Kodi Pali Amene Amasamaladi?
“Misozi ya otsenderezedwa” yakhala mtsinje wamphamvu. Iwo akhetsa misozi chifukwa cha “nsautso zonse [zimene] zimachitidwa” padziko lonse lapansi. Anthu amene amasautsidwa kaŵirikaŵiri amadzimva kuti “alibe wakuwatonthoza”—ndipo kuti palibe amene amasamaladi za iwo.—Mlaliki 4:1.
MOSASAMALA kanthu za mtsinje wamphamvu wa misozi umenewu, anthu ena sakhudzidwa ndi kuvutika kwa anthu anzawo. Iwo amangonyalanyaza mavuto a anthu ena, monga muja anachitira wansembe ndi Mlevi m’fanizo la Yesu Kristu lonena za munthu amene anamenyedwa, kum’bera, ndi kum’siya atakomoka m’mphepete mwa njira. (Luka 10:30-32) Malinga ngati zinthu zikuwayendera bwino ndi banja lawo, iwo saganizako za anthu ena. Inde, amangonena kuti, “Zawo zimenezo!”
Sitiyenera kudabwa ndi zimenezi. Mtumwi Paulo analosera kuti “masiku otsiriza” anthu ambiri adzakhala opanda “chikondi chachibadwidwe.” (2 Timoteo 3:1, 3) Munthu wina anadandaula chifukwa cha mtima wosasamala za ena womwe wakula kwambiri. “Khalidwe lakale lachiairishi ndi mwambo wawo wa kusamalana ndi kugaŵana,” iye anatero, “zikuloŵedwa m’malo ndi malamulo atsopano a dziŵa zako.” Padziko lonse lapansi, anthu amasamala zawo zokha, alibe n’chidwi chomwe ndi anthu ena.
Vuto Losoŵa Wina Wosamalira Mnzake
Ndithudi pali vuto losoŵa wina wosamalira mnzake. Mwachitsanzo, tangoganizirani za mwamuna wina wokhala yekha wa ku Germany amene “anapezeka alikhale patsogolo pa wailesi yake yakanema wakufa—ndipo anamwalira pa Khirisimasi zaka zisanu zapitazo.” Mwamuna “wosudzulidwa, wolumala komanso wokhala yekha ameneyu,” sankamuona ngati akusoŵa mpaka pamene ndalama ku akaunti yake ya kubanki yomwe inkamulipirira nyumbayo zinatha. Panalibe amene ankasamaladi za iye.
Taganiziraninso za anthu opanda chitetezo ku maulamuliro amphamvu ndi opondereza. M’dera lina, anthu pafupifupi 200,000 (limodzi la magawo anayi a chiŵerengero cha anthu onse m’deralo) “anafa ndi nkhanza ndi njala” atalandidwa malo awo. Komanso taganizirani za ana amene ankachitidwa nkhanza yosaneneka. Lipoti lina linati: “Chiŵerengero cha ana [m’dziko lina] amene anaonera nkhanza zochuluka—kuphedwa, kumenyedwa, kugwiriridwa, nthaŵi zina zochitidwa ndi ana anzawo azaka za kusinkhuka, n’chachikulu modabwitsa kwambiri.” Chotero mungamvetse chifukwa chake anthu amene akuvutika ndi kupanda chilungamo kotereku angafunsire kwinaku akukhetsa misozi kuti, “Kodi pali amene amasamaladi za ine?”
Malinga ndi lipoti la United Nations, anthu 1,300,000,000 m’mayiko omwe akutukuka kumene amakhala ndi moyo pogwiritsa ntchito ndalama zosakwana dola imodzi ya ku United States patsiku. Ayeneradi kudabwa ngati pali amene amasamaladi. Chimodzimodzinso anthu othaŵa kwawo zikwizikwi amene, malinga ndi lipoti la mu nyuzipepala ya The Irish Times “amakakamizika kukhala m’misasa yauve kapena m’mayiko odana ndi alendo kapenanso kungobwerera kwawo ngakhale kuti kuli nkhondo kapena kusankhana mitundu.” Lipoti lomwelo linanenanso zomvetsa chisoni izi: “Tsekani maso anu, ndipo ŵerengani kulekeza katatu. Mphindi zomwe mwatengazo, mwana mmodzi wafa. Ameneyo ndi mmodzi wa ana 35,000 amene adzafa lero chifukwa cha matenda a njala ndi matenda ena opeweka.” N’zosadabwitsa kuti ambiri amalira mozunzika chifukwa cha kupsinjika ndi ululu!—Yerekezani ndi Yobu 7:11.
Koma kodi mavuto onseŵa anayenera kukhala motere? Kunena zoona, kodi palibe amene kuwonjezera pa kusamala, ali nazonso mphamvu zothetsera mavuto ndi kuchotsa zoŵaŵa zonse zimene anthu akumana nazo?
[Mawu a Chithunzi patsamba 2]
Cover and page 32: Reuters/Nikola Solic/Archive Photos
[Mawu a Chithunzi patsamba 3]
A. Boulat/Sipa Press