“Nthawi ya Chikondi ndi Nthawi ya Chidani”
“MULUNGU ndiye chikondi.” M’mayiko ena anthu amalemba mawu amenewa n’kuwapachika pakhoma m’nyumba zawo. Mawuwa ndi osangalatsadi chifukwa amasonyeza mmene Mulungu alili. Amasonyeza kuti Mulungu ndi chitsanzo chabwino pa nkhani ya chikondi.
Koma anthu ambiri sadziwa kuti mawu amenewa akuchokera m’Baibulo. Mtumwi Yohane ndi amene analemba mawuwa pamene anati: “Munthu wopanda chikondi sadziwa Mulungu, chifukwa Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yohane 4:8) Yohane analembanso kuti Mulungu amakonda dziko, limene likuimira anthu amene Mulungu akufuna kuwapulumutsa. Iye anati: “Pakuti Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.”—Yohane 3:16.
Poona mfundo imeneyi, ena angaganize kuti nthawi zonse Mulungu amakhala wokonzeka kunyalanyaza chilichonse chimene tingachite. Zimene anthu ambiri amachita pa moyo wawo zimasonyeza kuti iwo amaganiza kuti ngakhale atachita chinthu chilichonse choipa, Mulungu sangawaimbe mlandu. Koma kodi zimenezo n’zoonadi? Kodi Mulungu amakonda aliyense, wabwino ndi woipa yemwe? Kodi pali nthawi imene Mulungu angadane ndi munthu?
Kodi Mulungu Amakonda Chiyani, Nanga Amadana ndi Chiyani?
Solomo, amene anali mfumu yanzeru ananena kuti: “Chilichonse chili ndi nthawi yake, ndipo chilichonse chochitika padziko lapansi chilidi ndi nthawi yake . . . nthawi ya chikondi ndi nthawi ya chidani ndi munthu.” (Mlaliki 3:1, 8) N’zoona kuti Mulungu ndi wachikondi komanso wachifundo, koma mogwirizana ndi mfundo ya palemba limeneli, nthawi zina angadane ndi munthu kapena zinthu zina.
Koma kodi mawu akuti “chidani” m’Baibulo amatanthauza chiyani? Buku lina limayankha kuti: “M’Malemba mawu akuti ‘chidani’ ali ndi matanthauzo ambiri. Angatanthauze kudana kwambiri ndi munthu kapena kuipidwa naye kwambiri mpaka kufika pomuchitira zankhanza. Munthu amene ali ndi chidani choterechi amangokhalira kuganizira zimenezi nthawi zonse, n’kumafunafuna njira yokhaulitsira munthu winayo.” Tanthauzo limeneli ndi lomwe tikulidziwa bwino, ndipo tikuona zotsatira za chidani choterechi padziko lonse. Koma buku lomweli limanenanso kuti: “Mawu akuti ‘chidani’ angatanthauzenso kudana kwambiri ndi chinthu kapena munthu koma osafuna kumupweteka mwanjira iliyonse.”
M’nkhani ino tikukambirana tanthauzo lachiwirili. Chidani chimenechi chikutanthauza kudana kwambiri ndi chinthu kapena munthu, kunyansidwa naye kwambiri, koma popanda kumuganizira zoipa kapena kufuna kumuvulaza. Kodi Mulungu angadane ndi munthu kapena zinthu m’njira yotereyi? Taonani zimene lemba la Miyambo 6:16-19 likunena. Lembali limati: “Pali zinthu 6 zimene Yehova amadana nazo. Zilipo zinthu 7 zimene moyo wake umanyansidwa nazo: Maso odzikweza, lilime lonama, manja okhetsa magazi a anthu osalakwa, mtima wokonzera ena ziwembu, mapazi othamangira kukachita zoipa, mboni yachinyengo yonena mabodza, ndi aliyense woyambitsa mikangano pakati pa abale.”
Monga tikuonera palembali, pali zinthu zina zimene Mulungu amadana nazo. Koma izi sizikutanthauza kuti iye amadana kwenikweni ndi munthu amene wachita zoipazo. Iye amaganizira zinthu zimene zingachititse munthu kuti achite zoipa, monga kupanda ungwiro, malo amene akukhala, mmene anakulira, komanso kusadziwa. (Genesis 8:21; Aroma 5:12) Amene analemba buku la Miyambo anagwiritsa ntchito chitsanzo chabwino pofotokoza mfundo imeneyi. Iye anati: “Yehova amadzudzula munthu amene amam’konda, monga momwe bambo amadzudzulira mwana amene amakondwera naye.” (Miyambo 3:12) Makolo angadane ndi zinthu zoipa zimene mwana wosamvera wachita. Koma makolowo amakondabe mwana wawoyo ndipo angayesetse kumuthandiza pomupatsa chilango kuti asinthe makhalidwe ake oipawo. Chifukwa cha chikondi chake, Yehova nayenso amachita zinthu zofanana ndi zimenezi pothandiza munthu wochimwa amene akuoneka kuti angasinthe.
N’chiyani Chimachititsa Kuti Yehova Afike Podana ndi Munthu?
Koma kodi chingachitike n’chiyani ngati munthu akudziwa zimene Mulungu akufuna, koma sakufuna kuzichita? Mulungu sangakonde munthu wotereyo. Yehova amadana ndi munthu amene amachita mwadala zinthu zimene Yehovayo amadana nazo. Mwachitsanzo, Baibulo limanena kuti: “Yehova amasanthula anthu olungama ndi oipa omwe, ndipo Mulungu amadana kwambiri ndi aliyense wokonda chiwawa.” (Salimo 11:5) Munthu wosalapa ngati ameneyo Mulungu sangamukhululukire. Pa mfundo imeneyi, mtumwi Paulo anafotokoza momveka bwino m’kalata yake yopita kwa Aheberi kuti: “Ngati tikuchita machimo mwadala pambuyo podziwa choonadi molondola, palibe nsembe ina yotsala imene ingaperekedwe chifukwa cha machimo athuwo. Koma pali chiyembekezo china choopsa cha chiweruzo, ndiponso pali nsanje yoyaka moto imene idzawononge otsutsawo.” (Aheberi 10:26, 27) N’chifukwa chiyani Mulungu, yemwe ndi wachikondi, angachite zimenezi?
Munthu akamachita machimo akuluakulu mwadala, machimowo amamulowerera kwambiri moti zimakhala zosatheka kuwasiya. Munthuyo angafike pokhala woipa kwambiri ndipo sangasinthe. Baibulo limayerekezera munthu wotero ndi kambuku amene sangasinthe mawanga ake. (Yeremiya 13:23) Popeza kuti munthuyo sangalape, malinga ndi zimene Baibulo limanena, ndiye kuti akuchita “tchimo losatha” limene silingakhululukidwe.—Maliko 3:29.
Izi n’zimene zinachitikira Adamu ndi Hava komanso Yudasi Isikariyoti. Adamu ndi Hava anali anthu angwiro ndipo lamulo limene Mulungu anawapatsa linali losapita m’mbali komanso lomveka bwino kwa onse. Choncho n’zoonekeratu kuti iwo anachimwa mwadala ndipo analibe chifukwa chomveka chochitira zoipazo. N’chifukwa chake Mulungu sanawapatse mwayi woti alape pamene ankalankhula nawo pambuyo poti achimwa. (Genesis 3:16-24) Ngakhale kuti Yudasi anali wopanda ungwiro, iye ankakhala pafupi kwambiri ndi Mwana weniweni wa Mulungu, komabe anamukonzera chiwembu. Motero Yesu ananena kuti Yudasi ndi “mwana wa chiwonongeko.” (Yohane 17:12) Baibulo limanenanso kuti Mdyerekezi wakhala akuchimwa kwa nthawi yaitali ndipo akungoyembekezera kuwonongedwa. (1 Yohane 3:8; Chivumbulutso 12:12) Choncho Mulungu amadana kwambiri ndi anthu amenewa.
Komabe sikuti munthu aliyense amene wachimwa sangasinthe, ndipo mfundo imeneyi ndi yolimbikitsa kwambiri. Izi zili choncho chifukwa Yehova ndi woleza mtima ndipo sasangalala kupereka chilango kwa anthu amene achimwa chifukwa chosadziwa. (Ezekieli 33:11) Iye akuwapempha kuti alape n’cholinga choti akhululukidwe. Timawerenga kuti: “Munthu woipa asiye njira yake ndipo wopweteka anzake asiye maganizo ake. Iye abwerere kwa Yehova ndipo adzamuchitira chifundo. Abwerere kwa Mulungu wathu, pakuti amakhululuka ndi mtima wonse.”—Yesaya 55:7.
Tiziona Chikondi ndi Chidani M’njira Yoyenerera
Apa n’zoonekeratu kuti Akhristu oona amene amatsanzira Mulungu, ayenera kudziwa “nthawi ya chikondi” komanso “nthawi ya chidani.” Munthu angalephere kumaona chikondi komanso chidani m’njira yoyenera chifukwa chongotengeka maganizo. Koma mawu a mtumwi Yuda angatithandize kuchita zinthu mosanyanyira pa nkhani ya kusonyeza chifundo komanso kudana ndi tchimo. Yuda anati: “Pitirizaninso kuchitira chifundo ena onse, koma ndi mantha. Iwo aipitsa zovala zawo zamkati ndi ntchito za thupi. Choncho pamene mukuwachitira chifundo, mutalikirane kwambiri ndi zovala zawo zoipitsidwazo.” (Yuda 22, 23) Chotero tiyenera kudana ndi zinthu zoipa, koma osati munthu amene wachita zoipazo.
Akhristu akulamulidwanso kuti azisonyeza chikondi kwa adani awo powachitira zinthu zabwino. Pa mfundo imeneyi, Yesu anati: “Koma ine ndikukuuzani kuti: Pitirizani kukonda adani anu ndi kupempherera amene akukuzunzani.” (Mateyu 5:44) N’chifukwa chake mobwerezabwereza, a Mboni za Yehova amalalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu kwa anthu, ngakhale kuti ena salabadira uthenga wawo. (Mateyu 24:14) Mogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo, a Mboni amaona kuti munthu aliyense angathe kusonyezedwa chikondi komanso chifundo ndi Yehova. Ndipo anthu akapanda kuyamikira zimene a Mboniwo akuchita powathandiza kapena akamakana uthenga wawo kapenanso akamawazunza, iwo amatsatira malangizo a mtumwi Paulo akuti: “Pitirizani kudalitsa anthu amene amakuzunzani. Muzidalitsa, osatemberera ayi . . . Musabwezere choipa pa choipa.” (Aroma 12:14, 17) Iwo akudziwa kuti Yehova ndi amene adzaweruze, ndipo iye adzaona woyenera kumusonyeza chikondi kapena woyenera kudana naye. Pa nkhani ya moyo ndi imfa, Yehova ndiye Woweruza wamkulu.—Aheberi 10:30.
Inde, “Mulungu ndiye chikondi.” Choncho ifeyo tiyenera kuyamikira chikondi chakecho ndipo tiziyesetsa kuti tidziwe zimene akufuna n’kumazichita. A Mboni za Yehova kwanuko ndi okonzeka kukuthandizani kuti mudziwe zimene Mulungu akufuna, pogwiritsa ntchito Baibulo lanu. Komanso iwo adzakuthandizani kuona mmene mungagwiritsire ntchito zimene mukuphunzirazo pa moyo wanu. Mukachita zimenezi Mulungu adzakukondani, ndipo mudzapewa kukhala mdani wake.
[Mawu Otsindika patsamba 23]
“Pali zinthu 6 zimene Yehova amadana nazo. Zilipo zinthu 7 zimene moyo wake umanyansidwa nazo: Maso odzikweza, lilime lonama, manja okhetsa magazi a anthu osalakwa, mtima wokonzera ena ziwembu, mapazi othamangira kukachita zoipa, mboni yachinyengo yonena mabodza, ndi aliyense woyambitsa mikangano pakati pa abale.”—MIYAMBO 6:16-19
[Mawu Otsindika patsamba 24]
“Ngati tikuchita machimo mwadala pambuyo podziwa choonadi molondola, palibe nsembe ina yotsala imene ingaperekedwe chifukwa cha machimo athuwo. Koma pali chiyembekezo china choopsa cha chiweruzo.”—AHEBERI 10:26, 27
[Mawu Otsindika patsamba 25]
“Munthu woipa asiye njira yake ndipo wopweteka anzake asiye maganizo ake. Iye abwerere kwa Yehova ndipo adzamuchitira chifundo . . . pakuti amakhululuka ndi mtima wonse.”—YESAYA 55:7
[Chithunzi patsamba 24]
Makolo achikondi amalanga mwana wawo kuti amuthandize
[Chithunzi patsamba 25]
Mulungu wasonyeza chikondi komanso chifundo kwa anthu ambiri amene ali m’ndende