Mawu Oyamba
KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI?
Ambiri amadziwa ulosi wonena za anthu 4 okwera pamahatchi wopezeka m’buku la Chivumbulutso. Ena amachita mantha akawerenga ulosiwu, pomwe ena umawasangalatsa. Taonani zimene Baibulo limanena zokhudza ulosiwu:
“Wodala ndi munthu amene amawerengera ena mokweza, ndiponso anthu amene akumva mawu a ulosi umenewu.”—Chivumbulutso 1:3.
Nsanja ya Olonda iyi ikufotokoza kuti ulosi umenewu ndi nkhani yosangalatsa kwa anthufe.