“Moyo Wosatha Adzaupeza”
“Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munamutuma.”—YOHANE 17:3.
KUDZIWA zinthu kungapulumutse moyo. Mwachitsanzo, mwana wina wa ku Niger wa miyezi 10, dzina lake Nouhou atadwala, mayi ake omwe amagwira ntchito zaumoyo anadziwa zoyenera kuchita. Mayiwo anapatsa mwanayo ORS amene anapanga pogwiritsa ntchito madzi aukhondo, shuga ndi mchere. Malinga ndi zimene bungwe la UNICEF linanena, “mwanayo sanachedwe kuchira chifukwa choti mayiyo anamuthandiza mwamsanga pogwiritsa ntchito njira yachipatala imene ankadziwa.”
Kudziwa zimene Baibulo limaphunzitsa kungathandizenso anthu kupulumuka. Mose, yemwe anali munthu woyamba kulemba Baibulo, anati: “Amenewa si mawu opanda pake kwa inu, chifukwa mawu amenewa ndiwo moyo wanu. Mwa kutsatira mawu amenewa mudzatalikitsa masiku anu.” (Deuteronomo 32:47) Kodi Baibulo lingatithandizedi kutalikitsa masiku a moyo wathu? Nanga kodi Baibulo ndi moyo wathu motani?
Nkhani zisanu zapitazi zasonyeza kuti, kuposa buku lina lililose, Baibulo ndi lodalirika pa nkhani ya maulosi, mbiri yakale komanso nkhani zokhudza ukhondo ndi thanzi labwino. Zasonyezanso kuti Baibulo lili ndi malangizo othandiza komanso nkhani zake n’zogwirizana. Zimenezi zikusonyeza kuti Baibulo ndi buku lapadera. Ndiyeno popeza Baibulo likunena kuti lingathandize munthu kukhala ndi moyo wautali kapena kuti wosatha, kodi simukuona kuti muyenera kulidziwa bwino Baibulo?
Tikukulimbikitsani kuti muphunzire Baibulo kuti muone mmene lingakuthandizireni kukhala ndi mtendere wamumtima panopa komanso kudzakhala wosangalala m’tsogolo. A Mboni za Yehova ndi okonzeka kukusonyezani mmene mungaphunzirire Baibulo.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 9]
Baibulo ndi lapaderanso chifukwa ndi lokhalo limene limapereka mayankho ogwira mtima a mafunso ofunika kwambiri monga awa:
• Kodi n’chifukwa chiyani tili ndi moyo?
• Kodi n’chifukwa chiyani padzikoli pali mavuto ochuluka chonchi?
• Kodi tidzaonananso ndi okondedwa athu amene anamwalira?
Mungapeze mayankho a m’Baibulo a mafunso amenewa m’buku ili, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.