Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w07 10/1 tsamba 31
  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga
  • Nsanja ya Olonda—2007
  • Nkhani Yofanana
  • Amapasa Amene Anali Osiyana
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Yakobo Analandira Madalitso
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Yakobo ndi Esau Akhululukirana
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Rebeka Anali Mkazi Wolimbikira Ntchito Ndiponso Woopa Mulungu
    Nsanja ya Olonda—2004
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2007
w07 10/1 tsamba 31

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Malinga ndi zimene timawerenga pa Genesis 27:18, 19, kodi Yakobo analakwa kunamizira kuti anali Esau?

Mwina nkhani imeneyi mumaidziwa bwino. Isake atakalamba anauza Esau kuti akamuphere nyama. Iye anati: ‘Ndidye; kuti moyo wanga ukadalitse iwe ndisanafe.’ Atamva zimene mwamuna wake ananena, Rebeka anakonza chakudya chokoma n’kuuza Yakobo kuti: ‘Upite nacho kwa atate wako, kuti adye, ndi kukudalitsa iwe asanafe.’ Kenako, Yakobo atavala zovala za Esau ndi zikopa za tiana ta mbuzi m’khosi ndi m’manja, anapita kwa bambo ake ndi chakudya chokomacho. Isake anafunsa kuti: “Ndani iwe mwana wanga?” Ndipo Yakobo anayankha kuti: “Ndine Esau mwana wanu wamkulu.” Isake anakhulupirira ndipo anamudalitsa.​—Genesis 27:1-29.

Baibulo silinena mwatsatanetsatane chifukwa chimene Rebeka ndi Yakobo anachitira zimenezi, koma limasonyeza kuti nkhaniyi inachitika mosayembekezereka. Tiyenera kudziwa kuti Mawu a Mulungu satsutsa kapena kuvomereza zimene Rebeka ndi Yakobo anachita. Motero, nkhani imeneyi silimbikitsa kunama kapena kuchita chinyengo. Komabe, Baibulo limatithandiza kumvetsa zimene zinachitika.

Choyamba, Baibulo limasonyeza kuti Yakobo ndi amene anali woyenera kudalitsidwa osati Esau. Yakobo anali atagula ukulu kwa mkulu wake wosayamikirayu yemwe anaugulitsa ndi chakudya chifukwa cha njala. Esau “ananyoza ukulu wake.” (Genesis 25:29-34) Choncho, mwa kupita kwa bambo ake, Yakobo amafuna madalitso amene analidi ake.

Chachiwiri, Isake atazindikira kuti wadalitsa Yakobo, sanafune kusintha. Mwina anakumbukira zimene Yehova anauza Rebeka ana amapasawa asanabadwe. Yehova anati: “Wamkulu adzakhala kapolo wa wamng’ono.” (Genesis 25:23) Tiyenera kukumbukiranso kuti pamene Yakobo anafuna kupita ku Harana, Isake anamupatsanso madalitso ena.​—Genesis 28:1-4.

Ndipo chomaliza, tiyenera kukumbukira kuti Yehova ankadziwa ndipo anali ndi chidwi ndi zomwe zinali kuchitika. Madalitso amene Isake anapereka anali ogwirizana ndi zimene Mulungu analonjeza Abulahamu. (Genesis 12:2, 3) Mulungu akanakhala kuti sanafune kuti madalitso apite kwa Yakobo akanachitapo kanthu koma sanatero. M’malo mwake, Yehova anauza Yakobo kuti: “Mu mbewu zako mabanja onse a dziko lapansi adzadalitsidwa.”​—Genesis 28:10-15.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena