Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w14 6/1 tsamba 16
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Nsanja ya Olonda—2014
  • Nkhani Yofanana
  • Mulungu Akulonjeza Kuti Dzikoli Lidzakhalanso Bwino
    Galamukani!—2023
  • Mphatso Yosatha Yochokera kwa Mlengi
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Pulaneti Lokhala ndi Zamoyo
    Kodi Zamoyo Zinachita Kulengedwa?
  • Zimene Zili M’magaziniyi
    Galamukani!—2023
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2014
w14 6/1 tsamba 16

KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO

Kodi pali chifukwa chilichonse chimene Mulungu analengera dziko lapansili?

Nyamata akuganizira za zinthu zachilengedwe

Mulungu analenga dzikoli kuti anthu azikhalamo mosangalala

Dziko lapansili linalengedwa m’njira yoti pazikhala zinthu zamoyo. Lili ndi madzi ambiri amene amathandiza kuti zamoyo zisamafe. Komanso mmene dzikoli limayendera, zimathandiza kuti madzi a m’nyanja zonse asamaundane chifukwa cha kuzizira kapena kuwira chifukwa cha kutentha. M’mlengalenga mwa dzikoli mulinso mpweya wosiyanasiyana umene umaliteteza. Palinso mphamvu inayake imene imachokera pansi pa nthaka yomwe imateteza dzikoli. Chinthu chinanso chogometsa kwambiri ndi kudalirana kumene kulipo pakati pa zomera, nyama komanso anthu padzikoli. Poganizira zinthu zonsezi, anthu ambiri amaona kuti Mulungu analenga dzikoli ndi cholinga.—Werengani Yesaya 45:18.

Koma mwina mungadzifunse kuti, ‘Kodi ndiye kuti zinthu zopanda chilungamo zimene zimachitika komanso mavuto ena onse, ndi mbali ya cholinga cha Mulungucho?’—Werengani Deuteronomo 32:4, 5.

Kodi Mulungu adzakwaniritsa cholinga chakechi?

Mulungu analenga dzikoli kuti anthu azikhalamo mosangalala, azikondana komanso azikonda Mlengi wawo. Choncho anthu ndi osiyana kwambiri ndi nyama komanso zomera. Anthufe tingathe kuphunzira zokhudza Mlengi wathu ndipo tingathe kutsanzira makhalidwe ake monga chikondi ndi chilungamo.—Werengani Mlaliki 12:13; Mika 6:8.

Mlengi wathu angathe kukwaniritsa zolinga zake zonse. Choncho tingakhale ndi chikhulupiriro choti adzathetsa mavuto onse padzikoli, ndipo anthu adzakhala angwiro ndiponso osangalala.—Werengani Salimo 37:11, 29; Yesaya 55:11.

Kuti mudziwe zambiri werengani mutu 3 m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova

Bukuli likupezekanso pa webusaiti yathu ya www.jw.org

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena