Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w04 3/1 tsamba 29
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
  • Nsanja ya Olonda—2004
  • Nkhani Yofanana
  • Yehova Ndi Cholowa Changa
    Nsanja ya Olonda—2011
  • “Ndidzatsitsimutsa Wolefuka”
    Zimene Mulungu Akutiuza Kudzera mwa Yeremiya
  • “Ndaika Mawu Anga M’kamwa Mwako”
    Zimene Mulungu Akutiuza Kudzera mwa Yeremiya
  • Yeremiya—Mneneri Wachilendo wa Ziweruzo za Mulungu
    Nsanja ya Olonda—1988
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2004
w04 3/1 tsamba 29

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Poti Alevi analibe choloŵa mu Israyeli wakale, kodi Hanameli yemwe anali Mlevi anagulitsa bwanji munda kwa msuweni wake Yeremiya yemwenso anali Mlevi, malinga ndi zimene zili pa Yeremiya 32:7?

Ponena za Alevi, Yehova anauza Aroni kuti: “Ulibe choloŵa m’dziko lawo, ulibe gawo pakati pawo [pa Aisrayeli].” (Numeri 18:20) Komabe, Alevi anapatsidwa midzi 48 pamodzi ndi mabusa ake, imene inali kupezeka m’Dziko lonse Lolonjezedwa. Kwawo kwa Yeremiya kunali ku Anatoti, umodzi wa midzi yomwe “ana a Aroni, ansembe,” anapatsidwa.​—Yoswa 21:13-19; Numeri 35:1-8; 1 Mbiri 6:54, 60.

Pa Levitiko 25:32-34, timaona kuti Yehova anapereka malangizo osapita m’mbali okhudza mphamvu zowombola malo a Alevi. Zikuoneka kuti mabanja achilevi pawokhapawokha ankatha kugwiritsa ntchito ufulu umene munthu ankakhala nawo akalandira choloŵa, wokhudza kukhala ndi malo enaake, kuwagwiritsa ntchito kwake, ndiponso kuwagulitsa. Izi mwachidziŵikire zinkaphatikizapo kugulitsa ndi kuwombola malo.a Nthaŵi zambiri, Alevi ankakhala ndi malo ndiponso kuwagwiritsa ntchito m’njira zofanana ndi mmene Aisrayeli a mafuko ena ankachitira.

Mwachionekere, malo omwe Aleviwo ankakhala nawo ankawapeza mwa choloŵa cha banja. Koma pankhani ‘yokhoza kuwawombola,’ izo zinkaloledwa pakati pa Alevi okhaokha. Komanso zikuoneka kuti ankawombola ndi kugulitsa malo okhawo a m’kati mwa midzi, chifukwa chakuti “dambo la podyera pawo” silinkayenera kugulitsidwa popeza kuti linkakhala “lawolawo kosatha.”​—Levitiko 25:32, 34.

Motero munda womwe Yeremiya anawombola kwa Hanameli ukuoneka kuti unali wotero moti ukanatha kukhala wa munthu wina mwa kuuwombola. N’kutheka kuti unali m’kati mwa mudzi. Yehova anasonyeza kuti “munda” womwe tikukambiranawu unalidi wa Hanameli ndi kuti Yeremiya anali ndi “mphamvu yakuombola.” (Yeremiya 32:6, 7) Yehova anagwiritsa ntchito malonda ameneŵa monga chizindikiro chotsimikizira lonjezo lake lakuti Aisrayeli adzakhalanso ndi malo amene anali choloŵa chawo nthaŵi ya ukapolo wa ku Babulo ikadzatha.​—Yeremiya 32:13-15.

Palibe chilichonse chomwe chikusonyeza kuti Hanameli anapeza malo mu Anatoti m’njira yolakwika. Palibe chomwe chikusonyeza kuti anaswa lamulo la Yehova pouza Yeremiya kuti agule munda wa ku Anatotiwu kapenanso kuti Yeremiya sanagwiritse ntchito bwino mphamvu yake ya kuwombola katundu pogula mundawu.​—Yeremiya 32:8-15.

[Mawu a M’munsi]

a M’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino, Barnaba yemwe anali Mlevi anagulitsa malo ake ndi kupereka ndalama zake kuti zithandize otsatira a Kristu okhala ku Yerusalemu omwe ankafunika chithandizo. Mwina maloŵa anali ku Palestina kapena ku Kupro. Kapenanso mwina anali malo omwe ankafuna kuti adzakhale manda ake omwe Barnaba anagula mu Yerusalemu.​—Machitidwe 4:34-37.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena