Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w11 11/1 tsamba 8-9
  • Kodi N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kutsatira Mfundo za M’Baibulo?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kutsatira Mfundo za M’Baibulo?
  • Nsanja ya Olonda—2011
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “Nthawi Yomweyo Mtima Wanga Unakhala M’malo”
  • Yehova Anamutchula Kuti “Mfumukazi”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2017
  • “Ndiwe Mkazi Wokongola”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2017
  • Kodi N’chifukwa Chiyani Kudziwa Zimenezi Kuli Kofunika?
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Ndizitsatira Mfundo za M’Baibulo Chifukwa Chiyani?
    Galamukani!—2007
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2011
w11 11/1 tsamba 8-9

Kodi N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kutsatira Mfundo za M’Baibulo?

KODI malangizo a m’Baibulo pa nkhani ya kugonana ndi achikale komanso okhwima? Ayi, chifukwa malangizo a m’Baibulo angatithandize kupewa:

▪ Kutenga matenda opatsirana pogonana

▪ Kutenga mimba zapathengo

▪ Mavuto amene amakhalapo ukwati ukatha

▪ Kuvutika ndi chikumbumtima

▪ Kudzichotsera ulemu

Mlengi wathu, Yehova Mulungu,a amafuna kuti tisangalale ndiponso kupindula ndi mphatso zimene watipatsa. Mulungu ‘amakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendereni bwino.’ (Yesaya 48:17) Munthu amene amatsatira mfundo za m’Baibulo pa nkhani ya kugonana amapindula chifukwa:

▪ Mulungu amakondwera naye

▪ Amakhala ndi mtendere wamumtima

▪ Banja lake limakhala lokondana komanso lolimba

▪ Amakhala ndi mbiri yabwino

▪ Anthu amamulemekeza

Komano bwanji ngati panopa simukutsatira mfundo za m’Baibulo? Kodi n’zotheka kusintha khalidwe lanu? Kodi Mulungu adzapitirizabe kukuonani ngati woipa ngakhale mutasintha?

Taganizirani mfundo iyi: M’nthawi ya atumwi, anthu ena omwe anali mumpingo wachikhristu, poyamba anali adama, achigololo komanso omwe ankagonana ndi amuna anzawo. Koma anthu amenewa anasintha khalidwe lawo ndipo anadalitsidwa kwambiri. (1 Akorinto 6:9-11) Masiku anonso, anthu ambiri padziko lonse lapansi asintha khalidwe loipa limene ankachita poyamba. Anthu amenewa asintha khalidwe lawo lachiwerewere, n’kuyamba kukhala moyo wogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo ndipo zimenezi zawabweretsera madalitso ambiri. Mwachitsanzo, taganizirani za Sarah amene tinamutchula m’nkhani yoyambirira ija.

“Nthawi Yomweyo Mtima Wanga Unakhala M’malo”

Sarah anazindikira kuti khalidwe lake lotayirira silinkam’patsa chimwemwe komanso ufulu umene ankafuna. Iye anati: “Chikumbumtima changa chinkandivutitsa kwambiri. Ndinkachita manyazi komanso ndinkada nkhawa kuti nditenga mimba kapena matenda oopsa. Ndinkakhulupirirabe kuti Mulungu aliko ndipo ndinkadziwanso kuti zochita zanga zimamukhumudwitsa. Ndinkaona kuti siine woyera pamaso pa Mulungu ndipo maganizo amenewa ankandisowetsa mtendere kwambiri.”

Kenako Sarah anatsimikiza mtima kuti akufuna kusintha khalidwe lake. Iye anapempha makolo ake, omwe ndi a Mboni za Yehova, kuti amuthandize. Anapemphanso thandizo kwa akulu a mumpingo wa Mboni za Yehova umene uli m’dera lawo. Iye anati: “Ndinadabwa kuona kuti makolo anga komanso akulu anandithandiza mwachifundo komanso mwachikondi kwambiri. Nthawi yomweyo mtima wanga unakhala m’malo.”

Panopa Sarah ali ndi ana awiri. Iye anati: “Sindimawabisira ana anga za khalidwe loipa limene ndinkachita. Ndimafuna kuti adziwe mavuto amene ndakumana nawo chifukwa chosatsatira malangizo a Mulungu. Ndimachita zimenezi n’cholinga chakuti ndiwathandize kudziwa kuti kutsatira mfundo za m’Baibulo zokhudza kugonana kumatithandiza kwambiri pa mbali zonse za moyo wathu. Ndikukhulupirira ndi mtima wonse kuti Mulungu amatipatsa mfundo za makhalidwe abwino pofuna kutiteteza.”

Inunso mungapindule chifukwa chotsatira malangizo achikondi a Mulungu. M’Baibulo muli lonjezo ili: “Malamulo ochokera kwa Yehova ndi olungama, amasangalatsa mtima. Chilamulo cha Yehova ndi choyera, chimatsegula maso. . . . Munthu wosunga zigamulozo amapeza mphoto yaikulu.”​—Salimo 19:8, 11.b

[Mawu a M’munsi]

a Baibulo limanena kuti dzina la Mulungu ndi Yehova.

b Kuti mudziwe zambiri zokhudza mfundo zothandiza za m’Baibulo, kambiranani ndi Mboni za Yehova za m’dera lanu. Kapena lembani kalata pogwiritsa ntchito adiresi yoyenera pa maadiresi amene ali patsamba 4. Kapenanso mungapite pamalo athu a pa Intaneti pogwiritsa ntchito adiresi iyi: www.jw.org.

[Mawu Otsindika patsamba 8]

Anthu amene satsatira mfundo za m’Baibulo amakhumudwitsa anzawo

[Mawu Otsindika patsamba 9]

Anthu amene amatsatira mfundo za m’Baibulo amakhala ndi chikumbumtima choyera komanso amakhala ndi banja losangalala

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena