Zimene Owerenga Amafunsa
Kodi Ndi Bwino Kubatiza Ana Akhanda?
▪ “Ndinkada nkhawa kuti mchimwene wanga John, yemwe anamwalira ali wakhanda azingokhala ku Limbo.” Mawu amenewa ananena ndi mtsikana wina, dzina lake Victoria. Kodi n’chifukwa chiyani iye ankada nkhawa chonchi? Victoria anafotokoza kuti: “John anamwalira asanabatizidwe ndipo wansembe wa tchalitchi cha Katolika anatiuza kuti zimenezi zichititsa kuti John akakhale ku Limbo mpaka kalekale.” Chiphunzitso chimenechi n’chochititsa mantha, koma kodi n’chogwirizana ndi zimene Baibulo limanena? Kodi Baibulo limaphunzitsa kuti ana amene amwalira asanabatizidwe amakangokhala kumalo kwinakwake?
Baibulo limaphunzitsa kuti Akhristu ayenera kubatizidwa. Yesu analangiza otsatira ake kuti: “Pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga. Muziwabatiza m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyera, ndi kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulirani.” (Mateyu 28:19, 20) Onani kuti Yesu ananena kuti anthu omwe ndi ophunzira ake ndi amene ayenera kubatizidwa. Izi zikutanthauza kuti anthu amenewa ayenera kukhala amene aphunzira za Yesu ndipo asankha kukhala otsatira ake. Koma mwana wakhanda sangathe kusankha pa nkhani imeneyi.
Koma anthu ambiri amaumirira kuti lamulo la Yesu loti anthu azibatizidwali, limagwiranso ntchito kwa ana akhanda. M’busa wina wa tchalitchi cha Lutheran, dzina lake Richard P. Bucher, ananenetsa kuti: “Aliyense ayenera kubatizidwa, ngakhalenso ana akhanda.” Iye anawonjezera kuti: “Kulephera kuwabatiza kungachititse kuti machimo awo asadzakhululukidwe komanso kuti adzalangidwe kwamuyaya.” Komatu pali mfundo zitatu zimene zikusonyeza kuti mawu amenewa amatsutsana ndi zimene Yesu ankaphunzitsa.
Choyamba, Yesu sanaphunzitse kuti ana aang’ono ayenera kubatizidwa. Kodi tikudziwa bwanji zimenezi? Kumbukirani kuti Yesu anaphunzitsa ophunzira ake mwakhama zinthu zimene Mulungu amafuna. Nthawi zina, mfundo zofunika kwambiri ankazinena mobwerezabwereza. Iye ankazibwereza n’cholinga choti ophunzira akewo amvetse mfundozo. (Mateyu 24:42; 25:13; Maliko 9:34-37; 10:35-45) Komatu Yesu sanaphunzitse, ngakhale kamodzi, kuti ana akhanda ayenera kubatizidwa. Kodi tingati Yesu anaiwala kutchula mfundo imeneyi? Zimenezi n’zosatheka. Zikanakhala kuti ana akhanda ayenera kubatizidwa, Yesu akanatchula mfundo imeneyo.
Chachiwiri, Yesu sanaphunzitsepo zoti anthu amazunzika akamwalira. Iye ankakhulupirira zimene Malemba amanena, kuti: “Amoyo amadziwa kuti adzafa, koma akufa sadziwa chilichonse.” (Mlaliki 9:5) Yesu ankadziwa kuti akufa sazunzika ku puligatoliyo, ku Limbo, kumoto kapena kwina kulikonse. M’malomwake iye anaphunzitsa kuti akufa sadziwa chilichonse ngati mmene zimakhalira munthu akagona tulo tofa nato.—Yohane 11:1-14.
Chachitatu, Yesu anaphunzitsa kuti “onse ali m’manda achikumbutso” adzaukitsidwa. (Yohane 5:28, 29) N’zosakayikitsa kuti anthu ochuluka amene anamwalira asanabatizidwe adzakhala m’gulu la anthu amenewa. Anthu amenewa akadzaukitsidwa adzapatsidwa mwayi wophunzira zimene Mulungu amafuna komanso wokhala ndi moyo kosatha m’Paradaiso padziko lapansi.a—Salimo 37:29.
Ndiyetu apa n’zoonekeratu kuti Baibulo siliphunzitsa kuti ana akhanda ayenera kubatizidwa.
[Mawu a M’munsi]
a Kuti mudziwe zambiri zokhudza Paradaiso wapadziko lapansi komanso chiyembekezo chakuti akufa adzauka, werengani mutu 3 ndi 7 m’buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.