Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Kodi Mboni za Yehova zimaona motani nkhani ya kuvota?
M’Baibulo muli mapulinsipulo ofotokozedwa bwino amene amapangitsa atumiki a Mulungu kukhala ndi malingaliro oyenera pa nkhani imeneyi. Komabe, kukuoneka kuti palibe pulinsipulo lomwe limaletsa kuvota kwenikweniko. Mwachitsanzo, palibe chifukwa chimene bungwe la oyang’anira siliyenera kuchitira voti kuti lisankhe mfundo zokhudza bungwe lawo. Nthaŵi zambiri mipingo ya Mboni za Yehova imasankha nthaŵi ya misonkhano ndi kagwiritsidwe ntchito ka ndalama za mpingo mwa kuvota pokweza manja.
Komabe, bwanji za kuvota pachisankho cha ndale? N’zoona, m’mayiko ena a demokalase, pafupifupi 50 peresenti ya chiŵerengero cha anthu sapita kukavota patsiku la chisankho. Ponena za Mboni za Yehova, izo siziloŵerera pa ufulu wa ena woponya voti; komanso mwa njira iliyonse siziuza anthu kuti asavote pazisankho za ndale. Zimalemekeza ndi kugwirizana ndi akuluakulu a boma amene asankhidwa moyenerera pa zisankho zimenezi. (Aroma 13:1-7) Pankhani yakuti kaya iwo akavotera winawake amene waima nawo pa chisankho, aliyense wa Mboni za Yehova amasankha chochita malinga ndi chikumbumtima chake chophunzitsidwa ndi Baibulo komanso mmene amaonera udindo wake kwa Mulungu ndi Boma. (Mateyu 22:21; 1 Petro 3:16) Posankha chochita chaumwini chimenechi, Mboni zimalingalira mfundo zingapo.
Yoyamba, Yesu Kristu ponena za otsatira ake anati: “Sakhala a dziko lapansi, monga Ine sindikhala wa dziko lapansi.” (Yohane 17:14) Mboni za Yehova sizipepuza pulinsipuloli. Popeza kuti ‘sali mbali ya dziko,’ saloŵerera m’zochitika za ndale za dziko.—Yohane 18:36.
Yachiŵiri, mtumwi Paulo anadzitcha kukhala “mtumiki [“kazembe,” NW]” woimira Kristu kwa anthu a m’tsiku lake. (Aefeso 6:20; 2 Akorinto 5:20) Mboni za Yehova zimakhulupirira kuti Kristu Yesu tsopano ndi Mfumu yoikidwa ya Ufumu wa Mulungu wakumwamba, ndipo iwo, monga akazembe, ayenera kulengeza zimenezi ku mitundu ya anthu. (Mateyu 24:14; Chivumbulutso 11:15) Akazembe amayembekezeredwa kusaloŵerera m’zochitika za m’mayiko amene iwo atumizidwako ndiponso kupeŵa kusokoneza zochitikazo. Monga oimira Ufumu wa Mulungu wakumwamba, Mboni za Yehova zimadzimva kukhala ndi malingaliro ofananawo osaloŵerera m’ndale za m’mayiko amene iwo akukhala.
Mfundo yachitatu yofunika kuilingalira ndiyo yakuti awo amene amavotera nawo munthu pa udindo angakhale ndi mlandu wa zimene munthu am’sankhayo wachita. (Yerekezani ndi 1 Timoteo 5:22, The New English Bible.) Akristu ayenera kulingalira mofatsa ngati akufuna kukhala ndi mlandu umenewu.
Yachinayi, Mboni za Yehova zimaona umodzi wawo wachikristu kukhala wamtengo wapatali kwambiri. (Akolose 3:14) Pamene zipembedzo ziloŵa m’ndale, kaŵirikaŵiri zotsatira zake zimakhala kugaŵanika kwa anthu awo. Motsanzira Yesu Kristu, Mboni za Yehova zimapeŵa kuloŵa m’ndale motero zimasunga umodzi wawo wachikristu.—Mateyu 12:25; Yohane 6:15; 18:36, 37.
Yachisanu komanso yomaliza, ndiyo yakuti kusakhala ndi mbali m’ndale kumapatsa Mboni za Yehova ufulu woyankhula za uthenga wofunika wa Ufumu ndi anthu a zipani zonse molimbika mtima.—Ahebri 10:35.
Mwa kulingalira mapulinsipulo a m’Malemba amene afotokozedwaŵa, Mboni za Yehova m’mayiko ambiri zimasankha aliyense payekha kusaponya voti pa zisankho za ndale, ndipo ufulu wawo wa kusankha n’ngwochirikizidwa ndi lamulo la dzikolo. Komabe, bwanji, ngati lamulo limafuna kuti nzika zivote? Pamenepo, Mboni iliyonse payokha ili ndi udindo wosankha mmene ingachitire ndi nkhaniyo, mogwirizana ndi chikumbumtima chophunzitsidwa ndi Baibulo. Ngati wina asankha kupita kokavota, chimenecho n’chosankha chake. Zimene iye amachita m’chipinda choponyera voti ndi nkhani yokhudza iye ndi Mlengi wake.
Nsanja ya Olonda yachingelezi ya November 15, 1950, pa masamba 445 ndi 446, inati: “Komwe Kaisara amakakamiza nzika zake kuvota . . . [Mboni] zingapite kumalo ovotera ndi kuloŵa m’zipinda zoponyera voti. Ndi mmenemu momwe amafunika kuti aike chizindikiro pa pepala lawo lovotera kapena kulembapo chimene iwo akuimira. Ovota amachita zimene akufuna ndi mapepala awo ovotera. Ndiyeno ndi munomo mmene, pamaso pa Mulungu, mboni zake ziyenera kuchita mogwirizana ndi malamulo ake komanso ndi chikhulupiriro chawo. Si udindo wathu kuwauza zochita ndi pepala lovotera.”
Bwanji ngati mwamuna wosakhulupirira akakamiza mkazi wake wachikristu kukavota? Eya, iye amagonjera mwamuna wake, monga Akristu amagonjera maulamuliro aakulu. (Aefeso 5:22; 1 Petro 2:13-17) Ngati amvera mwamuna wake ndi kupita kumalo ovotera, kumeneko n’kusankha kwake. Palibe amene ayenera kumuimba mlandu.—Yerekezani ndi Aroma 14:4.
Bwanji nanga za dziko limene lamulo silikakamiza kuvota koma anthu amene sapita kumalo ovotera amadedwa koopsa mwinanso moti angavulazidwe? Kapena bwanji ngati anthu, ngakhale kuti lamulo siliwakakamiza kuvota, ena amalangidwa kwadzaoneni m’njira inayake ngati sapita kumalo ovotera? M’mikhalidwe imeneyi kapena inanso yofanana nayo, Mkristu ayenera kudzisankhira chochita. “Yense adzasenza katundu wake wa iye mwini.”—Agalatiya 6:5.
Pangakhale anthu amene amakhumudwa pamene aona kuti panthaŵi yachisankho m’dziko mwawo, ena a Mboni za Yehova amapita kumalo ovotera ndipo ena sapita. Iwo anganene kuti, ‘Mboni za Yehova sizinena chimodzi.’ Komabe, anthu ayenera kuzindikira kuti pankhani zodalira chikumbumtima cha munthu monga imeneyi, Mkristu aliyense amasankha chochita cha iye mwini pamaso pa Yehova Mulungu.—Aroma 14:12.
Zosankha zaumwini zilizonse zimene Mboni za Yehova zimapanga pokumana ndi mikhalidwe yosiyanasiyana, zimachita mwanzeru kuti zisunge uchete wawo wachikristu ndi kukhala ndi ufulu wa kuyankhula. M’zinthu zonse, amadalira Yehova Mulungu kuti awalimbitse, awapatse nzeru, ndi kuwathandiza kuti asataye chikhulupiriro chawo mwa njira ina iliyonse. Chotero amasonyeza chikhulupiriro m’mawu a wamasalmo akuti: “Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa; ndipo chifukwa cha dzina lanu ndiyendetseni bwino, ndipo nditsogolereni.”—Salmo 31:3.