Kuyamikira “Mphatso za Amuna”
“Dziŵani iwo akugwiritsa ntchito mwa inu, . . . muwachitire ulemu woposatu mwa chikondi, chifukwa cha ntchito yawo.” —1 ATESALONIKA 5:12, 13.
1. Malinga n’kunena kwa Machitidwe 20:35, kodi kupatsa kuli ndi mphamvu yotani? Perekani fanizo.
KUPATSA kutidalitsa koposa kulandira.” (Machitidwe 20:35) Kodi mungakumbukire pamene mawu a Yesu ameneŵa anagwiradi ntchito kwa inu? Mwinamwake inali mphatso imene munapatsa munthu wina amene mumam’konda kwambiri. Muyenera kuti munaisankha bwino kwambiri, popeza munafuna ikhale mphatso imene wokondedwa wanuyo adzaikonda zedi. Pamenepo nkhope ya wokondedwa wanuyo inaŵala—ndipo mtima wanu unasangalala kwabasi! Ngati cholinga chake chili chabwino, kupatsa kumakhala njira yosonyezera chikondi, ndipo kusonyeza chikondi kuli ndi mphamvu yotipatsa chisangalalo.
2, 3. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti palibe aliyense ali ndi chimwemwe choposa cha Yehova, ndipo ndi motani mmene makonzedwe okhala ndi “mphatso za amuna” amasangalatsira mtima wake? (b) Kodi n’chiyani chimene sitingafune kuchitira mphatso yochokera kwa Mulungu?
2 Alipo kodi, amene angakhale ndi chimwemwe choposa cha Yehova, Mpatsi wa “mphatso iliyonse yabwino”? (Yakobo 1:17; 1 Timoteo 1:11) Mphatso iliyonse yochokera kwa iye amaipereka chifukwa cha chikondi chake. (1 Yohane 4:8) Zili chonchonso ndi mphatso imene Mulungu wapatsa mpingo kudzera mwa Kristu—“mphatso za amuna.” (Aefeso 4:8) Mphatso ya akulu oti aziyang’anira nkhosa ndi njira imodzi imene Mulungu wasonyezera chikondi chake chozama kwa anthu ake. Amuna ameneŵa amasankhidwa mosamala kwambiri—ayenera afikire ziyeneretso za m’Malemba. (1 Timoteo 3:1-7; Tito 1:5-9) Iwo amadziŵa kuti ayenera “kuchita ndi nkhosazo mwachifundo,” chifukwa pochita zimenezo nkhosazo zidzasangalala pokhala ndi abusa achikondi otero. (Machitidwe 20:29, NW; Salmo 100:3) Pamene Yehova aona kuti mitima ya nkhosa zake ikudzaza chisangalalo, mtima wakenso umasangalala kwabasi!—Miyambo 27:11.
3 Ndithudi sitingafune kuchepetsa mtengo wake wa mphatso yochokera kwa Mulungu; ndipo sitingafunenso kulephera kuyamikira mphatso zake. Zimenezi zimadzutsa mafunso aŵiri: Kodi akulu ayenera kuliona motani gawo lawo mumpingo? Ndipo ndi motani mmene nkhosa zinazo zingasonyezere kuti zimayamikira “mphatso za amuna”?
‘Tili Othandizana Nanu’
4, 5. (a) Kodi Paulo akufanizira mpingo ndi chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani fanizo limenelo lili loyenera? (b) Kodi fanizo la Paulo limasonyeza kuti tiyenera kuonana motani komanso kuchitirana motani?
4 Yehova wapatsa “mphatso za amuna” mlingo wina wa ulamuliro mumpingo. Zoonadi, akuluwo sangafune kugwiritsa ntchito molakwa ulamuliro wawo, koma amadziŵa kuti pokhala anthu opanda ungwiro, n’kosavuta kuti achite zimenezo. Choncho kodi iwo ayenera kudziona motani podziyerekeza ndi nkhosazo? Talingalirani fanizo limene mtumwi Paulo anagwiritsa ntchito. Atafotokoza chimene “mphatso za amuna” zimaperekedwera, Paulo analemba kuti: “Mwa chikondi tikakule m’zinthu zonse, kufikira Iye amene ali mutu ndiye Kristu; kuchokera mwa Iye thupi lonse, lokowanidwa ndi lolumikizidwa pamodzi, pothandizanapo mfundo yonse, monga mwa kuchititsa kwa chiŵalo chonse pa muyeso wake, lichita makulidwe a thupi, kufikira chimango chake mwa chikondi.” (Aefeso 4: 15, 16) Choncho Paulo akuyerekeza mpingo, kuphatikizapo akulu ndi ziŵalo zina zonse, ngati thupi la munthu. N’chifukwa chiyani fanizo limeneli lili loyenerera?
5 Thupi la munthu linapangidwa ndi ziŵalo zosiyanasiyana koma lili ndi mutu umodzi wokha. Komabe, palibe chiŵalo chopanda ntchito m’thupi—ngakhale mnofu, ngakhale mtsempha, ngakhalenso mnyewa weniweniwo. Chiŵalo chilichonse n’chofunika ndipo chimathandizira ku thanzi ndi kukongola kwa thupi lonse. Mofananamo, mpingo umapangidwa ndi ziwalo zosiyanasiyana, koma chiwalo chilichonse—kaya wamng’ono kapena wokalamba, wolimba kapena wofooka—onse amathandizira pathanzi lauzimu ndi kukongola kwa mpingo wonse. (1 Akorinto 12:14-26) Palibe amene ayenera kudziona ngati wosafunika wosayenera kum’dera nkhaŵa. Komanso, palibe aliyense ayenera kudziona kukhala wapamwamba kwambiri, pakuti tonse pamodzi—abusa ndi nkhosa zomwe—tili mbali ya thupi, ndipo mutu ndi umodzi, Kristu. Chotero Paulo akupereka chithunzi chabwino kwambiri cha chikondi, kusamala, ndi ulemu zimene tiyenera kusonyezana wina ndi mnzake. Kuzindikira zimenezi kumathandiza akulu kuona gawo lawo mumpingo m’njira yodzichepetsa, ndi yoyenera.
6. Ngakhale kuti Paulo anali ndi ulamuliro monga mtumwi, kodi anaonetsa motani mzimu wodzichepetsa?
6 “Mphatso za amuna” zimenezi siziyesa kulamulira miyoyo kapena chikhulupiriro cha alambiri anzawo. Ngakhale kuti Paulo anali ndi ulamuliro monga mtumwi, anauza Akorinto modzichepetsa kuti: “Sikuti tichita ufumu pa chikhulupiriro chanu, koma tikhala othandizana nacho chimwemwe chanu; pakuti ndi chikhulupiriro muimadi.” (2 Akorinto 1:24) Paulo sanakhumbe kulamulira chikhulupiriro ndi moyo wa abale ake. Ndithudi, iye sanaone chifukwa chochitira zimenezo, pakuti anaonetsa kuti anawadalira iwo chifukwa anali kale amuna ndi akazi okhulupirika m’gulu la Yehova pokhumba kuchita choyenera. Chifukwa chake, polankhula za iye mwini ndi mnzake woyenda naye Timoteo, tingatero kuti Paulo kwenikweni anali kunena kuti: ‘Ndi ntchito yathu kugwira ntchito limodzi nanu potumikira Mulungu mwachimwemwe.’ (2 Akorinto 1:1) Mzimu wodzichepetsa kwabasi!
7. Kodi akulu odzichepetsa amazindikira chiyani ponena za gawo lawo mumpingo, ndipo ali ndi chidaliro chotani mwa antchito anzawo?
7 “Mphatso za amuna” lerolino zili ndi ntchito imodzimodziyo. Iwonso ali ‘othandizana nafe kaamba ka chimwemwe chathu.’ Akulu odzichepetsa amazindikira kuti si kwawo kulamula mlingo umene ena angatumikire Mulungu. Amadziŵa kuti pamene kuli kwakuti atha kulimbikitsa ena kuŵirikiza kapena kuwongolera utumiki wawo, kutumikira Mulungu kuyenera kuchokera mumtima wodzipereka. (Yerekezani ndi 2 Akorinto 9:7.) Iwo ali ndi chidaliro chakuti ngati antchito anzawo ali achimwemwe, amachita zonse zimene angathe. Choncho iwo amafunitsitsa kuthandiza abale awo kuti ‘atumikire Yehova ndi chikondwerero.’—Salmo 100:2.
Kuthandiza Onse Kuti Atumikire Mokondwa
8. Kodi ndi njira zina ziti zimene akulu angathandizire abale awo kuti atumikire Yehova mokondwa?
8 Akulu, kodi mungatani kuti muwathandize abale anu kutumikira mokondwa? Mukhoza kuwalimbikitsa mwa chitsanzo chanu. (1 Petro 5:3) Sonyezani changu chanu ndi chimwemwe mu utumiki, ndipo ena adzasonkhezereka mtima pofuna kutengera chitsanzo chanu. Yamikirani ena chifukwa cha kuyesetsa kwawo kwa mtima wonse. (Aefeso 4:29) Kuyamikira kwachikondi ndi koona kumathandiza ena kudziona kukhala athandizo ndi ofunika. Kumalimbikitsa nkhosa kufuna kuchita zoposa potumikira Mulungu. Peŵani kuyerekeza kosayenera. (Agalatiya 6:4) Kuyerekeza koteroko kumalefula m’malo molimbikitsa ena kuti apite patsogolo. Ndi iko komwe, nkhosa za Yehova ndi anthu payekhapayekha—okhala ndi mikhalidwe yosiyanasiyana komanso maluso osiyanasiyana. Monga Paulo, onetsani kuti mumawadalira abale anu. Chikondi “chikhulupirira zinthu zonse,” chifukwa chake tingachite bwino kukhulupirira kuti abale athu amam’konda Mulungu ndipo amafuna kum’kondweretsa. (1 Akorinto 13:7) Pamene ‘muchitira ena ulemu,’ mumawakopa kuti achite zabwino. (Aroma 12:10) Dziŵani kuti ngati nkhosa zilimbikitsidwa ndi kutsitsimutsidwa, zambiri zimachita zonse zotheka potumikira Mulungu, ndipo zimapeza chimwemwe mu utumikiwo.—Mateyu 11:28-30.
9. Kodi akulu okhaokha ayenera kuonana motani kuti athandizane kutumikira mokondwa?
9 Kudziona modzichepetsa monga ‘wothandizana nawo’ kudzathandiza inuyo kutumikira ndi chimwemwe ndi kuyamikira mphatso zapadera za akulu anzanu. Mkulu aliyense ali ndi maluso ake amene angawagwiritse ntchito kupindulitsa mpingo. (1 Petro 4:10) Wina angakhale ndi mphatso yophunzitsa. Wina angakhale waluso kulinganiza zinthu. Winanso angakhale wofikirika kwambiri chifukwa cha kukoma mtima ndi chifundo chake. Mfundo ndi yakuti, palibe mkulu amene ali ndi mphatso zonse pamlingo wachikwanekwane mwa iye yekha. Kodi kukhala ndi mphatso ina—tinene kuti, mphatso yophunzitsa—kumakweza mkuluyo pamwamba pa wina? M’pang’ono pomwe! (1 Akorinto 4:7) Kumbali ina, sitifunikira kukhumudwa ndi mphatso ya wina kapena kudzimva kukhala wopereŵera pamene luso la mkulu wina lipangitsa ena kumam’thokoza. Kumbukirani, inunso muli ndi mphatso zimene Yehova akuziona mwa inu. Ndipo iye akhoza kukuthandizani kuti mukulitse mphatsozo ndi kuzigwiritsa ntchito popindulitsa nazo abale anu.—Afilipi 4:13.
‘Khalani Womvera ndi Wogonjera’
10. N’chifukwa chiyani kuli koyenera kuti tisonyeze kuyamikira pokhala ndi “mphatso za amuna”?
10 Tikalandira mphatso, tiyenera kuyamikira. Akolose 3:15, amati: “Khalani akuyamika.” Bwanji nanga za “mphatso za amuna,” mphatso zamtengo wapatali zimene Yehova watipatsa? Ndithudi tili oyamikira kwambiri kwa Yehova, Wopatsa Mphatso wamataya. Koma bwanji kwa “mphatso za amuna” zenizenizo? Tingasonyeze bwanji kuti timayamikira kukhala nazo?
11. (a) Kodi tingasonyeze motani kuti timayamikira kukhala ndi “mphatso za amuna”? (b) Ndipo mawu akuti “kumvera” ndi “kugonjera” amatanthauzanji?
11 Tikhoza kusonyeza kuti timayamikira kukhala ndi “mphatso za amuna” mwa kulabadira mwachangu uphungu ndi zosankha zawo zozikidwa m’Baibulo. Baibulo limatilangiza kuti: “Mverani atsogoleri anu, nimuwagonjere; pakuti alindirira moyo wanu, monga akuŵerengera; kuti akachite ndi chimwemwe, osati mwachisoni: pakuti ichi sichikupindulitsani inu.” (Ahebri 13:17) Onani kuti sitiyenera kukhala ‘omvera’ chabe komanso ‘ogonjera’ atsogoleri athu. Liwu lachigiriki lotembenuzidwa kuti ‘kugonjera’ kwenikweni limatanthauza ‘kulolera.’ Pothirira ndemanga pamawu akuti ‘kumvera’ ndi ‘kugonjera,’ katswiri wa Baibulo R.C.H. Lenski anati: “Munthu amamvera pamene avomereza chimene wauzidwa kuchita, pamene waona kuti n’cholondola ndi chopindulitsa; munthu amalolera . . . pamene ali ndi maganizo osiyana.” Pamene timvetsa ndi kuvomereza malangizo a atsogoleri athu, kumvera kungakhale kosavuta. Koma bwanji ngati sitikumvetsa chifukwa chimene apangira chosankha china?
12. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala ogonjera, kapena ololera, ngakhale pamene sitikumvetsa chifukwa chimene apangira chosankha chakutichakuti?
12 Apa tsopano m’pamene tifunikira kugonjera, kapena kulolera. Chifukwa chiyani? Choyamba, tiyenera kukhulupirira kuti amuna oyeneretsedwa mwauzimu ameneŵa amafuna kutichitira zabwino zokhazokha. Ndi iko komwe, iwo amadziŵa bwino lomwe kuti Yehova adzanena nawo mlandu wa nkhosa zimene waziikiza m’manja mwawo. (Yakobo 3:1) Komanso, tingachite bwino kukumbukira kuti sitingadziŵe zifukwa zachinsinsi zonse zimene iwo anapangira chosankha chimenecho chimene iwo akuchimvetsa bwino.—Miyambo 18:13.
13. Kodi chingatithandize n’chiyani kuti tikhale ogonjera ponena za zigamulo za akulu za milandu?
13 Bwanji ponena za kugonjera pazigamulo za nkhani zachiweruzo? Kunena zoona, zimenezo zingakhale zovuta, makamaka ngati chigamulocho chakhala chochotsa mumpingo munthu amene timam’konda—wachibale wathu kapena bwenzi lapamtima. Apanso, ndi bwino kwambiri kulolera chiweruzo cha “mphatso za amuna.” Iwo ali m’malo okhoza kuona bwino zinthu kuposa ife, ndipo angadziŵe zifukwa zambiri. Abale ameneŵa kaŵirikaŵiri amavutika maganizo kwambiri kuti afike pazigamulo zimenezo; ‘kuweruzira Yehova’ ndi udindo wofuna kusamala nawo kwambiri. (2 Mbiri 19:6) Iwo amayesetsa kukhala achifundo, poti amazindikira kuti Mulungu “ndi wokhululukira.” (Salmo 86:5) Koma ayeneranso kusungitsa chiyero cha mpingo, ndipo Baibulo limalangiza kuti iwo akayenera kuchotsa mumpingo ochimwa osalapa. (1 Akorinto 5:11-13) Nthaŵi zambiri wochimwayo amavomereza chigamulocho. Chilangocho chingakhale mankhwala ofunikira kuti athandize munthuyo kuzindikira kulakwa kwake. Ngati ifeyo, okondedwa akefe, tikhala ogonjera pamene chigamulo chiperekedwa, tidzam’thandiza kuti apindule ndi chilangocho.—Ahebri 12:11.
“Muwachitire Ulemu Woposa”
14, 15. (a) Malinga n’kunena kwa 1 Atesalonika 5:12, 13, n’chifukwa chiyani kuli kofunika kuti tiziwaganizira akulu? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti akulu ‘amagwiritsa ntchito pakati pathu’?
14 Tikhoza kusonyezanso kuyamikira kwathu “mphatso za amuna” mwa kuonetsa kuwaganizira. Polembera mpingo wa ku Tesalonika, Paulo analangiza ziwalo za mpingowo kuti: “Dziŵani iwo akugwiritsa ntchito mwa inu, nakhala akulu anu mwa Ambuye, nakuyambirirani inu; ndipo muwachitire ulemu woposatu mwa chikondi, chifukwa cha ntchito yawo.” (1 Atesalonika 5:12, 13.) “Akugwiritsa ntchito”—kodi ameneŵa sindiwo mawu ake, pofotokoza akulu amene amadzipereka mopanda dyera kaamba ka ife? Taimani pang’ono ndi kuganizira za mtolo wolemera umene abale okondedwa ameneŵa akuusenza.
15 Ambiri a iwo ndi amuna a mabanja awo amene amagwira ntchito zakuthupi kuti apezere mabanja awo zosoŵa zakuthupi. (1 Timoteo 5:8) Ngati mkulu ali ndi ana, iwo adzafunikira nthaŵi ndi chisamaliro cha bambo wawo. Angafunikire kuwathandiza ndi homuweki yawo, limodzinso ndi kuwapatulira nthaŵi yogwiritsa ntchito nyonga yawo yaunyamata kuchita zinthu zabwino zachisangalalo. (Mlaliki 3:1, 4) Chofunika koposa, iye amasamalira zosoŵa zauzimu za banja lake, kupangitsa phunziro la banja lokhazikika la Baibulo, kugwira nawo ntchito mu utumiki wakumunda, ndi kupita nawo kumisonkhano yachikristu. (Deuteronomo 6:4-7; Aefeso 6:4) Tisaiŵale kuti kuwonjezera pa maudindo ameneŵa amene ambiri tili nawo, akulu alinso ndi ntchito zina: kukonzekera misonkhano, kupanga maulendo aubusa, kusamalira zofunika zauzimu za mpingo, ndipo pamene kwakhala kofunikira, amasamalira milandu. Ena amasamaliranso maudindo ena owonjezera okhudzana ndi misonkhano yadera, misonkhano yachigawo, kumanga Nyumba za Ufumu, ndi Makomiti Olankhulana ndi Zipatala. Ndithudi, abale ameneŵa ‘amagwiritsa ntchito’ kwabasi!
16. Fotokozani njira zimene tingasonyezere kuwaganizira akulu.
16 Nanga tingasonyeze motani kuti timawaganizira? Mwambi wina wa m’Baibulo umati: “Mawu a pa nthaŵi yake kodi sali abwino?” (Miyambo 15:23; 25:11) Choncho mawu owayamikira moona mtima ndi owalimbikitsa angasonyeze kuti sitipeputsa ntchito yawo yaikuluyo. Ndiponso, tiyenera kukhala achikatikati pazimene timafuna kwa iwo. Komanso, tikhale omasuka powafikira iwo tikafuna thandizo. Nthaŵi zina ‘mtima wathu umaŵaŵa’ ndipo timafunikira chilimbikitso cha m’Malemba, chitsogozo, kapena uphungu kuchokera kwa aja “okhoza kuphunzitsa” Mawu a Mulungu. (Salmo 55:4; 1 Timoteo 3:2) Panthaŵi imodzimodzi, tifunikira kukumbukira kuti mkulu sangamawonongere nthaŵi yake yonse pa ife, pakuti sayenera kunyalanyaza zosoŵa za banja lake kapena za enanso mumpingo. Pochitira “chifundo” abale ogwira ntchito zolimba ameneŵa, sitikufuna kuti tiwapanikize ndi zofuna zathu mosaganizira. (1 Petro 3:8) M’malo mwake, tiyeni tiziyamikira nthaŵi ndi chisamaliro zimene angapereke kwa ife.—Afilipi 4:5.
17, 18. Kodi n’kudzimana kotani kumene akazi ambiri a akulu akuchita, ndipo tingasonyeze motani kuti alongo okhulupirika ameneŵa timawaganizira?
17 Bwanji nanga za akazi a akulu? Kodi iwonso safunikira kuwaganizira? Ndi iko komwe, iwo amagaŵana amuna awo ndi mpingo. Pachifukwa chimenechi, iwo amadzimana zinthu zambiri. Nthaŵi ndi nthaŵi, akulu amathera nthaŵi yamadzulo akusamalira nkhani za mpingo pamene anakayenera kukhala ndi mabanja awo. M’mipingo yambiri akazi achikristu okhulupirika amalolera kudzimana mwanjira imeneyo kotero kuti amuna awo asamalire nkhosa za Yehova.—Yerekezani ndi 2 Akorinto 12:15.
18 Kodi tingasonyeze motani kuti alongo achikristu okhulupirika ameneŵa timawaganizira? Inde, tingatero mwa kusatangwanitsa amuna awo mopambanitsa. Koma tisaiŵalenso mphamvu ya mawu ochepa chabe othokoza. Miyambo 16:24 imati: “Mawu okoma ndiwo chisa cha uchi, otsekemera m’moyo ndi olamitsa mafupa.” Taganizirani chochitika ichi. Pambuyo pa msonkhano wachikristu, mbale ndi mkazi wake anafikira mkulu wina napempha kulankhula naye za mnyamata wawo. Mmene mkuluyo amalankhula ndi aŵiri aja, mkazi wake anayembekeza moleza mtima. Atamaliza, mayi uja anapita kwa mkazi wa mkuluyo nati kwa iye: “Zikomo kwambiri kaamba ka nthaŵi imene amuna anu awononga pothandiza banja langa.” Mawu ochepa koma otsekemera othokoza amenewo anakhudzadi mtima wa mkazi wa mkulu uja.
19. (a) Kodi akulu, monga gulu, amakhala okhulupirika pokwaniritsa zolinga zotani? (b) Kodi tonsefe tiyenera kukhala otsimikiza mtima kuti tidzachitanji?
19 Makonzedwe okhala ndi akulu kuti azisamalira nkhosa ndi imodzi mwa ‘mphatso zabwino’ za Yehova. (Yakobo 1:17) Inde, amuna ameneŵa sali angwiro, monga tonsefe sitili angwiro, iwonso amalakwa. (1 Mafumu 8:46) Komabe, monga gulu, akulu mumpingo kuzungulira dziko lonse lapansi akukwaniritsa mokhulupirika cholinga chimene Yehova anawaikirapo—kukonza, kumangirira, ndi kuteteza nkhosa zake. N’kofunika kuti mkulu aliyense akhale ndi cholinga chopitiriza kusamalira nkhosa za Yehova mwachifundo, mwakutero akumatsimikizira kukhala mphatso, kapena dalitso, kwa abale ake. N’kofunikanso kuti tonsefe titsimikize mtima kuti tidzasonyeza kuyamikira kwathu “mphatso za amuna” zimenezi mwa kumvera akulu ndi kuwagonjera komanso kuwaganizira kaamba ka ntchito yawo yaikuluyo. Tikuthokoza Yehova koposa kuti mwachikondi watipatsa amuna, amene amati kwa nkhosa zake: ‘Ndi ntchito yathu yokuthandizani kuti mutumikire Mulungu mokondwa’!
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ N’chifukwa chiyani mpingo ungayerekezedwe bwino lomwe ndi thupi la munthu?
◻ Kodi akulu angathandize motani abale awo kuti atumikire Yehova mokondwa?
◻ N’chifukwa chiyani sitiyenera kungokhala omvera chabe komanso ogonjera atsogoleri athu?
◻ Kodi tingasonyeze kuwaganizira akulu m’njira zotani?
[Chithunzi patsamba 16]
Akulu, yamikirani ena pazoyesayesa zawo zoona mtima
[Chithunzi patsamba 17]
Mwa chitsanzo chawo pokhala achangu mu utumiki, akulu angathandize a m’banja lawo ndi ena kuti atumikire Yehova mokondwa
[Zithunzi patsamba 18]
Timawayamikira kwambiri akulu athu ogwira ntchito zolimba!