Ulamuliro wa Satana Utha Posachedwa
“Woipa sadzapeza bwino.”—MLAL. 8:13.
1. N’chifukwa chiyani zili zolimbikitsa kudziwa kuti oipa adzaweruzidwa?
TSIKU lina anthu ochita zoipa adzaimbidwa mlandu. Iwo adzaweruzidwa pa zimene akhala akuchita. (Miy. 5:22; Mlal. 8:12, 13) Nkhani imeneyi ndi yolimbikitsa kwambiri kwa anthu amene amakonda chilungamo omwenso akhala akuzunzidwa ndi anthu oipa. Pa oipa onse amene adzaweruzidwe, woipitsitsa ndi Satana Mdyerekezi amene anayambitsa zoipa zonse.—Yoh. 8:44.
2. N’chifukwa chiyani panafunika kuti papite nthawi ndithu kuti Mulungu athetse nkhani imene inayambika mu Edene?
2 Kalelo m’munda wa Edene, Satana anachititsa anthu kukana ulamuliro wa Yehova. Anachita zimenezi chifukwa cha mtima wodzikuza. Zitatero makolo athu oyambirira anamvera Satanayo potsutsa zoti Yehova ndi woyenera kulamulira ndipo izi zinachititsa kuti akhale ochimwa pamaso pa Yehova. (Aroma 5:12-14) Yehova ankadziwa mavuto amene angabwere chifukwa cha kupanduka ndiponso kusamvera kwawoko. Komabe, iye anafuna kuti angelo ndi anthu onse adzionere okha mavuto obwera chifukwa cha kupandukira Mulungu. Motero panafunika nthawi ndithu kuti nkhaniyi ithetsedwe ndiponso kuti aliyense adziwe kuti opandukawo analakwa kwabasi.
3. Kodi maulamuliro a anthu tiziwaona bwanji?
3 Popeza anthu anakana ulamuliro wa Yehova iwo anayenera kukhala ndi maulamuliro awo. M’kalata yake yopita kwa Akhristu a ku Roma, Paulo anatchula maboma a anthu amenewa kuti “olamulira aakulu.” M’nthawi ya Paulo, olamulira aakuluwa anali ulamuliro wa Roma ndipo mfumu yake inali Nero amene analamulira kuchokera mu 54 C.E. mpaka mu 68 C.E. Paulo ananena kuti olamulira aakuluwa “ali m’malo awo osiyanasiyana mololedwa ndi Mulungu.” (Werengani Aroma 13:1, 2.) Kodi Paulo ankatanthauza kuti maulamuliro a anthu ndi aakulu kuposa ulamuliro wa Mulungu? Ayi. Iye ankatanthauza kuti Yehova walola maulamuliro a anthuwa kukhalapo, choncho Akhristu ayenera kulemekeza olamulirawo chifukwa limeneli “ndi dongosolo la Mulungu.”
Njira Yotsogolera ku Chiwonongeko
4. N’chifukwa chiyani ulamuliro wa anthu umalephera?
4 Komatu ulamuliro wa anthu umene Satana anayambitsa utha posachedwapa. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa chimodzi n’chakuti olamulira ake sayendera nzeru za Mulungu. Ndi Yehova yekha amene ali ndi nzeru zangwiro. Motero ndi iye yekha amene angathandize kuti pakhale ulamuliro wabwino. (Yer. 8:9; Aroma 16:27) Mosiyana ndi anthu amene amaphunzira zinthu pambuyo polakwitsalakwitsa, Yehova nthawi zonse amadziwa njira yoyenera yochitira chilichonse. Palibe ulamuliro uliwonse umene ungayende bwino ngati olamulirawo satsatira malangizo a Yehova. Pachifukwa chimenechi, komanso chifukwa chakuti Satana anali ndi zolinga zoipa, timadziwa kuti ulamuliro wake wogwiritsa ntchito anthu, n’zimene zachititsa kuti ukhale ukulephera kuyambira pachiyambi.
5, 6. Kodi n’chiyani chikuoneka kuti chinachititsa Satana kupandukira Yehova?
5 Munthu wanzeru sayamba dala kuchita zinthu zimene akudziwa kuti zilephereka. Munthu wochita zimenezi ngakhale atalimbikira chotani amadzazindikira kuti zimene akufunazo n’zosatheka. Zinthu zimene zakhala zikuchitika zikusonyezeratu kuti kulimbana ndi ulamuliro wa Mlengi wamphamvuyonse n’kupusa kwambiri. (Werengani Miyambo 21:30.) Koma Satana anapandukira Yehova chifukwa cha kudzikuza ndiponso kunyada. Apa Mdyerekezi anasankha dala kuyenda pa njira ya kuchiwonongeko.
6 Mfumu ya ku Babulo inasonyeza kudzikuza kumene Satana ali nako. Malemba amanena kuti mfumuyo inati: “Ndidzakwera kumwamba, ndidzakweza mpando wanga wachifumu pamwamba pa nyenyezi za Mulungu; ndidzakhala pamwamba pa phiri la khamu, m’malekezero a kumpoto; ndidzakwera pamwamba pa mitambo, ndidzafanana ndi Wam’mwambamwamba.” (Yes. 14:13-15) Maganizo opusa amenewa sanaphule kanthu ndipo ulamuliro wa Babulo unatha mochititsa manyazi. Izi ndi zimene zidzachitikire Satana ndi anthu ake. Posachedwapa iye ndi dziko lakeli adzawonongedwa.
N’chifukwa Chiyani Mulungu Analola Zimenezi?
7, 8. Kodi anthu apindula motani chifukwa chakuti Yehova walola zoipa kuchitika kwa kanthawi?
7 Anthu ena angadzifunse kuti, n’chifukwa chiyani Yehova sanaletse anthu ndi Satana kuyambitsa maulamuliro awo osakhalitsa? Popeza Mulungu ndi Wamphamvuyonse akanatha kuchita zimenezi. (Eks. 6:3) Koma iye sanawaletse. Chifukwa cha nzeru zake, anaganiza zowasiya anthu kuti adzilamulire kwa kanthawi ndipo anadziwa kuti kuchita zimenezi kuli ndi ubwino wake. Yehova anadziwa kuti m’tsogolo, anthu ena adzadziwa kuti iye ndi woyenera kulamulira, amalamulira mwachilungamo ndiponso mwachikondi. Anadziwanso kuti anthu okhulupirika adzapindula ndi zimene anasankha kuchitazi.
8 Anthu sakanakumana ndi mavuto onsewa akanakhala kuti anakana bodza la Satana komanso akanakana kupandukira ulamuliro wa Mulungu. Komabe, zimene Yehova anachita polola kuti anthu adzilamulire kwa kanthawi zathandiza kwambiri. Zachititsa kuti anthu amitima yabwino adziwe kuti kumvera Mulungu ndiponso kumukhulupirira ndi chinthu chanzeru. Kwa zaka zambiri, anthu ayesa mitundu yosiyanasiyana ya maboma ndipo palibe boma limene lathandiza pa mavuto onse a anthu. Mfundo imeneyi yathandiza kuti anthu amene amalambira Mulungu azikhulupirira ndi mtima wonse kuti ulamuliro wa Yehova ndi wabwino kuposa uliwonse. N’zoona kuti anthu onse kuphatikizapo amene amalambira Yehova mokhulupirika amakumana ndi mavuto ankhaninkhani chifukwa chakuti iye walola Satana kulamulira. Ngakhale zili choncho, anthu amene amalambira Yehova mokhulupirikawa apindula chifukwa chakuti Yehova walola Satana kulamulira kwa kanthawi.
Kupanduka kwa Satana Kwachititsa Kuti Mulungu Alemekezedwe
9, 10. Fotokozani mmene ulamuliro wa Satana wachititsira kuti Yehova alemekezedwe.
9 Kulola kuti anthu azidzilamulira motsogoleredwa ndi Satana, sikunachititse kuti anthu onse anyoze ulamuliro wa Yehova kapena kusiya kuukhulupirira. M’malomwake, zimene zakhala zikuchitika zatsimikizira kuti mfundo imene Yeremiya ananena mouziridwa, ndi yoona. Iye ananena kuti anthu sangathe kudzilamulira okha. (Werengani Yeremiya 10:23.) Kuwonjezera pamenepo, kupanduka kwa Satana kwachititsa kuti Yehova asonyeze makhalidwe ake abwino m’njira yapadera kwambiri. Kodi zimenezi zachitika motani?
10 Popeza taona mavuto amene ulamuliro wa Satana wabweretsa, tadziwa makhalidwe abwino koposa a Yehova m’njira imene mwina sitikanaiganizirapo n’komwe. Izi zachititsa kuti anthu amene amamukonda azimulemekeza. Ngakhale kuti sizimene Satana ankafuna, ulamuliro wake wachititsa kuti anthu alemekeze Mulungu. Ulamuliro wa Satana wachititsanso kuti aliyense adziwe kwambiri nzeru za Yehova chifukwa cha mmene wayankhira otsutsa ulamuliro wake. Kuti timvetse mfundo imeneyi, tiyeni tione makhalidwe ena a Yehova ndiponso mmene ulamuliro wa Satana wathandizira kuti Yehova asonyeze makhalidwewo m’njira zinanso.
11. Kodi Yehova wasonyeza bwanji kuti amakonda anthu?
11 Chikondi. Malemba amatiuza kuti “Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yoh. 4:8) Kulenga anthu pakokha, ndi umboni wakuti Mulungu ndi wachikondi. Anthufe tinalengedwa modabwitsa kwambiri, ndipo uwu ndi umboni winanso wakuti Mulungu ndi wachikondi. Yehova anapatsanso anthu malo okhala abwino kwambiri omwe anali ndi chilichonse chowathandiza kuti akhale osangalala. (Gen. 1:29-31; 2:8, 9; Sal. 139:14-16) Koma pamene anthu anachimwa, Yehova anasonyezanso chikondi chake m’njira zina. Kodi anachita zimenezi motani? Mtumwi Yohane analemba kuti Yesu anati: “Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira mwa iye asawonongeke, koma akhale nawo moyo wosatha.” (Yoh. 3:16) Kodi pali njira inanso imene Mulungu akanasonyezera chikondi chake yoposa kutumiza Mwana wake wobadwa yekha padziko lapansi kuti adzapulumutse ochimwa? (Yoh. 15:13) Chikondi chapadera chimene Mulungu anasonyezachi, ndi chitsanzo kwa anthufe. Nafenso tiyenera kusonyeza chikondi pamoyo wathu wa tsiku ndi tsiku mwa kulolera kuvutikira ena ngati mmene Yesu anachitira.—Yoh. 17:25, 26.
12. Kodi Yehova wasonyeza bwanji kuti ndi wamphamvu?
12 Mphamvu. “Mulungu, Wamphamvuyonse,” ndi amene ali ndi mphamvu zolenga moyo. (Chiv. 11:17; Sal. 36:9) Munthu akangobadwa, amakhala ngati pepala losalemba chilichonse. Panthawi yomwalira, amakhala atadzaza pepala lija ndi zochita ndiponso zimene wakumana nazo m’moyo ndipo izi ndi zimene zimasonyeza kuti anali munthu wotani. Yehova amasunga zinthu zonsezi m’maganizo ake. Panthawi yake, Yehova angathe kudzamuukitsa munthu uja n’kukhala ndendende mmene analili asanafe. (Yoh. 5:28, 29) Choncho ngakhale kuti sichinali cholinga cha Mulungu kuti anthu azifa, imfa yachititsa kuti Yehova asonyeze kuti ali ndi mphamvu zoukitsa anthu. N’zoonadi, Yehova ndi “Mulungu, Wamphamvuyonse.”
13. Kodi nsembe ya Yesu imasonyeza bwanji kuti Yehova ndi chimake cha chilungamo?
13 Chilungamo. Yehova sanama, ndipo sachita zinthu zopanda chilungamo. (Deut. 32:4; Tito 1:2) Nthawi zonse iye alibe mnzake pankhani ya choonadi ndiponso chilungamo, ngakhale panthawi imene zingaoneke kuti kuchita zimenezi sikom’komera iyeyo. (Aroma 8:32) Mwachitsanzo, zinam’pweteka kwambiri Yehova kuona Yesu, Mwana wake wokondedwa, akufa pa mtengo wozunzikirapo ngati kuti anali munthu wosakhulupirika ndiponso wonyoza Mulungu. Koma chifukwa chakuti Yehova amakonda anthu ngakhale kuti ndi opanda ungwiro, iye analola kuti imfa yowawa imeneyi ichitike n’cholinga chakuti chilungamo chake changwiro chikwaniritsidwe. (Werengani Aroma 5:18-21.) Chifukwa chakuti m’dzikoli mulibe chilungamo ngakhale pang’ono, Yehova wakhala ndi mwayi wosonyeza kuti iye ndi chimake cha chilungamo.
14, 15. Kodi ndi njira zina ziti zimene Yehova wasonyezera nzeru zapamwamba komanso kuleza mtima kwake kosayerekezereka?
14 Nzeru. Adamu ndi Hava atangochimwa, Yehova ananena njira imene adzachotsere zoipa zonse zobwera chifukwa cha kupanduka kwawo. (Gen. 3:15) Chifukwa chakuti Yehova anachita zimenezi mwamsanga ndipo anayamba kuululira atumiki ake cholinga chimenechi mwapang’onopang’ono, zinasonyeza nzeru zake zapamwamba. (Aroma 11:33) Palibe chimene chingaletse Mulungu kukwaniritsa zimene akufuna. Yehova wakhala ndi mpata wosonyeza nzeru zenizeni kwa anthu ndi angelo ake, chifukwa dzikoli ladzaza ndi chiwerewere, nkhondo, kusaganizirana, kusamvera, nkhanza, tsankho ndiponso chinyengo. Yakobe yemwe anali wophunzira wa Yesu anati: “Nzeru yochokera kumwamba, choyamba, ndi yoyera, kenako yamtendere, yololera, yokonzeka kumvera, yodzala chifundo ndi zipatso zabwino, yopanda tsankho, yopanda chinyengo.”—Yak. 3:17.
15 Kupirira Ndiponso Kuleza Mtima. Makhalidwe a Yehova monga kupirira ndiponso kuleza mtima, sakanaonekera kwambiri pakanapanda kuti iye wakhala ndi mpata wochita zinthu ndi anthu opanda ungwiro, ochimwa ndiponso okhala ndi zophophonya zambiri. Yehova wachita zimenezi kwa zaka masauzande ambiri. Ndipo zimenezi zasonyeza bwino kwambiri kuti ali ndi makhalidwe ochititsa chidwi amenewa. Anthufe tiyenera kumuyamikira kwambiri chifukwa cha zimenezi. Mpake kuti mtumwi Petulo ananena kuti “muone kuleza mtima kwa Ambuye wathu kukhala chipulumutso.”—2 Pet. 3:9, 15.
16. N’chifukwa chiyani timasangalala kwambiri ndi mtima wokhululuka umene Yehova ali nawo?
16 Mtima Wokhululuka. Tonse ndife ochimwa ndipo timapunthwa nthawi zambiri. (Yak. 3:2; 1 Yoh. 1:8, 9) Tiyenera kuyamikira kwambiri chifukwa Yehova ali ndi mtima wokhululuka “koposa.” (Yes. 55:7) Taganiziranso mfundo iyi. Chifukwa chakuti timabadwa opanda ungwiro, timasangalala kwambiri Mulungu akatikhululukira machimo athu. (Sal. 51:5, 9, 17) Tikadziwa kuti Yehova watikhululukira, timayamba kumukonda kwambiri ndipo timafunitsitsa kutengera chitsanzo chake ndi kumakhululukiranso ena.—Werengani Akolose 3:13.
Dzikoli Likudwala
17, 18. Kodi n’chifukwa chiyani tinganene kuti ulamuliro wa Satana ndi wolephera ?
17 Kwa zaka zambirimbiri, dongosolo lonse la Satanali lalephera kuyendetsa bwino zinthu. Mu 1991, nyuzipepala ina inati: “Kodi dzikoli likudwala? Eya, tingatero . . . koma amene ayambitsa matendawa ndi anthu osati Mulungu.” (The European) Zimenezitu ndi zoona. Satana anachititsa makolo athu oyambirira kuti asankhe ulamuliro wa anthu m’malo molamulidwa ndi Yehova. Motero iwo anayambitsa ulamuliro woti sungapite patali. Mavuto adzaoneni amene anthu akukumana nawo ndi umboni wakuti ulamuliro wa anthu uli ngati matenda akayakaya.
18 Ulamuliro wa Satana ndi wokomera anthu a mtima wosaganizira ena. Komabe mtima umenewu sungagonjetse chikondi, chomwe ndi khalidwe limene Yehova amagwiritsa ntchito polamulira. Ulamuliro wa Satana walephera kubweretsa dziko la bata, losangalatsa ndiponso lotetezeka. Tsopano zatsimikizirika kuti ulamuliro wa Yehova ndi woyenerera. Kodi pali umboni wotsimikizira zimenezi masiku ano? Inde ulipo, ndipo m’nkhani yotsatira tikambirana zimenezi.
Pankhani ya Ulamuliro, Fotokozani Zimene Taphunzira pa Malemba Awa:
• Akolose 3:13.
[Chithunzi patsamba 25]
Ulamuliro wa Satana sunapindulitsepo anthu ngakhale pang’ono
[Mawu a Zithunzi]
U.S. Army photo
WHO photo by P. Almasy
[Chithunzi patsamba 26]
Yehova ali ndi mphamvu zotha kuukitsa akufa
[Chithunzi patsamba 27]
Yehova anasonyeza chikondi ndi chilungamo chake mwa kupereka Mwana wake nsembe