Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • T-24 tsamba 2-6
  • Yesu Kristu—Kodi Iye Ndani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yesu Kristu—Kodi Iye Ndani?
  • Yesu Kristu—Kodi Iye Ndani?
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Langizo Lake—Chikondi
  • Mmene Anasonyezera Chikondi Chake
  • Kodi Yesu Angasinthe Motani Moyo Wanu?
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Kodi N’kukhulupiriranji mwa Yesu Kristu?
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Kodi Mudzalabadira ku Chikondi cha Yesu?
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Kodi Yesu Anachita Zotani Ali Padzikoli?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
Onani Zambiri
Yesu Kristu—Kodi Iye Ndani?
T-24 tsamba 2-6

Yesu Kristu—Kodi Iye Ndani?

“PALI anthu ambiri amene ngakhale kuti iwo si Akristu, amakhulupirira kuti iye anali mphunzitsi wamkulu komanso wanzeru. Mosakayikitsa, Iye analidi m’modzi wa anthu amene anakhalako amene anakhudza miyoyo ya anthu koposa.” (The World Book Encyclopedia) Kodi “Iye” ndani? Yesu Kristu, amene anayambitsa Chikristu. Kodi inuyo mukumudziŵa? Kodi iye n’ngwofunika m’moyo wanu m’njira iliyonse?

Zimene Yesu anachita mu utumiki wake zinalembedwa m’Baibulo, m’mabuku anayi a mbiri otchedwa Uthenga Wabwino. Kodi nkhani zimenezi ndi zokhulupirika motani? Ataziŵerenga mosamala, wolemba mbiri wina wotchuka wotchedwa Will Durant analemba motere: “Chingakhale chinthu chozizwitsa kuposa zozizwitsa zonse zolembedwa mu Uthenga Wabwino, ngati zitatheka kuti mumbadwo umodzi wokha, anthu wamba angapo angathe kungopeka chabe munthu wamphamvu ndi wamakhalidwe okopa amene kwenikweni sanakhaleko. Komanso n’kupeka miyezo yapamwamba ya mikhalidwe ndiponso lingaliro lolimbikitsa kwambiri la ubale pakati pa mtundu wa anthu.”

Komabe, pali anthu mamiliyoni ambiri Kum’maŵa ndi kumadera ena amene Yesu Kristu sakumudziŵa. Mwina amakhulupirira kuti anakhalako, koma saganiza kuti iye ndi wofunika m’moyo wawo. Ena amaona kuti Yesu si woyenera kumuganizira chifukwa cha zinthu zimene anthu amene amati ndi atsatiri ake akhala akuchita. Anthu ena a ku Japan amanena kuti, odzitcha Akristuwo ‘anaphulitsa bomba mu mzinda wa Nagasaki, womwe uli mzinda wokhala ndi Akristu ochuluka koposa mizinda yambiri ku Japan.’

Komabe, kodi ngati wodwala sakuchira chifukwa choti sanatsatire malangizo a dokotala munganene kuti wolakwa ndi dokotalayo? N’zoona simungatero ayi. Anthu a m’matchalitchi achikristu kwa nthaŵi yaitali akhala akunyalanyaza malangizo a Yesu a momwe angathetsere mavuto awo a tsiku ndi tsiku. Choncho m’malo mokana kumva za Yesu chifukwa cha anthu amene amadzitcha kuti ndi Akristu, koma satsatira malangizo ake, bwanji inuyo osaphunzirapo kaye za iye panokha? Yang’anani m’Baibulo, kuti mudziŵe zenizeni za Yesu ndi mmene angasinthire moyo wanu.

Langizo Lake—Chikondi

Yesu Kristu anali mphunzitsi wamkulu amene ankakhala ku Palestina zaka 2000 zapitazo. Palibe nkhani zambiri zokhudza ubwana wake. (Mateyu, chaputala 1 ndi 2; Luka, chaputala 1 ndi 2) Pamene anakwanitsa zaka 30, Yesu anayamba ntchito yake ya ‘kuchitira umboni choonadi.’ (Yohane 18:37; Luka 3:21-23) Anthu anayi amene analemba mbiri ya moyo wa Yesu kwenikweni analemba za utumiki wake kwa anthu, umene anauchita kwa zaka zitatu mwa zaka zochepa zimene anakhalako padziko lapansi.

Mkati mwa utumiki wake, Yesu anauza ophunzira ake njira yothetsera mavuto osiyanasiyana m’moyo wawo. Kodi njira imeneyi inali chiyani? Chikondi. Pa ulaliki wina wotchuka kwambiri m’mbiri, wotchedwa Ulaliki wa Paphiri, Yesu anaphunzitsa ophunzira ake mmene angasonyezere anthu anzawo chikondi. Iye anati: “Zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero.” (Mateyu 7:12) Lamulo limeneli limatchedwa Lamulo Lalikulu Koposa la Makhalidwe. “Anthu” amene Yesu ankawanena pamenepawa akuphatikizapo adani. Pa ulaliki womwewu, iye anati: “Kondanani nawo adani anu, ndi kupempherera iwo akuzunza inu.” (Mateyu 5:44) Kodi chikondi choterechi sichikanathetsa mavuto ambiri amene timapezana nawo lero? Mtsogoleri wa Chihindu Mohandas Gandhi ankaganiza kuti chingathetse. Iye anati: “Ngati tonse titayamba kutsatira zimene Kristu anaphunzitsa pa Ulaliki wake wa Paphiri, ndiye kuti tathetsa mavuto . . . adziko lonse.” Ngati anthu onse atakondana monga momwe Yesu anaphunzitsira, mavuto amtundu wa anthu angathetsedwedi.

Mmene Anasonyezera Chikondi Chake

Yesu ankachitadi zimene ankaphunzitsa. Ankaganizira kaye ena asanadziganizire yekha ndipo anasonyeza chikondi mu zochitika zenizeni. Tsiku lina Yesu ndi ophunzira ake ankalalikira kwa anthu ambiri, osapuma kuti adye. Yesu anaona kuti n’kofunika kuti ophunzira akewo ‘apumule kamphindi,’ choncho ananyamuka kuti apite kwa okha. Koma chigulu cha anthu chinali chitatsogola kale ndipo chinali kuwadikira. Kodi inuyo mukanakhala Yesu mukanatani? Komabe, Yesu ‘anagwidwa chifundo ndi iwo, ndipo anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.’ (Marko 6:30-34) Chifundo chachikulu chimenechi chinam’chititsa kuthandiza ena.

Zimene Yesu anachitira anthu ena si zokhudza kuphunzira Mawu a Mulungu kokha. Ankawathandizanso pa mavuto awo enieni. Mwachitsanzo, anadyetsa amuna 5,000 (osaŵerengera akazi ndi ana) amene ankamvetsera ulaliki wake kufikira madzulo. Tsiku linanso anadyetsa anthu 4,000. Nthaŵi yoyambayo, anagwiritsa ntchito mikate isanu ndi nsomba ziŵiri ndipo, yachiŵiriyo anagwiritsa ntchito mikate isanu ndi iŵiri ndi tinsomba tingapo. (Mateyu 14:14-21; 15:32-38; Marko 6:35-44; 8:1-9) Zozizwitsa? Eetu, ankachita zozizwitsa.

Yesu anachiritsanso anthu ambiri odwala. Anachiritsa akhungu, opuwala, akhate, ndi ogontha. Ngakhale akufa anawaukitsa! (Luka 7:22; Yohane 11:30-45) Nthaŵi ina, munthu wakhate anam’pempha kuti: “Ngati mufuna, mukhoza kundikonza.” Kodi Yesu anatani? ‘Anatansa dzanja nam’khudza iye, nanena naye, ndifuna; khala wokonzedwa.’ (Marko 1:40, 41) Yesu anali wofunitsitsa kuwathandiza. Mwa njira ya zozizwitsa zimenezi, anasonyeza kuti amakonda anthu ovutika.

Kodi n’zovuta kukhulupirira? Komatu Yesu ankachita zozizwitsa zake zambiri poyera. Ngakhale anthu amene ankamutsutsa n’kumayesa kum’pezera zifukwa pa chinthu chilichonse chimene angachite, sanatsutsepo kuti ankachita zozizwitsa. (Yohane 9:1-34) Ndiponso kuwonjeza apo zozizwitsa zake zinali ndi cholinga. Zinathandiza anthu kuzindikira kuti Yesu ndi amene anatumidwa ndi Mulungu.—Yohane 6:14.

Kupenda mwachidule chabe ziphunzitso za Yesu ndi moyo wake kumatipangitsa ife kum’konda ndi kufuna kutsanzira chikondi chake. Koma, imeneyi si njira yokhayo imene Yesu alili wofunika m’moyo wanu. Si kuti anali chabe mphunzitsi wamkulu amene ankaphunzitsa chikondi. Iye anasonyezanso kuti anakhalapo kale monga Mwana wobadwa yekha wa Mulungu pamene anali asanabadwe monga munthu. (Yohane 1:14; 3:16; 8:58; 17:5; 1 Yohane 4:9) Komanso atasiya thupi lake la umunthu anakhalapobe ndipo n’chifukwa chake ali wofunika kwambiri kwa inu. Baibulo limasonyeza kuti Yesu anaukitsidwa ndipo tsopano wadzozedwa monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. (Chivumbulutso 11:15) Yesu ananena kuti: “Moyo wosatha ndi uwu, kumaloŵetsa kwawo chidziŵitso cha inu, Mulungu yekha woona, ndi cha iye amene munam’tuma, Yesu Kristu.” (Yohane 17:3, NW; 20:31) N’zoonadi, kulowetsa m’maganizo mwathu chidziŵitso cha Yesu Kristu kungatanthauze moyo wosatha pa dziko lapansi laparadaiso! Kodi zimenezi zingatheke bwanji? Bwanji osapitiriza kuphunzirabe zinthu zina za Yesu kuti muone mmene ‘chikondi cha Kristu chimatikakamizira’ kuti muthe kumutsanzira? (2 Akorinto 5:14) Mboni za Yehova zingakhale zosangalala kuti zikuthandizeni.— Yohane 13:34, 35.

Malemba onse atengedwa m’Baibulo la Revised Nyanja (Union) Version, kupatulapo ngati tasonyeza Baibulo lina.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena