Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w09 5/1 tsamba 22-25
  • Beteli ya ku Brooklyn Yakwanitsa Zaka 100

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Beteli ya ku Brooklyn Yakwanitsa Zaka 100
  • Nsanja ya Olonda—2009
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • N’chifukwa Chiyani Anasamukira ku Brooklyn?
  • N’chifukwa Chiyani Anasankha Dzina Lakuti Beteli?
  • Kulandira Alendo Mwansangala
  • Kodi Ntchito Iyi Ingakhale Yabwino Kwambiri kwa Inu?
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Kupenya ndi Chiyamikiro pa “Nyumba ya Mulungu”
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Mukuitanidwa!
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Kodi Beteli N’chiyani?
    Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
Nsanja ya Olonda—2009
w09 5/1 tsamba 22-25

Beteli ya ku Brooklyn Yakwanitsa Zaka 100

CHAKA cha 1909 chinali chapadera kwambiri kwa anthu a mu mzinda wa New York City. M’chakachi, mlatho wa Queensboro, womwe uli m’tauni ya Queens ndipo umalumikiza tauniyi ndi tauni ya Manhattan, unatseguliridwa. M’chaka chomwechi, mlatho wa Manhattan, womwe umalumikiza tauniyi ndi tauni ya Brooklyn, unatseguliridwanso.

Chakachi chinalinso chapadera kwambiri kwa Mboni za Yehova. M’mbuyomo, Charles Taze Russell, yemwe anali pulezidenti wa Watch Tower Bible and Tract Society, lomwe ndi bungwe la Mboni za Yehova lovomerezeka mwa lamulo, anaona kuti m’tsogolo, ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu, ingadzafalikire m’madera ambiri. (Mateyo 24:14) Iye ankakhulupirira kuti kusamutsa likulu la bungweli kuchokera ku mzinda wa Pittsburgh, ku Pennsylvania, kupita m’tauni ya Brooklyn, ku New York, kunali kofunika kwambiri kuti ntchito yolalikira ipite patsogolo. Motero, ntchito yokonzekera kusamuka inayamba mu 1908 ndipo m’chaka chotsatira, anasamukadi.

N’chifukwa Chiyani Anasamukira ku Brooklyn?

Anthu amene ankatsogolera ntchito yolalikira panthawiyo anaona kuti kusindikiza ulaliki m’manyuzipepala inali njira yabwino kwambiri yofalitsira choonadi cha m’Baibulo. N’chifukwa chake pofika mu 1908, ulaliki wa Russell unali ukufalitsidwa m’manyuzipepala okwana 11 ndipo manyuzipepalawa ankasindizidwa okwana 402,000 mlungu uliwonse.

Komabe, Russell analemba kuti: “Abale amene akudziwa bwino mmene makampani a nyuzipepala amagawanirana nkhani, . . . ananena kuti ngati uthenga wathu womwe umafalitsidwa m’manyuzipepala mlungu uliwonse utamachokera [mu mzinda winawake waukulu], zingachititse kuti uthengawo ufalikire m’dziko lonse la United States. Komanso zingachititse kuti makampani ambiri a nyuzipepala azisindikiza uthenga wathu nthawi zonse.” Choncho, ntchito yofunafuna malo abwino inayambika.

N’chifukwa chiyani anasankha kusamukira ku Brooklyn? Russell anati: “Titapemphera kwa Yehova za nkhaniyi, tonse tinagwirizana kuti tisamukire m’tauni ya Brooklyn, ku New York, mzinda womwe unali ndi anthu ambiri . . . womwenso unkadziwika kuti ‘Mzinda wa Matchalitchi.’ Choncho tinaona kuti ntchito yathu yokolola iyenda bwino kwambiri tikamaigwira tili mu mzindawu.” Ndipo zotsatira zake zinali zabwino kwambiri chifukwa patangopita nthawi yochepa chabe, chiwerengero cha manyuzipepala amene ankasindikiza ulaliki wa Russell, chinakwera kwambiri n’kufika pa 2,000.

Panali chifukwa chinanso chimene chinachititsa kuti mzinda wa New York ukhale wabwino kwambiri pa ntchito yathu. Pofika m’chaka cha 1909, maofesi a nthambi anali atatsegulidwa m’mayiko a Great Britain, Germany, ndi Australia ndipo m’zaka zotsatira, maofesi enanso anatsegulidwa m’mayiko ena. Choncho, zinali zoyeneradi kuti likulu la ntchitoyi likhale mu mzinda wa mphepete mwa nyanja, womwenso unali ndi misewu yambiri ndiponso njanji zolumikizana ndi madera ena.

N’chifukwa Chiyani Anasankha Dzina Lakuti Beteli?

Poyamba, m’zaka za m’ma 1880 likulu la Watch Tower Bible and Tract Society linali ku Allegheny (komwe tsopano ndi mbali ya mzinda wa Pittsburgh), ku Pennsylvania. Nthawi imeneyo, maofesiwa ankatchedwa Nyumba ya Baibulo. Ndipo pofika m’chaka cha 1896, anthu okwana 12 ndi omwe ankagwira ntchito ku maofesiwa.

Koma likululi litasamutsidwira ku Brooklyn mu 1909, nyumba yatsopano imene anthu ogwira ntchito ku maofesiwa ankagona, inkatchedwa ndi dzina lakuti Beteli.a N’chifukwa chiyani anasankha dzinali? Poyamba, maofesi amene bungwe la Watch Tower Society linagula ku 13-17 Hicks Street, anali a m’busa wina wotchuka, dzina lake Henry Ward Beecher ndipo maofesiwa ankatchedwa Beteli ya Beecher. Bungweli linagulanso nyumba imene Beecher ankakhala, yomwe inali ku 124 Columbia Heights. Magazini ya Nsanja ya Olonda ya March 1, 1909, inanena kuti: “Zinali zoyenera kugula Beteli ya Beecher ndipo tinachitanso mwayi wogula nyumba imene iye ankakhala. . . . Nyumbayi tsopano izidziwika ndi dzina loti ‘Beteli,’ ndipo maofesi atsopanowa pamodzi ndi holo yake azitchedwa ‘Chihema cha Brooklyn.’ Mayina amenewa alowa m’malo mwa dzina lakuti ‘Nyumba ya Baibulo.’”

Masiku ano, maofesi a ku Brooklyn ndiponso maofesi ena omwe ali ku Wallkill ndi ku Patterson m’dera la New York, kuphatikizapo nyumba zogona ndiponso nyumba zosindikizira mabuku, zimatchedwanso ndi dzina loti Beteli. Padziko lonse, nyumba za Beteli zilipo m’mayiko okwana 113, ndipo ku malowa kuli anthu oposa 19,000 omwe akugwira ntchito yothandiza kufalitsa uthenga wa m’Baibulo padziko lonse.

Kulandira Alendo Mwansangala

Mwambo wotsegulira maofesiwa unachitika pa January 31, 1909. Ndipo Lolemba pa September 6, 1909, linali tsiku lapadera lomwe anthu anabwera kudzaona malo ku Beteli ya ku Brooklyn. Anthu ambirimbiri a Mboni za Yehova, omwe panthawiyo ankatchedwa ndi dzina loti Ophunzira Baibulo, anabwera kudzaona malo. Ambiri mwa anthuwa anadzaona malowa akuchokera kumsonkhano wawo womwe unachitikira ku Saratoga Springs, mtunda wa makilomita 320 kuchokera ku New York City. Ndipotu alendo amenewa analandiridwa mwansangala kwambiri ndi Charles Taze Russell.b

Masiku anonso, alendo akapita ku Beteli amalandiridwa bwino kwambiri. Ndipo anthu oposa 40,000 amakaona malo ku Beteli ya Brooklyn chaka chilichonse. Beteli imeneyi ikupitirizabe kupititsa patsogolo ntchito yolengeza uthenga wa Ufumu wa Yehova ndipo anthu ochuluka kwambiri akupindula ndi zimenezi.

a Mawu a Chiheberi amene anawamasulira kuti “Beteli” amatanthauza “Nyumba ya Mulungu.” Pa mizinda yotchuka kwambiri yotchulidwa m’Baibulo, mzinda wa Beteli umaposedwa ndi mzinda wa Yerusalemu wokha basi.

b Kuti mudziwe zambiri za nkhaniyi, onani buku lachingelezi lakuti Jehovah’s Witnesses​—Proclaimers of God’s Kingdom, masamba 718-723, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

Kodi Mukudziwa Zotani Zokhudza Watch Tower Bible and Tract Society?

Bungwe lomwe masiku ano limadziwika ndi dzina lakuti Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania linakhazikitsidwa m’chaka cha 1884 ndipo linkatchedwa kuti Zion’s Watch Tower Tract Society. Cholinga cha bungweli chinali kufalitsa choonadi cha m’Baibulo, makamaka kudzera m’mabuku. Masiku ano, bungweli ndi limodzi mwa mabungwe ovomerezeka mwa lamulo amene Mboni za Yehova zimagwiritsa ntchito padziko lonse.c​—Afilipi 1:7.

Bungwe la Watch Tower Bible and Tract Society lasindikiza mabaibulo ndi mabuku ofotokoza za m’Baibulo m’zinenero 473. Bungweli lasindikizanso makope oposa 150 miliyoni a Baibulo la New World Translation of the Holy Scriptures, lathunthu kapena mbali zake zina, m’zinenero 72. Kuwonjezera pa Baibulo limeneli, bungweli lasindikiza lokha, kapenanso lasindikizitsa mabaibulo otsatirawa: American Standard Version, The Bible in Living English, The Emphatic Diaglott, Holman’s Linear Parallel Edition, King James Version (kuphatikizapo Baibulo la ophunzira) ndiponso The New Testament Newly Translated and Critically Emphasized, (losindikizidwa kachiwiri).

Kuwonjezera pa kusindikiza mabaibulo, Mboni za Yehova zatulutsa mabuku ndi zinthu zina zoposa 20 biliyoni pa zaka 10 zapitazi. Zina mwa zinthu zimenezi ndi mabuku, magazini, timapepala, ma CD, ndiponso ma DVD.d Zambiri mwa zinthu zimenezi, zimasindikizidwa, kuikidwa m’makatoni ndi kutumizidwa kuchokera ku nyumba za Beteli za m’mayiko monga otsatirawa: Argentina, Australia, Brazil, Britain, Canada, Colombia, Finland, Germany, India, Italy, Japan, Korea, Mexico, Myanmar, Nigeria, Philippines, South Africa, Spain ndiponso United States.

1998-2008

CHIWERENGERO CHA ZINTHU ZOMWE ZATULUTSIDWA KUYAMBIRA MU 1998 MPAKA 2008

Mabuku

458,230,708

Magazini

11,292,413,199

Timapepala

7,996,906,376

Timabuku

862,050,233

Ma CD ndi ma MP3

34,621,130

Ma DVD

13,500,125

Zinthu zina

129,083,031

Zonse pamodzi

20,786,804,802

c M’chaka cha 2008, anthu a Mboni za Yehova analipo 7,124,443 m’mayiko 236. Iwo ali m’mpingo yokwana 103,267.

d Zinthu zimenezi si zogulitsa ayi. Ntchito ya Mboni za Yehova yophunzitsa Baibulo imachirikizidwa ndi ndalama zimene anthu amapereka mwa kufuna kwawo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena