Kodi Mungakhale ndi Moyo Kwautali Wotani?
AMBIRI a ife timavomereza mosavuta kuti moyo uli ndi mavuto. Komabe, tili achimwemwe pokhala ndi moyo. Sitimakhutira ndi ubwana wathu wokha kapena ndi moyo waufupi; tingakonde kukhala ndi moyo kwa zaka zambiri. Chikhalirechobe, imfa imaonekera kukhala yosapeŵeka. Kodi nzowona?
Kodi kuli kotheka kuchedwetsa imfa? Kodi moyo wathu ungatalikitsidwe?
Moyo Wotalikitsidwa?
Mu 1990 lipoti la nyuzi linalengeza kuthekera kwa kutalikitsa moyo wa munthu ndi ‘zaka zana limodzi ndi khumi.’ Mosakayikira kumeneku kunali kutchula mwanjira ina mawu a Baibulo a wamasalmo Mose awa: “Masiku a zaka zathu ndiwo zaka [makumi asanu ndi aŵiri]; ndipo ngati chifukwa cha nyonga akhala zaka [makumi asanu ndi atatu], koma nyonga yawo njovutikira ndi yachisoni; pakuti posapita nthaŵi imatha, ndipo timauluka.” (Salmo 90:10, King James Version) Chotero Baibulo limapereka zaka 70 kapena 80 kukhala avareji ya moyo wa munthu. Koma kodi ndizaka zothekera zochuluka motani zimene munthu angayembekezere kukhala nazo lerolino?
Lipoti lofalitsidwa ndi WHO (World Health Organization) mu 1992 linaika avareji yoyembekezeredwa ya moyo wa munthu padziko lonse pa zaka 65. Malinga nkunena kwa WHO, umenewu unali “kuyembekezeredwa kuwonjezeka ndi pafupifupi miyezi inayi pachaka kwa zaka zisanu zotsatira, kwakukulukulu chifukwa cha kuchepetsa imfa za makanda.” Komabe, ngakhale ngati chozizwitsa cha zamankhwala chingaletse imfa ya munthu aliyense asakwanitse zaka 50, magazini a Time akunena kuti ku United States, “kuwonjezeka kwa avareji yoyembekezeredwa ya moyo wa munthu ingangokhala kokha ya zaka 3 1/2.”
Kodi Nchifukwa Ninji Moyo Uli Waufupi Kwambiri?
Dr. Jan Vijg wa pa Netherlands’ Institute of Experimental Gerontology akunena kuti monga momwe matenda ena amagwirizanitsidwira ndi kupunduka m’kapangidwe ka maselo a thupi la munthu, choteronso mchitidwe wa kukalamba ukuonekera kukhala ukumachititsidwa ndi mkhalidwe wa majini. Ofufuza ena amakhulupirira kuti tingathe kukhala ndi moyo wotalikirapo ngati “majini angapo ofunika koposa” amasinthidwa pamene tikukula. Ena amanena kuti lingaliro limenelo lili “kuona nkhaniyo mopepuka.”
Mulimonse mmene zingakhalire, asayansi akuvomereza kuti “kukuonekera kuti pali malire olinganizidwiratu a mphamvu ya moyo m’maselo a thupi la munthu,” akutero magazini a Time. Ngakhale awo amene amatsutsa kuti tili “olinganizidwiratu kukhalabe ndi moyo” amavomereza kuti “kanthu kena kamalakwika.” Ndithudi, pa zaka 65, 70, kapena 80 kapena zaka zina zingapo, moyo wathu ‘posapita nthaŵi umatha’ mu imfa, monga momwe Baibulo limanenera.
Komabe, mtumwi Wachikristu Paulo wa m’zaka za zana loyamba C.E. mwachidaliro analosera kuti: “Mdani wotsiriza amene adzathedwa ndiye imfa.” (1 Akorinto 15:26) Kodi imfa ingathetsedwe motani? Ngakhale ngati ingathetsedwe, kodi ndimotani mmene mungachitire ndi imfa ya okondedwa lerolino?