Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wp16 No. 2 tsamba 16
  • Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Baibulo Limanena Zotani?
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2016
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mdyerekezi ndi ndani?
  • Kodi Mdyerekezi angalamulire zochita za anthu?
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
    Nsanja ya Olonda—2013
  • “Tsutsani Mdyerekezi” Monga Anachitira Yesu
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Mdyerekezi Alipo Si Nthano Chabe
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Kanizani Satana, Ndipo Iye Adzathawa!
    Nsanja ya Olonda—2006
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2016
wp16 No. 2 tsamba 16
Yesu akukana mayesero a Satana

Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Kodi Mdyerekezi ndi ndani?

KODI MUNGAYANKHE KUTI Mdyerekezi ndi . . .

  • Mngelo?

  • Maganizo oipa a mumtima mwa munthu?

  • Munthu wongoyerekezera?

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Nthawi ina Mdyerekezi analankhulapo ndi Yesu ndipo ‘anamuyesa.’ (Mateyu 4:1-4) Choncho Mdyerekezi si munthu wongoyerekezera kapenanso maganizo oipa amene amakhala mumtima mwa munthu. Iye ndi mngelo woipa.

MFUNDO ZINANSO ZOMWE TIKUPHUNZIRA M’BAIBULO

  • Poyamba Mdyerekezi anali mngelo wabwinobwino koma kungoti “sanakhazikike m’choonadi.” (Yohane 8:44) Kenako anakhala wabodza ndiponso anaukira Mulungu.

  • Angelo enanso anakhala kumbali ya Satana poukira Mulungu.​—Chivumbulutso 12:9.

  • Mdyerekezi amachititsa anthu ambiri kuganiza kuti iye kulibeko.​—2 Akorinto 4:4.

Kodi Mdyerekezi angalamulire zochita za anthu?

ANTHU ENA AMAKHULUPIRIRA kuti n’zosatheka kulamuliridwa ndi Mdyerekezi, pomwe ena amachita mantha kwambiri kuti akhoza kugwidwa ndi mizimu yoipa. Kodi inuyo mukuganiza bwanji?

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

“Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Mdyerekezi amalamulira kwambiri zochita za anthu, koma sikuti amalamulira zochita za munthu aliyense.

MFUNDO ZINANSO ZOMWE TIKUPHUNZIRA M’BAIBULO

  • Mdyerekezi amagwiritsa ntchito chinyengo pofuna kupusitsa anthu.​—2 Akorinto 11:14.

  • Nthawi zina mizimu yoipa ikhoza kulamulira zochita za anthu.​—Mateyu 12:22.

  • Mulungu angakuthandizeni ‘kutsutsa Mdyerekezi.’​—Yakobo 4:7.

Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 10 m’buku ili, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?, lofalitsidwa ndi a Mboni za Yehova

Bukuli likupezekanso pawebusaiti yathu ya www.jw.org/ny

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena