Kodi Yesu Angasinthe Motani Moyo Wanu?
YESU KRISTU anali Mphunzitsi Wamkulu amene ankakhala ku Palestina pafupifupi zaka 2,000 zapitazo. Zochepa chabe n’zimene zimadziŵika ponena za ubwana wake. Komabe, n’zotsimikizirika kuti pamene anali ndi zaka pafupifupi 30 zakubadwa, anayamba utumiki wake ‘wochita umboni ndi choonadi.’ (Yohane 18:37; Luka 3:21-23) Ophunzira anayi amene analemba nkhani zonena za moyo wake anafotokoza kwambiri za pa zaka zitatu ndi theka zotsatirapo.
Panthaŵi ya utumiki wake, Yesu Kristu anapatsa ophunzira ake lamulo limene lingakhale mankhwala othetsera mavuto ambirimbiri a dziko lapansi. Kodi ilo linali lotani? Yesu anati: “Ndikupatsani inu lamulo latsopano, kuti mukondane wina ndi mnzake; monga ndakonda inu, kuti inunso mukondane wina ndi mnzake.” (Yohane 13:34) Inde, njira yothetsera mavuto ambirimbiri a mtundu wa anthu ndiyo chikondi. Nthaŵi ina pamene Yesu anafunsidwa za lamulo lalikulu koposa, iye anayankha kuti: “Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse. Ili ndilo lamulo lalikulu ndi loyamba. Ndipo lachiŵiri lolingana nalo ndi ili, Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini.”—Mateyu 22:37-40.
Yesu anasonyeza mwa mawu komanso zochita mmene tingakondere Mulungu ndi anthu anzathu. Tiyeni tipende zina mwa zitsanzo zochepa ndi kuona zimene tingaphunzire kwa iye.
Ziphunzitso Zake
Pa umodzi wa maulaliki otchuka m’mbiri, Yesu Kristu anauza otsatira ake kuti: “Palibe munthu angathe kukhala kapolo wa ambuye aŵiri: pakuti pena adzamuda mmodziyo, ndi kukonda winayo; pena adzakangamira kwa mmodzi, nadzanyoza wina. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Chuma.” (Mateyu 6:24) Kodi chiphunzitso cha Yesu chonena za kuika Mulungu patsogolo m’moyo wathu chingagwiredi ntchito lerolino pamene anthu ambiri akhulupirira kuti ndalama ndiyo imathetsa mavuto onse a munthu? Ndi zoona kuti timafunikira ndalama kuti tipeze zofunika pamoyo wathu. (Mlaliki 7:12) Komabe, ngati tilola “Chuma” kukhala mbuye wathu, “chikondi cha pandalama” chidzatilamulira, inde chidzalamuliranso moyo wathu wonse. (1 Timoteo 6:9, 10) Ambiri amene agwera mumsampha umenewu pomalizira pake athetsa nazo mabanja awo, kutayikidwa thanzi lawo labwino, ndiponso ngakhale kutaya miyoyo yawo kumene.
Komabe, kuyang’ana kwa Mulungu monga Mbuye wathu kumachititsa moyo wathu kukhala watanthauzo. Monga Mlengi, iye ndiye Gwero la moyo, choncho ndi iye yekha amene tiyenera kum’lambira. (Salmo 36:9; Chivumbulutso 4:11) Amene amaphunzira za mikhalidwe yake ndi kum’kondadi amasonkhezereka kumvera malamulo ake. (Mlaliki 12:13; 1 Yohane 5:3) Mwa kuchita zimenezi timapindula ife eni.—Yesaya 48:17.
Pa Ulaliki wa pa Phiri, Yesu anaphunzitsanso ophunzira ake mmene angasonyezere chikondi kwa anthu anzawo. Iye anati: “Chifukwa chake zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero.” (Mateyu 7:12) Liwu lakuti “anthu” limene Yesu anagwiritsa ntchito pano limaphatikizapo ngakhale adani a munthuwe. Paulaliki womwewo, iye anati: “Kondanani nawo adani anu, ndi kupempherera iwo akuzunza inu.” (Mateyu 5:43, 44) Kodi chikondi chotere sichingathe kuthetsa mavuto ambirimbiri amene tikukumana nawo lerolino? Mtsogoleri wachihindu Mohandas Gandhi anaganiza motero. Iye anagwidwa mawu akumati: “Ngati tingagwirizane pa ziphunzitso za Kristu zonenedwa pa Ulaliki wa pa Phiri umenewu, pamenepo tidzathetsa mavuto . . . a dziko lonse lapansi.” Ngati ziphunzitso za Yesu zonena za chikondi zingatsatiridwe, zingathetsedi mavuto ambirimbiri a mtundu wa anthu.
Zochita Zake
Yesu sanangophunzitsa choonadi chakuya chonena za mmene tingasonyezere chikondi komanso anachita zomwe anaphunzitsa. Mwachitsanzo, anaika zofuna za ena patsogolo kuposa zake. Tsiku lina Yesu ndi ophunzira ake anali otanganitsidwa kuthandiza anthu kwakuti analibe ndi mpata womwe woti adye. Yesu anaona kuti ophunzira ake afunika apume pang’ono, ndipo anawatengera kwaokha. Koma pamene anafika komweko, anapeza khamu la anthu likuwadikira. Kodi inu mukanachita motani ngati mukanaona khamu la anthu amene akufuna kuti muzigwirabe ntchito pamene inu mukuona kuti mukufunikira kupuma pang’ono? Chabwino, Yesu ‘anagwidwa chifundo ndi iwo’ ndipo “anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.” (Marko 6:34) Nthaŵi zonse kuganizira ena kumeneku kunasonkhezera Yesu kuwathandiza anthuwo.
Yesu anachitira anthu zinthu zambiri m’malo mongowaphunzitsa chabe. Anawathandizanso pa zinthu zina ndi zina. Mwachitsanzo, iye nthaŵi ina anadyetsa anthu oposa 5,000 amene anali kumvetsera kwa iye mpaka madzulo a tsikulo. Posapita nthaŵi kuchokera pamenepo, anadyetsanso khamu lina lalikulu—nthaŵi imeneyi panali anthu oposa 4,000—amene anakhala akumvetsera kwa iye masiku atatu ndipo analibe chakudya chilichonse. Nthaŵi yoyamba, anagwiritsa ntchito mitanda isanu ya mkate ndi nsomba ziŵiri, koma nthaŵi yomalizayi anagwiritsa ntchito mitanda isanu ndi iŵiri, ndi tinsomba pang’ono. (Mateyu 14:14-22; 15:32-38) Zozizwitsa? Inde, iye analidi kuchita zozizwitsa.
Yesu anachiritsanso odwala ambiri. Anachiritsa akhungu, opunduka, akhate, ndiponso ogontha. Inde, anaukitsanso akufa! (Luka 7:22; Yohane 11:30-45) Nthaŵi ina, wakhate anam’pempha kuti: “Ngati mufuna mukhoza kundikonza.” Kodi Yesu anayankha motani? “Ndipo Yesu anagwidwa chifundo, natansa dzanja nam’khudza iye, nanena naye, Ndifuna; khala wokonzedwa.” (Marko 1:40, 41) Kupyolera mwa zozizwitsa ngati zimenezi, Yesu anasonyeza chikondi chake kwa anthu amene anali kuvutika.
Kodi mumakuona kukhala kovuta kukhulupirira zozizwitsa za Yesu? Ena amatero. Komabe, kumbukirani kuti Yesu anachita zozizwitsa zakezo pagulu la anthu. Ngakhale adani ake, amene anayesetsa kuti am’peze chifukwa nthaŵi iliyonse, sanakane kuti iye analidi kuchita zozizwitsa. (Yohane 9:1-34) Ndiponso, zozizwitsa zakezo zinali ndi cholinga. Zimenezi zinathandiza anthu kudziwa kuti Iye ndiye wotumidwa ndi Mulungu.—Yohane 6:14.
Pochita zozizwitsa Yesu sanafune kudzionetsera iye mwini. Koma analemekeza Mulungu, Gwero la mphamvu yake. Nthaŵi ina yake ku Kapernao, iye anali m’nyumba yodzazidwa ndi khamu la anthu. Munthu wamanjenje anafuna kuti achiritsidwe koma sanathe kuloŵa m’nyumbamo. Ndipo mabwenzi ake anamuloŵetsera padenga la nyumbayo aligone pamphasa. Ndipo ataona chikhulupiriro chawo, Yesu anachiritsadi wamanjenjeyo. Zotsatirapo zake, anthu ‘analemekeza Mulungu,’ ndipo anati: “Zotere sitinaziona ndi kale lonse.” (Marko 2:1-4, 11, 12) Zozizwitsa za Yesu zinadzetsa chitamando kwa Yehova, Mulungu wake komanso zinathandiza aja osoŵa.
Komabe, kuchiritsa odwala mozizwitsa sindiko kunali cholinga chachikulu cha utumiki wa Yesu. Mmodzi wa olemba mbiri ya moyo wa Yesu anafotokoza kuti: “Zalembedwa izi kuti mukakhulupirire kuti Yesu ndiye Kristu Mwana wa Mulungu, ndi kuti pakukhulupira mukhale nawo moyo m’dzina lake.” (Yohane 20:31) Inde, Yesu anadza ku dziko lapansi kuti anthu okhulupirira akakhale nawo moyo.
Nsembe Yake
‘Yesu kubwera padziko lapansi?’ mwina mungafunse. ‘Kodi iye anachokera kuti?’ Yesu iye mwini anati: “Ndinatsika Kumwamba, sikuti ndichite chifuniro changa, koma chifuniro cha Iye amene anandituma Ine.” (Yohane 6:38) Iye anakhalako monga Mwana wobadwa yekha wa Mulungu asanakhale munthu. Nanga chifuniro cha Iye amene anamutuma ku dziko lapansi chinali chiyani? “Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha,” akutero Yohane, mmodzi wa olemba Uthenga Wabwino, “kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Kodi zimenezi zikanatheka motani?
Baibulo limavumbula momwe imfa inakhalira chinthu chosapeweka kwa mtundu wa anthu. Mwamuna ndi mkazi oyambirira analandira kwa Mulungu moyo ndi chiyembekezo chokhala kosatha. Komabe, anasankha kupandukira Mlengi wawo. (Genesis 3:1-19) Chifukwa cha kachitidwe kameneka, kutanthauza tchimo loyamba la anthu, mbadwa za Adamu ndi Hava zinalandira choloŵa cha imfa. (Aroma 5:12) Kuti apatse mtundu wa anthu moyo weniweni, uchimo ndi imfa ziyenera kuthetsedwa.
Palibe wasayansi ndi mmodzi yemwe amene angachotse imfa mwa kukonzanso magini a munthu. Komabe, Mlengi wa mtundu wa anthu ali nayo njira yobwezeretsanso anthu omvera ku ungwiro kuti akhale ndi moyo kosatha. M’Baibulo makonzedwe amenewa amatchedwa kuti dipo. Mwamuna ndi mkazi oyambirirawo anadzigulitsa iwo eni ndi mbadwa zawo ku ukapolo wa uchimo ndi imfa. Anasinthanitsa moyo monga anthu angwiro omvera Mulungu ndi moyo wosadalira Mulungu, akumadzitengera mphamvu yosankha okha chabwino kapena choipa. Kuti moyo wangwiro waumunthu ugulidwenso, panafunikira kupereka mtengo wofanana ndi uja wa moyo wangwiro waumunthu umene makolo athu oyamba anataya. Komano pokhala amabadwa opanda ungwiro, anthu sakanatha kupereka mtengo umenewo.—Salmo 49:7.
Chotero Yehova Mulungu analoŵererapo kuti athandize. Iye anasamutsira moyo wangwiro wa Mwana wake wobadwa yekha m’mimba mwa namwali, amene anabala Yesu. Zaka makumi angapo zapitazo, inu mukanakana zakuti namwali n’kukhala ndi mwana. Komabe, lero asayansi atha kupanga nyama yamtundu umodzi mwa kutenga majini a nyamayo ndi kuika m’mimba mwa nyama ina. Tsono, ndani amene angakayikire m’pang’ono pomwe kuti Mlengi ali ndi mphamvu yopeŵera njira yachibadwa imene munthu amabadwira?
Mwa kukhalapo kwa moyo wangwiro waumunthu, mtengo woombolera mtundu wa anthu ku uchimo ndi imfa unapezeka. Komabe, khanda lobadwa padziko lapansi monga Yesu linayenera kuti likule ndi kukhala “dokotala” wokhoza kupereka “mankhwala” ochizira matenda a mtundu wa anthu. Iye anachita zimenezi mwa kukhalabe ndi moyo wangwiro, wosachimwa. Yesu sanangoona nsautso ya mtundu wa anthu ochimwa komanso anafika podziŵa kupereŵera kwawo chifukwa chakuti ndi anthu. Zimenezi zinam’pangitsa kukhala dokotala wachifundo kwambiri. (Ahebri 4:15) Machiritso ozizwitsa omwe iye anachita nthaŵi imene anali ndi moyo padziko lapansi anachitira umboni kuti iye amafunitsitsa kuchiritsa odwala komanso kuti ali nayo mphamvu yowachiritsira.—Mateyu 4:23.
Pambuyo pa utumiki wa zaka zitatu ndi theka wa padziko lapansi, Yesu anaphedwa ndi adani ake. Iye anasonyeza kuti munthu wangwiro angakhalebe womvera kwa Mlengi mosasamala kanthu za chiyeso ngakhale chachikulu motani. (1 Petro 2:22) Moyo wake waumunthu komanso wangwiro umene anapereka nsembe unakhala mtengo wa dipo, woombolera mtundu wa anthu ku uchimo ndi imfa. Yesu Kristu anati: “Palibe munthu ali nacho chikondi choposa ichi, chakuti munthu ataya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake.” (Yohane 15:13) Patsiku lachitatu pambuyo pa imfa yake, Yesu anaukitsidwa ali ndi moyo wauzimu, ndipo pambuyo pa milungu ingapo anakwera kumwamba kukapereka mtengo wa dipo kwa Yehova Mulungu. (1 Akorinto 15:3, 4; Ahebri 9:11-14) Mwa kuchita zimenezi, Yesu anatha kugwiritsa ntchito mphamvu ya nsembe yake ya dipo kwa iwo amene amamutsatira iye.
Kodi mungakonde kuti mupindule ndi makonzedwe amenewa ochiritsa matenda auzimu, opsinjika mtima, komanso matenda enieni? Kuti zimenezi zitheke, pafunikira chikhulupiriro cholimba mwa Yesu Kristu. Bwanji osabwera kwa dokotala inu mwini? Mungachite zimenezi mwa kuphunzira za Yesu Kristu ndi udindo wake wa kupulumutsa mtundu wa anthu. Mboni za Yehova zidzakhala zokondwa kukuthandizani.
[Chithunzi patsamba 5]
Yesu amafunitsitsa kuchiritsa odwala komanso ali nayo mphamvu yowachiritsira
[Chithunzi patsamba 7]
Kodi imfa ya Yesu imakukhudzani motani?