Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w11 10/1 tsamba 3
  • Kodi Anakunamizani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Anakunamizani?
  • Nsanja ya Olonda—2011
  • Nkhani Yofanana
  • Mavuto Omwe Anabwera Chifukwa cha Bodza Loyamba
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
  • Petulo ndi Hananiya Ananama, Kodi Tikuphunzirapo Chiyani?
    Nsanja ya Olonda—2013
  • Kodi Nchifukwa Ninji Kunama Kuli Kosavuta Choncho?
    Nsanja ya Olonda—1992
  • N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kupewa Kunama ndiponso Kuba?
    Zimene Achinyamata Amafunsa
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2011
w11 10/1 tsamba 3

Kodi Anakunamizani?

ZIMAKHALA zokhumudwitsa kwambiri ukadziwa kuti munthu amene umamukhulupirira wakunamiza. Zimenezi zikachitika, umachita manyazi, kukwiya ndipo mwinanso umaona kuti wapusitsidwa. Bodza limadanitsa anthu, kuthetsa mabanja komanso limawonongetsa ndalama zambiri.

Ndiyeno kodi mungamve bwanji mutazindikira kuti zina zimene munaphunzitsidwa zokhudza Mulungu ndi zabodza? Ngati ndinu wokonda zopemphera, zimenezi zingakukhumudwitseni kwambiri ngati mmene zinakhalira ndi anthu amene ananena mawu ali m’munsiwa:

● “Ndinaona kuti tchalitchi changa chandipusitsa.”​—DEANNE.

● “Zinandikwiyitsa kwambiri ndipo ndinkaona kuti andipusitsa. Ndinazindikira kuti zonse zimene ndinkayembekezera komanso zolinga zanga zonse, zinali zopanda ntchito.”​—LUIS.

Mwina mungaone kuti n’zosatheka kuti zimene mwakhala mukuphunzira zokhudza Mulungu zingakhale zabodza. N’kutheka kuti amene anakuphunzitsani zimenezo ndi munthu amene mumaona kuti sangakunamizeni ndipo mumamukhulupirira kwambiri. Mwina munaphunzitsidwa ndi makolo anu, wansembe, m’busa, kapena mnzanu wapamtima. Mwinanso zina mwa zinthu zimenezi mwakhala mukuzikhulupirira kwa moyo wanu wonse. Koma kodi sizoona kuti zinthu zina zitha kukhala zabodza ngakhale kuti anthu ambiri akuzikhulupirira? Franklin D. Roosevelt, pulezidenti wakale wa dziko la United States, ankadziwa kuti mfundo imeneyi ndi yoona. Iye anati: “Ngakhale anthu atamabwerezabwereza nkhani inayake yomwe ndi yabodza, nkhaniyo singasinthe n’kukhala yoona.”

Kodi mungadziwe bwanji ngati zimene mumakhulupirira zili zabodza? Nthawi ina Yesu anapemphera kwa Mulungu kuti: “Mawu anu ndiwo choonadi.” (Yohane 17:17) Choncho, lembali likutitsimikizira kuti Baibulo, lomwe ndi Mawu a Mulungu, ndi limene lingatithandize kusiyanitsa zoona ndi zabodza.

Tikukupemphani kuti muwerenge nkhani zotsatirazi kuti muone mmene Baibulo limasonyezera kuti mfundo zina zimene anthu ambiri amakhulupirira zokhudza Mulungu, ndi zabodza. Tikambirana mfundo zisanu ndipo muona mmene kudziwa zoona pa nkhanizi kungakuthandizireni pa moyo wanu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena