Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w16 April tsamba 32
  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Zidindo Zakale Zinkagwira Ntchito Yanji?
    Nkhani Zina
  • ‘Mzimu Umachitira Umboni’
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2020
  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Mzimu Umachitira Umboni Limodzi ndi Mzimu Wathu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
w16 April tsamba 32

MAFUNSO OCHOKERA KWA OWERENGA

Kodi odzozedwa amalandira bwanji “chikole” nanga amadindidwa bwanji “chidindo”?—2 Akor. 1:21, 22.

Munthu akudinda chidindo padongo kuti aike pa kalata

Kale anthu ankadinda chidindo pachinthu potsimikizira kuti ndi chenicheni

Chikole: Buku lina limanena kuti mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “chikole” pa 2 Akorinto 1:22, “ankawagwiritsa ntchito pa zinthu zokhudza malamulo komanso malonda.” Mawuwa amatanthauza “ndalama zochepa zimene munthu amapereka choyamba, pogula chinthu. Ndalamazi zimatsimikizira kuti mwagwirizanadi kuti mudzagulitsana chinthucho ndipo malipiro onse adzaperekedwa.” Mkhristu akadzozedwa amakhala kuti walandira chikole, koma malipiro onse amene adzalandire afotokozedwa pa 2 Akorinto 5:1-5. Odzozedwa adzapita kumwamba ndipo adzakhala ndi moyo wosafa.—1 Akor. 15:48-54.

M’Chigiriki cha masiku ano, mawu ofanana ndi akuti chikole amawagwiritsanso ntchito ponena za mphete ya ukwati. Zimenezi n’zomveka tikaganizira mfundo yoti odzozedwa adzakhala ngati mkazi wa Khristu.—2 Akor. 11:2; Chiv. 21:2, 9.

Chidindo: Kale chidindo ankachigwiritsa ntchito ngati siginecha posonyeza mwini wa chinthu, potsimikizira kuti chinthucho n’chenicheni komanso posonyeza kuti anthu anagwirizana zinazake. Tingati Akhristu odzozedwa ‘anadindidwa’ ndi mzimu woyera posonyeza kuti ndi a Mulungu. (Aef. 1:13, 14) Komabe kutsimikizira kwenikweni kumachitika Mkhristu wodzozedwa akatsala pang’ono kumwalira ali wokhulupirika kapena kudzachitika chisautso chachikulu chitatsala pang’ono kuyamba.—Aef. 4:30; Chiv. 7:2-4.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena