Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w14 6/15 tsamba 3-6
  • “Salaza Njira ya Phazi Lako” Kuti Uyende Bwino

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Salaza Njira ya Phazi Lako” Kuti Uyende Bwino
  • Nsanja ya Olonda—2014
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • KONZANI NJIRA POSANKHA BWINO ZOCHITA
  • CHOTSANI CHOPINGA CHILICHONSE
  • MUSAPATUKE PANJIRA YOKUTHANDIZANI
  • Achinyamata, Kodi Mukuyesetsa Kukwaniritsa Zolinga Zauzimu?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
  • N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuwerenga Baibulo?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Achinyamata, Kumbukirani Mlengi Wanu Wamkulu
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Khalani ndi Zolinga Zauzimu Kuti Mulemekeze Nazo Mlengi Wanu
    Nsanja ya Olonda—2004
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2014
w14 6/15 tsamba 3-6
Msewu wokhala ndi zopinga zambiri

“Salaza Njira ya Phazi Lako” Kuti Uyende Bwino

PAMENE anthu a Mulungu ankachoka ku Babulo mu 537 B.C.E., Yehova anawauza kuti akonze bwino njira yawo yopita ku Yerusalemu. Iye anati: “Lambulani njira yodutsa anthu. Konzani msewu. Ukonzeni ndithu. Chotsanimo miyala.” (Yes. 62:10) Mwina Ayuda ena anatsogola kuti akalambule njira ndi kukwirira maenje. Zimenezi zikanathandiza abale awo kuti ayende bwinobwino popita kwawo.

Munthu amafunika kuchita zinthu ngati zimenezi kuti akwaniritse zolinga zake potumikira Yehova. Yehova amafuna kuti tizimutumikira popanda chopinga chilichonse. Mawu ake amatilimbikitsa kuti: “Salaza njira ya phazi lako, ndipo njira zako zonse zikhazikike.” (Miy. 4:26) Kaya ndinu achinyamata kapena achikulire, malangizo amenewa akhoza kukuthandizani.

KONZANI NJIRA POSANKHA BWINO ZOCHITA

Ponena za achinyamata, anthu amakonda kunena kuti, ‘Amene ujatu adzafika patali’ kapena amati, ‘Amene uja ali ndi tsogolo lowala.’ Achinyamata amakhala athanzi, amaganiza mwamsanga ndipo amayesetsa kuti zinthu ziwayendere bwino. M’pake kuti Baibulo limati: “Kukongola kwa anyamata ndiko mphamvu zawo.” (Miy. 20:29) Wachinyamata amene amagwiritsa ntchito luso ndi mphamvu zake potumikira Yehova akhoza kukwaniritsa zolinga zake n’kukhala wosangalala kwambiri.

Anthu m’dzikoli amachitanso chidwi ndi achinyamata ndipo amafuna kuti achite zambiri. Ngati wachinyamata wa Mboni amakhoza bwino kusukulu anthu ena monga aphunzitsi kapena anzake angamuuze kuti apitirize maphunziro n’cholinga choti zinthu zimuyendere bwino m’dzikoli. Achinyamata ena amene ali ndi luso pa masewera enaake amauzidwanso kuti alimbikire kuti adzakhale akatswiri. Kodi zimenezi zakuchitikirani inuyo kapena mnzanu? N’chiyani chingathandize Mkhristu kuti asankhe mwanzeru pa nkhaniyi?

Mfundo za m’Baibulo zingathandize munthu kuti akonze bwino njira yake. Lemba la Mlaliki 12:1 limanena kuti: “Kumbukira Mlengi wako Wamkulu masiku a unyamata wako.” Kodi inuyo kapena mnzanuyo ‘mungakumbukire bwanji Mlengi wanu wamkulu’?

Taganizirani zimene zinachitikira Erica wa ku West Africa. Iye ankakonda kwambiri mpira. Pamene ankakwanitsa zaka 15, anasankhidwa kuti azisewera mu timu ya dziko lake. Apatu mwayi unamutsegukira woti akaphunzire mpirawo m’mayiko a ku Ulaya n’kufika pokhala katswiri. Ndiyeno kodi malangizo oti ‘ukumbukire mlengi wako wamkulu’ anamuthandiza bwanji? Nanga inuyo kapena mnzanuyo mungaphunzire chiyani pa nkhaniyi?

Eric ali pa sukulu anayamba kuphunzira ndi Mboni za Yehova. Anaphunzira kuti Mlengi wake adzathetsa mavuto onse padzikoli. Iye anazindikira kuti ayenera kugwiritsa ntchito nthawi yake komanso mphamvu zake potumikira Mulungu. Izi zinamuchititsa kuti asiye zoyesetsa kukhala katswiri wa mpira. Iye anabatizidwa n’kuyamba kuchita zambiri potumikira Mulungu. Kenako anadzakhala mtumiki wothandiza ndipo anapita ku Sukulu Yophunzitsa Baibulo ya Abale Osakwatira.

Eric akanapitiriza mpira uja mwina akanatchuka komanso kulemera. Koma iye anazindikira mfundo ya m’Malemba yakuti: “Zinthu zamtengo wapatali za munthu wachuma ndizo mzinda wake wolimba, ndipo m’maganizo mwake zili ngati mpanda woteteza.” (Miy. 18:11) Anthu amaganiza kuti chuma chingawateteze koma si zoona. Ndipo amene amangokhalira kusakasaka chuma ‘amadzibweretsera zopweteka zambiri pathupi lawo.’—1 Tim. 6:9, 10.

Chosangalatsa n’chakuti achinyamata ambiri ayamba utumiki wa nthawi zonse ndipo akusangalala komanso ndi otetezeka. Eric anati: “Panopa ndinganene kuti ndalowa timu ya atumiki a nthawi zonse. Timu imeneyi ndi yabwino kwambiri ndipo ndikuyamikira Yehova chifukwa chondithandiza kuti ndikhale ndi moyo wabwino komanso wosangalatsa.”

Nanga bwanji inuyo? M’malo moyesetsa kuti mukhale ochita bwino m’dzikoli, muyenera ‘kukhazikitsa njira yanu’ potumikira Yehova. Mungachite zimenezi poyamba upainiya.—Onani bokosi lakuti “Zinthu Zabwino Zimene Simungazipeze ku Yunivesite.”

CHOTSANI CHOPINGA CHILICHONSE

Mlongo wina ndi mwamuna wake anapita kukaona ofesi ya nthambi ya ku United States ndipo anaona kuti anthu otumikira kumeneko ndi osangalala kwambiri. Mlongoyu analemba kuti: “Tinali titazolowera kwambiri zimene tinkachita pa moyo wathu.” Koma banjali linasankha kuti lisinthe zinthu zina ndi zina kuti liyambe kuchita zambiri mu utumiki.

Poyamba, iwo anaona kuti mwina sangakwanitse kuchita zimenezi. Koma tsiku lina atachita lemba la tsiku anaganizira kwambiri mfundo yake. Lembalo linali pa Yohane 8:31 pamene Yesu anati: “Mukamasunga mawu anga nthawi zonse, ndiye kuti ndinudi ophunzira anga.” Choncho malinga ndi lembali anaona kuti angachite bwino kwambiri kusintha zinthu kuti ayambe kukhala moyo wosalira zambiri. Ndiyeno anagulitsa nyumba yawo yaikulu komanso kusintha zinthu zina kuti asamukire kumpingo umene unalibe ofalitsa ambiri. Panopa iwo akuchita upainiya, amathandiza nawo pomanga Nyumba za Ufumu ndiponso amadzipereka kuthandiza pa misonkhano yachigawo. Kodi iwo amamva bwanji ndi zomwe anachitazi? Iwo anati: “Tikusangalala kwambiri chifukwa chokhala moyo wosalira zambiri ndiponso kutsatira malangizo a gulu la Yehova.”

MUSAPATUKE PANJIRA YOKUTHANDIZANI

Solomo analemba kuti: “Maso ako aziyang’ana patsogolo. Maso ako owala aziyang’anitsitsa patsogolo pako.” (Miy. 4:25) Munthu amene akuyendetsa galimoto amayang’ana kutsogolo kuti asachite ngozi. Kuti ifenso tikwaniritse zolinga zathu potumikira Yehova tiyenera kuyang’ana kutsogolo, osatengeka ndi zilizonse.

1. A Mboni za Yehova akukwaniritsa zolinga zawo ali achinyamata; 2. Achotsa zopinga mumsewu

Kodi mungakhale ndi zolinga ziti? Mwina mungayesetse kuti muyambe utumiki wa nthawi zonse. Apo ayi, mungapite kukathandiza kumpingo umene ulibe ofalitsa okwanira. Mwinanso mungasamukire mumpingo umene ulibe akulu ndi atumiki othandiza okwanira. Mungakambirane ndi woyang’anira dera kuti akuuzeni zimene mungachite. Ngati mukufuna kupita kugawo lakutali, mungachite bwino kufufuza kuti mudziwe kumene kukufunika thandizo.b

Tiyeni tikambiranenso mfundo ya pa Yesaya 62:10 ija. Ayuda ena ayenera kuti anagwira chintchito cholambula njira yopita kwawo kuti anthu a Mulungu ayende bwino. Ngati mukuyesetsa kukwaniritsa zolinga zinazake potumikira Yehova musabwerere m’mbuyo. Yehova akuthandizani kuti zolinga zanuzo zitheke. Pitirizani kupempha nzeru kwa Yehova kuti muchotse chopinga chilichonse. Mudzaona iye akukuthandizani ‘kusalaza njira ya mapazi anu.’—Miy. 4:26.

a Dzina lasinthidwa.

b Onani buku la Gulu Lochita Chifuniro cha Yehova, tsamba 111 ndi 112.

Zinthu Zabwino Zimene Simungazipeze ku Yunivesite

Flavia

PAMENE mlongo wina dzina lake Flavia anali mtsikana, agogo ake omwe anali a Mboni za Yehova anamuphunzitsa za Baibulo. Koma bambo ake anali mphunzitsi ndipo ankamulimbikitsa kuti aphunzire kwambiri za sayansi. Anthu ena ankamuuza kuti, “Achinyamatanu mukhoza kuteteza chilengedwe kuti dzikoli lisawonongeke.” Choncho bambo ake anamuthandiza kuti apite kuyunivesite inayake yapamwamba kumene anayamba kufufuza njira zopangira mafuta osawononga chilengedwe.

Koma pasanapite nthawi, Flavia anazindikira kuti ophunzira ambiri kumeneko analibe chidwi choteteza chilengedwe. Ndalama za kafukufuku wina wa ku yunivesiteyo zinkachokera ku makampani ena. Choncho nthawi zina anthu ankachita kafukufukuyo m’njira yokomera makampaniwo. Flavia sankasangalala ndi zimenezi. A Mboni za Yehova atabwera kudzamulalikira iye anachita chidwi ndi zimene Baibulo limanena pa nkhani ya Mulungu ndiponso tsogolo la dzikoli.

Flavia anaphunzira Baibulo ndipo anadzabatizidwa. Koma analibe nthawi yambiri yoti alalikire chifukwa anali kuphunzira kuti apeze digiri ina. Tsiku lina, anamvetsera nkhani ya woyang’anira dera imene inali yokhudza lemba la Yakobo 4:17 lomwe limati: “Ngati munthu akudziwa kuchita chabwino koma sakuchichita, akuchimwa.” Nkhaniyi inathandiza Flavia kuganizira kwambiri za moyo wake. Iye anati: “Ndinkafunitsitsa kuti Yehova andidalitse koma ndinkafunanso kupitiriza zasayansi zija. Choncho ndinafunika kusankha zochita.”

Flavia anasankha zosiya maphunziro ake kuyunivesite. Koma kodi ananong’oneza bondo? Iye anati:

“Ndapeza zinthu zabwino kwambiri potumikira Yehova zimene munthu sangazipeze kuyunivesite. Yehova wandidalitsa kwambiri. Wandiphunzitsa kukhala munthu wokoma mtima, wachikondi ndiponso kuti ndizithandiza anthu ena kukonda Mulungu. Ndili ndi mwamuna wabwino komanso tsogolo labwino kwambiri lomwe sindikanalipeza pophunzira zasayansi. Ndazindikira kuti Yehova yekha ndi amene angateteze dzikoli. Sindidzasiya kumutumikira mpaka kalekale.” Flavia ndi mwamuna wake amatumikira kulikulu la Mboni za Yehova ku New York.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena