbulutso 14:18, 19.
Polingalira zimenezi, n’zachionekere kuti chiweruzo cha Mulungu pa dziko chili pafupi chifukwa mikhalidwe padziko ikufanana ndi mikhalidwe imene inafuna kuti Mulungu apereke chiweruzo kalelo. Kulikonse kumene tingayang’ane, dziko ladzala chiwawa chokhachokha, monga mmene zinalili m’tsiku la Nowa chisanadze Chigumula. Maganizo a anthu akufanana kwambiri ndi amene akufotokozedwa pa Genesis 6:5 kuti: “Ndingaliro zonse za maganizo a mitima [ya anthu] zinali zoipabe zokhazokha.” Ngakhale machimo oipitsitsa amene anachititsa kuti Mulungu aweruze Akanani ali ponseponse lerolino.
Makamaka kuyambira Nkhondo Yadziko I, mtundu wa anthu waona kusintha koopsa. Waona dziko lapansi likudzaza magazi a anthu miyandamiyanda. Nkhondo, kupululutsa mafuko, uchigaŵenga, upandu, ndi kusaweruzika zili kulikonse kuzungulira dziko lapansi. Njala, matenda, ndi chiwerewere zasakaza dziko lathu lapansi. Umboni wonse ukuonetsa kuti tikukhala pakati pa mbadwo woipa umene Yesu anafotokoza kuti: “Mbadwo uwu sudzatha kuchoka, kufikira zinthu zonsezi zidzachitidwa.” (Mateyu 24:34) Tsopano dziko likudzaza “mlingo [wake] wa machimo.” “Matsango a munda wampesa wa m’dziko” akupsa kuti amwetedwe.
Nthaŵi Yakuti Muchitepo Kanthu
Mtumwi Yohane anauzidwa kuti pamene nthaŵi ya chiweruzo iyandikira, zinthu zidzapsa paŵiri. Kumbali ina, “iye wakukhala wosalungama achitebe zosalungama; ndi munthu wonyansa akhalebe wonyansa.” Komanso, “iye wakukhala wolungama achitebe cholungama; ndi iye amene ali woyera akhalebe woyeretsedwa.” (Chivumbulutso 22:10, 11) Izizi zikuchitika mogwirizana ndi ntchito yophunzitsa Baibulo kuzungulira dziko lonse imene Mboni za Yehova zikuchita. Cholinga cha ntchitoyo ndi kuphunzitsa anthu zimene Mulungu amafuna kwa iwo kuti akhale oyenerera kulandira moyo wosatha. Ntchito imeneyi tsopano yafika m’mayiko 233 m’mipingo pafupifupi 87,000.
Mulungu sazengereza. Iye moleza mtima wapatsa anthu nthaŵi yofunika kuti ‘avale umunthu watsopano’ kuti akalandire malonjezo ake. (Aefeso 4:24) Lero, Mulungu adakayembekeza, ngakhale kuti zinthu m’dziko lapansi zikuipiraipira. Mboni za Yehova kuzungulira dziko lonse zikuchita zonse zimene zingathe kugaŵana ndi ena chidziŵitso chotsogolera ku moyo wamuyaya. (Yohane 17:3, 17) Zosangalatsa n’zakuti chaka chilichonse, anthu oposa 300,000 amalabadira ndi kubatizidwa.
Pokhala moyo wosatha uli m’tsogolo, ino si nthaŵi yoyembekeza koma yochitapo kanthu. Pakuti posachedwapa, tidzaona kukwaniritsidwa kwa lonjezo la Yesu lakuti: “Yense wakukhala ndi moyo, nakhulupirira Ine, sadzamwalira nthaŵi yonse.”—Yohane 11:26.
[Mawu a M’munsi]
a Mawu a mtsinde a vesi limeneli mu The Soncino Chumash amati: “Oyenera kupitikitsidwa, pakuti Mulungu salanga mtundu kufikira mlingo wa machimo utakwanira.”
[Chithunzi patsamba 6]
Wonyonga woikidwa ndi Mulungu anauzidwa kutumiza zenga pamene mpesa wa m’dziko lapansi unapsa
[Chithunzi patsamba 7]
Mboni za Yehova kuzungulira dziko lonse zikuthandiza anthu kuti adzalandire madalitso osatha a Mulungu