Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w09 11/1 tsamba 16-17
  • Zokhudza Moyo wa Banja

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zokhudza Moyo wa Banja
  • Nsanja ya Olonda—2009
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi anthu okwatirana aziliona motani banja lawo kuti azikhala mosangalala?
  • N’chifukwa chiyani kukonda Mulungu kumathandiza kuti banja likhale losangalala?
  • Kodi mwamuna ndi mkazi wake angatani kuti aliyense azisangalatsa mnzake?
  • Kodi makolo angaphunzire chiyani pa zimene Yesu ankachitira ana?
  • Kodi ana angaphunzire chiyani kwa Yesu?
  • Zimene Mungachite Kuti Banja Lanu Lizisangalala
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Kodi Mulungu Ali Pamalo Oyamba m’Banja Lanu?
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Amuna, Muzitsanzira Umutu wa Khristu
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Kupangitsa Moyo Wabanja Kukhala Wabwino
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2009
w09 11/1 tsamba 16-17

Zimene Tikuphunzira kwa Yesu

Zokhudza Moyo wa Banja

Kodi anthu okwatirana aziliona motani banja lawo kuti azikhala mosangalala?

Ukwati ndi wopatulika. Yesu atafunsidwa ngati zinali zololeka kuti anthu okwatirana azisudzulana, iye anayankha kuti: “Kodi simunawerenge kuti iye amene analenga iwo pachiyambi pomwe anapanga iwo mwamuna ndi mkazi ndi kunena kuti, ‘Pa chifukwa chimenechi mwamuna adzasiya atate wake ndi amayi wake ndipo adzaphatikana ndi mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi’? Kotero kuti salinso awiri, koma thupi limodzi. Choncho, chimene Mulungu wachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse. . . . Aliyense wosudzula mkazi wake ndi kukwatira wina achita chigololo, kupatulapo ngati am’sudzula chifukwa cha dama.” (Mateyo 19:4-6, 9) Anthu okwatirana akamatsatira malangizo amenewa ndiponso akakhala okhulupirika kwa wina ndi mnzake, banja lawo limakhala losangalala.

N’chifukwa chiyani kukonda Mulungu kumathandiza kuti banja likhale losangalala?

Yesu ananena kuti: “‘Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.’ Limeneli ndilo lamulo lalikulu koposa komanso loyamba.” Nanga kodi lachiwiri kwa lamulo lalikulu kwambirili ndi liti? Yesu anati: “Uzikonda mnansi wako [kuphatikizapo anthu a m’banja mwanu] mmene umadzikondera wekha.” (Mateyo 22:37-39) Choncho, kuti banja lathu lizikhala mosangalala tiyenera kukonda kwambiri Mulungu chifukwa zimenezi zingatithandize kuti tizikondanso anthu ena.

Kodi mwamuna ndi mkazi wake angatani kuti aliyense azisangalatsa mnzake?

Mwamuna akamatsatira chitsanzo cha Yesu, amasangalatsa mkazi wake. Yesu ankakonda kwambiri mpingo, womwe uli ngati mkazi wake. (Aefeso 5:25) Yesu anati: “Mwana wa munthu sanabwere kudzatumikiridwa, koma kudzatumikira.” (Mateyo 20:28) Iye ankalimbikitsa anthu amene ankawayang’anira, osati kumangowalamula kapena kuwachitira nkhanza. (Mateyo 11:28) Choncho, amuna ayenera kuchita udindo wawo mokoma mtima, zomwe zingapindulitse onse m’banjamo.

Akazi nawonso ayenera kutsatira chitsanzo cha Yesu. Baibulo limati: “Mutu wa Khristu ndiye Mulungu.” Ndipo limanenanso kuti: “Mutu wa mkazi ndi mwamuna.” (1 Akorinto 11:3) Yesu sankaona kuti anyozeka akamagonjera Mulungu. Iye ankalemekeza kwambiri Atate wake. N’chifukwa chake ananena kuti: “Ndimachita zinthu zom’kondweretsa nthawi zonse.” (Yohane 8:29) Mkazi amene amagonjera mwamuna wake chifukwa chokonda ndiponso kulemekeza Mulungu, banja lake limasangalala.

Kodi makolo angaphunzire chiyani pa zimene Yesu ankachitira ana?

Yesu ankacheza ndi ana ndipo ankakonda kumva maganizo awo komanso ankazindikira mmene anawo akumvera. Baibulo limati: “Yesu anaitana anawo, nati: ‘Alekeni ana aang’onowo abwere kwa ine.’” (Luka 18:15, 16) Nthawi ina anthu anadzudzula anyamata ena omwe ankatamanda Yesu. Koma Yesu anayamikira anyamatawo ndipo anauza anthu omwe ankawadzudzulawo kuti: “Kodi simunawerenge zimenezi kuti, ‘M’kamwa mwa tiana ndi makanda oyamwa mwaikamo mawu otamanda’?”​—Mateyo 21:15, 16.

Kodi ana angaphunzire chiyani kwa Yesu?

Yesu anapereka chitsanzo chabwino kwambiri kwa ana kuti azikonda zinthu zauzimu. Panthawi ina ali ndi zaka 12, anapezeka “m’kachisi, atakhala pakati pa aphunzitsi. Anali kuwamvetsera ndi kuwafunsa mafunso.” Ndiyeno kodi chinachitika n’chiyani? Baibulo limapitiriza kuti: “Onse amene anali kumumvetsera anadabwa kwambiri chifukwa cha kumvetsa zinthu kwake ndi mayankho ake.” (Luka 2:42, 46, 47) Komabe, Yesu sankadzikuza chifukwa choti anali ndi nzeru. Koma zinam’pangitsa kuti azilemekeza kwambiri makolo ake. Baibulo limati: “Anapitiriza kuwamvera.”​—Luka 2:51.

Kuti mudziwe zambiri, onani mutu 14 m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?a

[Mawu a M’munsi]

a Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena