Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wp16 No. 5 tsamba 16
  • Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2016
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?
  • Kodi Ufumu wa Mulungu udzabwera liti?
  • Ufumu wa Mulungu
    Galamukani!—2013
  • Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2020
  • Kodi Pali Boma Lodalirika Limene Lingalamulire Dzikoli?—Kodi Baibulo Limanena Zotani?
    Nkhani Zina
  • Choonadi Chonena za Ufumu wa Mulungu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2020
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2016
wp16 No. 5 tsamba 16
Kuwala kukuchokera kumpando wachifumu kumwamba

Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?

ANTHU ENA AMAKHULUPIRIRA kuti Ufumuwu umangoimira zimene zimachitika munthu akalola kuti Mulungu azilamulira mumtima mwake, pomwe ena amaganiza kuti ukuimira zimene anthu adzachite pokhazikitsa mtendere komanso mgwirizano padzikoli. Kodi inuyo mukuganiza bwanji?

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

“Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu umene sudzawonongedwa ku nthawi zonse. . . . Udzaphwanya ndi kuthetsa maufumu ena onsewo [a anthu].” (Danieli 2:44) Choncho Ufumu wa Mulungu ndi boma lenileni.

MFUNDO ZINANSO ZOMWE TIKUPHUNZIRA M’BAIBULO

  • Ufumu wa Mulungu umalamulira kuchokera kumwamba.—Mateyu 10:7; Luka 10:9.

  • Mulungu amagwiritsa ntchito Ufumu umenewu pokwaniritsa chifuniro chake chokhudza kumwamba ndi padziko lapansi.—Mateyu 6:10.

Kodi Ufumu wa Mulungu udzabwera liti?

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Palibe akudziwa

  • Posachedwapa

  • Sudzabwera

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

“Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.” (Mateyu 24:14) Uthenga wabwino ukadzalalikidwa mokwanira padziko lonse, Ufumuwu udzabwera kuti udzachotse zinthu zonse zoipa padzikoli.

MFUNDO ZINANSO ZOMWE TIKUPHUNZIRA M’BAIBULO

  • Padzikoli palibe amene akudziwa nthawi imene Ufumu wa Mulungu udzabwere.—Mateyu 24:36.

  • Maulosi a m’Baibulo amasonyeza kuti Ufumu wa Mulungu watsala pang’ono kubwera.—Mateyu 24:3, 7, 12.

Nditumizireni buku lakuti, Zimene Baibulo Limaphunzitsa.

Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 8 m’buku ili, Zimene Baibulo Limaphunzitsa lofalitsidwa ndi a Mboni za Yehova

Bukuli likupezekanso pawebusaiti yathu ya www.jw.org/ny

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena