Kodi N’kukhulupiriranji mwa Yesu Kristu?
“NGAKHALE anthu ambiri amene sali Akristu amakhulupirira kuti Iye anali mphunzitsi wanzeru komanso wamkulu. Iye analidi mmodzi wa anthu amene anakhalako amene anakhudza miyoyo ya anthu kwambiri.” (The World Book Encyclopedia) Kodi “Iye” ndani? Yesu Kristu, woyambitsa Chikristu.
Koma ngakhale kuti insaikulopediya ikunena zimenezo, kwa anthu miyandamiyanda a Kummaŵa ndi kwina konse, Yesu Kristu ndi mlendo, ndipo dzina lokha angalikumbukire pamene aŵerenga mabuku awo akusekondale. Ngakhale m’matchalitchi a Dziko Lachikristu muli akatswiri a zaumulungu ndi atsogoleri achipembedzo amene amati samudziŵa Yesu ndipo zimenezo zachititsa anthu kukayikira ngati nkhani zinayi (Mauthenga Abwino) za moyo wake zopezeka m’Baibulo zili zoona.
Kodi zingakhale kuti olemba uthenga wabwino anangopeka nkhani ya moyo wa Yesu? Kutalitali! Wolemba mbiri wotchuka Will Durant atapenda mosamalitsa nkhani za m’Mauthenga Abwino analemba kuti: “Kunena kuti anthu wamba oŵerengeka chabe mumbadwo umodzi anapeka munthu wamphamvu ndi wachikoka kwambiri, chikhalidwe chapamwamba kwambiri ndi masomphenya osonkhezera kwambiri a ubale waumunthu, kungakhale chozizwitsa chosakhulupiririka kusiyana ndi china chilichonse cholembedwa m’Mauthenga Abwino. Pambuyo pa zaka mazana aŵiri za Maphunziro Apamwamba Ofufuza Baibulo nkhani zonena za moyo, khalidwe, ndi chiphunzitso cha Kristu, zidakali zomveka bwino ndithu, ndipo n’zochititsa chidwi kwambiri m’mbiri ya anthu a Kumadzulo.”
Chikhalirechobe, pali aja amene amanena kuti safuna kumva za Yesu Kristu chifukwa cha zimene achita anthu odzinenera kukhala otsatira ake. ‘Iwo anakaponya bomba la atomu ku Nagasaki,’ ena amatero ku Japan. ‘Ndipo ku Nagasaki kunali Akristu ambiri kuposa mizinda yambiri m’Japan.’ Komabe kodi mungaimbe mlandu dokotala chifukwa cha matenda a munthu wodwala ngati wodwalayo sanatsatire malangizo a dokotalayo? Anthu ambiri amene amadzinenera kuti ndi Akristu kwa nthawi yaitali akana mankhwala a Yesu ochizira matenda a mtundu wa anthu. Komabe, Yesu anapereka njira yothetsera mavuto athu a tsiku ndi tsiku ngakhalenso mavuto a mtundu wa anthu padziko lonse lapansi. Ndicho chifukwa chake tikukupemphani kuŵerenga nkhani yotsatirayi ndi kuona nokha kuti iye anali munthu wamtundu wotani.