Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w08 5/1 tsamba 24
  • Iye Amamvetsa Mavuto Athu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Iye Amamvetsa Mavuto Athu
  • Nsanja ya Olonda—2008
  • Nkhani Yofanana
  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga
    Nsanja ya Olonda—2013
  • Mamiliyoni Amene Ngakufa Tsopano Adzakhalanso ndi Moyo
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Chiyembekezo Chotsimikizirika cha Akufa
    Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira
  • Zimene Tikuphunzira pa Misozi ya Yesu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2008
w08 5/1 tsamba 24

Yandikirani Mulungu

Iye Amamvetsa Mavuto Athu

Yohane 11:33-35

MUNTHU wachifundo amamvetsa ululu umene munthu wina akumva. Yehova Mulungu ndi chitsanzo chabwino kwambiri cha munthu wachifundo. Anthu ake akamavutika nayenso amamva ululu. Kodi tikudziwa bwanji zimenezi? Yesu anasonyeza bwino kwambiri chifundo cha Yehova mwa zimene ananena komanso kuchita pamene anali padziko lapansi pano. (Yohane 5:19) Mwachitsanzo, taonani nkhani yopezeka pa Yohane 11:33-35.

Lazaro yemwe anali mnzake wa Yesu atamwalira, Yesu anapita kwawo kwa Lazaroyo. N’zomveka kuti Mariya ndiponso Marita, omwe anali alongo ake a Lazaro, anali ndi chisoni kwambiri. Ndipo Yesu ankalikonda kwambiri banja limeneli. (Yohane 11:5) Ndiyeno kodi Yesu akanachita chiyani? Nkhaniyo imati: “Yesu atamuona [Mariya] akulira, ndi Ayuda amene anabwera naye pamodzi akuliranso, anadzuma povutika mu mtima ndi kumva chisoni. Kenako anati: ‘Mwamuika kuti?’ Iwo anati kwa iye: ‘Ambuye tiyeni mukaone.’ Yesu anagwetsa misozi.” (Yohane 11:33-35) N’chifukwa chiyani Yesu analira? N’zoona kuti Lazaro, yemwe anali mnzake, anali atamwalira, komabe Yesu anali atatsala pang’ono kumuukitsa. (Yohane 11:41-44) Kodi pali chinthu chinanso chimene chinam’khudza mtima kwambiri Yesu?

Taonaninso mawu a m’Baibulo amene ali m’ndime yapitayi. Onani kuti Yesu ataona Mariya ndiponso anthu ena omwe anali naye akulira, iye “anadzuma” ndipo ‘anavutika mu mtima.’ Mawu a Chigiriki omwe anawagwiritsira ntchito palembali amasonyeza kukhudzidwa mtima kwambiri.a Zimene iye anaona zinamukhudza kwambiri. Umboni wa zimenezi ndi woti m’maso mwake munalengeza misozi. N’zoonekeratu kuti Yesu anakhudzidwa mtima ndi ululu umene anthu ena anali kumva. Kodi inuyo munayamba mwalirapo chifukwa choona munthu amene mumam’konda akulira?​—Aroma 12:15.

Chifundo chimene Yesu anasonyeza chimatithandiza kumvetsa bwino makhalidwe ndiponso mmene Atate wake Yehova amachitira zinthu. Kumbukirani kuti Yesu anasonyeza bwino kwambiri makhalidwe a Atate wake moti ananena kuti: “Amene waona ine waonanso Atate.” (Yohane 14:9) Motero tikamawerenga kuti “Yesu anagwetsa misozi” timadziwa kuti Yehova amamva ululu, olambira ake akamamva ululu. Ndipotu anthu ena amene analemba nawo Baibulo amatsimikizira zimenezi. (Yesaya 63:9; Zekariya 2:8) N’zoonadi, Yehova ndi Mulungu wachifundo zedi.

Timasangalala ndi anthu achifundo. Tikakhumudwa kapena kuthedwa nzeru, timafuna kukhala pafupi ndi munthu amene angamvetse vuto lathu, n’kutichitira chifundo. Koposa zonse, timafuna kukhala pafupi ndi Yehova, yemwe ndi Mulungu wachifundo, ndipo amamvetsa ululu umene tikumva ndiponso amamvetsa chifukwa chimene tikukhetsera misozi.​—Salmo 56:8.

[Mawu a M’munsi]

a Mawu a Chigiriki omwe anamasuliridwa kuti “anagwetsa misozi” nthawi zambiri amatanthauza “kusisima.” Koma mawu amene anawagwiritsira ntchito pofotokoza kulira kwa Mariya ndi anthu ena aja angatanthauze “kulira mofuula kapena kubuma.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena