Kodi Pali Chiyembekezo chotani cha Moyo Wotalikirapo?
“Munthu wobadwa kwa mkazi ali ndi moyo waufupi komanso ngwokhutha chisoni.”—Mawu a Yobu olembedwa pa Yobu 14:1, “The Jerusalem Bible.”
HA, Anthu afotokoza zambiri chotani nanga ponena za kufupika kwa moyo m’ndakatulo zawo! Monga Yobu, mlembi wa m’zaka za zana loyamba anati: “Muli utsi, wakuonekera kanthaŵi, ndi pamenepo ukanganuka.”—Yakobo 4:14.
Kodi inunso mwaona kuti moyo ngwaufupi kwambiri? Pafupifupi zaka 400 zapitazo, William Shakespeare analemba kuti: “Zima, zima, khandulo wamng’ono iwe! Moyo ndiwo chithunzithunzi chabe chomayenda.” Ndipo m’zaka za zana lapitalo, mfumu ya Amwenye a ku America inafunsa kuti: “Kodi moyo nchiyani?” Ndiyeno inayankha kuti: “Ndiwo kuphethima kwa chiphaniphani usiku.”
Kodi anthu angayembekeze kukhala ndi moyo wautali motani? Mneneri Mose anafotokoza za mkhalidwe wa m’tsiku lake, pafupifupi zaka 3,500 zapitazo kuti: “Masiku a zaka zathu ndiwo zaka makumi asanu ndi aŵiri, kapena tikakhala nayo mphamvudi zaka makumi asanu ndi atatu; koma teronso kukula kwawo kumati chivuto ndi chopanda pake; pakuti kumapitako msanga ndipo tithaŵa ife tomwe.”—Salmo 90:10.
Zaka 70—amenewo ndi masiku 25,567 chabe. Ndipo zaka 80 zimangokwana masiku 29,219 chabe. Alidi oŵerengeka! Kodi pali chimene chingachitidwe kutalikitsa moyo wa munthu?
Kodi Sayansi ya Mankhwala Ingathandize?
Magazini a Science anati: “Chiyembekezo cha utali wa moyo pakubadwa kwa munthu [mu United States] chinawonjezeka kuchokera pa zaka 47 mu 1900 kufika zaka pafupifupi 75 mu 1988.” Chifukwa cha kuchepetsa imfa za makanda kupyolera m’chisamaliro cha umoyo ndi chakudya chabwino, anthu ku United States tsopano angayembekezere kukhala ndi moyo zaka zimene Mose anatchula. Chikhalirechobe, kodi tingayembekezere kuwonjezeka kwakukulu kwa utali wa moyo umene anthu ochuluka amakhala nawo?
Leonard Hayflick, katswiri wotchuka pa za kukalamba, ananena mfundo yofunika m’buku lake lakuti How and Why We Age: “Kupita patsogolo pa kufufuza za mankhwala ndi kugwiritsira ntchito chisamaliro cha mankhwala chopita patsogolo m’zaka za zana lino mosakayika kwakhudzadi utali wa moyo wa munthu, koma mwa kungolola anthu ambiri kufika pogomera moyo wa munthu.” Chotero anafotokoza kuti: “Chiyembekezo cha utali wa moyo wa munthu chawonjezeka koma utali wa moyo wa munthu sunawonjezeke; kusiyana kwake nkwakukulu.”
Kodi “pogomera” utali wa moyo wa munthu ndi pati? Ena amati nzokayikitsa ngati m’zaka zaposachedwapa kwakhalako munthu amene anakhala ndi moyo kupyola pa zaka 115. Komabe, magazini a Science anati: “Pofika mu 1990, zaka zotsimikizirika zimene munthu wokalamba kopambana anali nazo zinangopyola pang’ono pa 120.” Ndipo kuchiyambiyambi kwa chaka chino nduna ya zaumoyo ya ku France, limodzi ndi khamu la atolankhani ndi otenga zithunzithunzi, anakachezera Jeanne Calment wa ku Arles, France, kukakumbukira naye tsiku lake la kubadwa la chaka cha 120. Nayenso Mose anakhala ndi moyo kufikira zaka 120, kupyoleratu pa avareji.—Deuteronomo 34:7.
Kodi asayansi akupereka chiyembekezo chakuti anthu ambiri angakhale ndi moyo zaka zimenezo kapena kuposapo? Ayi, ambiri samatero. Mutu wa nkhani mu Detroit News unati: “Ofufuza Akuti Zaka 85 Zingakhale Pogomera Avareji ya Utali wa Moyo wa Munthu.” M’nkhaniyo katswiri womveka pa za kukalamba, S. Jay Olshansky, anati: “Atangopyola zaka 85, anthu amafa chifukwa cha kulephera kwa ziŵalo zambiri m’thupi. Amasiya kupuma. Kwenikweni, amafa ndi ukalamba. Ndipo kulibe mankhwala ake.” Anawonjezera kuti: “Ngati sitiletsa maselo a munthu kukalamba, ndiye kuti chiyembekezo cha utali wa moyo wa munthu sichidzawonjezekanso.”
Magazini a Science anati mwinamwake “pogomera moyo wa munthu pafikidwa kale ndi kuti chiŵerengero cha imfa nchosatheka kutsikanso kwambiri.” Kwanenedwa kuti ngati zochititsa imfa zonse zolembedwa pa zikalata za imfa zingathetsedwe, chiyembekezo cha utali wa moyo chingawonjezeke ndi zaka zosakwana 20.
Chotero, asayansi ambiri amaona kuti utali wa moyo wa munthu ngwachibadwa ndi kuti ngwosasinthika. Komabe nchifukwa ninji kuli koyenera kukhulupirira kuti anthu potsirizira pake adzakhala ndi moyo wotalikirapo?