Kufunafuna Kwathu Moyo Wautali
“Munthu wobadwa ndi mkazi n’ngwa masiku owerengeka, nakhuta mavuto. Atuluka ngati duŵa, nafota; athawa ngati mthunzi, osakhalitsa.”—Yobu 14:1, 2.
NGAKHALE lerolino ndi oŵerengeka chabe amene angatsutse malingaliro onena za kufupika kwa moyo, ngakhale kuti analembedwa zaka 3,500 zapitazo. Anthu sakukhutirabe ndi moyo wapamwamba umene amasangalala nawo kwa kanthaŵi ndipo pambuyo pake kukalamba ndi kumwalira. Choncho, njira zoyesera kutalikitsa moyo, zafala zedi m’mbiri.
M’nthaŵi ya Yobu, Aigupto ankadya mavalo anyama poyesayesa kuti mwina angabwerere ku unyamata, koma zinali zosaphula kanthu. Chimodzi mwa zolinga za sayansi ya zamankhwala ya m’nyengo zapakati, chinali kupanga mankhwala opangitsa moyo kukhala wautali. Akatswiri ambiri amene anayesayesa kutalikitsa moyo, ankakhulupirira kuti golide wopangidwa ndi anthu angapangitse moyo kukhala wosafa, ndipo kudyera m’mbale zake kungatalikitse moyo. Atao a ku China wakale ankaganiza kuti angathe kusintha makemikolo a m’thupi pogwiritsa ntchito maluso monga kusinkhasinkha, maseŵero otulutsa mpweya wambiri m’kamwa, ndi kudya pang’ono ndipo potero ankati angathe kukhala ndi moyo wosafa.
Woyendera malo wa ku Spain, Juan Ponce de León amadziŵika chifukwa cha kufunafuna kwake kasupe wa unyamata. Dokotala wina wa m’zaka za zana la 18 analangiza m’buku lake lotchedwa Hermippus Redivivus kuti anamwali ataikidwa m’kachipinda m’nyengo ya masika ndi kutengera m’mabotolo mpweya umene amapuma m’kachipindamo, ungagwiritsidwe ntchito popanga mankhwala otalikitsa moyo. N’zachionekere kuti palibe ndi imodzi yomwe mwa njira zonsezo imene inapambana.
Lerolino, pambuyo pa zaka 3,500 kuchokera pamene Mose analemba mawu a Yobu, munthu watha kuyenda pamwezi, kupanga galimoto ndi makompyuta, ndiponso wafufuza ma atomu ndi maselo. Komabe, ngakhale pakhala kupita patsogolo koteroko m’sayansi, moyo wathu ‘n’ngwa masiku oŵerengeka ndi wokhuta mavuto.’ N’zoona kuti m’mayiko otukuka, zaka zimene munthu amayembekezeka kukhala ndi moyo zawonjezeka modabwitsa m’zaka 100 zapitazi. Koma zimenezi kwenikweni zachitika chifukwa cha njira zamakono zosamalira umoyo, njira zabwino zokhalira waukhondo, ndi zakudya zabwino. Mwachitsanzo, kuyambira m’katikati mwa zaka za zana la 19 kufika m’katikati mwa zaka za m’ma 1990, avareji ya zaka za anthu ambiri mu Sweden inakwera kuchoka pa zaka 40 kufika pa zaka 75 kwa amuna, ndiponso kuchoka pa zaka 44 kufika pa zaka 80 kwa akazi. Komabe, kodi zimenezi zikutanthauza kuti chifuno cha munthu chokhala ndi moyo wautali chakhutiritsidwa?
Ayi, chifukwa ngakhale kuti m’mayiko ena anthu ambiri amakhala ndi moyo mpaka ukalamba wawo, komabe mawu amene Mose analemba zaka zambiri zapitazo akugwirabe ntchito: “Masiku a zaka zathu ndiwo zaka makumi asanu ndi aŵiri, kapena tikakhala nayo mphamvu ndi zaka makumi asanu ndi atatu . . . , pakuti kumapitako msanga ndipo tithaŵa ife tomwe.” (Salmo 90:10) Kodi tiona kusintha kulikonse posachedwapa? Kodi munthu adzakhaladi ndi moyo kunthaŵi zosatha? Nkhani yathu yotsatira idzapereka mayankho a mafunso ameneŵa.