Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w02 9/15 tsamba 3
  • Kukonda Anthu “Oyera Mtima” Masiku Ano

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kukonda Anthu “Oyera Mtima” Masiku Ano
  • Nsanja ya Olonda—2002
  • Nkhani Yofanana
  • Oyera Mtima
    Kukambitsirana za m’Malemba
  • Kodi Anthu Oyera Mtima Enieni Angakuthandizeni Bwanji?
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Kodi Kupembedza Zotsala za Akufa Kumamkondweretsa Mulungu?
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Kodi N’zoyenera Kupemphera kwa Oyera Mtima?
    Nsanja ya Olonda—2013
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2002
w02 9/15 tsamba 3

Kukonda Anthu “Oyera Mtima” Masiku Ano

“Kodi mukukumbukira nthaŵi imene tinkaoneka ngati tikunyansidwa ndi mawu akuti woyera mtima? Koma zimenezi sizinawakhudze anthu a ku America okwana 4.2 miliyoni amene anaonera maliro a Mayi Teresa pa September 13. Kuyambira pa September 5, tsiku limene anamwalira, anthu akhala akuvutitsa ku Vatican kuti am’vomereze mayiyu kukhala munthu woyera mtima. Anthu ochepa akukayikira ngati zimenezi zitheke.”​—Sun-sentinel, United States, October 3, 1997.

ANTHU ambiri amaona kuti ntchito zothandiza anthu ovutika, zimene Mayi Teresa, mmishonale wachikatolika ankachita, n’zimene zimapangitsa munthu kukhala woyera mtima weniweni. M’zipembedzo zina mumapezekanso anthu oyera mtima. Koma palibe amene amavomerezedwa ndi anthu ambiri kuti ndi woyera mtima monga mmene amavomerezera woyera mtima woikidwa ndi Tchalitchi cha Roma Katolika.

Papa Yohane Paulo wachiŵiri, paudindo wake waupapa anaika anthu oposa 450 kukhala oyera mtima. Anthu ameneŵa anaposa chiŵerengero chonse cha anthu amene apapa a m’zaka za m’ma 1900 anawavomereza kukhala oyera mtima.a N’chifukwa chiyani anthu akukonda kwambiri anthu “oyera mtima,” amene ambiri a iwo si odziŵika kwenikweni kwa Akatolika ambiri?

Lawrence Cunningham katswiri wa zaumulungu pa yunivesite ya m’mzinda wa Notre Dame ku America anati: “Anthu amachita chidwi kumva kuti m’dzikoli muli anthu oyera mtima. Anthu oyera mtima amasonyeza kuti n’zotheka kukhala woyera mtima ngakhale masiku ano.” Komanso pali chikhulupiriro chakuti “oyera mtima” ali ndi mwayi wapadera wofika kwa Mulungu, zimene zimawapangitsa kukhala anthu oyenera kupempherera anthu amoyo. Akapeza zinthu kapena mafupa a munthu “woyera mtima” amazilambira pokhulupirira kuti zili ndi mphamvu ina yake.

Katekisimu wa Msonkhano wa ku Trent, amene anasindikizidwa m’zaka za m’ma 1500 wofuna kutsimikizira chikhulupiriro cha Akatolika anagamula kuti: “M’pake kunena kuti, kulemekeza anthu oyera mtima ‘amene anafa mwa Ambuye,’ kuwapempha kuti atipempherere, ndiponso kulambira zinthu zawo zopatulika ndi phulusa la mitembo yawo, sizichepetsa n’komwe ulemerero wa Mulungu koma zimauwonjezera. Chiyembekezo cha Mkristuyo chimalimbikitsidwa ndiponso zimamulimbikitsa kutsatira makhalidwe a anthu oyera mtimawo. (The Catechism of the Council of Trent, 1905) Akristu oona amafunadi kutsatira makhalidwe abwino pamoyo wawo, kum’fikira Mulungu moyenera, ndiponso kuti Mulungu awathandize. (Yakobo 4:7, 8) Choncho malinga ndi Mawu a Mulungu, kodi ndani akukwanira kukhala oyera mtima enieni? Ndipo kodi amagwira ntchito yanji?

[Mawu a M’munsi]

a Kuvomereza anthu kukhala oyera mtima kumapangitsa munthu watchalitchi cha Roma Katolika amene anamwalira kukhala woyenera kulemekezedwa ndi anthu onse.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena