Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w09 5/15 tsamba 18
  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga
  • Nsanja ya Olonda—2009
  • Nkhani Yofanana
  • Ufumu wa Mulungu Wabadwa
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
  • Olamulira Okhala m’Malo a Mizimu
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Khalani Maso Satana Akufuna Kukumezani
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Kodi Mumamudziwa Bwino Mdani Wanu?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2009
w09 5/15 tsamba 18

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi Satana anachotsedwa liti kumwamba?​—Chiv. 12:1-9.

Buku la Chivumbulutso silimatchula mwachindunji nthawi imene Satana anachotsedwa kumwamba, koma limatchula zinthu zofunika kwambiri zimene zingatithandize kudziwa nthawi imene zimenezi zinachitika. Chinthu choyamba ndicho kukhazikitsidwa kwa Ufumu wa Mesiya ndipo kenaka “kunabuka nkhondo kumwamba.” Pa nkhondoyo Satana anagonjetsedwa n’kuchotsedwa kumwambako.

Malemba amasonyeza momveka bwino kuti mu 1914 “nthawi zoikika za amitundu” zinatha ndipo Ufumu unakhazikitsidwa.a (Luka 21:24) Kodi nkhondo yochotsa Satana kumwamba inayamba zimenezi zitangochitika?

Lemba la Chivumbulutso 12:4 limati “Chinjokacho [Satana] chinangoimabe pamaso pa mkazi uja amene anali pafupi kubereka, kuti akabereka, chimudye mwana wakeyo.” Zimenezi zikusonyeza kuti Satana ankafunitsitsa kuwonongeratu Ufumuwo utangobadwa kumene. Ngakhale kuti Yehova anachitapo kanthu kuti zolinga za Satana zisatheke, Satana anachitabe khama kuti awononge Ufumu umene unali utangokhazikitsidwa kumenewo. N’chifukwa chake “Mikayeli ndi angelo ake” sanachedwechedwe koma anathamangitsa “chinjoka ndi angelo ake” kuwachotsa kumwambako n’cholinga choti Ufumuwo usawonongedwe. Izi zikutipatsa chithunzi chakuti Satana anachotsedwa kumwamba Ufumu utangokhazikitsidwa kumene mu 1914.

Mfundo ina imene tiyenera kuiganizira ndi yokhudza kuuka kwa Akhristu odzozedwa. Malemba amasonyeza kuti kuuka kumeneku kunayamba Ufumu utangokhazikitsidwa kumene.b (Chiv. 20:6) Baibulo silinena kuti Khristu anali ndi abale ake ena pomenyana ndi chinjoka ndiponso ziwanda. Zimenezi zikutanthauza kuti pa nthawi imene abale ake a Khristu anayamba kuuka, nkhondo yochotsa Satana ndi ziwanda zake kumwamba iyenera kuti inali itatha.

Motero, Baibulo silitchula nthawi yeniyeni imene Satana ndi ziwanda zake anachotsedwa kumwamba. Komabe, umboni umasonyeza kuti kuchotsedwa kwa Satana kumwamba kunachitika Yesu Khristu atangoikidwa kumene kukhala Mfumu kumwamba mu 1914.

[Mawu a M’munsi]

a Onani buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? tsamba 215 mpaka 218.

b Onani Nsanja ya Olonda ya January 1, 2007, patsamba 27 ndi 28, ndime 9 mpaka 13.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena