Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w12 11/1 tsamba 4-5
  • Funso Loyamba: Kodi Cholinga cha Moyo Wanga N’chiyani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Funso Loyamba: Kodi Cholinga cha Moyo Wanga N’chiyani?
  • Nsanja ya Olonda—2012
  • Nkhani Yofanana
  • Kufunafuna Cholinga Chabwino Pamoyo
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Chifuno Chenicheni cha Moyo
    Galamukani!—1992
  • Kodi Cholinga cha Moyo N’chiyani?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Kodi Cholinga cha Mulungu Ndi Choti Tikhale Ndi Moyo Wotani?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2012
w12 11/1 tsamba 4-5

Funso Loyamba: Kodi Cholinga cha Moyo Wanga N’chiyani?

ROSALIND, yemwe anakulira ku England ankafunitsitsa atadziwa yankho la funso limeneli. Iye ankafunanso kudzagwira ntchito yothandiza anthu. Atamaliza sukulu, anayamba ntchito yapamwamba ndipo ankathandizanso anthu osowa pokhala komanso anthu olumala. Ngakhale kuti iye anali pa ntchito yabwino ndiponso yandalama zambiri, ananena kuti: “Kwa zaka zambiri ndinkadzifunsa kuti, ‘Kodi Mulungu anatilengeranji anthufe? Nanga kodi cholinga cha moyo n’chiyani?’”

N’chifukwa chiyani anthu amafunsa funso limeneli?

Anthufe timasiyana ndi nyama chifukwa timatha kuphunzira kuchokera ku zinthu zakale, kukonza tsogolo lathu komanso kukhala ndi cholinga pa moyo wathu.

Kodi anthu ena amayankha bwanji funsoli?

Anthu ambiri amaganiza kuti cholinga chachikulu pa moyo wawo ndi kupeza chuma komanso kutchuka chifukwa amaona kuti zimenezi zingawapangitse kuti azisangalala.

Kodi mayankho amenewa akusonyeza kuti anthu ambiri ali ndi maganizo otani?

Anthuwa amaona kuti zofuna zawo ndiye zofunika kwambiri. Kwa iwo zofuna za Mulungu si zofunika kwenikweni.

Kodi Baibulo limaphunzitsa chiyani pa nkhaniyi?

Mfumu Solomo inali ndi chuma chambiri komanso inkaona kuti inkasangalala ndi moyo, koma pamapeto pake inaona kuti zinthu zimenezi sizithandiza munthu kukhala ndi chisangalalo chenicheni. Solomo anapeza chimene chingathandize munthu kukhaladi wosangalala ndipo analemba kuti: “Poti zonse zanenedwa, mfundo yaikulu ndi yakuti: Opa Mulungu woona ndi kusunga malamulo ake chifukwa zimenezi ndiye zimene munthu ayenera kuchita.” (Mlaliki 12:13) Kodi tingatani kuti tizisunga malamulo a Mulungu?

Cholinga china cha Mulungu n’choti tizisangalala ndi moyo. Solomo analemba kuti: “Kwa munthu, palibe chabwino kuposa kuti adye, amwe, ndi kusangalatsa mtima wake chifukwa choti wagwira ntchito mwakhama. Ineyo ndaona kuti zimenezinso n’zochokera m’dzanja la Mulungu woona.”—Mlaliki 2:24.

Mulungu amafunanso kuti tizikonda anthu a m’banja lathu ndiponso kuwasamalira. Taonani malangizo osavuta kuwatsatira komanso othandiza awa, opita kwa amuna, akazi komanso ana.

  • “Amuna akonde akazi awo monga matupi awo.”—Aefeso 5:28.

  • “Mkazi azilemekeza kwambiri mwamuna wake.”—Aefeso 5:33.

  • “Ananu, muzimvera makolo anu.”—Aefeso 6:1.

Ngati titatsatira mfundo za m’Baibulo zimenezi, tidzakhala ndi moyo wosangalala komanso waphindu. Komabe chinthu chofunika kwambiri chimene tiyenera kuchita ndi kuphunzira za Mlengi wathu komanso kukhala naye pa ubwenzi. Ndipotu Baibulo limatilimbikitsa kuti ‘tiyandikire Mulungu.’ Limatiuzanso kuti ‘iyenso adzatiyandikira.’ (Yakobo 4:8) Ngati mutachita zimene lembali likunena, mudzakhala wosangalala komanso moyo wanu udzakhala waphindu.

Rosalind, yemwe tamutchula poyamba uja, tsopano akuona kuti anapeza cholinga cha moyo. Patsamba 10 m’magazini ino, mungawerenge zimene zinachititsa kuti asinthe maganizo amene anali nawo poyamba.

Kuti mudziwe zambiri zimene mungachite kuti muzisangalatsa Mulungu, werengani mutu 12 m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Mungathenso kukopera bukuli pa Webusaiti yathu iyi: www.jw.org.

Zimene Yesu Ananena Zokhudza Cholinga cha Moyo

Yesu ankadziwa bwino cholinga cha moyo wake. Iye ananena kuti: “Chimene ndinabadwira, ndiponso chimene ndinabwerera m’dziko, ndicho kudzachitira umboni choonadi.” (Yohane 18:37) Nthawi zambiri Yesu ankaphunzitsa anthu choonadi komanso zolinga za Mulungu.

Moyo wathu ungakhale waphindu ngati tingatengere chitsanzo cha Yesu. Ndipotu n’chifukwa chake Yesu akutiuza kuti tiphunzire kuchokera kwa iye. (Mateyu 11:29) Taonani njira ziwiri zimene tingatsanzirire Yesu.

Yesu anaphunzitsa kuti, kuti tikhale osangalala tiyenera ‘kuzindikira zosowa zathu zauzimu.’ (Mateyu 5:3) Tingapeze zosowa zathu zauzimu, tikamaphunzira za “Mulungu yekhayo amene ali woona, ndi za Yesu Khristu,” amene iye anamutuma.—Yohane 17:3.

Yesu analamula otsatira ake kuti aziphunzitsa ena zimene aphunzira. Iye anati: “Choncho pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga. Muziwabatiza m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyera, ndi kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulirani.”—Mateyu 28:19, 20.

Anthu amene amapeza zosowa zawo zauzimu pophunzira Baibulo ndi kutsatira zimene aphunzirazo, amayamba kukhala ndi moyo wosangalala. Ndipo akayamba kuthandiza ena kuphunzira za Mulungu, amakhulupirira ndi mtima wonse kuti moyo wawo uli ndi cholinga.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena