Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w11 12/1 tsamba 3
  • Kodi Mulungu Akutilanga?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mulungu Akutilanga?
  • Nsanja ya Olonda—2011
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani ya Ngozi Zadzidzidzi?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • N’chifukwa Chiyani Masoka Achilengedwe Achuluka Chonchi?
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Kodi Masoka Achilengedwe Ndi Chilango Chochokera kwa Mulungu?
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Kodi Mulungu Amalanga Anthu Pogwiritsa Ntchito Masoka Achilengedwe?
    Galamukani!—2012
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2011
w11 12/1 tsamba 3

Kodi Mulungu Akutilanga?

M’dziko la Japan mutachitika chivomezi champhamvu kwambiri m’mwezi wa March 2011, chimene chinachititsanso tsunami, munthu wina wotchuka pa ndale m’dzikolo ananena kuti: “Anthu amene akhudzidwa ndi tsoka limeneli ndikuwamvera chisoni, komabe ndikuganiza kuti chimenechi ndi chilango chochokera kwa Mulungu.”

Anthu oposa 220,000 atafa pa chivomezi chimene chinachitika ku Haiti mu January 2010, m’busa wina wotchuka yemwe amalalikira pa TV ananena kuti anthuwo anakumana ndi tsokali chifukwa “anachita mgwirizano ndi mdyerekezi” ndipo ankafunika “kubwerera kwa mulungu.”

Anthu 79 atafa pambuyo popondedwapondedwa pa chipwirikiti chimene chinachitika ku Manila m’dziko la Philippines, wansembe wina wa Katolika anati: “Mulungu akufuna kuti adzutsenso chikumbumtima chathu, chomwe panopa n’chakufa ndiponso sichikhudzidwa ndi chilichonse.” Ndipo nyuzipepala ina m’dzikolo inati, “anthu 21 pa anthu 100 alionse amakhulupirira kuti Mulungu akuwasonyeza mkwiyo wake pogwiritsira ntchito mphepo zamkuntho, kugumuka kwa nthaka ndi miyala yochokera m’mapiri imene imakokolola zinthu, komanso masoka ena achilengedwe” amene amachitika pafupipafupi m’dzikolo.

CHIKHULUPIRIRO chakuti Mulungu amagwiritsa ntchito masoka achilengedwe polanga anthu oipa n’chakalekale. Mwachitsanzo, mu 1755, anthu pafupifupi 60,000 atafa chifukwa cha chivomezi, moto ndiponso tsunami, zimene zinachitika mumzinda wa Lisbon ku Portugal, katswiri wina wotchuka wa nzeru za anthu, dzina lake Voltaire anafunsa kuti: “Kodi anthu a ku Lisbon ndi ochimwa kwambiri kuposa anthu a ku Paris, kumene kuli kuchimake kwa chisangalalo ndi makhalidwe ena oipa?” Zoonadi, anthu ambirimbiri akhala akudzifunsa ngati Mulungu amagwiritsa ntchito masoka achilengedwe polanga anthu. Ndipo m’mayiko ambiri, anthu amachita kunena kuti Mulungu ndi amene amachititsa masoka ngati amenewa.

Choncho poganizira mfundo zonsezi, m’poyenera kufunsa kuti: Kodi Mulungu wakhala akugwiritsadi ntchito masoka achilengedwe polanga anthu? Kodi masoka ambirimbiri amene akhala akuchitika chaposachedwapa, n’chilango chochokera kwa Mulungu?

Anthu ena amafulumira kuimba Mulungu mlandu kuti amalanga anthu pogwiritsa ntchito masoka achilengedwe. Pofuna kutsimikizira mfundoyi, iwo amatchula nkhani za m’Baibulo zosonyeza kuti Mulungu anagwiritsa ntchito zinthu zachilengedwe powononga anthu. (Genesis 7:17-22; 18:20; 19:24, 25; Numeri 16:31-35) Koma tikaona nkhani za m’Baibulozi mosamala, timaona kuti pa nkhani iliyonse panali mfundo zikuluzikulu zitatu zosiyanitsa nkhanizi ndi masoka achilengedwe. Choyamba, Mulungu asanawononge anthu, ankawachenjeza kaye. Chachiwiri, mosiyana ndi masoka achilengedwe amene akuchitika masiku ano, omwe amapha anthu oipa ndi abwino omwe, Mulungu ankasankha akafuna kuwononga anthu. Iye ankawononga anthu oipitsitsa okha, kapena amene ankakana kumvera machenjezo. Chachitatu, Mulungu ankakonza njira yopulumutsira anthu osalakwa.​—Genesis 7:1, 23; 19:15-17; Numeri 16:23-27.

Koma tikaona masoka achilengedwe ambirimbiri amene apha anthu mamiliyoni ochuluka zedi masiku ano, palibe umboni wosonyeza kuti Mulungu ndi amene amachititsa zimenezi. Nanga n’chifukwa chiyani zikuoneka kuti masoka achilengedwewa akuchuluka kwambiri masiku ano? Kodi tingachite chiyani kuti tisavutike kwambiri ndi masoka achilengedwe? Kodi masoka achilengedwewa adzatha? Mupeza mayankho a mafunso amenewa munkhani zotsatirazi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena