Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w13 10/1 tsamba 3
  • N’chifukwa Chiyani Mukufunika Kulidziwa Bwino Baibulo?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • N’chifukwa Chiyani Mukufunika Kulidziwa Bwino Baibulo?
  • Nsanja ya Olonda—2013
  • Nkhani Yofanana
  • N’chifukwa Chiyani Muyenera Kuphunzira Baibulo?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Baibulo Ndi Buku Lomveka Bwino
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Kodi Baibulo Nlochokeradi kwa Mulungu?
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Ziphunzitso Zoona Zimene Zimakondweretsa Mulungu
    Nsanja ya Olonda—2005
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2013
w13 10/1 tsamba 3

NKHANI YA PACHIKUTO | KODI BAIBULO LILI NDI UTHENGA WOTANI?

N’chifukwa Chiyani Mukufunika Kulidziwa Bwino Baibulo?

Baibulo ndi buku lotchuka kwambiri kuposa buku lina lililonse. Chinthu chimodzi chimene chimachititsa kuti Baibulo likhale lotchuka ndi chakuti limanena zinthu zimene ifenso zimatichitikira. Limafotokoza nkhani zokhudza anthu enieni ndiponso zimene ankachita ndi anthu anzawo komanso ndi Mulungu. Nkhani zimenezi zimatiphunzitsa mfundo zothandiza pogwiritsa ntchito mawu osavuta kumva, omwe angathe kumasuliridwa m’zinenero zambirimbiri ndipo mtundu uliwonse wa anthu ukhoza kuzimvetsa. Komanso malamulo a m’Baibulo ndi othandiza nthawi zonse.

Mfundo yofunika kwambiri ndi yakuti, Baibulo silimangonena zokhudza Mulungu koma limanenanso kuti linachokera kwa Mulungu. Limatithandiza kudziwa dzina la Mulungu, makhalidwe ake komanso cholinga chake cholengera anthu ndiponso dziko lapansi. Cholinga chimenechi sichinasinthe ndipo sichidzasintha. Baibulo limanenanso za nkhani yakale kwambiri yomvetsa chisoni yomwe inachitika m’munda wa Edeni. Nkhani imeneyi imakhudza dziko lonse lapansi ndipo mapeto ake adzakhala osangalatsa. Choncho kuwerenga Baibulo ndi maganizo oti tidziwe zoona zenizeni kungatithandize kukhala ndi chikhulupiriro komanso chiyembekezo.

Baibulo limatiuza mfundo zothandiza zomwe sitingazipeze kwina kulikonse. Mwachitsanzo, limatiuza zoona pa nkhani zotsatirazi:

  • Zimene zinachitika kuti tizikumana ndi mavuto

  • Zimene Mulungu anachita kuti apulumutse anthu

  • Zimene Yesu watichitira

  • Tsogolo la anthu komanso dziko lapansi

Mungachite bwino kuwerenga nkhani zotsatirazi kuti mudziwe uthenga umene uli m’Baibulo.

MFUNDO ZACHIDULE ZOKHUDZA BAIBULO

  • Mfundo Yaikulu ya Baibulo Lonse: Mmene Ufumu wakumwamba wa Mulungu udzabwezeretsere chilungamo ndi mtendere padziko lapansi

  • Mabuku Amene Ali M’Baibulo: Mabuku 39 analembedwa m’Chiheberi (ena analembedwa m’Chiaramu) ndipo mabuku 27 analembedwa m’Chigiriki

  • Olemba: Linalembedwa ndi anthu 40 ndipo linatenga zaka 1,600 likulembedwa. Linayamba kulembedwa mu 1513 B.C.E. mpaka cha m’ma 98 C.E.

  • Zinenero: Panopa lamasuliridwa lonse kapena mbali imodzi chabe m’zinenero zoposa 2,500

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena